LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 26 tsa. 66-tsa. 67 pala. 1
  • Azondi 12

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Azondi 12
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Azondi 12
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Tsatilani Yehova na Mtima Wonse
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Rahabi Abisa Azondi
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yehova Asankha Yoswa
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 26 tsa. 66-tsa. 67 pala. 1
Amuna aciisiraeli azonda dziko la Kanani

PHUNZILO 26

Azondi 12

Aisiraeli anacoka pa Phili la Sinai na kuyenda kumalo ochedwa Kadesi kudutsila m’cipululu ca Parana. Ali kumeneko, Yehova anauza Mose kuti: ‘Tuma amuna 12, mmodzi pa fuko lililonse, kuti akazonde dziko la Kanani limene nidzapatsa Aisiraeli.’ Conco, Mose anasankha amuna 12 na kuŵauza kuti: ‘Pitani ku Kanani kuti mukaone ngati dzikolo ni labwino kulimako zakudya. Mukaonenso ngati anthu a m’dzikomo ni amphamvu kapena alibe mphamvu, komanso ngati amakhala m’matenti kapena m’mizinda.’ Azondi 12 amenewo, kuphatikizapo Yoswa na Kalebe, anapita ku Kanani.

Aisiraeli adandaula ndipo alefuka

Patapita masiku 40, azondi aja anabwelako. Anabwela na nkhuyu, makangaza, na mphesa. Azondiwo anati: ‘Ni dziko labwino, koma kuli anthu amphamvu, ndipo amakhala m’mizinda ya mipanda itali-itali.’ Koma Kalebe anati: ‘Tingawagonjetse. Tiyeni tipite lomba!’ Kodi udziŵa cimene Kalebe anakambila conco? Cifukwa iye na Yoswa anali kukhulupilila mwa Yehova. Koma azondi enawo 10 anati: ‘Tisapiteko! Kuli viŵanthu vikulu-vikulu matupi, vili monga viphona! Ise tinali monga tuziwala kwa iwo.’

Atamvela zimenezi, Aisiraeli analefuka. Anayamba kudandaula na kuuzana kuti: ‘Tiyeni tisankhe mtsogoleli wina, ndipo tibwelele ku Iguputo. Tisapiteko ku dziko limenelo cifukwa adzatipha.’ Yoswa na Kalebe anati: ‘Musam’pandukile Yehova, ndipo musacite mantha. Yehova adzatiteteza.’ Koma Aisiraeli sanawamvele. Ndipo anafuna ngakhale kupha Yoswa na Kalebe.

Kodi Yehova anacita ciani? Anauza Mose kuti: ‘Ngakhale kuti nawacitila zinthu zonse zabwino, Aisiraeli akupitiliza kusanimvela. Conco, adzakhala m’cipululu zaka 40, ndipo adzafela mmenemo. Koma ana awo cabe, pamodzi na Yoswa na Kalebe, ndiwo adzaloŵa m’dziko limene n’nalonjeza kuwapatsa na kukhalamo.’

“N’cifukwa ciani mukucita mantha conci, anthu acikhulupililo cocepa inu?”—Mateyu 8:26

Mafunso: N’ciani cinacitika pamene azondi 12 anabwelako ku Kanani? Nanga Yoswa na Kalebe anaonetsa bwanji kuti anakhulupilila mwa Yehova?

Numeri 13:1–14:38; Deuteronomo 1:22-33; Salimo 78:22; Aheberi 3:17-19

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani