Kodi Cipembedzo Mungacikhulupilile Pankhani ya Makhalidwe?
Sylvia amene amagwila nchito ya zacipatala anati: “Ndinali pa koleji ndi anthu ambili amene anali kunena kuti amapita kuchalichi. Komabe, io anali kucita cinyengo polemba mayeso ndipo anali kumwa mankhwala oletsedwa. Cipembedzo cinalephela kusintha khalidwe lao.”
Mwamuna wochedwa Lionel anati: “Anthu amene ndimagwila nao nchito amanama kuti adwala pofuna kuti asapite ku nchito. Iwo ali ndi cipembedzo, koma samatsatila mfundo za makhalidwe abwino.”
Cipembedzo calephela kuthandiza anthu kukhala ndi makhalidwe abwino. Masiku ano, anthu ambili ‘amaoneka ngati odzipeleka kwa Mulungu, koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe.’ (2 Timoteyo 3:5) Abusa a cipembedzo sapeleka citsanzo cabwino pa nkhani ya makhalidwe kwa anthu ao. Ngakhale atsogoleli a cipembedzo sapeleka uphungu wa m’Malemba kwa nkhosa zao kuti zizikhala ndi khalidwe labwino. N’cifukwa cake anthu ambili amakhulupilila kuti kaya munthu ali ndi khalidwe lotani, Mulungu alibe nazo kanthu.
ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA
Baibo imasonyeza kuti Mulungu amakhudzidwa kwambili ndi zimene timacita. Pamene Aisiraeli akale anali kupandukila Mulungu, io “anali kumukhumudwitsa.” (Salimo 78:40) Komabe, ‘kumwamba kumakhala cisangalalo coculuka’ ngati munthu wocimwa wasinthadi khalidwe lake loipa. (Luka 15:7) Munthu akayamba kuyamikila makhalidwe abwino a Atate wathu wakumwamba, cikondi cake pa Mulungu cimakula. Cikondi cimeneco cimamulimbikitsa kukonda zinthu zimene Mulungu amakonda ndi kudana ndi zinthu zimene iye amadana nazo.—Amosi 5:15.
KODI MBONI ZA YEHOVA ZIMACITA BWANJI PANKHANIYI?
Nyuzipepala ina ya ku America inanena kuti, Mboni za Yehova “zimathandiza anthu kukhala ndi mabanja olimba, kulimbikila pa nchito ndi kukhala oona mtima.” Inanenso kuti: “Mboni za Yehova zimatsatila mfundo zapamwamba za makhalidwe. Iwo amakhulupilila kuti kusuta fodya, kumwa kwambili moŵa, kugwilitsila nchito mankhwala molakwika, kuchova njuga, ciwelewele ndi kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha kumaononga unansi wao ndi Mulungu.—The Deseret News of Salt Lake City, Utah, U.S.A.
Kodi kuphunzila za makhalidwe a Mulungu kumawathandiza bwanji a Mboni? Sylvia, amene tam’chula kuciyambi kwa nkhani ino anati: “Cinyengo ndi cofala kwa ogwila nchito zacipatala. Ndipo n’zosavuta kutengela khalidwe limeneli. Koma kudziŵa mmene Yehovaa amaonela cinyengo, kumandithandiza kucita zoyenela. Ndine munthu wosangalala ndipo ndili ndi mtendele wa mumtima.” Sylvia amakhulupilila kuti kukhala ndi moyo mogwilizana ndi zimene amaphunzila ku cipembedzo cake kwam’thandiza kukhala ndi makhalidwe abwino.
[Mau apansi]
a Yehova ndi dzina la Mulungu monga mmene Baibo imanenela.
[Mau okopa papeji 6]
Kodi atsogoleli a cipembedzo athandiza nkhosa zao kugwilitsila nchito miyezo ya Mulungu ya makhalidwe abwino?