LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 30 tsa. 76
  • Rahabi Abisa Azondi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Rahabi Abisa Azondi
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Rahabi Anakhulupilila Yehova
    Phunzitsani Ana Anu
  • Rahabi Abisa Azondi
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Mpanda Wa Yeriko
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 30 tsa. 76
Rahabi ateteza azondi pouza asilikali kuloŵela njila ina

PHUNZILO 30

Rahabi Abisa Azondi

Azondi aciisiraeli atafika ku mzinda wa Yeriko, anakhala ku nyumba kwa mzimayi wina, dzina lake Rahabi. Mfumu ya Yeriko itamva zimenezo, inatuma asilikali ku nyumba kwa Rahabi. Koma Rahabi anabisa azondi aŵili amenewo pa mtenje, ndipo anauza asilikaliwo kuti ‘alondoleni aloŵela uku.’ Koma kumene anaŵauzako kunali kolakwika. Ndiyeno anauza azondiwo kuti: ‘N’dzakuthandizani cifukwa nidziŵa kuti Yehova ali ku mbali yanu, na kuti mudzagonjetsa dzikoli. Conde, nilonjezeni kuti mudzapulumutsa a m’banja langa.’

Azondiwo anauza Rahabi kuti: ‘Tikulonjeza kuti aliyense amene adzakhala mkati mwa nyumba yako adzapulumuka.’ Ndipo iwo anamuuza kuti: ‘Mangilila nthambo yofiila pawindo ya nyumba yako, ndipo a m’banja lako adzapulumuka.’

Nyumba ya Rahabi, ili na nthambo yofiila pawindo, siikugwa pamene mpanda wa mzinda wa Yeriko uli kugwa

Rahabi anatulutsa azondi aja pawindo poseŵenzetsa nthambo. Iwo anapita kukabisala ku mapili kwa masiku atatu asanabwelele kwa Yoswa. Ndiyeno, Aisiraeli anawoloka Mtsinje wa Yorodano na kukonzekela kulanda dziko la Kanani. Mzinda wa Yeriko ndiwo unali woyamba kugonjetsedwa. Yehova anauza Aisiraeli kuyenda mozungulila mzindawo kamodzi patsiku kwa masiku 6. Koma pa tsiku la 7, anazungulila mzindawo maulendo 7. Kenako, ansembe analiza malipenga awo, ndipo asilikali anafuula mokweza kwambili. Pamenepo mpanda wa mzinda wa Yeriko unaundumuka wonse kugwela pansi! Koma nyumba ya Rahabi, imene inali pa mpandawo, siinagwe. Rahabi komanso a m’banja lake anapulumuka cifukwa cokhulupilila Yehova.

‘N’cimodzi-modzinso ndi Rahabi. Kodi Rahabi . . . sanaonedwe ngati wolungama cifukwa ca nchito zake, powalandila bwino azondi aja ndi kuwabweza kwawo powasonyeza njila ina?’—Yakobo 2:25

Mafunso: N’cifukwa ciani Rahabi anathandiza azondi aja? Nanga Aisiraeli anaugonjetsa bwanji mzinda wa Yeriko? N’ciani cinacitika kwa Rahabi komanso a m’banja lake?

Yoswa 2:1-24; 6:1-27; Aheberi 11:30, 31; Yakobo 2:24-26

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani