LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 75 tsa. 178-tsa. 179 pala. 4
  • Mdyelekezi Ayesa Yesu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mdyelekezi Ayesa Yesu
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Baibulo Limakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 75 tsa. 178-tsa. 179 pala. 4
Yesu akana kulumpha kucokela pa kacisi

PHUNZILO 75

Mdyelekezi Ayesa Yesu

Yesu akana kusandutsa miyala kuti ikhale cakudya

Pambuyo pakuti Yesu wabatizika, mzimu woyela unamutsogolela ku cipululu. Iye sanadye ciliconse kwa masiku 40, ndipo anamvela njala kwambili. Pamenepo Mdyelekezi anabwela kudzamuyesa. Iye anauza Yesu kuti: ‘Ngati ndimwe Mwana wa Mulungu zoona, uzani miyala iyi kuti isanduke cakudya.’ Yesu anagwila Malemba poyankha. Iye anati: ‘Malemba amakamba kuti munthu sangakhale na moyo cifukwa ca cakudya cabe, koma afunikanso kumvela mawu onse a Yehova.’

Mdyelekezi anabwelanso kaciŵili kudzayesa Yesu. Iye anati: ‘Ngati ndimwe Mwana wa Mulungu zoona, lumphani kucokela pamwamba pa kacisi. Malemba amati Mulungu adzatumiza angelo ake kuti adzakunyamuleni kuti musavulale.’ Koma Yesu anagwilanso Malemba. Anati: ‘Malemba amakambanso kuti usamuyese Yehova.’

Yesu akana maufumu a dziko lonse amene Satana afuna kum’patsa

Kacitatu, Satana anaonetsa Yesu maufumu onse a pa dziko lapansi, pamodzi na ulemelelo wawo komanso cuma cawo. Kenako Satana anati: ‘Nidzakupatsani maufumu onse aya ngati munganilambileko kamodzi cabe.’ Koma Yesu poyankha anati: ‘Coka Satana! Malemba amati muzilambila Yehova yekha cabe.’

Pamenepo Mdyelekezi anacokapo. Ndipo angelo anabwela na kum’patsa cakudya Yesu. Kucokela apa, Yesu anayamba kugwila nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Ndiye nchito imene Mulungu anatumila Yesu pa dziko lapansi. Anthu anali kukondwela na zimene Yesu anali kuwaphunzitsa, cakuti anali kumulondola kulikonse kumene anali kuyenda.

“Pamene [Mdyelekezi] akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, cifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”—Yohane 8:44

Mafunso: Kodi ni mayeselo atatu ati amene Yesu anayesedwa nawo? Nanga kodi Yesu anali kumuyankha bwanji Mdyelekezi?

Mateyu 4:1-11; Maliko 1:12, 13; Luka 4:1-15; Deuteronomo 6:13, 16; 8:3; Yakobo 4:7

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani