July
Mande, July 1
Ukhale citsanzo kwa okhulupilika m’kalankhulidwe.—1 Tim. 4:12.
Kulankhula ni mphatso yocokela kwa Mulungu wathu wacikondi. Komabe, mphatso ya kulankhula inagwilitsidwa nchito molakwika. Satana Mdyelekezi ananamiza Hava, ndipo bodzalo linapangitsa anthu kukhala ocimwa komanso opanda ungwilo. (Gen. 3:1-4) Adamu anaseŵenzetsa lilime lake molakwika pamene anaimba mlandu Hava, ngakhalenso Yehova, pa zimene iye mwini analakwitsa. (Gen. 3:12) Kaini ananena bodza kwa Yehova atapha m’bale wake Abele. (Gen. 4:9). N’covuta kupeza filimu imene mulibe mawu onyoza kapena otukwana. Cinanso, ana a sukulu amamva mawu otukwana kusukulu, ngakhalenso akulu-akulu ku malo anchito. Tikaleka kusamala, tingazolowele kwambili kumva mawu oipa moti nafenso tingayambe kumawakamba. Pokhala Akhristu, timafuna kukondweletsa Yehova, ndipo kucita izi kumafuna zambili kuposa kungopewa mawu otukwana. Timafuna kuseŵenzetsa mphatso ya mtengo wapatali ya kulankhula m’njila yabwino, imene ni kutamanda Mulungu wathu. w22.04 4 ¶1-3
Ciŵili, July 2
Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.—Mat. 6:24.
Yesu anali kuona zinthu zakuthupi moyenela. Anali kusangalala na cakudya komanso zakumwa. (Luka 19:2, 6, 7) Pa cocitika cina, iye anapanga vinyo wokoma kwambili. Ici cinali cozizwitsa cake coyamba. (Yoh. 2:10, 11) Ndipo patsiku limene anafa, anavala covala ca mtengo wapatali. (Yoh. 19:23, 24) Koma iye anapewa kuika maganizo ake pa zinthu zakuthupi. Yesu anaphunzitsa kuti ngati tifuna-funa Ufumu coyamba, Yehova adzaonetsetsa kuti watipatsa zonse zimene tifunikila. (Mat. 6:31-33) Ambili apindula cifukwa coseŵenzetsa malangizo anzelu a Mulungu pa nkhani ya ndalama. Ganizilani citsanzo ca m’bale wina amene ni mbeta, dzina lake Daniel. Iye anati: “Nili wacinyamata, n’nadziikila colinga cakuti zinthu zakuuzimu zikakhale patsogolo mu umoyo wanga.” Cifukwa cokhala na umoyo wosalila zambili, Daniel wakhala akuseŵenzetsa nthawi yake na maluso ake pa nchito zambili za m’gulu lathu. Anawonjezela kuti: “Ndalama sizingalingane na madalitso amene Yehova wanipatsa.” w22.05 21-22 ¶6-7
Citatu, July 3
[Yehova] anakuitanani kucoka mu mdima kuloŵa m’kuwala kwake kodabwitsa.—1 Pet. 2:9.
Timaonetsa kuti coonadi timacikonda mwa kuŵelenga Baibo, na zofalitsa zozikika pa Baibo. Kaya takhala m’coonadi nthawi yoculuka motani, nthawi zonse pamakhala zambili zofunika kuphunzila. Kuphunzila kumafuna khama, koma kumapindulitsa. Si tonse amene timakonda kuŵelenga na kuphunzila. Koma Yehova akutipempha kuti ‘tizifuna-funa’ coonadi na ‘kucifufuza’ kuti ticimvetsetse. (Miy. 2:4-6) Tikamayesetsa mwakhama, tidzapindula. Ponena za kuŵelenga Baibo payekha, m’bale Corey anakamba kuti amafufuza vesi iliyonse payokha. Iye anati: “Nimaŵelenga mawu a m’munsi, mavesi ena ofotokoza mfundo yofanana na ya vesiyo, ndiponso kufufuza m’mabuku ena. . . . Nimadziŵa zambili cifukwa coŵelenga mwa njila imeneyi.” Kaya timagwilitsa nchito njila imeneyi kapena ina, timaonetsa kuti timayamikila coonadi pothelapo nthawi yociphunzila, komanso kuikilapo mtima.—Sal. 1:1-3. w22.08 17 ¶13; 18 ¶15-16
Cinayi, July 4
Ine ndinali pambali pake monga mmisili waluso. Tsiku ndi tsiku, iye anali kusangalala kwambili ndi ine. Ineyo ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.—Miy. 8:30.
Yesu atabwela padziko lapansi, anagwilitsa nchito zacilengedwe pophunzitsa za Atate wake. Tiyeni tioneko imodzi mwa mfundo zimene anaphunzitsa. Yehova amakonda anthu onse. Pa ulaliki wake wa pa phili, Yesu anakamba za dzuŵa na mvula, zinthu zimene anthu ambili saziganizila kwenikweni. Koma zinthuzi n’zofunika kwambili kuti tikhalebe na moyo. Yehova akanafuna, akanapatsa zinthuzo anthu okhawo amene amam’tumikila. Koma iye mwacikondi amapeleka dzuŵa na mvula kwa anthu onse. (Mat. 5:43-45) Yesu anagwilitsa nchito mfundo imeneyi pophunzitsa ophunzila ake kuti, Yehova amafuna kuti tizionetsa cikondi kwa munthu aliyense. Nthawi zonse tikamaona kuloŵa kwa dzuŵa kokongola, na kamvula kowaza kotsitsimula, tizikumbukila cikondi ca Yehova copanda tsankho. Citsanzo cake cingatilimbikitse kuonetsa cikondi cofananaco mwa kulalikila kwa anthu onse. w23.03 17 ¶9-10
Cisanu, July 5
Ndinadabwa kwambili.—Chiv. 17:6.
Kodi mtumwi Yohane anadabwa na ciyani? Na mkazi amene anakwela pa cilombo cofiila kwambili. Mkaziyo amamuonetsa kuti ni “hule lalikulu,” ndipo amachedwa “Babulo Wamkulu.” Iye amacita “dama” na “mafumu a dziko lapansi.” (Chiv. 17:1-5) Kodi “Babulo Wamkulu” ndani? Mkaziyu saimila mabungwe andale cifukwa amanenedwa kuti amacita ciwelewele na atsogoleli andale. (Chiv. 18:9) Ndipo iye amayesetsa kutsogolela olamulila amenewa, pokwela pa msana pawo mophiphilitsa. Komanso, mkaziyu saimila mabungwe amalonda adyela a dziko ili la Satana. M’mavesi ena m’buku la Chivumbulutso, mabungwewo amachedwa “amalonda oyenda-yenda a padziko lapansi.” (Chiv. 18:11, 15, 16) Babulo wakale anali cimake ca kulambila konyenga. Conco, tingati Babulo Wamkulu aimila kulambila kulikonse konyenga. Mkaziyu ni ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga.—Chiv. 17:5, 18. w22.05 11 ¶14-16
Ciŵelu, July 6
Mdani wanu Mdyelekezi akuyenda-yenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.—1 Pet. 5:8.
Nthawi zina, mayi amadela nkhawa ngati ana ake adzasankha kutumikila Yehova. Makolo amadziŵa mavuto amene ana awo amakumana nawo m’dzikoli la Satana. Cina, alongo ambili amavutika kulela ana awo popanda mwamuna, kapena mwamuna angakhale naye koma salambila Yehova. Makolo amene mnzawo wa mu ukwati si Mboni, si ndiwo okha amene amakumana na zovuta pothandiza ana awo kukonda Yehova. Ngakhale makolo amene onse ni Mboni, cingakhale covuta kwa iwo kufika ana awo pamtima kuti akhale atumiki a Yehova okhulupilika. Ngati umu ni mmene zilili kwa inu, musamade nkhawa kwambili. Yehova adzakuthandizani. Bwanji osafunsilako maganizo kwa makolo aciyambakale kuti akuuzenkoni moseŵenzetsela zida zimene tili nazo pa kulambila kwa pabanja? (Miy. 11:14) Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kugwilitsila nchito mafunso oyenelela, kuti mudziŵe zimene ana anu akuganiza, komanso mmene akumvelela.—Miy. 20:5. w22.04 17 ¶4, 7; 18 ¶9
Sondo, July 7
Ine ndikupitiliza kupemphela kuti cikondi canu cipitilile kukula, limodzi ndi kudziŵa zinthu molondola.—Afil. 1:9.
Tingakule m’cikondi cathu pa Yehova mwa kum’dziŵa bwino Mwana wake, amene anaonetsa bwino kwambili makhalidwe a Atate wake. (Aheb. 1:3) Njila yabwino yomudziŵila Yesu, ni kuphunzila mabuku anayi a Uthenga Wabwino. Ngati mulibe cizoloŵezi coŵelenga Baibo tsiku lililonse, bwanji osayamba palipano? Mukamaŵelenga nkhani za Yesu, muziganizila kwambili makhalidwe ake. Iye anali wofikilika, ndipo anali kunyamula ana aang’ono mwacikondi n’kuwafukatila. (Maliko 10:13-16) Yesu anali wokoma mtima komanso waubwenzi, moti ophunzila ake anali kumasuka kumuuza mmene anali kumvela mumtima. (Mat. 16:22) Mwakutelo, Yesu anatengela citsanzo ca Atate wake wakumwamba. Nayenso Yehova ni wofikilika kwambili. Tingamufikile m’pemphelo. Popemphela, tingam’khuthulile za mumtima mwathu, tili na cidalilo cakuti sadzatidzudzula. Iye amatikonda, komanso amatisamalila.—1 Pet. 5:7. w22.08 3 ¶4-5
Mande, July 8
Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.—Sal. 86:5.
Popeza Yehova ndiye anatilenga, iye amadziŵa zonse zokhudza ife. Tangoganizani! Iye amadziŵa zonse zokhudza munthu aliyense padzikoli. (Sal. 139:15-17) Conco, amaona ucimo wonse umene tinatengela kwa makolo athu. Kuwonjezela apo, iye amadziŵa zonse zinacitika mu umoyo wathu zimene zinaumba umunthu wathu. Kodi kuwadziŵa bwino anthu mwa njila imeneyi kumasonkhezela Yehova kucita ciyani? Kumamusonkhezela kucita nawo mwacifundo. (Sal. 78:39; 103:13, 14) Yehova anaonetsa kuti ni wofunitsitsa kutikhululukila. Iye amadziŵa kuti cifukwa ca zocita za munthu woyamba, Adamu, tonsefe tinalandila tembelelo la ucimo na imfa. (Aroma 5:12) Panalibe njila ina iliyonse yodziwombola tokha ku tembelelo limeneli, kapena kuwombola munthu wina. (Sal. 49:7-9) Koma Mulungu wathu wacikondi anaonetsa cifundo na kukonza zakuti adzatiwombole. Monga mmene Yohane 3:16 imakambila, Yehova anapeleka Mwana wake wobadwa yekha kuti adzatifele.—Mat. 20:28; Aroma 5:19. w22.06 3 ¶5-6
Ciŵili, July 9
Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake.—Miy. 11:17.
Zakuti okhululukila ena nawonso adzakhululukidwa, Yehova ananena mfundo imodzimodziyo kwa mtumiki wake Yobu. Munthu wokhulupililika ameneyu anali atakhumudwa kwambili na mawu olasa a anzake atatu—Elifazi, Bilidadi, na Zofari. Yehova anauza Yobu kuti apemphelele anzakewo. Iye atacita zimenezo, Yehova anam’dalitsa. (Yobu 42:8-10) Kusunga cakukhosi kumavulaza. Yehova amafuna kuti tipeze mpumulo umene umabwela tikapewa kusunga cakukhosi, kumene kuli ngati kunyamula cikatundu colema. (Aef. 4:31, 32) Iye amatilimbikitsa kuti: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.” (Sal. 37:8) Timapindula tikatsatila ulangizi umenewu. Kusunga cakukhosi kungativulaze kuthupi, na kutibweletsela matenda a maganizo. (Miy. 14:30) Mwacitsanzo, tikamwa poizoni, thanzi lathu n’limene limawonongeka, osati la wina. Mofananamo, tikasunga cakukhosi timadzivulaza ife eni, osati anthu amene anatikhumudwitsa. Conco, tikamakhululukila ena, timapindulitsa moyo wathu. Timakhala na mtendele wa maganizo, ndipo timapitiliza kutumikila Yehova. w22.06 10 ¶9-10
Citatu, July 10
Tivale codzitetezela pacifuwa cacikhulupililo ndi cikondi. Tivalenso ciyembekezo cacipulumutso monga cisoti.—1 Ates. 5:8.
Ciyembekezo cathu cili ngati cisoti cophiphilitsa cimene cimateteza maganizo athu, na kutithandiza kupewa umoyo wongofuna kudzisangalatsa, umene ungawononge ubale wathu na Yehova. (1 Akor. 15:33, 34) Ciyembekezo cathu cingatithandizenso kupewa maganizo akuti sitingathe kukondweletsa Yehova olo pang’ono. Kumbukilani kuti maganizo amenewa, ni amene Elifazi wotonthoza wabodza anawagwilitsa nchito pokamba na Yobu. Elifazi anati: “Kodi munthu ndani kuti akhale woyela?” Ponena za Mulungu, iye anati: “Iyetu alibe cikhulupililo mwa angelo ake, ndipo kumwamba si koyela m’maso mwake.” (Yobu 15:14, 15) Ili linali bodza lamkunkhuniza! Kumbukilani kuti Satana amafuna kuti muziganiza conco. Iye adziŵa kuti mukamaganizila kwambili zimenezi, mudzataya ciyembekezo canu. Conde, kanizani mabodza amenewo. Musakayikile ngakhale pang’ono kuti Yehova afuna kuti mukakhale na moyo kwamuyaya, komanso kuti adzakuthandizani kucita zimenezo.—1 Tim. 2:3, 4. w22.10 25-26 ¶8-10
Cinayi, July 11
Yobu sanacimwe ndi milomo yake.—Yobu 2:10.
Colinga ca Satana cinali cakuti Yobu aziona kuti akuvutika cifukwa anakwiyitsa Yehova. Mwacitsanzo, Satana anagwilitsa nchito cimphepo camphamvu kugwetsa nyumba mmene ana onse 10 a Yobu anali kudya cakudya mosangalala. (Yobu 1:18, 19) Iye anapangitsanso moto kugwa kucokela kumwamba umene unapha ziŵeto zonse za Yobu, pamodzi na abusa amene anali kuziyang’anila. (Yobu 1:16) Popeza cimphepoco na moto zinacokela kumwamba, Yobu anaganiza kuti zacokela kwa Yehova Mulungu. Izi zinam’pangitsa kukhulupilila kuti anali atakwiyitsa Yehova mwa njila ina yake. Ngakhale n’telo, iye anakana kunyoza Atate wake wakumwamba. Yobu sanaiŵale kuti zabwino zonse zimene analandila pa zaka zonsezo, ni Yehova anam’patsa. Conco, anaganiza kuti ngati anali kukondwela kulandila zabwino, ayenelanso kucivomeleza kulandila zoipa. Ndiye cifukwa cake Yobu ananena kuti: “Dzina la Yehova lipitilize kutamandidwa.”—Yobu 1:20, 21. w22.06 21 ¶7
Cisanu, July 12
Anthu onse adzadana nanu cifukwa ca dzina langa. Koma amene adzapilile mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.”—Maliko 13:13.
Yesu anauza ophunzila ake zofanana na zimenezi pa Yohane 17:14. Takhala tikuona kukwanilitsidwa kwa mbali ya ulosi umenewu maka-maka pa zaka 100 zapitazo. Kodi wakwanilitsidwa motani? Yesu atangokhala Mfumu Yaumesiya mu 1914, anapitikitsa Satana kumwamba. Pano tikamba, iye ali pano padziko lapansi, kuyembekezela ciwonongeko. (Chiv. 12:9, 12) Koma sikuti akungoyembekezela popanda kucitapo kanthu. Iye ali pa kalikiliki, ni wokwiya ndipo akukhuthulila mkwiyo wakewo pa anthu a Mulungu. (Chiv. 12:13, 17) Pa cifukwa cimeneci, cidani ca anthu m’dzikoli cakulilatu pa anthu a Mulungu akulitsa. Koma palibe cifukwa coopela Satana na otsatila ake. M’malo mwake, timakhala na cidalilo monga ca mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?” (Aroma 8: 31) Conco, tiyenela kukhala na cidalilo conse mwa Yehova. w22.07 18 ¶14-15
Ciŵelu, July 13
Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.—Mat. 24:14.
Yesu sanade nkhawa zakuti padzakhala anthu ocepa ogwila nchito yolalikila m’nthawi ya mapeto a dongosolo lino la zinthu. Iye anadziŵa kuti mawu a ulosi a wamasalimo adzakwanilitsidwa. Mawuwo amati: “Anthu ako adzadzipeleka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolela asilikali ako kunkhondo.” (Sal. 110:3) Ngati mumagwilako nchito yolalikila, ndiye kuti mukuthandizila Yesu pamodzi na kapolo wokhulupilika, komanso mukukwanilitsa ulosi umenewo. Nchitoyi ikupitabe patsogolo, koma pali zovuta zina. Vuto loyamba limene alengezi a Ufumu amakumana nalo, ni kutsutsidwa. Ampatuko, atsogoleli a cipembedzo, komanso andale, amakamba mabodza ponena za nchito yathu. Acibale athu, anthu amene timadziŵa, ndiponso anzathu a kunchito akauzidwa mabodza amenewo, amatikakamiza kuti tileke kutumikila Yehova komanso kulalikila. M’maiko ena, citsutso cimabwela m’njila zosiyana-siyana monga kuopsezedwa, kumangidwa, ngakhale kuponyedwa m’ndende kumene. w22.07 8 ¶1; 9 ¶5-6
Sondo, July 14
Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.—Mac. 14:22.
Yehova amafuna kuti tizipatula nthawi yoŵelenga Baibo nthawi zonse na kusinkhasinkha zimene timaŵelengazo. Tikamagwilitsa nchito zimene timaphunzila, cikhulupililo cathu cimalimba, ndipo timamuyandikila kwambili Atate wathu wakumwamba. Mwa ici, timakwanitsa kupilila mayeso. Yehova amapelekanso mzimu wake woyela kwa aja amene amadalila Mawu ake. Ndipo mzimuwo umatipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti tipilile mayeselo alionse. (2 Akor. 4:7-10) Na thandizo la Yehova, “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” amakonza nkhani, mavidiyo, na nyimbo zotithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu, na kukhalabe maso mwauzimu. (Mat. 24:45) Yehova waphunzitsa anthu ake kuti azikondana na kutonthozana panthawi ya mavuto. (2 Akor. 1:3, 4; 1 Ates. 4:9) Abale na alongo athu amakhala okonzeka kutithandiza kuti tikhalebe okhulupilika pamene takumana na mavuto. w22.08 12 ¶12-14
Mande, July 15
Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.—Aef. 4:3.
Mwa kumasuka kuchula makhalidwe abwino a abale na alongo athu, timawathandiza kukhala okondana kwambili. Izi ndiye zimamangiliza mpingo m’cikondi. Nthawi zina, ngakhale Akhristu okhwima angasemphane maganizo kapena kukangana wina na mnzake. N’zimene zinacitika kwa mtumwi Paulo na mnzake wapamtima Baranaba. Amuna aŵiliwa anakangana kwambili pa nkhani yakuti atenge Maliko pa ulendo wawo wotsatila wa umishonale. Panali “mkangano woopsa” pakati pawo moti anapatukana. (Mac. 15:37-39) Koma Paulo, Baranaba, na Maliko anakonzanso ubale wawo. Pambuyo pake, Paulo anakamba zabwino za Baranaba na Maliko. (1 Akor. 9:6; Akol. 4:10) Nafenso tiyenela kuthetsa kusamvana kulikonse na ena mu mpingo, na kupitiliza kuona zabwino mwa iwo. Tikatelo, tidzalimbikitsa mtendele na mgwilizano. w22.08 23 ¶10-11
Ciŵili, July 16
Lekani kuweluza ena kuti inunso musaweluzidwe.—Mat. 7:1.
Pamene tikuyesetsa kutsatila malamulo a Yehova olungama, tizipewa kuweluza ena na kudziona kukhala olungama. Tizikumbukila kuti Yehova ndiye “Woweluza wa dziko lonse lapansi.” (Gen. 18:25) Yehova sanatipatse udindo woweluza ena. Ganizilani citsanzo ca Yosefe munthu wolungama. Iye anapewa kuweluza ena, ngakhale anthu amene anam’cita zoipa. Abale ake enieniwo anamuukila, anamugulitsa ku ukapolo, ndipo anaonetsa atate awo umboni wakuti Yosefe wamwalila. Patapita zaka, Yosefe anakumananso na banja lake. Panthawiyo, iye anali wolamulila wamphamvu, ndipo akanaweluza abale akewo mwankhaza pofuna kuwabwezela. Abale ake a Yosefe anaopa kuti mwina adzawacita zimenezo, ngakhale kuti panthawiyi iwo anali atalapa pa zimene anacita. Koma Yosefe anawauza kuti: “Musaope ayi. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu?” (Gen. 37:18-20, 27, 28, 31-35; 50:15-21) Modzicepetsa, Yosefe anasiila Yehova kuti aweluze abale akewo. w22.08 30 ¶18-19
Citatu, July 17
Usalephele kucitila zabwino anthu amene akufunikila zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kucita zimenezo.—Miy. 3:27
Kodi mudziŵa kuti Yehova angakuseŵenzetseni poyankha pemphelo locokela pansi pa mtima la munthu wina? Angakuseŵenzetseni kaya ndinu mkulu, mtumiki wothandiza, mpainiya, kapena wofalitsa mu mpingo. Inde, mungathandize wina mosasamala kanthu kuti ndinu wacicepele kapena wacikulile, m’bale kapena mlongo. Munthu wokonda Yehova akafuulila kwa iye kuti am’thandize, Mulungu wathu nthawi zambili amagwilitsa nchito atumiki ena okhulupilika kuti ‘athandize ndi kulimbikitsa’ munthuyo. (Akol. 4:11) Ni mwayi wapadela cotani nanga kutumikila Yehova na abale athu mwa njila imeneyi! Tingatelo pa nthawi ya mlili, ya tsoka, kapena ya mazunzo. Mwina tingafunenso kuthandiza ena, koma kucita izi nakonso kungakhale kovuta ngati ena m’banja lathu akudwala. Ngakhale n’conco, timafunabe kuthandiza abale athu, ndipo Yehova amakondwela tikacita zimene tingathe kuti tiwathandize.—Miy. 19:17. w22.12 22 ¶1-2
Cinayi, July 18
Lamulo langa ndi ili, mukondane monga mmene inenso ndakukondelani.—Yoh. 15:12.
Cikondi ndico maziko a kukhala wodalilika. Yesu anapeleka malamulo aŵili aakulu kwambili—kukonda Yehova komanso kukonda mnzako. (Mat. 22:37-39) Cikondi cathu pa Yehova cimatisonkhezela kutengela citsanzo cake ca kudalilika kwake. Mwacitsanzo, ngati abale na alongo timawakonda, tidzawasungila nkhani zawo zacinsinsi. Sitingayese olo pang’ono kuulula zinthu zimene zingawacititse manyazi kapena kuwaika m’mavuto. Kudzicepetsa nakonso kudzatithandiza kukhala odalilika. Mkhristu wodzicepetsa sakhala na maganizo akuti ‘nifuna nizikhala woyamba ndine kuuza anthu nkhani.’ (Afil. 2:3) Komanso, munthu wodzicepetsa sapangitsa ena kumuona kuti amadziŵa nkhani zacinsinsi zimene n’kosaloledwa kuuzako ena. Kudzicepetsa kudzatithandizanso kupewa kufalitsa nkhani zimene Baibo kapena zofalitsa zozikika pa Baibo sizinakambepo. w22.09 12 ¶12-13
Cisanu, July 19
[Anthu] adzadziŵa zinthu zambili zoona.—Dan. 12:4.
Mngelo anauza Danieli kuti anthu a Mulungu adzawamvetsa bwino kwambili mawu a ulosi opezeka m’buku la Danieli. Koma “palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa.” (Da 12:10) Ino ndiyo nthawi yoonetsa mwa zocita zathu kuti sitili pakati pa anthu oipa amenewo. (Mal. 3:16-18) Yehova akusonkhanitsa anthu amene amawaona kuti ni “cuma capadela,” kapena kuti anthu amtengo wapatali kwa iye. Kukamba zoona, timafuna titakhala mmodzi wa anthu amenewa. Ndithudi, tikukhala m’nthawi ya zocitika zocititsa cidwi. Koma posacedwa, kudzacitika zinthu zina zocititsa cidwi kuposa pamenepa. Mwacitsanzo, kuipa konse kudzatha posacedwa. Cotsatila, tidzaona kukwanilitsidwa kwa zimene Yehova analonjeza Danieli kuti: “Udzauka kuti ulandile gawo lako pa mapeto a masikuwo.” (Dan. 12:13) Kodi mumalakalaka kudzaona nthawi pamene Danieli pamodzi na okondedwa anu adzaukitsidwa? Ngati n’conco, citani zonse zotheka kuti mukhalebe wokhulupilika palipano. Mukatelo, mudzakhala otsimikiza kuti dzina lanu silidzacotsedwamo m’buku la moyo la Yehova. w22.09 24 ¶17; 25 ¶19-20
Ciŵelu, July 20
Ndikukutumiza.—Ezek. 2:3.
Mawu amenewa ayenela kuti anam’limbikitsa Ezekieli. Cifukwa ciyani? Mosakayikila, iye anakumbukila kuti Yehova anagwilitsa nchito mawu ofananawo posankha Mose na Yesaya kuti akhale aneneli ake. (Eks. 3:10; Yes. 6:8) Ndipo Ezekieli anali kudziŵa mmene Yehova anathandizila aneneli aŵiliwo kucita mautumiki awo ovuta. Conco, pamene Yehova anauza Ezekieli kaŵili konse kuti: “ Ndikukutumiza,” mneneliyu anali na cifukwa cabwino cokhulupilila kuti Yehova adzam’thandiza. Kuwonjezela apo, m’buku la Ezekieli timapezamo mawu angapo akuti: “Yehova analankhula nane.” (Ezek. 3:16) Cina, mawu akuti “Yehova anapitiliza kulankhula nane,” amapezeka maulendo ambili m’buku la Ezekieli. (Ezek. 6:1) Ndithudi, Ezekieli anali wotsimikiza kuti anatumidwa na Yehova. Komanso, popeza iye anali mwana wa wansembe, n’kutheka kuti atate ake anam’simbila mmene Yehova anatsimikizila aneneli ake ena kuti adzawathandiza. Kwa Isaki, Yakobo, na Yeremiya, Yehova analankhula mawu akuti: “Ine ndili ndi iwe.”—Gen. 26:24; 28:15; Yer. 1:8. w22.11 2 ¶3
Sondo, July 21
Moyo wosatha adzaupeza.—Yoh. 17:3.
Ngakhale kuti Adamu na Hava anacimwa, komanso kubweletsa imfa kwa ana awo, Yehova sanasinthe maganizo ake pa colinga cake. (Yes. 55:11) Colinga cake cikali cakuti anthu okhulupilika adzakhale na moyo kwamuyaya. Tangoganizilani zimene anakamba na kucita kuti akwanilitse colinga cakeco. Yehova analonjeza kuti adzaukitsa akufa, na kuwapatsa mwayi wodzakhala na moyo kwamuyaya. (Mac. 24:15; Tito 1:1, 2) Munthu wokhulupilika Yobu anali wotsimikiza kuti Yehova ni wofunitsitsa kuukitsa akufa. (Yobu 14:14, 15) Nayenso mneneli Danieli anali kudziŵa kuti anthu ali na ciyembekezo codzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi wodzakhala na moyo kwamuyaya. (Sal. 37:29; Dan. 12:2, 13) Cinanso, Ayuda m’nthawi ya Yesu anali kudziŵa kuti Yehova adzapatsa atumiki ake okhulupilika “moyo wosatha.” (Luka 10:25; 18:18) Yesu anakamba za lonjezo limeneli mobweleza-bweleza, ndipo iye mwini anaukitsidwa na Atate ŵake.—Mat. 19:29; 22:31, 32; Luka 18:30; Yoh. 11:25. w22.12 4-5 ¶8-9
Mande, July 22
Cikhulupililo canga cili mwa inu Yehova.—Sal. 31:14.
Yehova akutipempha kuti timuyandikile. (Yak. 4:8) Iye amafuna kuti akhale Mulungu wathu, Tate wathu, komanso Bwenzi lathu. Amayankha mapemphelo athu, na kutithandiza panthawi zovuta. Ndipo amagwilitsa nchito gulu lake kuti atiphunzitse na kutiteteza. Yehova tingamuyandikile mwa kupemphela kwa iye, komanso kuŵelenga Mawu ake na kuwasinkhasinkha. Tikatelo, tidzam’konda kwambili na kumuyamikila. Cina, tidzalimbikitsidwa kumumvela na kum’patsa citamando comuyenelela. (Chiv. 4:11) Tikam’dziŵa bwino Yehova, tidzakulitsa cidalilo cathu pa iye na gulu lake limene wapeleka kuti lizitithandiza. Komabe, Mdyerekezi amayesa kutilekanitsa na Yehova, maka-maka tikakumana na mavuto. Kodi amacita bwanji zimenezi? Mwapang’ono-pang’ono iye amacepetsa cidalilo cathu pa Yehova na gulu lake. Koma n’zotheka kukaniza macenjela ake. Cikhulupililo cathu mwa Yehova cikakhala colimba, komanso ngati cidalilo cathu mwa iye n’cosagwedela, sitidzamusiya Mulungu wathu na gulu lake.—Sal. 31:13, 14. w22.11 14 ¶1-3
Ciŵelu, July 23
Anali okonzeka kufa cifukwa sanafune kutumikila ndi kulambila mulungu wina aliyense kupatulapo Mulungu wawo.—Dan. 3:28.
Akhristu ambili oona aika miyoyo yawo pa ciwopsezo cifukwa cokonda Yehova monga Wolamulila wawo Wamkulu. Akhristu amenewa amasungabe umphumphu wawo ndipo amafanana na Akhristu atatu aciheberi amene anapulumutsidwa m’ng’anjo yamoto cifukwa cokhalabe wokhulupilika kwa Wamkulukulu. Wamasalimo Davide analemba za kufunika kokhalabe okhulupilika kwa Mulungu. Anati: “Yehova adzapeleka cigamulo ku mitundu ya anthu. Ndiweluzeni inu Yehova, mogwilizana ndi cilungamo canga, komanso mogwilizana ndi mtima wanga wosagawanika.” (Sal. 7:8) Iye analembanso kuti: “Mtima wanga wosagaŵanika ndiponso wowongoka unditeteze.” (Sal. 25:21) Kuti tikhale na umoyo wabwino, tiyenela kukhalabe okhulupilika kwa Yehova na kusagonja pa cikhulupililo cathu kwa iye! Tikatelo, tidzamva monga mmene wamasalimo anamvela amene analemba kuti: “Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu . . . , amene akutsatila cilamulo ca Yehova.”—Sal. 119:1. w22.10 17 ¶18-19
Citatu, July 24
Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.—Aroma 1:20.
Pa umoyo wake wonse Yobu, makambilano ake na Yehova Mulungu ndiwo anali ofunika kwambili kuposa ena alionse. Pa makambilano amenewo, Yehova anauza Yobu kuti ayang’ane mwacidwi zinthu zimene iye analenga. Izi zinali kudzathandiza Yobu kudziŵa kuti Yehova ni wanzelu. Zinam’thandizanso kulimbitsa cidalilo cake cakuti Yehova amasamalila zosoŵa za atumiki ake. Mwacitsanzo, Yobu anakumbutsidwa kuti Mulungu amasamalila nyama. Conco, sakanalephela kum’samalila Yobu. (Yobu 38:39-41; 39:1, 5, 13-16) Mwa kuyang’ana mwacidwi zinthu zacilengedwe, Yobu anadziŵa zambili zokhudza makhalidwe a Mulungu. Nafenso tingaphunzile zambili za Mulungu tikamayang’ana mwacidwi zinthu zimene analenga. Komabe, nthawi zina cingakhale covutilapo kucita zimenezo. Ngati tikhala m’tauni, sitingaone zambili zimene Mulungu analenga. Koma ngakhale kumadela akumidzi, kumene zacilengedwe zili paliponse, tingamaone kuti tilibe nthawi yokwanila yosinkhasinkha zinthuzo. Komabe, kupatula nthawi yoyang’ana zacilengedwe n’kopindulitsa. w23.03 15 ¶1-2
Cinayi, July 25
Wocenjela ndi amene amati akaona tsoka amabisala.—Miy. 22:3.
Yesu anakamba kuti “zivomezi zamphamvu” komanso matsoka ena acilengedwe adzacitika mapeto asanafike. (Luka 21:11) Anakambanso kuti kudzakhala “kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo,” ndipo upandu, ciwawa, komanso za ucigaŵenga ni umboni wa zimenezi. (Mat. 24:12) Yesu sanakambe kuti mavuto amenewa adzagwela anthu okhawo amene Yehova waakana. Atumiki ambili a Yehova okhulupilika akumanapo na matsoka. (Yes. 57:1; 2 Akor. 11:25) Yehova sangatiteteze mozizwitsa ku matsoka onse. Koma adzatipatsa zofunikila kuti tikhale na mtendele wa mumtima komanso bata. Tikamakonzekela matsoka a zacilengedwe pasadakhale, tizitha kukhalabe osatekeseka matsokawo akacitika. Koma kodi tikakonzekela zitanthauza kuti tilibe cikhulupililo mwa Yehova? Ayi. Kukonzekela matsoka a zacilengedwe kumaonetsa kuti tili na cidalilo mwa iye cakuti adzatisamalila. Motani? Mawu a Mulungu amatilangiza kuti tizikonzekela matsoka. w22.12 18 ¶9-10
Cisanu, July 26
Mulungu ndiye ananditumiza patsogolo panu kuti ndidzapulumutse miyoyo yanu.—Gen. 45:5.
Yosefe ali m’ndende, Yehova anapangitsa mfumu ya Iguputo kulota maloto aŵili ovutitsa maganizo. Mfumuyo itadziŵa kuti Yosefe amakwanitsa kumasulila maloto, inamuitana. Mwa thandizo la Yehova, Yosefe anamasulila malotowo. Ndipo Farao anakondwela na ulangizi wabwino umene Yosefe anam’patsa. Farao ataona kuti Yehova anali na Yosefe, anaika mnyamatayo kukhala woyang’anila cakudya ca dziko lonse la Iguputo. (Gen. 41:38, 41-44) Patapita nthawi, kunagwa njala yaikulu imene inakhudza dziko la Iguputo, ngakhalenso dziko la Kanani, kumene kunali banja la Yosefe. Apa Yosefe anatha kupulumutsa banja lake ku njalayo, n’kuteteza mzele wobadwila Mesiya. Mosakaika konse, Yehova ndiye anali kudalitsa zonse zimene Yosefe anali kucita. Ngakhale kuti abale a Yosefe anafuna kumupha, Yehova anasintha zinthu kuti colinga cake cikwanilitsidwe. w23.01 17 ¶11-12
Ciŵelu, July 27
Samalani.—Luka 21:34.
Munthu amene amakhala wosamala, amakhala maso ku zilizonse zingawononge ubale wake na Yehova, ndipo amayesetsa kuzipewa. Mwa kutelo, iye amakhalabe m’cikondi ca Mulungu. (Miy. 22:3; Yuda 20, 21) Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti azisamala m’zocita zawo. Mwacitsanzo, iye anauza Akhristu a ku Efeso kuti: “Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anzelu.” (Aef. 5:15, 16) Uzimu wathu umakhala pa ciwopsezo nthawi zonse. N’cifukwa cake Baibo imatilimbikitsa kuti ‘tipitilize kuzindikila cifunilo ca Yehova,’ kuti tigonjetse mayeso alionse amene angawononge ubwenzi wathu na iye. (Aef. 5:17) Koma kuti tipange zisankho zanzelu, tiyenela kuzindikila “cifunilo ca Yehova.” Tingatelo mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse na kuwasinkhasinkha. Tikafika pocimvetsa bwino cifunilo ca Yehova, n’kukhala na “maganizo a Khristu,” cidzakhala capafupi kuyenda “ngati anzelu,” ngakhale pamene palibe lamulo lacindunji lotiuza zoyenela kucita.—1 Akor. 2:14-16. w23.02 16-17 ¶7-9
Sondo, July 28
Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.—Aroma 12:2.
Kodi mumasesamo kangati m’nyumba mwanu? Mwina musanasamukile m’nyumbayo, munaiyeletsa bwino kwambili. Koma bwanji ngati pambuyo pake mwaleka kuiyeletsa? Mosakayikila, posapita nthawi m’nyumbamo mungakhale fumbi na dothi. Kuti nyumba yanu ikhalebe yaukhondo, muyenela kumaiyeletsa nthawi zonse. Mofananamo, tiziyesetsa kuwongolela kaganizidwe kathu na umunthu wathu. N’zoona kuti tisanabatizike, tinayesetsa kupanga masinthidwe ofunikila mu umoyo wathu kuti ‘tidziyeletse na kucotsa cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu.’ (2 Akor. 7:1) Ngakhale n’telo, tiyenela kutsatila uphungu wa mtumwi Paulo wakuti “pitilizani kukhala atsopano.” (Aef. 4:23, NWT) M’maganizo mwathu mungaloŵe fumbi na dothi la m’dzikoli. Kuti tipewe zimenezi na kukhalabe oyela pamaso pa Yehova, tiyenela kupitiliza kusanthula maganizo athu, umunthu wathu, na zikhumbo zathu. w23.01 8 ¶1-2
Mande, July 29
Anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzamutela.—Mat. 3:16.
Ganizilani mmene zinalili kumvetsela Yesu akuphunzitsa. Nthawi zambili, iye anali kugwila mawu Malemba Oyela, ndipo malembawo anacita kuwaloŵeza pamtima. Pa nthawi imene Yesu anabatizika na kudzozedwa na mzimu woyela, iye anayamba kukumbukila zinthu zonse zokhudza nthawi imene anali kumwamba asanabwele padziko lapansi. M’mawu ake oyamba pambuyo pa ubatizo wake, komanso m’mawu ake othela atatsala pang’ono kufa, Yesu anagwila mawu Malemba. (Deut. 8:3; Sal. 31:5; Luka 4:4; 23:46) Pa utumiki wake wonse wa zaka zitatu na hafu, Yesu nthawi zambili anali kuŵelenga Malemba poyela, kuwagwila mawu, na kuwafotokozela. (Mat. 5:17, 18, 21, 22, 27, 28; Luka 4:16-20) Kukali zaka kuti ayambe utumiki wake, Yesu nthawi zambili anali kuŵelenga na kumvetsela kuŵelengedwa kwa Mawu a Mulungu. Panyumba, mosakaika konse anali kumva Mariya na Yosefe akugwila mawu Malemba. (Deut. 6:6, 7) Cina, Yesu anali kupita ku Sunagoge Sabata iliyonse pamodzi na banja lawo. (Luka 4:16) Kumeneko ayenela kuti anali kumvetsela mwachelu Malemba akamaŵelengedwa. w23.02 8 ¶1-2
Ciŵili, July 30
Uzikonda Yehova Mulungu wako.—Maliko 12:30.
Tili na zifukwa zambili zom’kondela Yehova. Mwacitsanzo, mwafika podziŵa kuti iye ni “kasupe wa moyo,” komanso kuti ni Mpatsi wa “mphatso ili yonse yabwino ndi yangwilo.” (Sal. 36:9; Yak. 1:17) Ciliconse cabwino cimene mumasangalala naco, cimacokela kwa Mulungu wathu wacikondi komanso woolowa manja. Dipo ni mphatso yabwino ngako imene Yehova anatipatsa. Tikutelo cifukwa ciyani? Ganizilani mgwilizano umene ulipo pakati pa Yehova na Mwana wake. Yesu anati: ‘Atate amandikonda’ ndipo “ndimakonda Atate.” (Yoh. 10:17; 14:31) Mgwilizano wawo unalimba kwambili cifukwa cokhala pamodzi zaka mabiliyoni. (Miy. 8:22, 23, 30) Tsopano tangoganizilani mmene cinamuŵaŵila Mulungu kulola Mwana wake kuvutika mpaka kufa. Yehova amawakonda kwambili anthu—kuphatikizapo inu—moti anapeleka Mwana wake wokondeka monga nsembe kuti inuyo na ena mukakhale na moyo kwamuyaya. (Yoh. 3:16; Agal. 2:20) Ici ndico cifukwa cacikulu kwambili cimene timam’kondela Mulungu. w23.03 4-5 ¶11-13
Citatu, July 31
Gwilani mwamphamvu . . . zimene muli nazo.—Chiv. 2:25.
Tizipewa ziphunzitso za ampatuko. Yesu anadzudzula anthu ena amene anali kulimbikitsa magaŵano ku Pegamo. (Chiv. 2:14-16) Iye anayamikila Akhristu a ku Tiyatira cifukwa anapewa “zinthu zozama za Satana,” ndipo anawalimbikitsa ‘kugwila mwamphamvu’ coonadi. (Chiv. 2:24-26) Koma Akhristu ofooka kumeneko amene anayamba kutsatila ziphunzitso zabodza anafunika kusintha. Nanga bwanji ife masiku ano? Tizipewa ziphunzitso zosagwilizana na mfundo za Yehova. Ampatuko angaoneke “odzipeleka kwa Mulungu, koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe.” (2 Tim. 3:5) Cidzakhala copepuka kudziŵa na kupewa ziphunzitso zabodza, kokha ngati timaŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama. (2 Tim. 3:14-17; Yuda 3, 4) Tizionetsetsa kuti kulambila kwathu n’kovomelezeka kwa Yehova. Ngati timacita zina zake zimene zikupangitsa kulambila kwathu kukhala kosavomelezeka, tiyenela kucitapo kanthu mwamsanga kuti tikonze zinthu.—Chiv. 2:5, 16; 3:3, 16. w22.05 4 ¶9; 5 ¶11