LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es24 masa. 47-57
  • May

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • May
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2024
  • Tumitu
  • Citatu, May 1
  • Cinayi, May 2
  • Cisanu, May 3
  • Ciŵelu, May 4
  • Sondo, May 5
  • Mande, May 6
  • Ciŵili, May 7
  • Citatu, May 8
  • Cinayi, May 9
  • Cisanu, May 10
  • Ciŵelu, May 11
  • Sondo, May 12
  • Mande, May 13
  • Ciŵili, May 14
  • Citatu, May 15
  • Cinayi, May 16
  • Cisanu, May 17
  • Ciŵelu, May 18
  • Sondo, May 19
  • Mande, May 20
  • Ciŵili, May 21
  • Citatu, May 22
  • Cinayi, May 23
  • Cisanu, May 24
  • Ciŵelu, May 25
  • Sondo, May 26
  • Mande, May 27
  • Ciŵili, May 28
  • Citatu, May 29
  • Cinayi, May 30
  • Cisanu, May 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2024
es24 masa. 47-57

May

Citatu, May 1

Zimenezi zitatha, . . . ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliŵelenga, locokela m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse.​—Chiv. 7:9.

Pambuyo poona gulu lakumwamba, Yohane anaona “khamu lalikulu.” Mosiyana na a 144,000, khamu limeneli palibe angathe kuliŵelenga. Tiphunzilapo ciyani zokhudza iwo? Yohane anauzidwa kuti: “Amenewa ndi amene atuluka m’cisautso cacikulu, ndipo acapa mikanjo yawo ndi kuiyeletsa m’magazi a Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:14) Likadzapulumuka cisautso cacikulu, “khamu lalikulu” limeneli lidzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi, ndipo lidzapindula na madalitso osaneneka. (Sal. 37:9-11, 27-29; Miy. 2:21, 22; Chiv. 7:16, 17) Kaya tinasankhidwa kuti tikapite kumwamba kapena kukhala padziko lapansi, kodi timakhulupilila kuti tidzaona kukwanilitsidwa kwa Chivumbulutso caputala 7? Inde, tiyenela kukhulupilila. Iyi idzakhala nthawi yokondweletsa kwambili ku magulu onse aŵili a atumiki a Mulungu. Pa nthawiyo, tidzakhala na cimwemwe codzaza tsaya poona kuti tinasankha kucilikiza ulamulilo wa Yehova. w22.05 16 ¶6-7

Cinayi, May 2

Yehova amapeleka nzelu.​—Miy. 2:6.

Ngati munapangapo cisankho cofunika kwambili, mosakayikila munapempha nzelu popanga cisankhoco. (Yak. 1:5) Mfumu Solomo analemba kuti: “Nzelu ndiyo cinthu cofunika kwambili.” (Miy. 4:7) Apa Solomo sanali kutanthauza nzelu ina iliyonse ayi. Anali kukamba za nzelu yocokela kwa Yehova Mulungu. Koma kodi nzelu yaumulungu imeneyi ingatithandize kuthana na mavuto amene timakumana nawo? Inde ingatithandize. Njila imodzi imene ingatithandize kukhala na nzelu zenizeni, ni kuphunzila na kuseŵenzetsa zimene amuna aŵili amene anali anzelu kwambili anaphunzitsa. Coyamba, ganizilani za Solomo. Baibo imati Mulungu ‘anapatsa Solomo nzelu zopanda malile ndi luso lomvetsa zinthu losaneneka.’ (1 Maf. 4:29) Kenaka, ganizilani za Yesu amene anali wanzelu kwambili kuposa wina aliyense. (Mat. 12:42) Ponena za iye, ulosi unati: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzelu [komanso] womvetsa zinthu.”​—Yes. 11:2. w22.05 20 ¶1-2

Cisanu, May 3

Kufikila nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatila.​—Sal. 71:18.

Kudziikila zolinga zauzimu na kuzikwanilitsa kulibe msinkhu. Onani citsanzo ici ca mlongo wina wa zaka 75 dzina lake Beverley. Iye anali na matenda aakulu amene anali kumulepheletsa kuyenda. Koma anali kufunitsitsa kutengako mbali mokwanila pa kampeni yoitanila anthu ku Cikumbutso. Conco, anadziikila zolinga. Mlongo Beverley anakondwela ngako atakwanilitsa colinga cake cotengako mbali pa kampeniyo. Khama lake linalimbikitsa ena kukhala okangalika mu ulaliki. Yehova amayamikila utumiki umene abale na alongo okalamba amacita, olo kuti mikhalidwe siwalola kucita zambili. (Sal. 71:17) Dziikileni zolinga zimene muona kuti mungakwanilitse. Kulitsani makhalidwe amene adzapangitsa kuti Yehova akukondeni. Komanso, phunzilani maluso amene angapangitse kuti Mulungu akugwilitsileni nchito kwambili kudzela m’gulu lake. Yesani kupeza mipata yotumikila abale na alongo anu mokwanila. Monga Timoteyo, Yehova adzakuthandizani kuti ‘anthu onse aone kuti mukupita patsogolo.’​—1 Tim. 4:15. w22.04 27 ¶18-19

Ciŵelu, May 4

Kuyambila pamene unali wakhanda, wadziŵa malemba oyela.​—2 Tim. 3:15.

Nanga bwanji ngati inu monga kholo mwacita zonse zotheka, koma mwana wanu wina n’kukuuzani kuti safuna kutumikila Yehova? Pewani kuganiza kuti inu monga kholo mwalephela udindo wanu. Yehova anapatsa aliyense wa ife, kuphatikizapo mwana wanu, ufulu wosankha kaya kum’tumikila kapena ayi. Musataye mtima cifukwa tsiku lina adzabwelela kwa iye. Muzikumbukila fanizo la mwana woloŵelela. (Luka 15:11-19, 22-24) Mwanayo analoŵelela m’makhalidwe oipa, koma pamapeto pake iye anabwelela. Inu makolo, mwapatsidwa udindo wabwino kwambili wothandiza ana anu kukhala alambili a Yehova. (Sal. 78:4-6) Iyi si nchito yopepuka. Conco, timakuyamikila mocokela pansi pa mtima cifukwa coyesetsa kuthandiza ana anu kukonda Yehova, komanso kuwalela m’malangizo ake na kuwaphunzitsa kaganizidwe kake. Mungakhale otsimikiza kuti Atate wathu wacikondi wakumwamba adzakondwela nanu.​—Aef. 6:4. w22.05 30-31 ¶16-18

Sondo, May 5

Thupi lonselo limakula podzimanga lokha.​—Aef. 4:16.

Kuti tilimbikitse mtendele na mgwilizano mu mpingo, aliyense payekha ayenela kupatsa Mulungu zimene angakwanitse. Ganizilani za Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Iwo anali na mphatso komanso ma utumiki osiyana-siyana. (1 Akor. 12:4, 7-11) Koma izi sizinawapangitse kuyamba kupikisana kapena kubweletsa magaŵano pakati pawo. M’malo mwake, Paulo analimbikitsa aliyense kucita zimene zikanathandiza kuti “amange thupi la Khristu.” Iye analembela Aefeso kuti: “Thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwacikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwilizana mwa mfundo iliyonse yogwila nchito yake yofunikila.” (Aef. 4:1-3, 11, 12) Amene anacita zimenezo analimbikitsa mtendele na mgwilizano, zimene timaona m’mipingo masiku ano. Muziyesetsa kupewa kudziyelekezela na ena. M’malo mwake, phunzilani kwa Yesu na kuyesetsa kutengela makhalidwe ake.Khalani wotsimikiza kuti Yehova “si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu.” (Aheb. 6:10) Iye amayamikila kufunitsitsa kwanu kuti mum’kondweletse. w22.04 14 ¶15-16

Mande, May 6

Khristu Yesu anabwela m’dziko kudzapulumutsa ocimwa.​—1 Tim. 1:15.

Zili bwino kuti si udindo wathu kugamula kuti Yehova akhululukile wocimwa kapena ayi. Ngakhale n’conco, pali mbali imene tilipo na udindo. Kodi ni mbali iti? Nthawi zina, munthu angatilakwile kwambili. Komabe, iye angapepese kwa ife, na kupempha kuti tim’khululukile. Koma nthawi zina sangacite zimenezo. Zikakhala conco, tingam’khululukilebe m’lingalilo lakuti tingapewe kum’sungila cakukhosi kapena kumukwiyila. Kukamba zoona, izi zingatenge nthawi yaitali komanso khama, maka-maka ngati cimene anatilakwila cikutipweteka mtima kwambili. Nsanja ya Mlonda ya September 15, 1994 inati: “Mukakhululukila wocimwayo, zimenezo sizikutanthauza kuti mukulekelela chimolo. Mkhristu amene amakhululukila ena, amakhala na cidalilo cakuti Yehova adzaweluza nkhaniyo mwacilungamo. Iye ni Woweluza wolungama wa cilengedwe conse, ndipo adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika panthawi yake.” w22.06 9 ¶6-7

Ciŵili, May 7

Yembekezela Yehova.​—Sal. 27:14.

Yehova analonjeza kuti m’nthawi yathu ino, iye adzasonkhanitsa anthu kucokela ku dziko lililonse, fuko lililonse, komanso cinenelo ciliconse, kuti adzamulambile mogwilizana. Masiku ano, gulu lapadela limeneli limachedwa “khamu lalikulu.” (Chiv. 7:9, 10) Ngakhale kuti m’gulu limeneli muli amuna, akazi, komanso ana a zikhalidwe zosiyana-siyana, onse ni banja limodzi lamtendele ndiponso logwilizana la padziko lonse. (Sal. 133:1; Yoh. 10:16) Iwo ni okonzeka nthawi zonse kuuzako aliyense za ciyembekezo cawo ca dziko labwino. (Mat. 28:19, 20; Chiv. 14:6, 7; 22:17) Ngati ndinu wa khamu lalikulu, ndithudi muli na ciyembekezo ca tsogolo lowala. Mdyerekezi amafuna kutitayitsa ciyembekezo cathu. Colinga cake ni kutipangitsa kukhulupilila kuti Yehova sadzasunga malonjezo ake. Satana akatitayitsa ciyembekezo cathu, sitingakhale olimba mtima ndipo tingaleke kutumikila Yehova. w22.06 20-21 ¶2-3

Citatu, May 8

Ciyembekezo cimene tili nacoci cili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika.​—Aheb. 6:19.

Ciyembekezo cathu colimba cimatithandiza kusasunthika pokumana na mavuto okhala ngati cimphepo camkuntho, cifukwa timadziŵa kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Kumbukilani kuti Yesu anakambilatu kuti tidzazunzidwa. (Yoh. 15:20) Conco, kuganizila mphoto imene anatilonjeza m’tsogolo kudzatithandiza kusasunthika pa umoyo wathu wacikhristu. Onani mmene ciyembekezo cinathandizila Yesu kuimabe nji, mosasamala kanthu za imfa yoŵaŵa imene inali patsogolo pake. Pa Pentekosite mu 33 C.E., mtumwi Petulo anagwila mawu ulosi wa m’buku la Masalimo, wofotokoza mmene Yesu analili wodekha komanso wacidalilo. Iye anati: “Ine ndidzakhala ndi ciyembekezo, cifukwa simudzasiya moyo wanga m’Manda, ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupilika wanu livunde. . . . Cifukwa ca nkhope yanu ndidzakhala ndi cimwemwe cosefukila.” (Mac. 2:25-28; Sal. 16:8-11) Yesu anali na ciyembekezo cotsimikizika mwa Mulungu kuti adzamuukitsa, komanso kuti adzabwelela kumwamba kukakhalanso na Atate wake.​—Aheb. 12:2, 3. w22.10 25 ¶4-5

Cinayi, May 9

Tonsefe timapunthwa nthawi zambili.​—Yak. 3:2.

Pa nthawi ina, atumwi ake aŵili​—Yakobo na Yohane—​anapempha amayi awo kuti apite kwa Yesu kukawapemphela udindo wapamwamba mu Ufumu wa Mulungu. (Mat. 20:20, 21) Mwakutelo, Yakobo na Yohane anaonetsa mzimu wodzikuza komanso wodzikonda. (Miy. 16:18) Yakobo na Yohane sindiwo okha anaonetsa mzimu wosayenela pa cocitikaco. Ponena za atumwi ena, Baibo imati: “Ophunzila 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya ndi amuna aŵili apachibalewo.” (Mat. 20:24) Tangoganizilani mkangano umene unabuka pakati pa Yakobo, Yohane, komanso atumwi enawo. Kodi Yesu anacitanji na cocitikaci? Iye sanakhumudwe nawo atumwiwo. Ndipo sanakambe kuti adzawasiya n’kufuna-funa atumwi ena amene ni odzicepetsa kwambili, komanso amene azikondana nthawi zonse. Komabe, Yesu anakambilana nawo moleza amuna oona mtima amenewo. (Mat. 20:25-28) Iye anapitiliza kucita nawo mwacikondi atumwiwo. w23.03 28-29 ¶10-13

Cisanu, May 10

Mwana wanga, khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.​—Miy. 27:11.

Mwacita kale zambili. Mwakhala mukuphunzila Baibo mwina kwa zaka zingapo. Ndipo kuphunzilako kwakuthandizani kukhulupilila kuti Baibo ni Mawu a Mulungu. Kuposa pamenepo, mwadziŵanso Mwiniwake wa Mawu a m’buku lopatulika, na kuyamba kum’konda. Cikondi canu pa Yehova cinakula moti munafika pokhala mtumiki wodzipatulila wobatizika. Munapanga cisankho cabwino kwambili. Mosakayikila, cikhulupililo canu cinayesedwa m’njila zambili musanabatizike. Ndipo mudzakumanabe na mayeso ena pamene mukukula mwauzimu. Satana adzafuna kufooketsa cikondi canu pa Yehova, kuti muleke kum’tumikila. (Aef. 4:14) Koma conde, musalole zimenezo kukucitikilani. Kodi n’ciyani cingakuthandizeni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova na kusungabe lonjezo limene munapeleka podzipatulila? Muyenela kupitabe patsogolo, kapena kuti ‘kuyesetsa mwakhama’ kuti mukhale Mkhristu wokhwima.​—Aheb. 6:1. w22.08 2 ¶1-2

Ciŵelu, May 11

Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako monga mmene Yehova Mulungu wako anakulamulila, kuti masiku ako atalike, ndi kuti zinthu zikuyendele bwino.​—Deut. 5:16.

M’banja, aliyense ali na udindo wosunga nkhani zacinsinsi za banja lawo. Mwacitsanzo, mkazi wacikhristu angakhale na kacizolowezi kamene mwamuna wake amakaona kuti n’koseketsa. Kodi mwamunayo ayenela kuuzako ena zimenezo, na kunyazitsa mkazi wake? Ayi. Cifukwa comukonda mkazi wake, sangacite zinthu zimene zingam’kwiyitse akazimva. (Aef. 5:33) Anyamata na atsikana amafunikila ulemu wowayenelela, ndipo makolo ayenela kuikumbukila mfundo imeneyi. Iwo sayenela kucititsa manyazi ana awo amenewo pomauza ena zimene amalakwitsa. (Akol. 3:21) Ana nawonso ayenela kukhala osamala kuti asamaulule nkhani zacinsinsi za m’banja mwawo, kuti asacititse manyazi a m’banja mwawo. Aliyense m’banja akamacita mbali yake mwa kusunga nkhani zacinsinsi zokhudza banja, banjalo limakhala logwilizana kwambili. w22.09 10 ¶9

Sondo, May 12

Mvetselani izi inu a Yobu: Imani cilili ndi kuganizila.​—Yobu 37:14.

Yehova analankhula na Yobu kuti am’kumbutse nzelu zake zakuya, na cikondi cake cacikulu pa zolengedwa zake. Iye anakamba pa nyama zambili zocititsa cidwi. (Yobu 38:1, 2; 39:9, 13, 19, 27; 40:15; 41:1, 2) Yehova anagwilitsanso nchito mnyamata wina wokhulupilika dzina lake Elihu kuti alimbikitse Yobu na kum’tonthoza. Elihu anam’tsimikizila kuti Yehova nthawi zonse amapeleka mphoto kwa alambili ake cifukwa ca kupilila kwawo. Cina, Yehova anasonkhezela Elihu kuti apeleke uphungu wacikondi kwa Yobu. Elihu anathandiza Yobu kusaganizila kwambili za iye mwini pom’kumbutsa kuti iye ni wocepa poyelekezela na Yehova, Mlengi wa cilengedwe conse. Yehova anapatsanso Yobu zocita. Anamuuza kuti apemphelele anzake atatu amene anali atacimwa. (Yobu 42:8-10) Kodi Yehova amatithandiza bwanji masiku ano tikakumana na mayeso aakulu? Yehova sakamba nafe mwacindunji monga anacitila kwa Yobu. Koma amakamba nafe kupitila m’Mawu ake Baibo.​—Aroma 15:4. w22.08 11 ¶10-11

Mande, May 13

Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusacita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.​—Aroma 14:21.

Mu mpingo wa ku Roma, munali Akhristu Aciyuda komanso amitundu ina. Cilamulo ca Mose citatha, alambili a Yehova analoledwa kudya cakudya ciliconse. (Maliko 7:19) Kucokela nthawiyo, Akhristu ena Aciyuda anamasuka n’kuyamba kudya zakudya zamitundu yosiyana-siyana. Koma ena sanatelo. Conco, mu mpingowo munakhala magaŵano cifukwa ca nkhani imeneyi. Mtumwi Paulo anaonetsa kufunika kosungitsa mtendele. Iye anathandiza Akhristu anzake kuona kuti kusamvana kumeneko kukanawononga mgwilizano wawo komanso wa mpingo. (Aroma 14:19, 20) Analinso wokonzeka kusintha kacitidwe ka zinthu kuti apewe kukhumudwitsa ena. (1 Akor. 9:19-22) Nafenso tingalimbikitse ena na kusungitsa mtendele mwa kupewa kukangana pa nkhani zimene zangokhala makonda a munthu mwini. w22.08 22 ¶7

Ciŵili, May 14

Yehova . . . amakonda munthu wocita cilungamo.​—Miy. 15:9.

Tikadziikila colinga mu utumiki wa Yehova, timayesetsa kuti ticikwanilitse. N’cimodzimodzinso ngati tikufuna kukhala anthu ocita zacilungamo. Ndipo Yehova adzatithandiza moleza mtima kuti pang’ono-m’pang’ono tikulitse khalidwe limeneli. (Sal. 84:5, 7) Mwa cikondi cake, Yehova amatikumbutsa kuti kucita cilungamo si kolemetsa. (1 Yoh. 5:3) M’malo mwake, kumatiteteza, ndipo timafunikila citetezo cimeneco tsiku lililonse. Kumbukilani zida zankhondo zauzimu zimene mtumwi Paulo anafotokoza. (Aef. 6:14-18) Kodi ni cida citi cimene cinali kuteteza mtima wa msilikali? Cinali “codzitetezela pacifuwa cacilungamo,” cimene cimaimila malamulo a Yehova olungama. Monga mmene codzitetezela pacifuwa cacilungamo cimatetezela mtima weniweniwo, nawonso malamulo a Yehova olungama amateteza mtima wathu wophiphilitsa, umene ni umunthu wathu wamkati. Conco pa zida zathu zankhondo, tizionetsetsa kuti tavalanso codzitetezela pacifuwa cacilungamo.​—Miy. 4:23. w22.08 29 ¶13-14

Citatu, May 15

Mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kale-kale.​—Yes. 40:8.

Mawu a Mulungu akhala akupeleka citsogozo cabwino kwa amuna na akazi okhulupilika kwa zaka masauzande. Kodi zimenezi zatheka bwanji? Yehova anaonetsetsa kuti akatswili akopela malemba opatulika. Ngakhale kuti akatswiliwo anali opanda ungwilo, iwo anakopela malembawo mosamala kwambili. Mwacitsanzo, ponena za Malemba a Ciheberi, katswili wina wa Baibo anakamba kuti: “Ndife otsimikiza kuti palibe buku lamakedzana limene analikopolola molondola kwambili kuposa Baibo.” Conco, ndife otsimikiza kuti zimene timaŵelenga m’Baibo ni maganizo a Yehova, Mwiniwake wa Baibo. Yehova ndiye Gwelo la “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.” (Yak. 1:7) Baibo ni imodzi mwa mphatso zabwino koposa zimene Yehova anatipatsa. Munthu akatipatsa mphatso, zimaonetsa kuti iye amatidziŵa bwino komanso amadziŵa zimene timafunikila. N’cimodzi-modzi na Mulungu amene anatipatsa Baibo. Tikamaiŵelenga timaphunzila zambili za Yehova. Timaphunzila kuti iye amatidziŵa bwino komanso zimene timafunikila. w23.02 2-3 ¶3-4

Cinayi, May 16

Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova.​—Yes. 11:9.

Idzakhala nthawi yokondweletsa ngako anthu akadzayamba kuukitsidwa pano padziko lapansi mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000. Onse amene okondedwa awo anamwalila amalakalaka kudzawaonanso. Nayenso Yehova amalakalaka kudzawaonanso. (Yobu 14:15) Tangoganizani cimwemwe cimene aliyense padziko lapansi adzakhala naco podzawaonanso okondedwa ake. “Olungama,” amene maina awo analembedwa m’buku la moyo, “adzauka kuti alandile moyo.” (Mac. 24:15; Yoh. 5:29) N’kutheka kuti ambili mwa okondedwa athu amene anamwalila, adzakhala pakati pa anthu oukitsidwa koyambilila pano padziko lapansi. Kuwonjezela apo, “osalungama,” amene analibe mwayi wodziŵa Yehova kapena kum’tumikila mokhulupilika asanamwalile, “adzauka kuti aweluzidwe.” Anthu onse oukitsidwa adzafunika kuphunzitsidwa. (Yes. 26:9; 61:11) Motelo, padzakhazikitsidwa pulogilamu yaikulu yophunzitsa imene sinacitikepo m’mbili yonse ya anthu.​—Yes. 11:10. w22.09 20 ¶1-2

Cisanu, May 17

Iye ndi Mulungu wamoyo.​—Dan. 6:26.

Yehova anaonetsa kuti ali na ulamulilo waukulu koposa pa mgwilizano wa mafumu. Iye anamenyela nkhondo Aisiraeli, powathandiza kugonjetsa mgwilizano wa mafumu acikanani okwana 31, komanso kugonjetsa madela aakulu a dziko lolonjezedwa. (Yos. 11:4-6, 20; 12:1, 7, 24) Mobwelezabweleza, Yehova wakhala akuonetsa kuti ni Wamkulukulu. Pamene Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inadzitama cifukwa ca ‘mphamvu zake zazikulu na ulemelelo wake waukulu,’ m’malo movomeleza modzicepetsa kuti Yehova ndiye woyenela kutamandidwa, Mulungu anamucititsa misala. Koma Nebukadinezara atacila misala yake ‘anatamanda Wam’mwambamwamba,’ ndipo iye anavomeleza kuti “ulamulilo [wa Yehova] udzakhalapo mpaka kalekale.” Anakambanso kuti: “Palibe aliyense amene angaletse dzanja lake.” (Dan. 4:30, 33-35) Wamasalimo anati: “Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala colowa cake.” (Sal. 33:12) Ha! tili na cifukwa cabwino cotani nanga cosungila umphumphu wathu kwa Yehova. w22.10 15-16 ¶13-15

Ciŵelu, May 18

Mawu anu onse ndi coonadi.​—Sal. 119:160.

Maulosi ambili a m’Baibo amene akwanilitsika kale amalimbitsa cidalilo cathu kuti malonjezo a Mulungu okhudza tsogolo lathu adzakwanilitsika. Timamva mmene anamvela wamasalimo amene anapemphela kwa Yehova kuti: ‘Ndikulakalaka cipulumutso canu, pakuti ndayembekezela mawu anu.’ (Sal. 119:81) Kupyolela m’Baibo, Yehova mokoma mtima watipatsa “ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino.” (Yer. 29:11) Ciyembekezo cathu ca za mtsogolo sicidalila zoyesa-yesa za anthu koma pa malonjezo a Yehova. Tiyeni tipitilize kulimbitsa cikhulupililo cathu m’Mawu a Mulungu mwa kuphunzila maulosi a m’Baibo mwakhama. Umboni wina umene watithandiza kuikhulupilila Baibo, ni zotulukapo zabwino zimene zimakhalapo anthu akamaseŵenzetsa uphungu wake. (Sal. 119:66, 138) Mwacitsanzo, okwatilana amene panthawi ina anatsala pang’ono kusudzulana, tsopano ni ogwilizana ndipo ni acimwemwe. Ana awo lomba amakondwela kukhala m’banja lacikhristu mmene makolo awo amawasamalila bwino na kuwakonda.​—Aef. 5:22-29. w23.01 5 ¶12-13

Sondo, May 19

Kondwelani ndi ciyembekezoco.​—Aroma 12:12.

Ganizilani cabe mmene mwapindulila na malonjezo a m’Mawu a Mulungu amene akwanilitsidwa kale. Mwacitsanzo, Yesu analonjeza kuti Atate wake adzakupatsani zofunikila pa umoyo. (Mat. 6:32, 33) Cina, Yesu anakutsimikizilani kuti Yehova adzakupatsani mzimu woyela mukam’pempha. (Luka 11:13) Yehova wakwanilitsadi malonjezo amenewa. Mungaganizilenso malonjezo ena amene iye wakwanilitsa pa inu. Mwacitsanzo, anakulonjezani kuti adzakukhululukilani, kukutonthozani, na kukudyetsani mwauzimu. (Mat. 6:14; 24:45; 2 Akor. 1:3) Conco, mukamaganizila zimene Mulungu wakucitilani, ciyembekezo canu pa zimene adzakucitilani m’tsogolo cidzalimbilako. Sitikayikila kuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake. Wamasalimo analemba kuti: “Wodala ndi munthu . . . amene ciyembekezo cake cili mwa Yehova Mulungu wake, . . . Wosunga coonadi mpaka kalekale.”​—Sal. 146:5, 6. w22.10 27 ¶15; 28 ¶17

Mande, May 20

Koma kuwala kwa Yehova kudzafika pa iwe.​—Yes. 60:2.

Kodi ulosi wokamba za kubwezeletsa kulambila koyela umatikhudza masiku ano? Inde! Motani? Kungoyambila mu 1919, anthu mamiliyoni amasuka mu ukapolo wa Babulo Wamkulu, amene ni ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga. Iwo atsogoleledwa ku malo abwino kwambili kuposa Dziko Lolonjezedwa la Isiraeli. Malo amenewo ni paradaiso wauzimu. (Yes. 51:3; 66:8) Kungoyambila mu 1919, Akhristu odzozedwa akhala akusangalala m’paradaiso wauzimu ameneyu. Nawonso amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, amene ni a nkhosa zina, aloŵa m’paradaiso wauzimu ameneyu, ndipo akusangalala na madalitso a Yehova oculuka. (Yoh. 10:16; Yes. 25:6; 65:13) Paradaiso wauzimu amene iwo alimo ali padziko lonse lapansi. Motelo, kaya tikukhala dziko liti, tingakhale m’paradaiso wauzimu ameneyu malinga ngati ticilikiza kulambila koona mokhulupilika. w22.11 11-12 ¶12-15

Ciŵili, May 21

Inu Yehova, inutu mwakhalapo kuyambila kalekale. Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyela, inu simufa.​—Hab. 1:12.

Kodi mumavutika kumvetsa kuti Yehova wakhalapo “mpaka kalekale”? (Yes. 40:28) Ngati mumaona conco, si inu nokha. Ponena za Mulungu, Elihu anati: “Zaka zake n’zosaŵelengeka.” (Yobu 36:26) Ngati sitinamvetsetse zinazake, sizitanthauza kuti zinthu zimenezo n’zabodza. Mwacitsanzo, ngakhale kuti sitimvetsa zonse zokhudza mmene magetsi amaseŵenzela, kodi zitanthauza kuti magetsiwo kulibe? Ayi! Mofananamo, mfundo yakuti Yehova wakhala alipo kucokela muyaya ndipo adzakhalapobe mpaka muyaya, ife anthu sitingaimvetse. Koma kusamvetsa kumeneku sikutanthauza kuti mfundo imeneyi si yoona. Kudziŵa zoona ponena za Mlengi wathu sikudalila zimene timamvetsa zokhudza iye, kapena zimene sitingamvetse. (Aroma 11:33-36) Iye analipo kale zolengedwa zonse zisanakhaleko, kuphatikizapo dzuŵa na nyenyezi. Inde, iye anakhalako ‘asanayale kumwamba.’​—Yer. 51:15. w22.12 2-3 ¶3-4

Citatu, May 22

Pemphelo langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu.​—Sal. 141:2.

Nthawi zina, timapemphedwa kuti tiimileko ena m’pemphelo. Mwacitsanzo, mlongo amene akucititsa phunzilo la Baibo angapemphe mlongo mnzake kupeleka pemphelo. Popeza kuti mlongoyo angakhale kuti sakum’dziŵa bwino wophunzilayo, mwina iye angakonde kupeleka pemphelo lotsiliza pa phunzilolo. Izi zingam’patse mwayi wodziŵa zosoŵa za wophunzilayo zimene angachule m’pemphelo. M’bale angapemphedwe kuti apemphele pa kukumana kotenga malangizo a ulaliki, kapena pa msonkhano wa mpingo. Abale amene apatsidwa mwayi umenewu ayenela kukumbukila colinga ca msonkhanowo. Pemphelo siyenela kukhala njila yopelekela uphungu ku mpingo kapena zilengezo. Pa misonkhano yambili ya mpingo, mphindi 5 zimakhala za nyimbo na pemphelo. Conco, m’bale akapemphedwa kuti apemphele, sayenela kukamba “mawu ambili-mbili,” maka-maka kuciyambi kwa msonkhano.​—Mat. 6:7. w22.07 24 ¶17-18

Cinayi, May 23

Mudzamva phokoso la nkhondo ndi mbili za nkhondo. Izitu zisadzakucititseni mantha. Pakuti zimenezi ziyenela kucitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.​—Mat. 24:6.

Yesu analosela kuti m’masiku otsiliza, kudzakhala milili, kapena kuti kufalikila kwa matenda “m’malo osiyana-siyana.” (Luka 21:11) Kodi kudziŵa izi kumatithandiza bwanji kukhala na mtendele? Ife sitidabwa pakabuka matenda, cifukwa tikudziŵa kuti zikukwanilitsa mawu a Yesu. Conco, tili na cifukwa cabwino comvela langizo la Yesu kwa anthu okhala m’nthawi ya mapeto. Iye anati: “Izitu zisadzakucititseni mantha.” Panthawi ya mlili, cimakhala covuta kucita zinthu zimene tinali kucita kale. Koma musalole kuti mliliwo usokoneze phunzilo la inu mwini na kupezeka ku msonkhano. Zocitika zenizeni za anthu ena zopezeka m’zofalitsa zathu na mavidiyo, zidzakukumbutsani kuti abale na alongo auzimu akhalabe okhulupilika ngakhale kuti akukumana na mavuto. w22.12 17 ¶4, 6

Cisanu, May 24

Zinthu zosayembekezeleka zimagwela onsewo.​—Mlal. 9:11.

Yakobo anali kuonetsa poyela kuti mwana wake Yosefe amam’konda kwambili. (Gen. 37:3, 4) Izi zinapangitsa kuti ana ena a Yakobo ayambe kum’citila nsanje mng’ono wawo. Mpata utapezeka, iwo anam’gulitsa Yosefe kwa amalonda acimidiyani. Amalondawo anatenga Yosefe kupita naye ku dziko lakutali ku Iguputo, kumene anagulitsidwanso. Kumeneko anagulitsidwa kwa Potifara, mkulu wa asilikali olondela Farao. Umoyo wa Yosefe unasintha mosayembekezela. Anacoka pa kukhala mwana wokondeka, n’kukhala kapolo wacabe-cabe wa Mwiguputo! (Gen. 39:1) Nthawi zina timakumana na mavuto “amene amagwela anthu”​—kutanthauza mavuto amene anthu onse amakumana nawo. (1 Akor. 10:13) Kapena tingakumane na mavuto cabe cifukwa ndife ophunzila a Yesu. Mwacitsanzo, tinganyozedwe, kutsutsidwa, ngakhale kumangidwa kumene cifukwa ca cikhulupililo cathu. (2 Tim. 3:12) Kaya mukumane na mavuto otani, Yehova angakuthandizeni kuti mupambane. w23.01 14-15 ¶3-4

Ciŵelu, May 25

Popanda nkhuni moto umazima.​—Miy. 26:20.

Nthawi zina, tingaone kuti tiyenela kukambilana naye Mkhristu mnzathu amene anatilakwila. Koma coyamba, tingacite bwino kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi nikudziŵa bwino zonse zimene zinacitika?’ (Miy. 18:13) ‘Kodi n’kutheka kuti sicinali colinga cake kuti anikhumudwitse?’ (Mlal. 7:20) ‘Kodi inenso n’nalakwilapo wina mwanjila imeneyi?’ (Mlal. 7:21, 22) ‘Ngati ningakambilane naye nkhaniyo, kodi zidzangowonjezela mavuto?’ Tikamaganizila mafunso ngati amenewa, cikondi cathu pa m’bale wathuyo cidzatilimbikitsa kungonyalanyaza colakwaco. Ndipo aliyense payekha amaonetsa kuti ni wotsatila weniweni wa Yesu, akamaonetsa cikondi codzimana kwa abale na alongo, mosayang’ana zophophonya zawo. Mwakutelo, timathandiza ena kuzindikila cipembedzo coona, komanso kugwilizana nafe pa kulambila Yehova. Conco, tiyeni tiziyesetsa kumaonetsana cikondi, cimene cimadziŵitsa Akhristu oona. w23.03 31 ¶18-19

Sondo, May 26

Mulungu ndiye cikondi.​—1 Yoh. 4:8.

Baibo imaonetsa khalidwe lalikulu limene Mwinawake ali nalo, khalidwe la cikondi. Cifukwa Yehova amatikonda, iye sanatiunjikile malamulo ambili-mbili ovuta kuwatsatila. (Yoh. 21:25) Yehova amaonetsanso kuti amatikonda polankhula nafe m’Baibo m’njila imene imatilemekeza. Iye sanaikemo malamulo ambili-mbili, kapena kutitsogolela pa kalikonse komwe tingacite pa moyo wathu. M’malo mwake, iye anaikamo zitsanzo zenizeni za anthu, maulosi ocititsa cidwi, komanso uphungu wanzelu wotithandiza kupanga zisankho zabwino. Pa cifukwa cimeneci, Baibo imatisonkhezela kum’konda Mulungu na kumumvela kucokela pansi pa mtima. Baibo imaonetsa kuti Yehova amasamala kwambili za ife. Motani? M’mawu ake muli nkhani zoonetsa mmene anthu amamvela. Tingathe kumvetsa mmene anthuwa anali kumvela cifukwa iwonso anali ‘anthu monga ife tomwe.’ (Yak. 5:17) Coposa zonse, tikaona mmene Mulungu anali kucitila zinthu na anthuwo, timafika pomvetsa bwino kuti “Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.”​—Yak. 5:11. w23.02 6 ¶13-15

Mande, May 27

Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso.​—1 Pet. 5:8.

Buku lothela m’Baibo limayamba na mawu akuti: “Civumbulutso copelekedwa ndi Yesu Khristu, cimene Mulungu anamupatsa, kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene ziyenela kucitika posacedwapa.” (Chiv. 1:1) Conco, timacita cidwi kwambili na zocitika za m’dzikoli, kuti tidziŵe mmene zingakwanilitsile maulosi a m’Baibo. Ndipo tingakhale ofunitsitsa kukambilana zocitikazo pakati pathu. Komabe, tikamakambilana maulosi a m’Baibo, tizipewa kukamba zongoganizila. Cifukwa ciyani? Cifukwa sitifuna kulankhula zinthu zimene zingasokoneze mgwilizano mumpingo. Mwacitsanzo, tingamve atsogoleli andale akukambilana mmene angathetsele mkangano wina wake kuti abweletse bata na mtendele. M’malo molankhula zongoganizila kuti mawu amenewo akukwanilitsa ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:3, tiyenela kukhala na kamvedwe katsopano pa nkhani ngati zimenezi. Ngati makambilano athu azikika m’zofalitsa za gulu la Yehova, tidzathandiza mpingo kukhalabe wogwilizana pa “maganizo amodzi.”​—1 Akor. 1:10; 4:6. w23.02 16 ¶4-5

Ciŵili, May 28

Kwela pahachi yako cifukwa ca coonadi, kudzicepetsa ndi cilungamo, ndipo dzanja lako lamanja lidzakulangiza mu zinthu zocititsa mantha.​—Sal. 45:4.

N’cifukwa ciyani mumam’konda Yesu Khristu? Yesu amakonda coonadi, kudzicepetsa, na cilungamo. Ngati mumakonda coonadi na cilungamo, n’zosakayikitsa kuti mumam’kondanso Yesu Khristu. Tangoganizilani mmene Yesu anatetezela molimba mtima coonadi na cilungamo. (Yohane 18:37) Koma kodi Yesu amalimbikitsa bwanji khalidwe la kudzicepetsa? Yesu amalimbikitsa kudzicepetsa mwa citsanzo cake. Mwacitsanzo, iye amapeleka ulemelelo wonse kwa Atate wake, osati kwa iye mwini. (Maliko 10:17, 18; Yoh. 5:19) Kodi kudzicepetsa ngati kumeneku kumakukhudzani bwanji? Kodi sikumakulimbikitsani kukonda Mwana wa Mulungu na kutengela citsanzo cake? N’zosacita kufunsa. N’cifukwa ciyani Yesu ni wodzicepetsa? Cifukwa amakonda Atate wake amene ni wodzicepetsa, na kutengela citsanzo cawo. (Sal. 18:35; Aheb. 1:3) Kodi simukopeka kutengela Yesu amene amaonetsa bwino kwambili makhalidwe a Yehova? w23.03 3-4 ¶6-7

Citatu, May 29

Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.​—Mac. 24:15.

Baibo imakamba za magulu aŵili a anthu amene adzaukitsidwa kuti adzakhale na moyo kwamuyaya pa dziko lapansi. Magulu aŵili amenewa ni anthu “olungama” komanso “osalungama.” “Olungama” ni anthu amene anatumikila Yehova mokhulupilika pamene anali moyo. Kumbali inayo, “osalungama” ni anthu amene sanali kulambila Yehova asanafe. Popeza magulu onse aŵiliwa adzaukitsidwa, kodi tingati maina awo analembedwa m’buku la moyo? Anthu “olungama” asanafe, maina awo anali atalembedwa kale m’buku la moyo. Kodi maina awo anacotsedwamo m’bukulo atafa? Ayi, cifukwa m’maganizo mwa Yehova, iwo akali “amoyo.” Yehova “ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Izi zitanthauza kuti olungama akadzaukitsidwa padziko lapansi, maina awo adzakhala alimobe m’buku la moyo, ngakhale kuti poyamba adzakhala olembedwa na “pensulo.”​—Luka 14:14. w22.09 16 ¶9-10

Cinayi, May 30

Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni kuti aziulima ndi kuusamalila.​—Gen. 2:15.

Yehova anali kufuna kuti munthu woyamba azikondwela na zimene iye analenga. Mulungu atalenga Adamu, anam’patsa paradaiso wokongola kuti audziŵe bwino, kuusamalila, komanso kufutukula malile ake. (Gen. 2:8, 9) Tangoganizilani cimwemwe cimene Adamu anali kukhala naco akaona mbewu zikumela, komanso maluŵa akuphukila. Ha! unali mwayi wapadela cotani nanga kwa Adamu kusamalila munda wa Edeni. Yehova anapatsanso Adamu nchito yopatsa nyama maina. (Gen. 2:19, 20) Yehova akanafuna, akanapatsa yekha nyama zonse maina. Koma anapeleka mwayi umenewo kwa Adamu. Mosakayikila, Adamu asanazipatse maina nyama, anali kuyang’anitsitsa mwacidwi makhalidwe na zocita za nyamazo. Iye ayenela kuti anakondwela nayo kwambili nchito imeneyi. Izi zinam’thandiza kuyamikila nzelu na luso la kulenga zinthu la Atate wake. w23.03 15 ¶3

Cisanu, May 31

Udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kale-kale.​—Dan. 2:44.

Britain na America, amene akuimilidwa na mapazi a cifanizilo cacikulu, ndiwo ulamulilo wothela wamphamvu padziko lonse umene Baibo inakambilatu. (Dan. 2:31-33) Sudzaloŵedwa m’malo na ulamulilo wina wa anthu. M’malo mwake, ulamulilowu pamodzi na maboma ena onse a anthu udzawonongedwa na Ufumu wa Mulungu pa Aramagedo. (Chiv. 16:13, 14, 16; 19:19, 20) Kodi ulosi umenewu umatipindulila bwanji? Ulosi wa Danieli umapeleka umboni winanso woonetsa kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto. Zaka zoposa 2,500 zapitazo, Danieli anakambilatu kuti ufumu wa Babulo ukadzatha, maulamulilo ena anayi amphamvu padziko lonse adzakhudza kwambili zocita za anthu a Mulungu. Kuwonjezela apo, iye anaonetsa kuti ulamulilo wa Britain na America udzakhala wothela pa maulamulilo amenewa. Izi zimatilimbikitsa na kutipatsa ciyembekezo cakuti posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzaseselatu maboma onse a anthu, ndipo udzalamulila dziko lonse lapansi. w22.07 4 ¶9; 5 ¶11-12

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani