LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 81 tsa. 190-tsa. 191 pala. 2
  • Ulaliki wa pa Phili

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ulaliki wa pa Phili
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • “Nakuchani Mabwenzi”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mufunikila Kuphunzila za Mulungu
    Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
  • Khalani Pafupi Ndi Yehova
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • “Bwelani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 81 tsa. 190-tsa. 191 pala. 2
Yesu aphunzitsa khamu la anthu pa Ulaliki wa pa Phili

PHUNZILO 81

Ulaliki wa pa Phili

Yesu atatsiliza kusankha atumwi ake 12, anatsika m’phili n’kupita kumene khamu la anthu linasonkhana. Anthuwo anacokela ku Galileya, Yudeya, Turo, Sidoni, Siriya, na kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano. Anabweletsa anthu odwala, komanso amene anali kuvutitsidwa na ziŵanda. Yesu anawacilitsa onse. Ndiyeno anakhala pansi kumbali kwa phililo na kuyamba kuwaphunzitsa. Anafotokoza zimene tiyenela kucita kuti tikhale mabwenzi a Mulungu. Tifunikila Yehova kuti azititsogolela, ndipo tiyenela kumukonda. Koma sitingakonde Mulungu ngati sitikonda anthu anzathu. Tiyenela kukhala acifundo komanso acilungamo kwa anthu onse, ngakhale amene amatizonda.

Yesu anati: ‘Musamakonde mabwenzi anu cabe. Muzikondanso adani anu, ndiponso kukhululukila ena na mtima wonse. Ngati mwakhumudwitsa wina, mwamsanga pitani mukam’pepese. Citilani ena zimene mungafune kuti akucitileni.’

Yesu aphunzitsa khamu la anthu pa Ulaliki wa pa Phili

Yesu anathandizanso anthuwo kupewa maganizo okonda cuma. Iye anati: ‘Ubwenzi na Yehova ni wofunika kuposa ndalama zambili. Kawalala angakubeleni ndalama, koma palibe munthu angakubeleni ubwenzi wanu na Yehova. Lekani kuda nkhawa kuti mudzadya ciani, mudzamwa ciani, kapena mudzavala ciani. Yang’anani mbalame. Mulungu amazipatsa cakudya cokwanila nthawi zonse. Nkhawa sizingawonjezele moyo wanu ngakhale na tsiku limodzi. Kumbukilani kuti Yehova amadziŵa zimene mufunikila.’

Anthuwo sanamvelepo munthu aliyense akuphunzitsa mmene Yesu anaŵaphunzitsila. Atsogoleli awo acipembedzo sanawaphunzitsepo zinthu zimenezo. N’cifukwa ciani Yesu anali mphunzitsi wabwino kwambili? Cifukwa zonse zimene anaphunzitsa zinacokela kwa Yehova.

“Senzani goli langa ndipo phunzilani kwa ine, cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa”—Mateyu 11:29

Mafunso: Tiyenela kucita ciani kuti tikhale mabwenzi a Yehova? Kodi Yehova afuna kuti anthu ena uzicita nawo bwanji zinthu?

Mateyu 4:24–5:48; 6:19-34; 7:28, 29; Luka 6:17-31

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani