NKHANI YOPHUNZILA 24
NYIMBO 98 Malemba ni Ouzilidwa na Mulungu
Maphunzilo Omwe Tikutengapo pa Malailano a Yakobo Olosela Zam’tsogolo—Mbali 1
“Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzacitike kwa inu mʼtsogolo.”—GEN. 49:1.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Maphunzilo othandiza amene tingatengepo pa mawu othela amene Yakobo anauza Rubeni, Simiyoni, Levi, ndi Yuda.
1-2. Kodi Yakobo anacita ciyani atatsala pang’ono kumwalila? Nanga n’cifukwa ciyani? (Onaninso cithunzi .)
ZAKA 17 zapitapo kucokela pamene mtumiki wa Yehova wokhulupilika Yakobo anacoka ku Kanani kupita ku Iguputo ndi banja lake. (Gen. 47:28) Pa nthawi yonseyi, iye wakhala ndi cimwemwe cacikulu poonananso ndi mwana wake wokondeka Yosefe, ndi kuona banja lake lonse litakhalanso pamodzi. Koma tsopano, Yakobo wazindikila kuti moyo wake uli kumapeto. Conco akuitanitsa msonkhano wa banja wofunika kwambili.—Gen. 49:28.
2 M’masiku amenewo zinali zofala mutu wa banja amene watsala pang’ono kumwalila kusonkhanitsa anthu onse a m’banja lake kuti awapatse malangizo othela. (Yes. 38:1) Pa msonkhano umenewo, iye anali kusankhanso munthu amene adzakhala mutu wa banja iye akamwalila.
Yakobo akufotokoza ulosi kwa ana ake aamuna 12 pomwe ali pa bedi lomwe anafela. (Onani ndime 1-2)
3. Malinga ndi Genesis 49:1, 2, n’cifukwa ciyani mawu a Yakobo ndi apadela?
3 Welengani Genesis 49:1, 2. Koma msonkhano umene Yakobo anaitanitsa sunali msonkhano wamba. Unali wapadela. Yakobo anali mneneli. Pa msonkhanowu, Yehova anauzila mtumiki wakeyu kunena za zinthu zofunika za m’tsogolo zimene zinali kudzacitikila mbadwa zake. Pa cifukwa cimeneci, mawu amene Yakobo anauza ana ake atatsala pang’ono kumwalila anali ulosi.
4. Kodi tiyenela kuganizila ciyani pamene tikusanthula mawu othela a Yakobo? (Onaninso bokosi lakuti “Banja la Yakobo.”)
4 M’nkhani ino, tikambilana mawu amene Yakobo ananena kwa ana ake anayi oyambilila: Rubeni, Simiyoni, Levi, ndi Yuda. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zimene Yakobo ananena kwa ana ake ena 8. Monga tionele, mawu a Yakobo sanangokhudza ana ake okha, koma anakhudzanso mbadwa zawo, zimene m’kupita kwa nthawi zinakhala mtundu wa Isiraeli. Kukambilana zimene zinacitikila mtundu wa Isiraeli kumbuyoku, kudzationetsa mmene mawu a Yakobo anakwanilitsidwila. Ndipo tikawasanthula mawu akewo tidzatengapo maphunzilo amene angatithandize kukondweletsa Atate wathu wakumwamba, Yehova.
RUBENI
5. Kodi Rubeni ayenela kuti anali kuyembekezela kulandila ciyani kwa atate ake?
5 Yakobo anayamba mwa kuuza Rubeni kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga woyamba kubadwa.” (Gen. 49:3) Pokhala woyamba kubadwa, n’kutheka kuti Rubeni anali kuyembekezela kulandila magawo awili a cuma ca atate ake. Ayenela kuti anali kuyembekezelanso kukhala mutu wa banjalo atate ake akadzamwalila, komanso kuti mbadwa zake zidzapitiliza kutsogolela banjalo.
6. N’cifukwa ciyani Rubeni sanapatsidwe gawo lake monga mwana woyamba kubadwa? (Genesis 49:3, 4)
6 Komabe, Rubeni sanapatsidwe gawo limene anayenela kulandila monga woyamba kubadwa. (1 Mbiri 5:1) N’cifukwa ciyani? Zaka zingapo m’mbuyomo, iye anagona ndi Biliha, mkazi wamng’ono wa Yakobo. Biliha anali kapolo wa Rakele. Ndipo Rakele anali mkazi wokondeka wa Yakobo amene anali atamwalila. (Gen. 35:19, 22) Rubeni anali mwana wa Leya, mkazi wina wa Yakobo. N’kutheka kuti Rubeni anakopeka ndi Biliha ndipo sanadziletse, moti anagona naye. N’kuthekanso kuti anagona naye pofuna kuti Yakobo anyansidwe naye Biliha kuti asatenge malo a Leya. Mulimonsemo, zimene anacita zinakhumudwitsa kwambili Yehova ndi atate ake.—Welengani Genesis 49:3, 4.
7. N’ciyani cinacitikila Rubeni ndi mbadwa zake? (Onaninso bokosi lakuti “Malailano Olosela a Yakobo.”)
7 Yakobo anauza Rubeni kuti: “Sudzakhala wapamwamba kuposa abale ako.” Mawuwa anakwanilitsika. Tikutelo cifukwa cakuti Baibo siikambapo kuti pali aliyense wa fuko la Rubeni amene anakhalapo mfumu, wansembe, kapena mneneli mu Isiraeli. Ngakhale n’telo, Yakobo sanamukane mwana wake, ndipo mbadwa za Rubeni zinakhala umodzi mwa mafuko a Isiraeli. (Yos. 12:6) Pa zocitika zina, Rubeni anaonetsa makhalidwe abwino, ndipo mbili ionetsa kuti sanacitenso ciwelewele.—Gen. 37:20-22; 42:37.
8. Tiphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Rubeni?
8 Kodi tiphunzilapo ciyani? Tiyenela kucita khama kuti tikhale odziletsa komanso kuti tipewe khalidwe laciwelewele. Tikayesedwa kuti ticite chimo, tiyenela kuima n’kuganizila mmene zocita zathu zidzakhumudwitsila Yehova, a m’banja lathu, komanso anthu ena. Tizikumbukilanso kuti “ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco.” (Agal. 6:7) Kumbali ina, zimene zinacitikila Rubeni zimatikumbutsa cifundo ca Yehova. Ngakhale kuti Yehova sangatichinjilize ku zotsatilapo za kulakwa kwathu, iye adzatidalitsa tikayesetsa kucita zoyenela.
SIMIYONI NDI LEVI
9. N’cifukwa ciyani Yakobo sanakondwele naye Simiyoni ndi Levi? (Genesis 49:5-7)
9 Welengani Genesis 49:5-7. Cotsatila, Yakobo anagwilitsa nchito mawu osapita m’mbali pokamba ndi Simiyoni ndi Levi poonetsa kuti sanali wokondwa ndi zimene anacita. Zaka zingapo m’mbuyomo, Dina, mwana wamkazi wa Yakobo, anagwililidwa ndi mwamuna wacikanani dzina lake Sekemu. M’pomveka kuti ana onse a Yakobo anakhumudwa kwambili ndi zimene zinacitikila mlongo wawo. Koma Simiyoni ndi Levi anacita kunyanya nawo ukali. Iwo mwacinyengo analonjeza amuna a ku Sekemu kuti akavomela kucita mdulidwe, adzakhala nawo pa mtendele. Amunawo anavomela. Pamene anthuwo anali pa ululu cifukwa ca mdulidwewo, Simiyoni ndi Levi anatenga malupanga awo “nʼkukalowa mumzindawo [pamene anthuwo sanali kuyembekezela] ndipo anapha mwamuna aliyense.”—Gen. 34:25-29.
10. Kodi ulosi umene Yakobo anakamba wonena za Simiyoni ndi Levi unakwanilitsika motani? (Onaninso bokosi lakuti “Malailano Olosela a Yakobo.”)
10 Yakobo anakwiya kwambili ndi zimene ana ake awili anacita. Analosela kuti iwo adzamwazidwa ndi kubalalitsidwa mu Isiraeli. Ulosiwu unakwanilitsika patapita zaka zoposa 200 pomwe mtundu wa Isiraeli unalowa m’Dziko Lolonjezedwa. Malo amene fuko la Simiyoni linalandila monga colowa anali dela la fuko la Yuda. (Yos. 19:1) Ndipo colowa cimene fuko la Levi linalandila cinali mizinda 48 imene inali yomwazikana mu Isiraeli.—Yos. 21:41.
11. N’zinthu zabwino ziti zimene a fuko la Simiyoni ndi la Levi anacita?
11 Mbadwa za Simiyoni ndi Levi sizinabweleze zolakwa za makolo awo. Fuko la Levi linaonetsa kuti linali kucilikiza kulambila koyela mokhulupilika. Pamene Mose analandila Cilamulo kwa Yehova pa Phili la Sinai, Aisiraeli ambili anayamba kulambila mwana wa ng’ombe. Koma Alevi anakhala kumbali ya Mose pom’thandiza kuthetsa mcitidwe woipa umenewo. (Eks. 32:26-29) Yehova anasankha amuna mu mtundu wa Levi kuti akhale ansembe. (Eks. 40:12-15; Num. 3:11, 12) M’kupita kwa nthawi, a fuko la Simiyoni anathandiza a fuko la Yuda pomenyana ndi Akanani pofuna kulanda Dziko Lolonjezedwa.—Ower. 1:3, 17.
12. Mwaphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Simiyoni ndi Levi?
12 Kodi tiphunzilapo ciyani? Musamacite zinthu cifukwa ca ukali. Ngati inu kapena munthu amene mumakonda wacitidwa zopanda cilungamo, m’pomveka kukhumudwa. (Sal. 4:4) Koma tisaiwale kuti Yehova sangakondwele tikakamba mawu kapena tikacita zinthu cifukwa ca ukali. (Yak. 1:20) Ngati wina waticita zopanda cilungamo, kaya ndi Mkhristu mnzathu kapena ayi, tiyenela kuthetsa nkhaniyo motsatila mfundo za m’Baibo. Tikatelo, tidzapewa mavuto amene amabwela cifukwa cosaletsa mkwiyo wathu. (Aroma 12:17, 19; 1 Pet. 3:9) Ngati makolo anu akucita zinthu zosakondweletsa Yehova, musaganize kuti basi muyenela kutengela citsanzo cawo. Musaganize kuti n’zosatheka kwa inu kukondweletsa Yehova. Yehova sadzalephela kukupatsani mphoto mukapitiliza kucita zoyenela.
YUDA
13. N’cifukwa ciyani Yuda ayenela kuti anacita mantha itafika nthawi yoti atate ake am’lankhule?
13 Kenako Yakobo analankhula kwa mwana wake Yuda. Yuda ayenela kuti anacita mantha atamva zimene atate ake anauza abale ake. Zinali conco cifukwa naye anali atacitapo zolakwa zazikulu. Iyenso anatengapo gawo pa kufunkha katundu mu mzinda wa Sekemu. (Gen. 34:27) Cina, pa nthawi ina iye anagwilizana ndi abale ake zoti agulitse Yosefe mu ukapolo ndi kunamiza atate awo za nkhaniyo. (Gen. 37:31-33) Patapita nthawi, Yuda anagona ndi mpongozi wake Tamara pomuganizila kuti anali hule.—Gen. 38:15-18.
14. Kodi Yuda anacitapo zinthu ziti zabwino? (Genesis 49:8, 9)
14 Komabe, Yakobo mouzilidwa anangomudalitsa Yuda ndi kumuyamikila. (Welengani Genesis 49:8, 9.) Pa nthawi ina, Yuda anaonetsa kuti anakhudzika kwambili ndi mmene atate ake acikalambilewo anali kumvela. Ndipo anali ataonetsapo cifundo kwa m’bale wake Benjamini.—Gen. 44:18, 30-34.
15. Kodi Yuda anadalitsidwa m’njila ziti?
15 Yakobo analosela kuti Yuda adzakhala mtsogoleli pakati pa abale ake. Komabe, ulosiwu unakwanilitsika pambuyo pa nthawi yaitali, patapita zaka ngati 200. Pa nthawiyi, fuko la Yuda ndi limene linali kutsogolela mafuko ena potuluka mu Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa. (Num. 10:14) Patapita zaka, fuko la Yuda ndilo linali patsogolo pogonjetsa Akanani kuti alande Dziko Lolonjezedwa. (Ower. 1:1, 2) Pa mafumu onse ocokela mu fuko la Yuda, Davide ndiye anali woyamba kukhala mfumu. Koma ulosi umenewu unakwanilitsikanso m’njila zina.
16. Kodi ulosi uli pa Genesis 49:10 unakwanilitsika motani? (Onaninso bokosi lakuti “Malailano Olosela a Yakobo.”)
16 Yakobo ananena kuti munthu amene adzalamulile monga Mfumu adzacoka m’fuko la Yuda. (Welengani Genesis 49:10 ndi mawu am’munsi.) Wolamulila ameneyo ndi Yesu Khristu, amene Yakobo anamucha Silo. Ponena za Yesu, mngelo anati: “Yehova Mulungu adzamupatsa mpando wacifumu wa Davide atate wake.” (Luka 1:32, 33) Yesu amachedwanso “Mkango wa fuko la Yuda.”—Chiv. 5:5.
17. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova pa nkhani ya mmene timaonela ena?
17 Kodi tiphunzilapo ciyani? Yehova anadalitsa Yuda ngakhale kuti Yudayo analakwitsapo zinthu zina zazikulu. N’kutheka kuti abale a Yuda anayamba kudzifunsa kuti ndi makhalidwe abwino ati amene Yehova anaonamo mwa iye. Mulimonsemo, Yehova anaonamo zabwino mwa Yuda ndipo anamudalitsa. Kodi tingatengele motani citsanzo ca Yehova? Mkhristu mnzathu akalandila utumiki winawake wapadela, tingayambe kuganiza kuti si woyenelela ngati timadziwa zofooka zake. Koma tizikumbukila kuti Yehova akusangalala naye cifukwa ca makhalidwe ake abwino. Yehova amaonamo zabwino mwa alambili ake. Ifenso tiyeni tiyesetse kucita zimenezo.
18. N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala oleza mtima?
18 Phunzilo lina limene tingatengepo pa zimene zinacitikila Yuda n’lokhala oleza mtima. Yehova amakwanilitsa malonjezo ake nthawi zonse. Koma nthawi zina amacita izi pa nthawi komanso m’njila imene sitikuyembekezela. Poyamba, atsogoleli a anthu a Mulungu sanali a fuko la Yuda. Koma a fuko la Yudawo anacilikiza mokhulupilika aja amene Yehova anawaika kukhala otsogolela monga Mose wa fuko la Levi, Yoswa wa fuko la Efuraimu, komanso Mfumu Sauli wa fuko la Benjamini. Ifenso tiyenela kucilikiza aliyense amene Yehova wasankha kuti azititsogolela masiku ano.—Aheb. 6:12.
19. Kodi taphunzilapo ciyani pa malailano olosela a Yakobo ponena za Yehova?
19 Pofika pano, kodi taphunzilanji pa malailano olosela a Yakobo? N’zosacita kufunsa kuti “mmene munthu amaonela si mmene Mulungu amaonela.” (1 Sam. 16:7) Yehova ndi woleza mtima kwambili ndipo ndi wokhululuka. Ngakhale kuti salekelela makhalidwe oipa, iye sayembekezelanso alambili ake kucita zinthu mosalakwitsa. Iye angadalitse ngakhale amene anacitapo zolakwa zazikulu kumbuyoku ngati alapa kucokela pansi pa mtima n’kuyamba kucita zinthu zabwino. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zimene Yakobo ananena kwa ana ake ena 8.
NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse