LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 44
  • Rahabi Abisa Azondi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Rahabi Abisa Azondi
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Rahabi Anakhulupilila Yehova
    Phunzitsani Ana Anu
  • Rahabi Abisa Azondi
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mpanda Wa Yeriko
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Azondi 12
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 44

Nkhani 44

Rahabi Abisa Azondi

APA zinthu zavuta. Amuna aŵili awa afunika kuti athaŵe msanga-msanga cifukwa anthu angawaphe. Iwo ndi Aisiraeli ndipo ndi azondi. Mkazi uyu amene awathandiza ni Rahabi. Iyi ni nyumba ya Rahabi ndipo ili pamwamba pa cipupa ca mzinda wa Yeriko. Tiye tione cifukwa cake amuna amenewa apezeka mu vuto limeneli.

Aisiraeli akonzekela kuoloka mtsinje wa Yorodano kuti aloŵe mu dziko la Kanani. Koma akalibe kuoloka, Yoswa atuma azondi aŵili. Awauza kuti: ‘Yendani mukaone dziko lija ndi mzinda wa Yeriko.’

Pamene azondi aja afika ku Yeriko, ayenda kunyumba ya Rahabi. Koma anthu ena auza mfumu ya Yeriko kuti: ‘Muno mwaloŵa Aisiraeli aŵili usiku uno kuti aone dziko lathu.’ Pamenepo mfumu itumiza anthu kwa Rahabi, ndipo anthuwo auza Rahabi kuti: ‘Bweletsa amuna amene ali mu nyumba mwako!’ Koma Rahabi abisa azondi aja mu mtenje wa nyumba. Conco ayankha kuti: ‘Inde, amuna amenewo anali abwela mu nyumba muno, koma sindinadziŵe kumene anacokela. Iwo acoka pamene kwayamba kucita kamdima, geti ya mzinda uno ikalibe kutsekedwa. Thamangani, mudzawapeza.’ Motelo, io acoka ndi kuthamangila azondi aja.

Iwo atacoka, Rahabi athamangila pamtenje. Pamenepo auza azondi aja kuti: ‘Ndidziŵa kuti Yehova adzakupatsani dziko lino. Tinamvela mmene Yehova anaumitsila madzi a mu Nyanja Yofiira pamene munali kutuluka ku Iguputo, ndi mmene munaphela mafumu awa, Sihoni ndi Ogi. Ine ndakukomelani mtima. Conco munilonjeze kuti inunso mudzanikomela mtima. Mukapulumutse atate ndi amai anga, ndi abale ndi alongo anga.’

Azondi aja alonjeza kuti adzacita zimenezo. Koma Rahabi afunika kucita mbali yake. Azondi amuuza kuti: ‘Tenga nthambo yofiila iyi, uimangilile pawindo. Ndipo usonkhanitse acibanja ako onse mu nyumba mwako muno. Tikabwela kudzalanda mzinda wa Yeriko, tidzaona nthambo imeneyi pawindo ndipo sitidzapha munthu aliyense m’nyumba mwako.’ Azondi aja apita kwa Yoswa, ndipo amuuza zonse zimene zacitika.

Yoswa 2:1-24; Aheberi 11:31.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani