LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 74 tsa. 176-tsa. 177 pala. 4
  • Pamene Yesu Anakhala Mesiya

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pamene Yesu Anakhala Mesiya
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yohane Abatiza Yesu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Yohane Anakonza Njila
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Kodi Yesu Khiristu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 74 tsa. 176-tsa. 177 pala. 4
Yohane atabatiza Yesu, mzimu wa Mulungu wooneka ngati nkhunda utsikila pa iye

PHUNZILO 74

Pamene Yesu Anakhala Mesiya

Yohane anali kulalikila kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwela.’ Pamene Yesu anali na zaka pafupi-fupi 30, ananyamuka kucoka ku Galileya kupita ku Mtsinje wa Yorodano. Kumeneko anapeza Yohane akubatiza anthu. Nayenso Yesu anapempha Yohane kuti am’batize. Koma Yohane anakana. Anati: ‘Ine siniyenela kubatiza imwe. Imwe muyenela kubatiza ine.’ Yesu anauza Yohane kuti: ‘Yehova afuna kuti iwe unibatize.’ Conco onse aŵili analoŵa pa Mtsinje wa Yorodano, ndipo Yohane anamiza Yesu thupi lonse m’madzi.

Yesu atavuuka m’madzi, anapemphela. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo mzimu wa Mulungu wooneka monga nkhunda unatsikila pa iye. Ndiyeno panamveka mawu a Yehova kucokela kumwamba akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.”

Pamene mzimu wa Yehova unabwela pa Yesu, m’pamene iye anakhala Khristu kapena kuti Mesiya. Tsopano anafunikila kuyamba nchito imene Yehova anamutumizila pa dziko lapansi.

Atangobatizika, Yesu anapita ku cipululu, ndipo anakhalako masiku 40. Atabwelako, anapita kwa Yohane. Yohane ataona Yesu akubwela ca apo, anati: ‘Uyu ndiye Mwanawankhosa wa Mulungu amene adzacotsa ucimo wa dziko.’ Mwa kukamba izi, Yohane anathandiza anthu kudziŵa kuti Yesu ndiye Mesiya. Kodi udziŵa zinam’citikila Yesu ku cipululu? Tidzaona.

“Panamveka mawu ocokela kumwamba akuti: ‘Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwela nawe.’”—Maliko 1:11

Mafunso: Kodi Yesu anabatizika cifukwa ciani? Nanga Yohane anatanthauzanji pokamba kuti Yesu ndiye Mwanawankhosa wa Mulungu?

Mateyu 3:13-17; Maliko 1:9-11; Luka 3:21-23; Yohane 1:29-34; Yesaya 42:1; Aheberi 10:7-9

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani