LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 90 tsa. 210
  • Yesu Aphedwa ku Gologota

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Aphedwa ku Gologota
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yesu Aphedwa
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 90 tsa. 210
Yesu am’pacika pa mtengo, mkulu wa asilikali na ophunzila a Yesu ena, komanso Mariya na Yohane aimilila capafupi

PHUNZILO 90

Yesu Aphedwa ku Gologota

Ansembe aakulu anatenga Yesu kupita naye ku nyumba kwa bwanamkubwa Pilato. Pilato anafunsa anthuwo kuti: ‘Kodi munthu uyu mwam’peza na mlandu wanji?’ Iwo anati: ‘Iye akuti ni mfumu!’ Pilato anafunsa Yesu kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.”

Kenako Pilato anatumiza Yesu kwa Herode, wolamulila wa ku Galileya. Anacita izi kuti aone ngati angam’peze na mlandu uliwonse. Koma nayenso Herode sanam’peze na mlandu uliwonse, ndipo anam’bwezanso kwa Pilato. Ndiyeno Pilato anauza anthuwo kuti: ‘Ine na Herode sitinam’peze na mlandu uliwonse munthu uyu. Conco nim’masula.’ Koma anthuwo anayamba kufuula, amvekele: ‘Aphedwe! Aphedwe!’ Basi asilikali anayamba kum’kwapula Yesu, kum’thila mata, na kum’menya. Anamuvalika cisoti caminga, n’kumutonza, amvekele: ‘Tikuoneni Mfumu ya Ayuda.’ Pilato anauzanso anthuwo kuti: ‘Sin’namupeze na mlandu uliwonse munthu uyu.’ Koma iwo anafuulabe kuti: “Apacikidwe ameneyo!” Conco, Pilato anapeleka Yesu kuti akam’pacike.

Asilikaliwo anatenga Yesu n’kupita naye ku malo ochedwa Gologota. Kumeneko anam’khomelela pa mtengo na kuuimilika. Yesu anapemphela kuti: ‘Atate, akhululukileni, sadziŵa zimene akucita.’ Anthuwo anayamba kum’seka Yesu, amvekele: ‘Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu, seluka pa mtengo apo! Dzipulumutse tione.’

Munthu wacifwamba amene anam’pacika pambali pake anati: “Mukandikumbukile mukakaloŵa mu Ufumu wanu.” Yesu analonjeza munthuyo kuti: ‘Udzakhala na ine m’Paradaiso.’ Ndiyeno kumasana, kunacitika mdima m’dzikomo kwa maola atatu. Ena mwa ophunzila ake anali ciimilile pa mtengo umene anam’pacikapo, kuphatikizapo Mariya, mayi wake wa Yesu. Ndipo Yesu anauza Yohane kuti azisamalila Mariya, pomutenga ngati mayi wake wom’bala.

Pothela pake, Yesu anati: “Ndakwanilitsa cifunilo canu!” Anaŵelamila pansi n’kumwalila. Pamenepo kunacitika civomezi camphamvu. Mu kacisi, cinsalu colekanitsa Cipinda Coyela na Cipinda Coyela Koposa cinang’ambika pakati. Ndipo msilikali anati: ‘Uyu analidi Mwana wa Mulungu.’

“Malonjezo a Mulungu, kaya akhale oculuka cotani, akhala inde kudzela mwa iye.”—2 Akorinto 1:20

Mafunso: N’cifukwa ciani Pilato analola kuti Yesu aphedwe? Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuganizila kwambili za anthu ena kuposa iyemwini?

Mateyu 27:11-14, 22-31, 38-56; Maliko 15:2-5, 12-18, 25, 29-33, 37-39; Luka 23:1-25, 32-49; Yohane 18:28–19:30

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani