LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es25 masa. 47-57
  • May

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • May
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
  • Tumitu
  • Cinayi, May 1
  • Cisanu, May 2
  • Ciŵelu, May 3
  • Sondo, May 4
  • Mande, May 5
  • Ciŵili, May 6
  • Citatu, May 7
  • Cinayi, May 8
  • Cisanu, May 9
  • Ciŵelu, May 10
  • Sondo, May 11
  • Mande, May 12
  • Ciŵili, May 13
  • Citatu, May 14
  • Cinayi, May 15
  • Cisanu, May 16
  • Ciŵelu, May 17
  • Sondo, May 18
  • Mande, May 19
  • Ciŵili, May 20
  • Citatu, May 21
  • Cinayi, May 22
  • Cisanu, May 23
  • Ciŵelu, May 24
  • Sondo, May 25
  • Mande, May 26
  • Ciŵili, May 27
  • Citatu, May 28
  • Cinayi, May 29
  • Cisanu, May 30
  • Ciŵelu, May 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
es25 masa. 47-57

May

Cinayi, May 1

Padziko lonse lapansi padzagwa njala yaikulu.​—Mac. 11:28.

Akhristu oyambilila nawonso anakhudzidwa pamene kunagwa njala yaikulu “padziko lonse lapansi.” Mosakayikila, mitu ya mabanja inada nkhawa mmene ingasamalile mabanja awo. Nanga bwanji acinyamata amene anali kufuna kuwonjezela utumiki wawo? Kodi n’kutheka kuti iwo anaganiza zokankhila kutsogolo zolinga zawozo? Mosasamala kanthu za mikhalidwe yovutayo, Akhristuwo sanalefuke. Iwo anapitiliza kulalikila m’njila iliyonse imene akanatha, ndipo anali okondwa kugaŵana zinthu zakuthupi na Akhristu anzawo ku Yudeya. (Mac. 11:29, 30) Aja amene analandila zosoŵa zawo zakuthupi, anadzionela okha thandizo la Yehova. (Mat. 6:31-33) Iwo ayenela kuti anamva kuti amakondedwa kwambili na okhulupilila anzawo amene anapeleka thandizolo. Ndipo aja amene anacita copeleka kapena kutengako gawo pa nchito yopeleka thandizo, anapeza cimwemwe cimene cimabwela cifukwa copatsa.​—Mac. 20:35. w23.04 16 ¶12-13

Cisanu, May 2

Timakhala ndi cikhulupililo kuti tilandila zinthu zimene tamupemphazo.​—1 Yoh. 5:15.

Nthawi zina, Yehova amayankha mapemphelo a anthu ake mwa kusonkhezela anthu osakhulupilila kuti awathandize. Mwacitsanzo, iye anasonkhezela Mfumu Aritasasita kuti alole Nehemiya kubwelela ku Yerusalemu kukathandiza pa nchito yomanganso mzinda. (Neh 2:3-6) Masiku anonso, Yehova angapangitse anthu amene samulambila kuti atithandize tikafunikila thandizo. Nthawi zambili, mapemphelo athu sayankhidwa mogometsa ayi. Koma mayankho amene timalandila amakhala okwanila potithandiza kukhalabe okhulupilika kwa Atate wathu wakumwamba. Conco, muzikhala chelu kuona mmene Yehova akuyankhila mapemphelo anu. Conco, nthawi na nthawi tiziima na kuganizila mmene Yehova akuyankhila mapemphelo athu. (Sal. 66:19, 20) Timaonetsa cikhulupililo mwa kupemphela kwa Yehova, komanso kuvomeleza yankho yake mulimonse mmene angayankhile.​—Aheb. 11:6. w23.05 11 ¶13; 12 ¶15-16

Ciŵelu, May 3

Ndimasangalala kucita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga.​—Sal. 40:8.

Pamene tinadzipatulila kwa Yehova, tinalonjeza kuti tizim’lambila na kucita cifunilo cake. Tiyenela kulisunga lonjezolo. Kucita zimene tinalonjeza si mtolo wolemetsa ayi. Tikutelo cifukwa Yehova anatilenga kuti tizicita cifunilo cake. (Chiv. 4:11) Iye anatilenga m’cifanizilo cake, ndipo anaika mwa ife cikhumbo cofuna kum’dziŵa komanso kum’lambila. Mwa ici, timatha kumuyandikila na kusangalala pocita cifunilo cake. Kuwonjezela apo, tikamacita cifunilo ca Mulungu na kutsatila Mwana wake, ‘timatsitsimulidwa.’ (Mat. 11:28-30) Conco, pitilizani kulimbikitsa cikondi canu pa Yehova mwa kuganizila zabwino zimene wakucitilani, komanso madalitso amene wakusungilani. Cikondi canu pa Mulungu cikamakula, kudzakhala kwapafupi kumumvela. (1 Yoh. 5:3) Yesu anapambana pocita cifunilo ca Mulungu cifukwa anali kupempha thandizo kwa iye, komanso anakhazikitsa maganizo ake pa mphoto imene anali kudzalandila. (Aheb. 5:7; 12:2) Monga Yesu, muzipemphela kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu. Cina, musaleke kuganizila za ciyembekezo ca moyo wosatha. w23.08 27-28 ¶4-5

Sondo, May 4

Sukudziŵa kuti Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, kusakwiya msanga komanso kuleza mtima nʼcolinga coti ulape?​—Aroma. 2:4.

Tonsefe timawayamikila anthu oleza mtima. Inde, timawalemekeza anthu amene amatha kuyembekezela popanda kukhumudwa. Timayamikilanso kuti anthu ena amatilezela mtima tikalakwitsa. Ndiponso timayamikila kuti amene anatiphunzitsa Baibo analeza nafe mtima pamene tinali kuvutikila kuphunzila mfundo za m’Baibo, kuzivomeleza, na kuzigwilitsa nchito. Coposa zonse, timayamikila kwambili kuti Yehova Mulungu amaleza nafe mtima. Ngakhale kuti timayamikila kuleza mtima kwa anthu ena, nthawi zina ife tomwe zingamativuke kukhala oleza mtima. Mwacitsanzo, kuleza mtima kungativute tikakhala pa mzele wautali kucipatala, maka-maka nthawi ikatithela yocitanso zinthu zina. Kapena tingalephele kuugwila mtima ena akatikhumudwitsa. Ndipo nthawi zina, cingakhale covuta kuyembekezela lonjezo la Yehova la dziko latsopano. Komabe, pa zocitika zonsezi, tiyenela kukhala oleza mtima kwambili. w23.08 20 ¶1-2

Mande, May 5

Iye anabweza amuna ena onse a Isiraeli nʼkutsala ndi amuna 300 aja.​—Ower. 7:8.

Atauzidwa na Yehova, Gidiyoni anacepetsa ciŵelengelo ca asilikali mpaka kukhala na ocepa kwambili. Mwina anadzifunsa kuti, ‘Kodi masinthidwewa ni ofunikiladi? Kodi adzathandizadi?’ Mulimonsemo, Gidiyoni anatsatila zimenezo. Masiku ano, akulu amatengela Gidiyoni mwa kutsatila masinthidwe alionse a gulu. (Aheb. 13:17) Olo kuti Gidiyoni anali na mantha komanso anaika moyo wake pa ciwopsezo, iye anamvelabe Yehova. (Ower. 9:17) Atalandila citsimikizo kwa Yehova, anakhala na cidalilo conse kuti adzam’thandiza kuteteza anthu ake. Akulu okhala m’madela mmene nchito yathu ni yoletsedwa amatengela citsanzo ca Gidiyoni. Molimba mtima, iwo amakhala patsogolo kupezeka ku misonkhano na mu ulaliki, mosasamala kanthu za kuopsezedwa kuti adzamangidwa, kufunsidwa mafunso, kucotsedwa nchito, kapena kucitidwa ciwawa. Pa cisautso cacikulu, akulu adzafunika kukhala olimba mtima kuti akatsatile malangizo amene adzalandila, ngakhale kuti kucita zimenezo kungadzaike moyo wawo pa ciwopsezo. w23.06 5-6 ¶12-13

Ciŵili, May 6

Amene akundilemekeza ndidzawalemekeza.​—1 Sam. 2:30.

Yehova analola kuti nkhani ya Mkulu Wansembe Yehoyada ilembedwe m’Baibo kuti tiphunzilepo kanthu. (Aroma 15:4) Ndipo Yehoyada atamwalila, analemekezedwa mwapadela poikidwa “m’manda a mafumu mu Mzinda wa Davide, cifukwa anacita zabwino mu Isiraeli ndiponso kwa Mulungu woona ndi nyumba Yake.” (2 Mbiri 24:15, 16) Nkhani ya Yehoyada ingatithandize tonsefe kumaopa Mulungu. Akulu angatengele Yehoyada mwa kukhalabe chelu, komanso kuteteza nkhosa za Mulungu. (Mac. 20:28) Okalamba angaphunzile kwa Yehoyada kuti akamaopa Yehova na kukhalabe okhulupilika kwa iye, angawagwilitse nchito kucita cifunilo cake. Acicepele naonso angaganizile mmene Yehova anali kucitila naye Yehoyada, na kutengela citsanzo cake mwa kulemekeza acikulile, maka-maka aja amene atumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili. (Miy. 16:31). Tiyeni tizithandiza “amene akutsogolela” mwa kuwamvela.​—Aheb. 13:17. w23.06 17 ¶14-15

Citatu, May 7

Milomo ya wolungama imathandiza anthu ambili.​—Miy. 10:21.

Pa misonkhano khalani wozindikila kuona kuti muyankhapo kangati. Tikamakweza dzanja pafupi-pafupi, wotsogoza angamakakamizike kutilata kaŵili-kaŵili, ngakhale pamene ena sanapelekeko ndemanga. Izi zingalefule ena kuti asamakweze manja. (Mlal. 3:7) Ngati ofalitsa ambili akukweza manja, sitingayankhe kaŵili-kaŵili mmene tingafunile. Nthawi zina, wotsogoza sangatilate n’komwe. Zimenezi zingatilefuleko, koma tisakhumudwe. (Mlal. 7:9) Ngati simukuyankhapo kaŵili-kaŵili mmene mukufunila, mvetselani mwachelu pamene ena akupeleka ndemanga, ndipo ayamikileni pambuyo pa msonkhano. Kuwayamikila kudzawalimbikitsa monga mmene mukanawalimbikitsila na ndemanga zanu. Kuyamikila ena ni njila inanso yolimbikitsila abale na alongo. w23.04 23-24 ¶14-16

Cinayi, May 8

Ndatsimikiza mtima, Inu Mulungu.​—Sal. 57:7.

Muziŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha. Mtengo umakhala wolimba ngati mizu yake inazikika pansi mozama. Mofananamo, tingakhalebe olimba ngati cikhulupililo cathu n’cozikika mozama m’Mawu a Mulungu. Mtengo ukamakula, mizu yake imaloŵa pansi kwambili na kutambalala. Tikamaŵelenga Baibo na kusinkhasinkha, timalimbitsa cikhulupililo cathu, komanso timakhala otsimikiza kothelatu kuti mfundo za Yehova ndizo zabwino koposa. (Akol. 2:6, 7) Ganizilani mmene malangizo a Yehova, citsogozo, na citetezo cake, cinathandila atumiki ake akale. Mwacitsanzo, Ezekieli anayang’anitsitsa pamene mngelo anali kuyesa kacisi m’masomphenya. Masomphenya amenewo anam’limbikitsa Ezekieli. Ndipo amatiphunzitsa mmene tingatsatilile miyeso ya Yehova pa nkhani ya kulambila koyela. (Ezek. 40:1-4; 43:10-12) Timapindula tikamapatula nthawi yoŵelenga na kusinkhasinkha zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu. Tingatsimikize mtima mwa kudalila Yehova na mtima wonse.​—Sal. 112:7. w23.07 18 ¶15-16

Cisanu, May 9

Uteteze . . . kuganiza bwino.​—Miy. 3:21.

M’Baibo muli zitsanzo zambili zimene acinyamata angatengele. Amuna a m’nthawi zakale amenewo anali kumukonda Mulungu ndipo anasenza maudindo osiyana-siyana posamalila anthu ake. Mungapezenso zitsanzo zabwino za Akhristu okhwima m’banja mwanu komanso mu mpingo mwanu. (Aheb. 13:7) Ndipo mulinso na citsanzo cabwino kwambili ca Yesu Khristu. (1 Pet. 2:21) Pamene musinkhasinkha zitsanzo zimenezi mofatsa, ganizilani makhalidwe abwino amene mumasilila kwa iwo. (Aheb. 12:1, 2) Ndiyeno onani mmene mungatengele citsanzo cawo. Mwamuna woganiza bwino amaganizila zosankha zake asanacitepo kanthu. Conco limbikilani kuti mukhale oganiza bwino. Yambani mwa kuphunzila mfundo za m’Baibo na kuona cifukwa cake mfundozo n’zothandiza. Ndiyeno seŵenzetsani mfundozo kupanga zisankho zokondweletsa Yehova. (Sal. 119:9) Ili ndilo sitepe lalikulu lofunika kuti mukhale Mkhristu wokhwima.​—Miy. 2:11, 12; Aheb. 5:14. w23.12 24-25 ¶4-5

Ciŵelu, May 10

Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za ciyembekezo canu, koma muziwayankha mofatsa ndiponso mwaulemu kwambili.​—1 Pet. 3:15.

Makolo angaphunzitse ana awo mmene angayankhile modekha cikhulupililo cawo cikatsutsidwa. (Yak. 3:13) Makolo ena amasankha kuyeseza pa kulambila kwa pa banja mmene angayankhile modekha. Amasankha nkhani zimene zingabuke ku sukulu na kuzikambilana. Kenako amacita citsanzo na kuphunzitsa ana awo mmene angayankhile modekha komanso mofika pa mtima. Kuyeseza kungathandize Akhristu kupeleka mayankho okhutilitsa. Kungawathandizenso kutsimikizila paokha kuti zimene amakhulupilila ni coonadi. Nkhani zakuti “Zimene Acinyamata Amafunsa” pa jw.org ku Chichewa, zili na mbali yakuti zoti achinyamata achite. Mbali imeneyi, inakonzedwa kuti ithandize acinyamata kulimbitsa cikhulupililo cawo, na kuwathandiza kukhala okonzeka kuyankha anthu m’mawu awo-awo. Mwa kuŵelenga nkhanizi monga banja, tonse tingaphunzile kukhalila kumbuyo cikhulupililo cathu mofatsa. w23.09 17 ¶10; 18 ¶15-16

Sondo, May 11

Tisasiye kucita zabwino, cifukwa pa nthawi yake tidzakolola tikapanda kutopa.​—Agal. 6:9.

Kodi munadziikilapo colinga cauzimu, koma cinakuvutani kucikwanilitsa? Ngati n’telo, sindinu nokha. Mwacitsanzo, m’bale Philip anadziikila colinga cakuti awongolele mapempelo ake komanso kupemphela pafupi-pafupi. Koma cinali kumuvuta kupeza nthawi yopemphela. Mlongo Erika anadziikila colinga cofika mofulumila pa kukumana kotenga malangizo a ulaliki. Ngakhale n’conco, iye anali kufikabe mocedwa. Ngati palipano simunakwanilitse colinga canu, dziŵani kuti sindinu wolephela. Ngakhale kukwanilitsa colinga cacing’ono kumafuna nthawi na kulimbika. Kuyesetsa kuti mukwanilitse colinga canu, kumaonetsa kuti mumaona ubale wanu na Yehova kukhala wofunika kwambili, komanso kuti mumafuna kum’patsa zabwino kopambana. Yehova amayamikila kuyesetsa kwanu. Komabe, iye sayembekezela kuti mucite zimene simungathe. (Sal. 103:14; Mika 6:8) Conco, dziikileni colinga cimene mungacikwanilitse, malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wanu. w23.05 26 ¶1-2

Mande, May 12

Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?​—Aroma 8:31.

Anthu olimba mtima angacite mantha, koma samalola kuti manthawo awalepheletse kucita zoyenela. Danieli anali mnyamata wolimba mtima kwambili. Iye anali kuŵelenga zolemba za aneneli a Mulungu, kuphatikizapo maulosi a Yeremiya. Mwa kutelo, iye anazindikila kuti Ayuda amene anali mu ukapolo kwa zaka zambili ku Babulo anali pafupi kumasulidwa. (Dan. 9:2) Cidalilo ca Danieli mwa Yehova cinalimba ngako ataona kukwanilitsika kwa maulosi a m’Baibo. Ndipo anthu amene amadalila Yehova na mtima wonse amakhala olimba mtima kwambili. (Yelekezelani na Aroma 8:32, 37-39.) Coposa zonse, Danieli anali kupemphela nthawi zonse kwa Atate wake wakumwamba. (Dan. 6:10) Anavomeleza macimo ake kwa Yehova, na kumuuza mmene anali kumvela, ndipo anali kupempha thandizo lake. (Dan. 9:4, 5, 19) Iye anali munthu ngati ife tomwe. Conco, kulimba mtima sanacite kubadwa nako. M’malo mwake, anakulitsa khalidweli mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu, kupemphela, na kudalila Yehova. w23.08 3 ¶4; 4 ¶7

Ciŵili, May 13

Muzionetsa kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino nʼkulemekeza Atate wanu wakumwamba.​—Mat. 5:16.

Kumvela akulu-akulu a boma kumatipindulila ife eni komanso anthu ena. Motani? Mwa zina, timapewa cilango cobwela cifukwa cosamvela malamulo. (Aroma 13:1, 4) Kumvela kwathu kungakhudze mmene akulu-akulu a boma amaonela gulu lonse la Mboni za Yehova. Mwacitsanzo, zaka zambili kumbuyoku, asilikali ku Nigeria analoŵa mu Nyumba ya Ufumu misonkhano ili mkati. Iwo anali kufuna-funa anthu amene anali kucita zionetselo cifukwa cosafuna kulipila misonkho ina yake. Mkulu wa asilikali anauza asilikaliwo kuti “tiyeni ticoke, Mboni za Yehova zimalipila misonkho nthawi zonse.” Mukamamvela malamulo, mumathandiza kukometsela mbili ya Mboni za Yehova​—ndipo zimenezi zikhoza kudzathandiza abale na alongo m’tsogolo. w23.10 9 ¶13

Citatu, May 14

Mukufunika kukhala opilila komanso kucita cifunilo ca Mulungu kuti mudzalandile zimene Mulunguyo walonjeza.​—Aheb. 10:36.

Atumiki ena a Yehova akhala akuyembekezela mapeto a dzikoli kwa nthawi yaitali. M’kaonedwe kaumunthu, zingaoneke ngati Mulungu akucedwa kukwanilitsa malonjezo ake. Yehova amadziŵa nkhawa za atumiki ake. N’cifukwa cake anatsimikizila mneneli Habakuku kuti: “Masomphenyawa akuyembekezela nthawi yake yoikidwilatu ndipo akuthamangila kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengeleza, uziwayembekezelabe cifukwa adzakwanilitsidwa ndithu. Iwo sadzacedwa.” (Hab. 2:3) Kodi ni Habakuku yekha amene analimbikitsidwa na citsimikizo ca Mulungu cimeneci? Kapena nafenso timalimbikitsidwa na mawu amenewa masiku ano? Mouzilidwa, mtumwi Paulo analunjikitsa mawu amenewo kwa Akhristu amene akuyembekezela dziko latsopano. (Aheb. 10:37) Conco, ndife otsimikiza kuti lonjezo la Mulungu lakuti adzatipulumutsa ‘lidzakwanilitsidwa ndithu,’ ngakhale lingaoneke ngati likucedwa. w23.04 30 ¶16

Cinayi, May 15

Aisiraeli onse anayamba kungʼungʼudzila Mose.​—Num. 14:2.

Aisiraeli anakana umboni woonekelatu wakuti Yehova anali kuseŵenzetsa Mose monga womuimilako. (Num. 14:10, 11) Mobweleza-bweleza, iwo anakana zakuti Yehova ndiye anali kugwilitsa nchito Mose. Zotulukapo zake zinali zakuti m’badwo umenewo sunaloledwe kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:30) Koma panali Aisiraeli ena amene anatsatila citsogozo ca Yehova. Mwacitsanzo, Yehova anati: “Kalebe . . . wakhala akunditsatila ndi mtima wonse.” (Num. 14:24.) Yehova anam’dalitsa Kalebe mwa kum’patsa malo amene iye anasankha m’dziko la Kanani. (Yos. 14:12-14) Nawonso m’badwo wotsatila wa Aisiraeli unapeleka citsanzo cabwino pa nkhani yotsatila citsogozo ca Yehova. Yoswa ataloŵa m’malo mwa Mose monga mtsogoleli wa Aisiraeli, iwo “anayamba kumulemekeza kwambili masiku onse a moyo wake ngati mmene ankalemekezela Mose.” (Yos. 4:14) Zotulukapo zake, Yehova anawadalitsa mwa kuwaloŵetsa m’dziko limene anawalonjeza.​—Yos. 21:43, 44. w24.02 21 ¶6-7

Cisanu, May 16

Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso mʼbale wake.​—1 Yoh. 4:21.

Monga mmene dokotala amadziŵila thanzi la mtima wathu akatigwila pa dzanja kuti adziŵe mmene ukuthamangila, nafenso tingadziŵe kukula kwa cikondi cathu pa Mulungu tikaona mmene timakondela ena. Tikaona kuti cikondi cathu pa okhulupilila anzathu cikucepa, cingakhale cizindikilo cakuti cikondi cathu pa Mulungu naconso cikucepa. Koma ngati timaonetsa cikondi kwa okhulupilila anzathu, cingakhale cizindikilo cabwino cakuti cikondi cathu pa Mulungu n’colimba. Tiyenela kuda nkhaŵa ngati cikondi cathu pa abale na alongo cikucepa. Cifukwa ciyani? Cifukwa izi zingatanthauze kuti uzimu wathu uli pa ciopsezo. Mtumwi Yohane anamveketsa bwino mfundoyi pamene anatikumbutsa kuti: “Pakuti amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Tiphunzilapo ciyani? Yehova amasangalala nafe ngati ‘timakondana.’​—1 Yoh. 4:7-9, 11. w23.11 8 ¶3; 9 ¶5-6

Ciŵelu, May 17

Bambo ako ndi mayi ako adzasangalala.​—Miy. 23:25.

Ali wacicepele, Mfumu Yehoasi anapanga cisankho cabwino. Popeza analibe tate, iye anatsatila citsogozo ca Mkulu wa Ansembe wokhulupilika Yehoyada. Mkulu wa a ansembeyo analangiza Yehoasi monga mwana wake wodzibalila. Zotulukapo zake, Yehoasi anasankha kutumikila Yehova na kutsogolela pa kulambila koona. Iye anafika mpaka pokonzanso kacisi wa Yehova. (2 Mbiri 24:1, 2, 4, 13, 14) Ngati wina akukuphunzitsani kukonda Yehova na kutsatila miyeso yake, ndiye kuti akukupatsani mphatso ya mtengo wapatali. (Miy. 2:1, 10-12) Makolo anu angakuphunzitseni m’njila zambili. Mukamaseŵenzetsa ulangizi wa m’Malemba umene makolo anu amapeleka, mudzawasangalatsa kwambili. Koma koposa zonse, mudzakondweletsa Mulungu ndipo ubwenzi wanu na iye udzalimba. (Miy. 22:6; 23:15, 24) Izi ni zifukwa zabwino kwambili zotipangitsa kutengela citsanzo ca Yehoasi ali mwana. w23.09 8-9 ¶3-5

Sondo, May 18

Ndidzakumvetselani.​—Yer. 29:12.

Yehova akulonjeza kuti adzamvetsela mapemphelo athu. Mulungu wathu amawakonda alambili ake okhulupilika ndipo sadzanyalanyaza mapemphelo awo. (Sal. 10:17; 37:28) Komabe izi sizitanthauza kuti iye adzatipatsa zilizonse zimene timam’pempha. Tingafunike kuyembekeza mpaka m’dziko latsopano kuti tikalandile zina mwa zinthu zimene timapempha. Yehova amafuna kuona ngati mapemphelo athu amagwilizana na colinga cake cacikulu. (Yes. 55:8, 9) Colinga cimeneco ciphatikizapo kudzaza dziko lapansi na anthu acimwemwe komanso ogwilizana pansi pa ulamulilo wake. Koma Satana amanena kuti anthu angakhale osangalala atadzilamulila okha. (Gen. 3:1-5) Pofuna kuonetsa kuti maganizo a Mdyelekezi amenewa ni abodza, Yehova walola kuti anthu adzilamulile okha. Ndipo ulamulilo wa anthu wabweletsa mavuto ambili amene aliko masiku ano. (Mlal. 8:9) Tidziŵa kuti Yehova sadzacotsapo mavuto onsewa pali pano. w23.11 21 ¶4-5

Mande, May 19

Ndakusankha kuti ukhale bambo wa mitundu yambili.​—Aroma 4:17.

Yehova analonjeza kuti mwa Abulahamu “mitundu yambili” idzadalitsidwa. Komabe, pamene Abulahamu anafika zaka 100 komanso Sara ali na zaka 90, mwana amene analonjezedwa anali asanabadwe. M’kaonedwe kaumunthu, zinali zosatheka kwa Abulahamu na Sara kukhala na mwana. Zimenezi zinayesa cikhulupililo ca Abulahamu pa mlingo waukulu. Komabe iye “anali ndi ciyembekezo ndiponso cikhulupililo cakuti adzakhala tate wa mitundu yambili.” (Aroma 4:18, 19) Ndipo patapita nthawi, lonjezo litakwanilitsidwa, iye anakhala tate wa Isaki, mwana yemwe anali atalonjezedwa kalelo. (Aroma 4:20-22) N’zotheka kuyanjidwa na Mulungu, komanso kuonedwa kukhala wolungama pokhala bwenzi lake monga zinalili kwa Abulahamu. Ndipo Paulo ananenapo za mfundo imeneyi pomwe anati: “Komabe, zonena kuti anayesedwa wolungama sizinalembedwele [Abulahamu] yekha, komanso ife amene tidzayesedwa otelo, cifukwa cakuti timakhulupilila iye amene anaukitsa Yesu.” (Aroma 4:23, 24) Monga Abulahamu, ifenso tifunikila cikhulupililo komanso nchito zake kuphatikizapo ciyembekezo. w23.12 7 ¶16-17

Ciŵili, May 20

Mwaona kusautsika kwanga. Mukudziwa mavuto aakulu amene ndili nawo.​—Sal. 31:7.

Mukakumana na vuto lokucititsani mantha, kumbukilani kuti Yehova amadziŵa za vutolo komanso mmene lakukhudzilani. Mwacitsanzo, Yehova anali kudziŵa bwino mazunzo amene Aisiraeli anali kukumana nawo ku Iguputo komanso “ululu umene [anamva].” (Eks. 3:7) Mwina mungakaikile zakuti Yehova akukuthandizani pokumana na vuto loopsa. Zikatelo, m’pempheni kuti akuthandizeni kuona thandizo lake. (2 Maf. 6:15-17) Ndiyeno ganizilani izi: Kodi munalimbikitsidwapo na nkhani kapena ndemanga pa msonkhano wa mpingo? Kodi munalimbikitsidwapo na cofalitsa, vidiyo, kapena nyimbo yopekedwa koyamba? Kodi munthu wina anakugaŵilam’poni mfundo yolimbikitsa kapena lemba? Tingaiŵale mwamsanga mmene timapindulila na cikondi ca abale na alongo komanso cakudya cauzimu cimene timalandila. Zimenezi ni mphatso za mtengo wapatali zocokela kwa Yehova. (Yes. 65:13; Maliko 10:29, 30) Zimaonetsa kuti Yehova amasamala za ife. (Yes. 49:14-16) Ndipo zimatipatsanso cifukwa comudalila. w24.01 4-5 ¶9-10

Citatu, May 21

Tithandizeni ife akapolo anu kuti tipitilize kulankhula mawu anu molimba mtima.​—Mac. 4:29.

Atatsala pang’ono kubwelela kumwamba, Yesu anakumbutsa ophunzila ake za utumiki umene anapatsidwa wocitila umboni za iye “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; Luka 24:46-48) Patangopita nthawi yocepa, atsogoleli aciyuda anagwila mtumwi Petulo na Yohane n’kuwapeleka ku Khoti Lapamwamba la Ayuda. Kumeneko, amuna okhulupilika amenewa analamulidwa kuti aleke kulalikila, ndipo anawaopseza. (Mac. 4:18, 21) Petulo na Yohane anati: “Weluzani nokha, ngati n’zoyenela pamaso pa Mulungu kumvela inu m’malo momvela Mulunguyo. Koma ife sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:19, 20) Petulo na Yohane atamasulidwa, ophunzilawo anapemphela kwa Yehova mofuula kuti aŵathandize kucita cifunilo cake. Yehova anayankha pemphelo lawo locokela pansi pa mtima.​—Mac. 4:31. w23.05 5 ¶11-12

Cinayi, May 22

Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.​—Mat. 17:5.

Kwa zaka zosaŵelengeka, Yehova na Mwana wake wokondeka anasangalala na ubwenzi wathithithi wa cikondi. Ubale wawo ndiwo wakhalitsa kwambili m’cilengedwe conse. Mu lemba la lelo, Yehova anaonetsa bwino mmene amam’kondela Yesu. Akanafuna Yehova akanangonena kuti, ‘Uyu ndiye amene ndikukondwela naye.’ Komabe iye anafuna kuti tidziŵe mmene amakondela Yesu. Conco, iye anamucha “Mwana wanga wokondedwa.” Yehova anam’nyandila Yesu maka-maka cifukwa cakuti anali kudzapeleka moyo wake. (Aef. 1:7) Ndipo Yesu anali kudziŵa mmene Atate wake anali kumvela pa iye. Cikondi ca Yehova pa Yesu cinali ceni-ceni, ndipo Yesu anali kudziŵa kuti Atate ake amamukonda. Mobweleza-bweleza Yesu ananena motsimikiza kuti Atate wake amamukonda.​—Yoh. 3:35; 10:17; 17:24. w24.01 28 ¶8

Cisanu, May 23

Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi cuma coculuka.​—Miy. 22:1.

Yelekezani kuti munthu amene mumadalila wanena zinthu zoipa zokhudza inu. Inu mudziŵa kuti nkhaniyo ni yabodza; koma ena akuikhulupilila. Coposa pamenepa, iwo akuifalitsa, ndipo anthu ambili akuikhulupilila. Kodi mungamve bwanji? Mosakayikila, bodza limenelo lingakupangitseni kumva kuipa kwambili, si conco? Citsanzoci, citithandiza kumvetsa mmene Yehova anamvela pomwe dzina lake linaipitsidwa. Mmodzi wa ana ake auzimu ananena bodza lokhudza iye kwa mkazi woyamba, Hava. Ndipo iye analikhulupilila. Bodzalo linacititsa kuti makolo athu oyambilila apandukile Yehova. Zotsatila zake n’zakuti ucimo na imfa zinaloŵa m’banja la anthu. (Gen. 3:1-6; Aroma 5:12) Mavuto onse amene timaona m’dzikoli​—imfa, nkhondo, kuvutika—​anabwela cifukwa ca bodza limene Satana akufalitsa. Ndipo mosapeneka konse, bodzalo limamuŵaŵa ngako Yehova, komanso zotulukapo zake. Ngakhale n’telo, Yehova sanasunge msunamo kapena kusunga cakukhosi. M’malo mwake, iye akupitilizabe kukhala “Mulungu wacimwemwe.”​—1 Tim. 1:11. w24.02 8 ¶1-2

Ciŵelu, May 24

Ndingacitilenji coipa cacikulu conci nʼkucimwila Mulungu?​—Gen. 39:9.

Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yosefe? Mwa kusankhilatu pali pano zimene mudzacita mukakumana na mayeselo. Phunzilani kukaniza mwamsanga zinthu zimene Yehova amadana nazo ngakhale kupewa kuziganizila. (Sal. 97:10; 119:165) Mwa kutelo, simudzagonja mukayesedwa. Pa inu nokha, mungakhale wotsimikiza kuti munapeza coonadi, ndipo mukufunitsitsa kutumikila Yehova na mtima wanu wonse. Ngakhale n’telo, mungakhalebe na cina cake comwe cingakulepheletseni kudzipatulila na kubatizika. Ngati n’conco, mungatengele citsanzo ca Mfumu Davide. Mungamucondelele Yehova kuti “Ndifufuzeni inu Mulungu, ndipo mudziwe mtima wanga. Ndifufuzeni ndipo mudziwe maganizo anga amene akundidetsa nkhawa. Muone ngati mwa ine muli ciliconse coipa, ndipo munditsogolele mʼnjila yamuyaya.” (Sal. 139:23, 24) Yehova amadalitsa “anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Kulimbikila kwanu kuti mukwanilitse colinga ca kudzipatulila na kubatizika cimaonetsa kuti mumamufuna-funa na mtima wonse.​—Aheb. 11:6 w24.03 6 ¶13-15

Sondo, May 25

Iye safunikila kupeleka tsiku ndi tsiku nsembe.​—Aheb. 7:27.

Mkulu wa ansembe anapatsidwa udindo woimilako anthu kwa Mulungu. Mkulu wa ansembe woyamba Aroni, anadzozedwa na Yehova pamene anapatulila cihema cokumanako. Koimabe, monga anakambila mtumwi Paulo, “pankafunika ansembe ambili olowa mʼmalo cifukwa imfa inkacititsa kuti munthu asapitilize kukhala wansembe.” (Aheb. 7:23-26) Cifukwa cakuti anali opanda ungwilo, akulu ansembe amenewa anayenela kupeleka nsembe cifukwa ca macimo awo. Pamenepa paonetsa kusiyana kwakukulu komwe kulipo pakati pa akulu ansembe a mu Isiraeli komanso Mkulu wa Ansembe wopambana onse, Yesu Khristu. Mkulu wathu Wansembe Yesu Khristu “ndi mtumiki . . . m’cihema ceniceni, comangidwa ndi Yehova, osati munthu.” (Ahe. 8:1, 2) Paulo anafotokoza kuti “cifukwa cokhala ndi moyo kosatha [Yesu] palibe womuloŵa m’malo pa unsembe wake.” Anawonjezela kuti Yesu ni “wosaipitsidwa wosiyana ndi anthu ocimwa” ndipo mosiyana na akulu ansembe a mu Isiraeli, “iye safunikila kupeleka tsiku ndi tsiku nsembe zamacimo ake.” w23.10 26 ¶8-9

Mande, May 26

Kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitacoka.​—Chiv. 21:1

“Kumwamba kwakale” kuimila maboma andale omwe ali pansi pa ulamulilo wa Satana na ziŵanda zake. (Mat. 4:8, 9; 1 Yoh. 5:19) Monga imaonetsela Baibo, mawu akuti “dziko lapansi” angatanthauze anthu okhala pa dziko lapansi. (Gen. 11:1; Sal. 96:1) Conco, “dziko lapansi lakale” limatanthauza anthu oipa omwe alipo masiku ano. Sikuti Yehova adzangokonzanso “kumwamba” na “dziko lapansi” ayi; koma adzazicotselatu na kubweletsapo zatsopano. Adzalenga “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano”​—kutanthauza boma latsopano lolamulila anthu olungama. Yehova adzapanga dziko kukhala latsopano komanso anthu mwa kubwezeletsa ungwilo. Monga Yesaya ananenela, Yehova adzapanga dziko lonse lapansi kukhala Paradaiso wokongola. Ifenso tidzapangidwa kukhala atsopano, aliyense payekha-payekha. Anthu aulemali, osakhoza kuona kapena kumva adzacilitsidwa. Ngakhale akufa adzaukitsidwa.​—Yes. 25:8; 35:1-7. w23.11 4 ¶9-10

Ciŵili, May 27

Khalani okonzeka.​—Mat. 24:44.

“Cisautso cacikulu” cidzayamba mwadzidzidzi. (Mat. 24:21) Mosiyana na matsoka ena, kwa ife atumiki a Mulungu cisautso cacikulu sicidzatidzidzimutsa ayi. Tikutelo cifukwa zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo, Yesu anauza otsatila ake kuti akhale okonzeka za tsikulo. Tikakhala okonzeka, cidzakhala capafupi kuipilila nthawi yovuta kwambili imeneyo, komanso kuthandizako ena kucita cimodzimodzi. (Luka 21:36) Tidzafunikila khalidwe la kupilila kuti tikamvele Yehova, na kum’khulupilila kuti adzatiteteza. Kodi tidzacita ciyani abale athu akadzataikilidwa zina mwa zinthu zawo zakuthupi kapena zonse? (Hab. 3:17, 18) Tidzafunikila khalidwe la cifundo limene lidzatilimbikitsa kukapeleka thandizo lofunikila kwa iwo. Kodi tidzacita bwanji tikadzafunika kukhalila pamodzi na abale na alongo athu cifukwa coukilidwa na mgwilizano wa mitundu? (Ezek. 38:10-12) Tidzafunikila cikondi cacikulu kuti tikawathandize kupilila nthawi yovuta imeneyo. w23.07 2 ¶2-3

Citatu, May 28

Samalani kwambili kuti mukamayenda, musamayende ngati anthu opanda nzelu koma ngati anthu anzelu. Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.​—Aef. 5:15, 16.

Okwatilana angaphunzile zambili kwa Akula na Purisikila. Banja limenelo linali kukondedwa na Akhristu oyambilila. (Aroma 16:3, 4) Iwo anali kucitila zinthu pamodzi, monga kugwila nchito, kulalikila, na kuthandiza anthu ena. (Mac. 18:2, 3, 24-26) Ndipo nthawi zonse, Baibo imachula Akula na Purisikila ali limodzi. Kodi okwatilana angatengele bwanji citsanzo ca Akula na Purisikila? Ganizilani nchito zambili zimene inu muli nazo, na zimene mnzanu wa mu ukwati ali nazo. Kodi mungagwilile pamodzi zina mwa nchitozo, m’malo mocita payekha-payekha? Mwacitsanzo, Akula na Purisikila anali kulalikila pamodzi. Kodi inunso mumacita zimenezi kaŵili-kaŵili? Akula na Purisikila analinso kuseŵenzela pamodzi. Mwina inu na mnzanu wa mu ukwati simugwila nchito yofanana. Koma kodi mungagwilileko pamodzi nchito zapakhomo? (Mlal. 4:9) Mukamagwilila pamodzi nchitozo, mumakhala ogwilizana, ndipo mumakhala na mpata woceza. w23.05 22-23 ¶10-12

Cinayi, May 29

Ine ndidzadalila inu, tsiku lililonse limene ndingacite mantha.​—Sal. 56:3.

Munthu aliyense amacita mantha nthawi zina. Mwacitsanzo, pamene Mfumu Sauli anali kusakasaka Davide kuti amuphe, Davide anathaŵila ku mzinda wa Afilisiti wochedwa Gati. Posakhalitsa, Akisi Mfumu ya ku Gati, anatulukila kuti Davide anali msilikali wamphamvu yemwe anthu anali kumuimbila nyimbo yakuti wakantha Afilisiti “masauzande makumimakumi.” Davide “anacita mantha kwambili.” (1 Sam. 21:10-12) Iye anada nkhawa na zimene Akisi adzamucita. Kodi Davide anagonjetsa bwanji mantha ake? Mu Salimo 56, Davide anafotokoza mmene anali kumvela ali ku Gati. Salimo limeneli lifotokoza cifukwa cake Davide anacita mantha, komanso cimene cinam’thandiza kuwagonjetsa. Iye anaika cidalilo cake mwa Yehova. (Sal. 56:1-3, 11) Davide anali na zifukwa zabwino zodalila Yehova. Na thandizo la Yehova, Davide anapanga nzelu ina yake yom’thandiza: Anadzipanga kukhala wamisala! Akisi anayamba kuona Davide kukhala munthu wacabe-cabe womunyansa, m’malo momuona monga munthu woopsa. Basi Davide anakwanitsa kuthawa.​—1 Sam. 21:13–22:1. w24.01 2 ¶1-3

Cisanu, May 30

Oitanidwa aja, omwe ndi osankhidwa mwapadela ndiponso okhulupilika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.​—Chiv. 17:14.

Kodi omwe akuchulidwa m’lemba la lelo n’ndani? Odzozedwa amene aukitsidwa! Conco, odzozedwa othela akadzatengedwela kumwamba cakumapeto kwa cisautso cacikulu, umodzi wa mautumiki awo oyamba udzakhala kumenya nkhondo. Pambuyo popita kumwamba, adzatumikila limodzi na Khristu komanso angelo ake oyela, pomenya nkhondo yothela yolimbana na adani a Mulungu. Ganizilani mfundo iyi. Padziko lapansi, ena mwa Akhristu odzozedwa ni acikulile ndipo alibe mphamvu. Koma akadzaukitsidwa kukakhala kumwamba, adzakhala zolengedwa zauzimu zamphamvu, komanso zosakhoza kufa. Ndiponso adzatumidwa kukamenya nkhondo pamodzi na Yesu Khristu, Mfumu yawo yacisilikali. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, iwo adzagwila nchito pamodzi na Yesu kuthandiza anthu kufika pa ungwilo. Mosakaikila, iwo akadzakhala kumwamba adzacitila abale na alongo awo zinthu zambili zabwino, zomwe sakanakwanitsa kucita ali anthu opanda ungwilo! w24.02 6-7 ¶15-16

Ciŵelu, May 31

Pitilizani kuyenda motsogoleledwa ndi mzimu, ndipo simudzacita zimene thupi lomwe si langwilo likulakalaka ngakhale pangʼono.​—Agal. 5:16.

Ngakhale kuti ena amakhala okonzeka kudzipatulila na kubatizidwa, amazengeleza. Angakhale na nkhawa yakuti, ‘Bwanji ngati pambuyo pobatizika nacita chimo lalikulu na kucotsedwa mu mpingo?’ Ngati mumamva conco, musakaikile zakuti Yehova adzakupatsani zonse zofunikila kuti “mukhale ndi khalidwe logwilizana ndi zimene [iye] amafuna.” (Akol. 1:10) Adzakupatsaninso mphamvu yokuthandizani kucita zoyenela. Angakwanitse kucita zimenezi cifukwa anathandizapo kale ena m’mbuyomu kucita zoyenela. (1 Akor. 10:13) Ici n’cimodzi mwa zifukwa zimene zimapangitsa kuti pakhale anthu ocepa amene amacotsedwa mu mpingo wa Cikhristu. Yehova amapeleka zonse zofunikila kwa anthu ake zowathandiza kukhalabe okhulupilika. Munthu aliyense wopanda ungwilo amakhalako pa mayeselo ofuna kucita zoipa. (Yak. 1:14) Koma ufulu umakhala wanu, kusankha kucita coipaco kapena kukana. Zoona zake n’zakuti, inuyo ndinu muli na mphamvu zosankha mmene umoyo wanu udzakhalila. Ngakhale kuti anthu ena amanena kuti n’zosatheka kulamulila mmene mukumvela kapena kulamulila moyo wanu, koma n’zotheka ndithu. w24.03 5 ¶11-12

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani