LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 82 tsa. 192-tsa. 193 pala. 2
  • Yesu Anaphunzitsa Otsatila Ake Kupemphela

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Anaphunzitsa Otsatila Ake Kupemphela
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Tiyenela Kupemphela kwa Yesu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mungapemphele Bwanji Kuti Mulungu Azimva Mapemphelo Anu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 82 tsa. 192-tsa. 193 pala. 2
Mfarisi apemphela pa mphambano ya njila, ndipo anthu amuyan’gana

PHUNZILO 82

Yesu Anaphunzitsa Otsatila Ake Kupemphela

Zonse zimene Afarisi anali kucita, colinga cawo cinali kudzionetsela kwa anthu. Akacitila wina cinthu cabwino, anali kufuna kuti anthu ena aone. Anali kupemphelela pamalo oonekela kuti anthu aziŵaona. Anali kuloŵeza pa mtima mapemphelo atali-atali, na kupeleka mapemphelowo kumalo opezekako anthu oculuka, monga m’masunagoge na m’misewu, kuti anthu ambili aziŵamvela. Conco anthu anadabwa pamene Yesu anaŵauza kuti: ‘Osapemphela monga Afarisi. Iwo amaganiza kuti Mulungu angakondwele na mawu ambili-mbili popemphela. Pemphelo ni pakati pa munthu payekha na Yehova. Musamabweleze zinthu zimodzi-modzi nthawi zonse. Yehova amafuna kuti muzimuuza zakukhosi kwanu.

Wacicepele wagwada, ndipo apemphela

Koma muzipemphela conco: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.”’ Yesu anaŵauzanso kuti azipempha cakudya ca tsikulo, kukhululukidwa macimo, komanso nkhani zina zaumwini.

Yesu anati: ‘Osaleka kupemphela. Pitilizani kupempha zinthu zabwino kwa Atate wanu Yehova. Kholo iliyonse imafuna kupatsa ana ake zinthu zabwino. Ngati mwana wanu wakupemphani cakudya, kodi mungam’patse mwala? Ngati wapempha nsomba, mungam’patse njoka kodi?’

Ndiyeno Yesu anafotokoza tanthauzo lake kuti: ‘Ngati inu mumadziŵa kupatsa mphatso zabwino ana anu, kuli bwanji Atate wanu Yehova? Kodi iye sangakupatseni mzimu woyela? Cofunika ni kupempha basi.’ Kodi umatsatila malangizo a Yesu amenewa? Nanga ni zinthu ziti zimene ungapemphelele?

“Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulilani.” —Mateyu 7:7

Mafunso: Kodi Yesu anakamba ciani pophunzitsa otsatila ake kupemphela? Kodi ni zinthu zofunika ziti zimene umapemphelela?

Mateyu 6:2-18; 7:7-11; Luka 11:13

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani