Moseŵenzetsela Kabuku Kano
Pa mapeji otsatila, mudzapezapo lemba la tsiku lililonse na ndemanga yake. Ngakhale kuti mungaŵelenge lemba na ndemanga yake nthawi iliyonse, ambili amakonda kuŵelenga m’mwaŵa, cifukwa kumawathandiza kumaganizilapo pa lembalo tsiku lonse. Kukambilana lemba monga banja n’kopindulitsa ngako. Mabanja a Beteli zungulile dziko lapansi amacita zimenezi pa cakudya cam’maŵa.
Ndemanga zake zinatengedwa mu Nsanja ya Mlonda (w) ya April 2021 mpaka March 2022. Nambala yotsatila deti ya Nsanja ya Mlonda ni nambala ya peji (mapeji) m’magazini imeneyo, ndiyeno pabwela manambala a ndime mmene mwacokela ndemangayo. (Onani citsanzo pansipa.) Mungaŵelenge mfundo zina zowonjezela m’nkhani yonse.