LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es23 masa. 17-26
  • February

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • February
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
  • Tumitu
  • Citatu, February 1
  • Cinayi, February 2
  • Cisanu, February 3
  • Ciŵelu, February 4
  • Sondo, February 5
  • Mande, February 6
  • Ciŵili, February 7
  • Citatu, February 8
  • Cinayi, February 9
  • Cisanu, February 10
  • Ciŵelu, February 11
  • Sondo, February 12
  • Mande, February 13
  • Ciŵili, February 14
  • Citatu, February 15
  • Cinayi, February 16
  • Cisanu, February 17
  • Ciŵelu, February 18
  • Sondo, February 19
  • Mande, February 20
  • Ciŵili, February 21
  • Citatu, February 22
  • Cinayi, February 23
  • Cisanu, February 24
  • Ciŵelu, February 25
  • Sondo, February 26
  • Mande, February 27
  • Ciŵili, February 28
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
es23 masa. 17-26

February

Citatu, February 1

Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye.—Sal. 145:18.

Yehova amasamala kwambili za alambili ake onse. Iye ali pafupi na aliyense wa ife, ndipo amadziŵa tikakhwethemuka na maganizo olefula. (Sal. 145:18, 19) Onani mmene Yehova anaonetsela kuti anali kumudela nkhawa mneneli Eliya. Munthu wokhulupilika ameneyu anakhalako pa nthawi yovuta m’mbili ya Aisiraeli. Alambili a Yehova anali kuzunzidwa koopsa, ndipo adani amphamvu otsutsa Mulungu anali kufuna kupha Eliya. (1 Maf. 19:1, 2) Mwina cina cimene cinavutitsa maganizo Eliya ni kuona kuti anali atatsala yekha-yekha monga mneneli wotumikila Yehova. (1 Maf. 19:10) Mwamsanga Mulungu anagwapo kuti am’thandize Eliya. Yehova anatumiza mngelo kukam’tsimikizila mneneli wake kuti sanali yekha, koma panalinso Aisiraeli ena ambili oopa Mulungu! (1 Maf. 19:5, 18) Yesu analimbikitsa ophunzila ake mwa kuwatsimikizila kuti adzakhala m’banja lalikulu lauzimu. (Maliko 10:29, 30) Ndipo Yehova Mutu wa banja lathu lauzimu analonjeza kuti adzacilikiza onse amene amafuna kum’tumikila.—Sal. 9:10. w21.06 8-9 ¶3-4

Cinayi, February 2

Wocokela kwa Mulungu amamvetsela mawu a Mulungu.—Yoh. 8:47.

Ambili amakhumudwa cifukwa cakuti ziphunzitso zathu za m’Baibo, zimavumbula ziphunzitso zabodza za cipembedzo. Atsogoleli acipembedzo amaphunzitsa nkhosa zawo kuti Mulungu amalanga anthu oipa ku helo. Iwo amaseŵenzetsa ciphunzitso cabodza cimeneci kuti azitha kulamulila anthu awo. Ife atumiki a Yehova, amene timalambila Mulungu wacikondi, timavumbula ciphunzitso cabodza cimeneci. Atsogoleli acipembedzo amaphunzitsanso kuti moyo sumafa. Timavumbula kuti ciphunzitso cimeneci, cinacokela ku cikunja. Ndipo ciphunzitso cimeneci cikanakhala coona kuuka kwa akufa kukanakhala kosafunikila. Ndipo mosiyana na ciphunzitso ca zipembedzo zambili cakuti Mulungu analembelatu za tsogolo lathu, ife timaphunzitsa kuti munthu ali na ufulu ndipo angasankhe kutumikila Mulungu. Kodi atsogoleli acipembedzo amatani tikawavumbula kuti amaphunzitsa zabodza? Nthawi zambili amakwiya ngako! Ngati timakonda coonadi tifunika kumvela na kukhulupilila mawu a Mulungu. (Yoh. 8:45, 46) Mosiyana na Satana Mdyelekezi, ife timaima zolimba m’coonadi. Timapewa kucita ciliconse cosagwilizana na zimene timakhulupilila. (Yoh. 8:44) Mulungu amafuna kuti anthu ake ‘azinyansidwa ndi coipa’, na kugwilitsitsa cabwino,’ monga mmene Yesu anacitila.—Aroma 12:9; Aheb. 1:9. w21.05 10 ¶10-11

Cisanu, February 3

Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthaŵani.—Yak. 4:7.

Bwanji ngati tazindikila kuti tinagwela kale mu msampha wa kunyada kapena dyela? Tingathe kuwonjokamo! Mtumwi Paulo anakamba kuti anthu amene Mdyelekezi “wawagwila amoyo” angawonjokemo mu msampha. (2 Tim. 2:26) Tisaiŵale kuti Yehova ni wamphamvu kuposa Satana. Conco, ngati tilandila thandizo la Yehova, tingawonjoke mu msampha uliwonse umene Mdyelekezi angachele. Koma m’malo moyembekezela kuti mpaka tikagwele m’misampha ya Satana kenako n’kuwonjokamo, tiyenela kuipewelatu misamphayo. Tingaipewe kokha mwa thandizo la Mulungu. Conco m’condeleleni Yehova tsiku lililonse, kuti akuthandizeni kuzindikila ngati makhalidwe oipa amenewo ayamba kusonkhezela kaganizidwe kanu na zocita zanu. (Sal. 139:23, 24) Musalole kuti makhalidwewo azike mizu mwa inu! Kwa zaka masauzande, Satana wakhala nkhumbalume. Koma posacedwa adzamangidwa, ndipo pa mapeto pake adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 10) Tiiyembekezela mwacidwi nthawi imeneyo. Mpaka nthawiyo, tiyeni tikhalebe chelu ku misampha ya Satana. Citani zonse zotheka kuti musalole kunyada kapena dyela kukulamulilani. Tsimikizani mtima ‘kutsutsa Mdyelekezi ndipo adzakuthawani.’ w21.06 19 ¶15-17

Ciŵelu, February 4

Pemphani Mwini zokolola kuti atumize anchito kukakolola. —Mat. 9:38.

Yehova amakondwela kwambili ngati munthu walandila coonadi ca m’Baibo, ndipo amauzako ena zimene amaphunzilazo. (Miy. 23:15, 16) Iye ayenela kuti amakondwela kwambili akaona anthu ake akulalikila na kuphunzitsa mwakhama masiku ano! Mwacitsanzo, olo kuti m’caka ca utumiki ca 2020 panali mlili wa dziko lonse, tinatha kutsogoza maphunzilo a Baibo okwana 7,705,765, ndipo izi zinathandiza kuti anthu okwana 241,994 adzipatulile kwa Yehova na kubatizika. Ndipo nawonso ophunzila a Yesu atsopano amenewa, azitsogoza maphunzilo a Baibo na kupanga ophunzila ambili. (Luka 6:40) Mosakayika konse, timakondweletsa Yehova ngati titengako mbali m’nchito yopanga ophunzila. Kupanga ophunzila si nchito yopepuka, koma na thandizo la Yehova tingathe kutengapo gawo kuphunzitsa acatsopano kukonda Atate wathu wakumwamba. Kodi tingadziikile colinga coyambitsa phunzilo la Baibo olo limodzi cabe na kumalitsogoza? Tingadabwe na zimene zingacitike ngati tiseŵenzetsa mpata uliwonse kufunsa amene timakumana nawo ngati angakonde kuphunzila nawo Baibo. w21.07 6-7 ¶14-16

Sondo, February 5

Cifukwa cakuti ndikusangalala ndi nyumba ya Mulungu wanga, ndili ndi cuma capadela comwe ndi golide ndi siliva. Ndikupeleka cuma cimeneci kunyumba ya Mulungu wanga.—1 Mbiri 29:3.

Mfumu Davide anapeleka zinthu zambili pa cuma cake kuti zithandizile pa nchito yomanga kacisi. (1 Mbiri 22:11-16) Ngati tilibenso mphamvu zakuti tigwile nawo nchito zamamangidwe, tingacilikizebe nchitoyo mwa kupanga zopeleka mmene tingathele. Cina, tingathandize acinyamata kupindula na maluso amene taphunzila. Pa nkhani ya kuwolowa manja, ganizilaninso citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anapempha Timoteyo kuti azigwila naye nchito ya umishonale. Ndipo anaphunzitsa wacinyamatayu njila zolalikila na kuphunzitsa. (Mac. 16:1-3) Zimene Timoteyo anaphunzila kwa Paulo, zinam’thandiza kuti azilalikila mogwila mtima. (1 Akor. 4:17) Nayenso Timoteyo anaseŵenzetsa zimene anaphunzila kwa Paulo kuphunzitsa ena. w21.09 12 ¶14-15

Mande, February 6

Mukucitilana nsanje ndi kukangana nokha-nokha.—1 Akor. 3:3.

Kodi tingaphunzilepo ciyani pa citsanzo ca wophunzila Apolo na mtumwi Paulo? Amuna aŵiliwa anali na cidziŵitso cokwana ca m’Malemba. Onse anali odziŵika komanso aphunzitsi aluso. Ndipo onse aŵili anapanga ophunzila ambili. Koma sanali kucitilana kaduka. (Mac. 18:24) Patapita nthawi pambuyo pakuti Apolo wacokako ku Korinto, Paulo anam’limbikitsa kubwelela kumeneko. (1 Akor. 16:12) Apolo anaseŵenzetsa maluso ake m’njila yabwino—polengeza uthenga wabwino na kulimbikitsa abale. Tingakhalenso otsimikiza kuti Apolo anali wodzicepetsa. Mwacitsanzo, Baibo siionetsa kuti Apolo anakhumudwa pamene Akula na Purisikila “anamufotokozela njila ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:24-28 ) Mtumwi Paulo anali kudziŵa za nchito yabwino imene Apolo anali kucita. Koma Paulo sanade nkhawa kuti anthu adzayamba kuona Apolo kukhala womuposa. Uphungu umene anapatsa mpingo wa ku Korinto unaonetsa kuti Paulo anali wodzicepetsa komanso wololela.—1 Akor. 3:4-6. w21.07 18-19 ¶15-17

Ciŵili, February 7

Ambili adzakhala olungama. —Aroma 5:19.

Adamu na Hava anacitila dala kusamvela Mulungu. Conco, panali poyeneladi kuŵacotsa m’banja la Mulungu. Nanga bwanji za ana awo? Yehova mwacikondi anakonza zakuti anthu omvela awatenge kukhala ana a m’banja lake. Iye anacita zimenezi kupitila mu nsembe ya dipo la Mwana wake wobadwa yekha. (Yoh. 3:16) Cifukwa ca nsembe ya Yesu imeneyi, anthu okhulupilika okwana 144,000 amatengedwa kukhala ana a Mulungu. (Aroma 8:15-17; Chiv. 14:1) Kuwonjezela apo, anthu okhulupilika mamiliyoni osaŵelengeka amacita cifunilo ca Mulungu. Iwo ali na ciyembekezo codzakhala ziwalo zacikwane-kwane m’banja la Mulungu, pambuyo pa mayeso othela kumapeto kwa zaka Cikwi. (Sal. 25:14; Aroma 8:20, 21) Iwo ngakhale pali pano amachulabe Yehova, Mlengi wawo, kuti “Atate.” (Mat. 6:9) Anthu amene adzaukitsidwe nawonso adzapatsidwa mwayi wophunzila zimene Yehova afuna kuti iwo azicita. Awo amene adzasankhe kumvela malangizo a Mulungu, pothela pake iwonso adzakhala m’banja lake. w21.08 5 ¶10-11

Citatu, February 8

Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti. —Afil. 1:10.

Mtumwi Paulo anapatsidwa nchito yolalikila, ndipo kwa zaka zambili anaona nchitoyo kukhala cinthu cofunika kwambili. Anali kulalikila “poyela komanso kunyumba ndi nyumba.” (Mac. 20:20) Komanso, anali kulalikila pa mpata uliwonse wapezeka. Mwacitsanzo, pamene anali kuyembekezela mabwenzi ake ku Atene, analalikila kagulu ka anthu ochuka amene ena a iwo analabadila uthenga wake. (Mac. 17:16, 17, 34) Ngakhale pamene Paulo anali ‘womangidwa,’ analalikila anthu amene anabwela kwa iye. (Afil. 1:13, 14; Mac. 28:16-24) Paulo anali kugwilitsila nchito bwino nthawi yake. Kambili, anali kupita na ena mu ulaliki. Mwacitsanzo, pa ulendo wake wa umishonale woyamba, anapita na Yohane Maliko, ndipo pa ulendo waciŵili anapita na Timoteyo. (Mac. 12:25; 16:1-4) Mosakaikila, Paulo anaphunzitsa amuna amenewa mokhazikitsila mpingo, mocitila maulendo aubusa, komanso mmene angakhalile aphunzitsi aluso.—1 Akor. 4:17. w22.03 27 ¶5-6

Cinayi, February 9

[Mulungu] sali kutali ndi aliyense wa ife.—Mac. 17:27.

Ena sakhulupilila mwa Mlengi cifukwa amakamba kuti amakhulupilila cabe zinthu zooneka na maso. Komabe, iwo amakhulupilila kuti kuli mphamvu yokoka zinthu kuti zigwe pansi ngakhale kuti samatha kuiona. Cikhulupililo cochulidwa m’Baibo cimaphatikizapo ‘umboni wa zinthu zenizeni zosaoneka.’ (Aheb. 11:1) Zimatenga nthawi, komanso zimafuna khama kuti tiphunzile maumboni amenewo patokha. Ndipo anthu ambili alibe cidwi cocita zimenezo. Munthu amene sapenda maumboni payekha, angayambe kukhulupilila kuti kulibe Mulungu. Pambuyo popenda maumboni, asayansi ena afika pokhulupilila kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse. Poyamba, ena anali kuganiza kuti kulibe Mlengi cifukwa sanaphunzilepo za cilengedwe ku mayunivesiti. Komabe, iwo afika podziŵa Yehova na kum’konda. Ndipo tonsefe tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu, mosasamala kanthu za maphunzilo amene tili nawo. w21.08 14 ¶1; 15-16 ¶6-7

Cisanu, February 10

Yehova amakomela mtima aliyense, ndipo nchito zake zonse amazicitila cifundo. —Sal. 145:9.

Yesu anaseŵenzetsa fanizo la mwana woloŵelela, pofuna kuonetsa kuti Yehova amakonda kwambili kuonetsa cifundo. Mwanayo anacoka panyumba, na ‘kukasakaza cuma cake conse mwa kuloŵelela m’makhalidwe oipa.’ (Luka 15:13) Patapita nthawi, iye analapa mwa kuleka makhalidwe oipawo, anadzicepetsa, ndipo anabwelela ku nyumba. Kodi atate wake anacita motani poona zimenezo? Yesu anati: “[Mwanayo] ali capatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa cifundo. Pamenepo anamuthamangila ndi kumukumbatila ndipo anamupsompsona mwacikondi.” Tateyo sanacititse manyazi mwana wake. M’malomwake, anam’citila cifundo na kumukhululukila, ndipo anam’landila na manja aŵili. Mwana woloŵelelayo anali atacimwa kwambili. Koma cifukwa colapa, atate wake anamukhululukila. Tate wacifundo m’fanizoli aimila Yehova. Pophunzitsa mogwila mtima conco, Yesu anaonetsa kuti Yehova ni wofunitsitsa kukhululukila ocimwa amene alapa moona mtima.—Luka 15:17-24. w21.10 8 ¶4; 9 ¶6

Ciŵelu, February 11

Mulungu anaceukila anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziŵika ndi dzina lake.—Mac. 15:14.

Masiku ano, atsogoleli acipembedzo ambili acita zonse zotheka kuti aphimbe coonadi cakuti Mulungu ali na dzina lake-lake. Iwo alicotsa m’ma Baibo awo, ndipo afika ngakhale poletsa anthu kuti asamalichule m’machalichi mwawo. Kodi alipo amene angatsutse mfundo yakuti a Mboni za Yehova ndiwo okha amalemekeza dzina lakuti Yehova mofunikila? Timadziŵikitsa dzina la Mulungu kwambili kuposa cipembedzo cina ciliconse. Ndipo timayesetsa kucita zinthu mogwilizana na dzina lathu lakuti, Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Tafalitsa makope a Baibulo la Dziko Latsopano oposa 240 miliyoni. M’Baibo imeneyi tinabwezeletsa dzina la Mulungu m’malo amene omasulila ma Baibo analicotsa. Ndipo timatulutsa zofalitsa zozikidwa pa Baibo zokhala na dzina la Mulungu m’zinenelo zoposa 1,000. w21.10 20-21 ¶9-10

Sondo, February 12

Wina mwa abale ako akasauka pakati panu . . . usamuumile mtima kapena kumuumitsila dzanja lako.—Deut. 15:7.

Timalambila Yehova tikamathandiza Akhristu anzathu ofunikila thandizo. Yehova analonjeza kuti adzabwezela Aisiraeli amene anali kucitila cifundo osauka. (Deut. 15:10) Inde, nthawi iliyonse tikathandiza Mkhristu mnzathu, Yehova amaona kuti thandizolo ni mphatso kwa iye. (Miy. 19:17) Mwacitsanzo, Akhristu a ku Filipi atatumiza mphatso kwa Paulo mkaidi, iye anacha mphatsoyo kuti “nsembe yovomelezeka yosangalatsa kwa Mulungu.” (Afil. 4:18) Ganizilani anthu a mu mpingo mwanu, na kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali wina amene ningathandize?’ Yehova amakondwela kwambili tikamaseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, maluso athu, komanso zinthu zathu zakuthupi pothandiza ena. Iye amaona zimenezo kuti ni mbali ya kulambila kwathu. (Yak. 1:27) Kulambila koona kumafuna nthawi komanso khama. Koma si kolemetsa. (1 Yoh. 5:3) Cifukwa ciyani? Cifukwa timalambila Yehova kaamba komukonda, komanso kaamba kokonda abale na alongo athu. w22.03 24 ¶14-15

Mande, February 13

Amawalitsila dzuŵa lake pa anthu oipa ndi abwino.—Mat. 5:45.

Kuti tikwanitse kuonetsa cifundo abale na alongo athu, coyamba tiyenela kudziŵa mavuto amene akukumana nawo. Mwacitsanzo, mlongo angakhale kuti adwala matenda aakulu. Iye mwina sakambapo za matenda ake, koma n’kutheka kuti angayamikile thandizo limene angapatsidwe. Kodi tingamuthandize kuphika cakudya kapena kuyeletsa m’nyumba? M’bale angakhale kuti nchito inatha. Kodi mungamupatseko mphatso ya ndalama mosaonetsela kuti yacokela kwa imwe, kuti ithandizile pa zosoŵa zake mpaka atapeza nchito ina? Conco, tisacite kuyembekezela kuti abale na alongo athu acite kutipempha thandizo m’pamene tiwaonetse cifundo. Mofanana na Yehova, tingawathandize iwo asanatipemphe n’komwe. Iye amatiwalitsila dzuŵa tsiku lililonse popanda kum’pempha. Kuthuma kwa dzuŵa kumapindulitsa aliyense, osati cabe anthu oyamikila. Kodi simungavomeleze kuti Yehova amationetsa cikondi mwa kutipatsa zofunikila? Timam’konda ngako Yehova cifukwa ni wokoma mtima komanso wopatsa! w21.09 22-23 ¶12-13

Ciŵili, February 14

Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.—Sal. 86:5.

Cikondi cosasintha ca Mulungu cimamusonkhezela kukhululuka. Yehova akaona kuti munthu wocimwa walapa na kusiyila njila yake yoipa, cikondi cake cosasintha cimamusonkhezela kukhululukila munthuyo. Ponena za Yehova, wamasalimo Davide anati: “Sanaticitile mogwilizana ndi macimo athu, kapena kutipatsa cilango cogwilizana ndi zolakwa zathu.” (Sal. 103:8-11) Davide anali kudziŵa bwino lomwe mmene cimamvekela kukhala na cikumbumtima cokuimba mlandu. Koma anadziŵanso kuti Yehova ni “wokonzeka kukhululuka.” N’ciani cimasonkhezela Yehova kukhululuka? Yankho tilipeza mu lemba la tsiku lalelo. Inde, malinga na zimene Davide anakamba m’pemphelo, Yehova amakhululuka cifukwa amaonetsa cikondi cake cosasintha kwa onse oitana pa iye. Tikacimwa, m’poyenela komanso n’cinthu cabwino kumvela cisoni pa zimene tinacita. Kumva cisoniko kungatilimbikitse kulapa, na kutenga masitepe ofunikila kuti tikonze zimene tinalakwitsa. w21.11 5 ¶11-12

Citatu, February 15

Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.—Mat. 6:9.

Yehova amalikonda dzina lake, ndipo amafuna kuti anthu onse azililemekeza. (Yes. 42:8) Koma kwa zaka ngati 6,000 zapitazo, dzina lake labwino lakhala likutonzedwa. (Sal. 74:10, 18, 23) Izi zinayamba pamene Mdyelekezi (kutanthauza “Woneneza”) anaimba mlandu Mulungu wakuti anamana Adamu na Hava cina cake cimene anali kufunikila. (Gen. 3:1-5) Kucokela panthawiyo, Yehova wakhala akuimbidwa mlandu wabodza wakuti amamana anthu zinthu zabwino zimene afunikila. Yesu anakhudzidwa kwambili kuona mmene dzina la Atate wake linali kutonzedwela. Yehova ndiye woyenela kulamulila kumwamba na padziko lapansi, ndipo ulamulilo wake ndiye wabwino koposa. (Chiv. 4:11) Koma Satana wayesa kunamiza angelo na anthu kuganiza kuti Mulungu si woyenela kulamulila. Posacedwa, nkhaniyi idzathetsedwa mosavuta. Ndipo anthu adzadziŵa kuti iye yekha ndiye woyenela kulamulila, ndiponso kuti Ufumu wake ndiwo wokha umene udzakhazikitse bata ndi mtendele weniweni padziko lapansi. w21.07 9 ¶5-6

Cinayi, February 16

Ine ndidzakondwelabe mwa Yehova ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wacipulumutso canga.—Hab. 3:18.

Mwacibadwa, mutu wa banja amafuna kupezela mkazi wake na ŵana zakudya zokwanila, zovala, komanso nyumba. Kodi mukumana na mavuto azacuma? Ngati n’telo, iyi ni nthawi yovuta kwa imwe. Komabe, mungaseŵenzetse nthawi yovutayo kuti mulimbitse cikhulupililo canu. Pemphelani kwa Yehova, na kuŵelenga mawu a Yesu apa Mateyu 6:25-34, komanso kuwasinkhasinkha. Ganizilani zitsanzo zamakono zoonetsa kuti Yehova amasamalila awo amene amakhala otangwanika na zinthu zauzimu. (1 Akor. 15:58) Kucita izi kudzalimbitsa cidalilo canu cakuti Atate wanu wakumwamba adzakusamalilani, monga anacitila kwa ena omwe anali m’mikhalidwe yofanana na yanu. Iye amadziŵa zimene mufunikila, ndipo amadziŵanso mmene adzakuthandizilani. Mukamaona Yehova akukuthandizani, cikhulupililo canu cidzalimbilako, ndipo mudzatha kupilila mayeso aakulu m’tsogolo. w21.11 20 ¶3; 21 ¶6

Cisanu, February 17

Wina akacita chimo, tili ndi mthandizi wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.—1 Yoh. 2:1.

Akhristu ambili cikhulupililo cawo calimba cifukwa cophunzila za dipo. Iwo apitilizabe kulalikila ngakhale pamene akutsutsidwa ndipo apilila mayeso osiyana-siyana mpaka ukalamba wawo. Ganizilani citsanzo ca mtumwi Yohane. Iye mokhulupilika analalikila za coonadi ca Khristu na dipo mwina kwa zaka zoposa 60. Ali na zaka pafupi-fupi 100, anam’ganizila kuti akupeleka ciopsezo ku Ufumu wa Roma, cakuti anaponyedwa m’ndende pacisumbu ca Patimo. Pa mlandu wanji? ‘Kulankhula za Mulungu ndi kucitila umboni za Yesu.’ (Chiv. 1:9) Ndithudi, iye ni citsanzo cabwino ngako pa cikhulupililo na kupilila! Yohane anaonetsa kuti amakonda kwambili Yesu na kuyamikila dipo lake mwa zimene analemba m’mabuku ake ouzilidwa. Koposa maulendo 100, iye anachula za dipo kapena mapindu amene tidzapeza kaamba ka dipo. (1 Yoh. 2:2) N’zoonekelatu kuti Yohane analiyamikila kwambili dipo. w21.04 17 ¶9-10

Ciŵelu, February 18

Usatembelele munthu wogontha, ndipo usaikile munthu wakhungu cinthu copunthwitsa.—Lev. 19:14.

Yehova anafuna kuti anthu ake azikomela mtima olemala. Mwacitsanzo, anauza Aisiraeli kuti sayenela kutembelela munthu wogontha. Kutembelelako kunaphatikizapo kuopseza munthu kapena kum’kambila zoipa. Kucita izi kunali kum’lakwila kwambili munthu wogonthayo! Popeza sanali kumva zoipa zimene anali kum’kambila, iye sakanatha kudziteteza. Cinanso, pa Levitiko 19:14 timaphunzila kuti kunali kosayenela atumiki a Mulungu ‘kuikila munthu wakhungu cinthu copunthwitsa.’ Ponena za anthu olemala, buku lina linati: “Kalelo ku Middle East, [olemala] anali kuwacitila nkhanza komanso zopanda cilungamo.” Mwina munthu wosaganizila ena anali kuika copunthwitsa kutsogolo kwa munthu wosaona cifukwa comuzonda, kapena kumupanga kukhala coseketsa. Uku kunali kupanda cifundo! Kupitila mu lamulo limeneli, Yehova anathandiza anthu ake kuona kuti ayenela kucitila cifundo anthu olemala. w21.12 8-9 ¶3-4

Sondo, February 19

Yakobo anacita mantha ndi kuda nkhawa kwambili.—Gen. 32:7.

Yakobo anakuda nkhawa kwambili kuti mwina mkulu wake akali kumsungila cidani. Conco, iye anapemphelela nkhaniyo kwa Yehova. Kenako, anatumiza mphatso kwa Esau. (Gen. 32:9-15) Potsilizila pake, iwo ataonana patapita zaka zambili, Yakobo anaonetsa ulemu kwa Esau. Iye anaŵelamila Esau, osati kamodzi kapena kaŵili kokha, koma maulendo 7! Mwa kucita zinthu modzicepetsa komanso mwaulemu, Yakobo anakhazikitsa mtendele na m’bale wake. (Gen. 33:3, 4) Pali zimene tiphunzilapo kwa Yakobo tikaona zimene iye anacita pokonzekela kukaonana na m’bale wake Esau, na mmene anafikila kwa iye. Modzicepetsa, Yakobo anapempha thandizo kwa Yehova. Ndiyeno, iye anacita zinthu mogwilizana na pemphelo lake mwa kucita zofunikila kuti ayanjanenso na m’bale wake. Atakumana, Yakobo sanayambe kukangana na Esau zakuti anali wolakwa ndani. Colinga cake cinali kukhazikitsa mtendele basi. Kodi mungatengele citsanzo ca Yakobo?—Mat. 5:23, 24. w21.12 25 ¶11-12

Mande, February 20

Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziŵa zonse.—1 Yoh. 3:20.

Mukaganizila zakuti Yesu anakufelani kuti aphimbe macimo anu, mwina mungakambe kuti, ‘Sindine woyenela kucitilidwa zimenezo.’ N’cifukwa ciani mungamvele conco? Cifukwa mtima wathu wopanda ungwilo ungatinamize, na kutipangitsa kudziona wosafunika kapena wosakondedwa. (1 Yoh. 3:19) Panthawi ngati zimenezi tiyenela kukumbukila kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” Cikondi ca Atate wathu wakumwamba na cikhululuko cake n’zamphamvu kuposa maganizo otilefula amene tingakhale nawo m’mitima yathu. Tiyenela kukhulupilila mumtima mwathu kuti Yehova amatikondadi. Kuti ticite zimenezi tiyenela kuŵelenga Mawu ake kaŵili-kaŵili, kupemphela mosalekeza, na kuyanjana na anthu ake okhulupilika. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika? Mudzadziŵa makhalidwe abwino a Yehova. Mudzaona kuti amakukondani kwambili. Kusinkha-sinkha pa Mawu a Mulungu tsiku lililonse kungakuthandizeni kukhala woganiza bwino, “kuwongola zinthu” m’maganizo na mu mtima mwanu.—2 Tim. 3:16. w21.04 23-24 ¶12-13

Ciŵili, February 21

Ndithu, ndidzafuulila Mulungu, ndipo iye adzachela khutu lake kwa ine.—Sal. 77:1.

Kuwonjezela pa kukhala na cidziŵitso, palinso zina zimene tingacite kuti tilimbitse cikhulupililo cathu. Tiyenela kusinkhasinkha zimene tikuphunzila. Ganizilani citsanzo ca wolemba Salimo 77. Iye anapsinjika maganizo cifukwa coona kuti Yehova waleka kumuyanja iye na Aisiraeli anzake. Izi zinali kumusoŵetsa tulo. (Vesi 2-8) Kodi anacita ciani? Anauza Yehova kuti: “Ndidzasinkhasinkha za nchito zanu zonse, ndipo ndiziganizila zocita zanu.” (Vesi 12) Olo kuti wa masalimoyo anali kudziŵa bwino zimene Yehova anacitila anthu ake m’mbuyomu, iye anadzifunsabe kuti: “Kodi Mulungu waiŵala kukhala wokoma mtima, kapena watsekeleza cifundo cake mwaukali?” (Vesi 9) Iye anasinkhasinkha nchito za Yehova, komanso maumboni oonetsa cifundo cimene Mulungu anamuonetsa m’mbuyomu. (Vesi 11) Cotulukapo cake n’cakuti anakhala wotsimikiza kuti Yehova sasiya anthu ake. (Vesi 15) w22.01 30-31 ¶17-18

Citatu, February 22

Kwa iye onsewa ndi amoyo. —Luka 20:38.

Kodi Yehova amamvela bwanji akakumbukila za amuna na akazi okhulupilika amene anamwalila? Iye amafunitsitsa kukawaonanso! (Yobu 14:15) Tangoganizilani mmene Yehova amayewela bwenzi lake Abulahamu. (Yak. 2:23) Kapena Mose amene analankhula naye “pamasom’pamaso.” (Eks. 33:11) Iye amayembekezela mwacidwi kudzamva Davide komanso olemba masalimo ena akuimba nyimbo zokoma zacitamando! (Sal. 104:33) Ngakhale kuti mabwenzi a Mulungu amenewa anagona mu imfa, Yehova sanawaiŵale. (Yes. 49:15) Iye amakumbukila zonse zokhudza iwo. Tsiku lina, adzawaukitsa, ndipo adzamvelanso mapemphelo awo ocokela pansi pa mtima na kuvomeleza kulambila kwawo. Ngati munataikilidwa okondedwa anu mu imfa, lolani zimenezi zikulimbitseni na kukutonthozani. Pamene kupanduka kunayamba mu Edeni, Yehova anadziŵa kuti zinthu zidzaipila-ipilabe kutsogolo. Yehova amadana na zoipa, kupanda cilungamo, na ciwawa, zimene zili m’dzikoli. w21.07 10 ¶11; 12 ¶12

Cinayi, February 23

[Tizikondana] m’mawu . . . ndi m’zocita zathu.—1 Yoh. 3:18.

Ngati tikonda abale na alongo athu, timaonetsanso kuti timayamikila dipo. Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka ife, komanso kaamba ka abale na alongo athu. Conco ngati iye anali wokonzeka kuwafela, ndiye kuti amawaona kukhala ofunika kwambili. (1 Yoh. 3:16-18) Timaonetsa cikondi pa abale na alongo athu malinga na mmene timacitila nawo zinthu. (Aef. 4:29, 31–5:2) Mwacitsanzo, timawathandiza akadwala kapena pamene akupilila mavuto aakulu, kuphatikizapo matsoka a zacilengedwe. Koma kodi tiyenela kucita ciani ngati wokhulupilila mnzathu wakamba kapena kucita zinthu zimene zatikhumudwitsa? Kodi mumakonda kusunga cakukhosi wokhulupilila mnzanu akakulakwilani? (Lev. 19:18) Ngati mumatelo, conde tsatilani malangizo aya: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.” (Akol. 3:13) Nthawi zonse tikakhululukila m’bale kapena mlongo wathu, timaonetsa Atate wathu wakumwamba kuti dipo timaliyamikila kwambili. w21.04 18 ¶12-13

Cisanu, February 24

Igwilitseni nchito [mphatso yanu] potumikilana.—1 Pet. 4:10.

Tingamatumikile Yehova mwakhama na kuthandiza anthu ambili kupita patsogolo mpaka kukabatizika. Koma timadziŵa kuti zonsezi zimatheka cifukwa ca thandizo la Yehova. Citsanzo ca Apolo komanso mtumwi Paulo citiphunzitsanso kuti ngati tili na maudindo ambili mu mpingo, tingacite zambili polimbikitsa mtendele. Timayamikila kwambili ngati amuna apaudindo amalimbikitsa mtendele na mgwilizano mwa kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu popeleka uphungu, komanso ngati amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu Khristu m’malo modzifunila ulemelelo! (1 Akor. 4:6, 7) Aliyense wa ife ali na maluso amene Mulungu anam’patsa. Tingaone monga timacita mbali yocepa kwambili. Koma zinthu zing’ono-zing’ono zimene tingacite polimbikitsa mgwilizano, zili monga nchelwa iliyonse imene imakhala yofunikila kuti nyumba imangidwe. Tiyeni tonsefe tiyesetse kuthetselatu mzimu wampikisano. Tiyeni tionetsetse kuti tikucita zonse zotheka kuti tilimbikitse mtendele na mgwilizano mu mpingo.—Aef. 4:3. w21.07 19 ¶18-19

Ciŵelu, February 25

Mlongo wako adzauka. —Yoh. 11:23.

Mungakhale na cikhulupililo cakuti mudzawaonanso okondedwa anu amene anamwalila. Kugwetsa misozi kwa Yesu potonthoza mabwenzi ake acisoniwo, ni umboni wakuti iye ni wofunitsitsa kukaukitsa akufa. (Yoh. 11:35) Muzilimbikitsa amene akulila. Yesu sanangolila pamodzi na Marita komanso Mariya, koma anawamvetsela na kuwalimbikitsa. (Yoh. 11:25-27) Nafenso tizicita cimodzi-modzi kwa amene akulila. M’bale Dan, amene ni mkulu ku Australia, anati: “Mkazi wanga atamwalila, n’nali kufunikila cilimbikitso. Mabanja angapo anali kubwela usana na usiku kudzanimvetsela. Iwo anali kunilola kulila, ndipo sanacite nane manyazi. Kuwonjezela apo, anadzipeleka kugwila nchito za pakhomo monga kutsuka motoka, kugula zinthu, na kuphika, nikalephela kucita zimenezi panekha. Komanso anali kupemphela nane kaŵili-kaŵili. Iwo anaonetsa kuti ni mabwenzi azoona, komanso abale amene ‘anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.’”—Miy. 17:17. w22.01 16 ¶8-9

Sondo, February 26

Munthu amene khutu lake limamvetsela cidzudzulo copatsa moyo, amakhala pakati pa anthu anzelu.—Miy. 15:31.

Yehova amatifunila zabwino. (Miy. 4:20-22) Iye akatipatsa uphungu kupitila m’Mawu ake, m’zofalitsa zozikika pa Baibo, kapena Mkhristu wokhwima mwauzimu, ndiye kuti amatikonda. (Aheb. 12:9, 10) Ikani maganizo pa uphunguwo osati mmene aupelekela. Nthawi zina, tingaone kuti uphungu sunapelekedwe m’njila yabwino. N’zoona kuti aliyense wopeleka uphungu, ayenela kuupeleka m’njila yakuti zisakhale zovuta kuulandila. (Agal. 6:1) Koma ngati ndife tikupatsidwa uphungu, tingacite bwino kusumika maganizo pa phindu la uphunguwo, ngakhale pamene taona kuti sunapelekedwe m’njila yabwino. Tingadzifunse kuti: ‘Ngakhale kuti sin’nakonde mmene uphungu wapelekedwela, kodi pali cina cake cimene niphunzilapo pa uphunguwo? Kodi sininganyalanyaze zophophonya za wopeleka uphunguwo n’colinga cakuti nipindule nawo?’ N’cinthu canzelu kwa ife kuona mmene tingaseŵenzetsele uphunguwo kuti tipindule. w22.02 12 ¶13-14

Mande, February 27

Zikumbutso za Yehova ndi zodalilika, zimapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu.—Sal. 19:7.

Yehova amadziŵa kuti zimafuna nthawi komanso khama, kuti tithetse maganizo olakwika na zizolowezi zoipa. (Sal. 103:13, 14) Koma kupitila m’Mawu ake, mzimu wake, na gulu lake, Yehova amatipatsa nzelu, mphamvu, na thandizo kuti tisinthe umunthu wathu. Gwilitsilani nchito Baibo kuti mudzisanthule mofikapo. Mawu a Mulungu ali ngati galasi. Angakuthandizeni kusanthula maganizo anu, zokamba zanu, na zocita zanu. (Yak. 1:22-25) Ndipo nthawi zonse Yehova ni wokonzeka kukuthandizani. Iye angakuthandizeni bwino kwambili, cifukwa amadziŵa za mumtima mwanu. (Miy. 14:10; 15:11) Conco, muzipemphela kwa iye nthawi zonse, na kuŵelenga Mawu ake tsiku lililonse. Khulupililani kuti miyezo ya Yehova ni yabwino koposa. Zonse zimene Yehova amatiuza kucita zimakhala zopindulitsa. Aja amene amatsatila miyezo yake amadzipezela ulemu, amakhala na umoyo waphindu, ndiponso amakhala na cimwemwe ceniceni.—Sal. 19:8-11. w22.03 4 ¶8-10

Ciŵili, February 28

Ganizilani mofatsa za khoma lake lolimba. Yendelani nsanja zake zokhalamo, kuti mudzasimbile m’badwo wam’tsogolo.—Sal. 48:13.

Timalambila Yehova tikamamanga malo olambilila na kuwasamalila. Baibo imakamba kuti nchito yomanga cihema colambilila na kucikongoletsa, inali ‘nchito yopatulika.’ (Eks. 36:1, 4) Masiku anonso, Yehova amaona nchito yomanga Nyumba za Ufumu na zimango zina za gulu kukhala yopatulika. Abale na alongo ena amataila maola oculuka pogwila nchito zimenezi. Timawayamikila kwambili abale athu amene amadzipeleka pocilikiza nchito ya Ufumu. Cina, iwo amagwilanso nchito yolalikila. Ndipo ena a iwo angafune kuyamba upainiya. Akulu mu mpingo angacilikize nchito ya mamangidwe mwa kusazengeleza kuika abale na alongo athu akhama amenewa kukhala apainiya ngati iwo ayenelela. Kaya tili na luso la mamangidwe kapena ayi, tonsefe tingatengeko mbali posamalila malo athu olambilila ndiponso kuti akhale mumkhalidwe wabwino. w22.03 22 ¶11-12

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani