LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 8/1 masa. 13-17
  • ‘Musakwiile Yehova’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • ‘Musakwiile Yehova’
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIANI CINGATIPANGITSE ‘KUKWIILA YEHOVA’?
  • KODI TINGAPEWE BWANJI ‘KUKWIILA YEHOVA’?
  • ONANI UBWENZI WANU NDI YEHOVA KUKHALA WAMTENGO WAPATALI
  • Yehova Amakukondani Kwambili!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Kodi Mumakhulupilila Mmene Yehova Amacitila Zinthu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Mulungu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • “Khulupilila Yehova Ndipo Cita Zabwino”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 8/1 masa. 13-17

‘Musakwiile Yehova’

“Kupusa kwa munthu wocokela kufumbi n’kumene kumapotoza njila yake, conco mtima wake umakwiila Yehova.”—MIY. 19:3.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi n’ciani cingatipangitse ‘kukwiila Yehova’?

Kodi ndi mfundo zisanu ziti zimene zingatithandize kuti tipewe kukwiila Mulungu?

Kodi tiyenela kukumbukila ciani tikakumana ndi mavuto?

1, 2. N’cifukwa ciani sitiyenela kuimba mlandu Yehova kaamba ka mavuto amene mtundu wa anthu ukukumana nao? Pelekani citsanzo.

TIYELEKEZELE kuti ndinu mwamuna amene mwakhala m’banja zaka zambili, ndipo mukusangalala. Koma tsiku lina mutafika kunyumba, mwapeza kuti zinthu m’nyumba zili mbwee. Mipando yathyoledwa, ziwiya za kukhichini zaonongedwa, ndipo mawindo aphwanyidwa. Nyumba yanu yakhala monga malo amene pacitika ngozi. Kodi mokwiya mungafunse kuti, “N’cifukwa ciani mkazi wanga wacita zimenezi?” Kapena mungafunse kuti, “Kodi ndani wacita zimenezi?” Mwacionekele mungafunse funso lomalizali. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti mukudziŵa kuti mkazi wanu wokondedwayo sangaononge zinthu conco.

2 Masiku ano timaona kuti dziko lapansi laipa kaamba ka kuonongedwa kwa cilengedwe ndiponso makhalidwe oipa monga ciwawa ndi ciwelewele. Popeza kuti timaphunzila Baibo, timadziŵa kuti si Yehova amene amacititsa mavuto amenewa. Iye analenga dziko lapansili kuti likhale paladaiso wokongola. (Gen. 2:8, 15) Yehova ndi Mulungu wacikondi. (1 Yoh. 4:8) Kuphunzila Malemba kwatithandiza kudziŵa amene amapangitsa kuti padziko lapansi pakhale mavuto ambili. Satana Mdyelekezi amene ndi “wolamulila wa dziko” ndiye amacititsa mavuto.—Yoh. 14:30; 2 Akor. 4:4.

3. Kodi maganizo athu angasokonezeke bwanji?

3 Komabe, sikuti ndi Satana amene amacititsa masoka onse amene timakumana nao. N’cifukwa ciani tikunena conco? Cifukwa cakuti mavuto ena amene timakumana nao ali kaamba ka zolakwa zathu. (Ŵelengani Deuteronomo 32:4-6.) N’zoona kuti tingavomeleze mfundo imeneyi, koma cifukwa ca kupanda ungwilo kwathu tingasokonezeke maganizo ndi kuyamba kucita zinthu zimene zingatibweletsele mavuto. (Miy. 14:12) Kodi zimenezo zingacitike bwanji? M’malo modziimba mlandu kapena kuimba mlandu Satana cifukwa ca mavuto athu, tingayambe kuimba mlandu Yehova. Tingafike mpaka ‘pokwiila Yehova.’—Miy. 19:3.

4, 5. Kodi n’ciani cingapangitse Mkristu ‘kukwiila Yehova’?

4 Kodi n’zothekadi kuti ‘tingakwiile Yehova’? Kucita zimenezo kungakhale kupanda nzelu. (Isa. 41:11) Palibe phindu limene tingapeze ngati tikwiila Mulungu. Munthu wina wolemba ndakatulo anati: “Dzanja lako ndi lalifupi kwambili cakuti sungakwanitse kumenyana ndi Mulungu.” Mwina sitingafike pokamba mau oonetsa kuti takwiila Yehova. Koma lemba la Miyambo 19:3, limanena kuti kupusa kwa munthu “kumapotoza njila yake, conco mtima wake umakwiila Yehova.” Inde, munthu angakwiile Mulungu mumtima mwake. Iye angaonetse kuti wakwiila Mulungu mwa zocita zake zing’ono-zing’ono. M’mau ena tinganene kuti wayamba kusungila cakukhosi Yehova. Cifukwa ca zimenezi munthuyo angaleke kupezeka pamisonkhano kapena angaleke kucilikiza mokwanila zinthu zina zokhudza kulambila Yehova.

5 N’ciani cingatipangitse ‘kukwiila Yehova’? Nanga tingapewe bwanji msampha umenewu? Ndi cinthu cofunika kwambili kudziŵa mayankho a mafunso amenewa. Tikutelo cifukwa cakuti zimakhudza ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu.

N’CIANI CINGATIPANGITSE ‘KUKWIILA YEHOVA’?

6, 7. N’cifukwa ciani Aisiraeli anayamba kudandaula ndi mmene Yehova anali kucitila zinthu m’nthawi ya Mose?

6 Kodi n’ciani cingapangitse mtumiki wokhulupilika wa Yehova kuyamba kudandaula mumtima ponena za Mulungu wake? Tiyeni tikambilane zinthu zisanu zimene zingayambitse vuto limeneli. Tidzapendanso zitsanzo za m’Baibo za anthu amene anagwela mu msampha umenewu.—1 Akor. 10:11, 12.

7 Zonena za anthu ena zingatipangitse kukwiila Mulungu. (Ŵelengani Deuteronomo 1:26-28.) Aisiraeli anali atangoomboledwa kumene mu ukapolo ku Iguputo. Mozizwitsa Yehova anabweletsa milili 10 pa mtundu wankhanza umenewo, ndipo pambuyo pake anaononga Farao ndi asilikali ake pa Nyanja Yofiila. (Eks. 12:29-32, 51; 14:29-31; Sal. 136:15) Anthu a Mulungu anali okonzeka kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma panthawi imeneyo, Aisiraeli anayamba kudandaula ndi zocita za Yehova. Kodi n’ciani cinapangitsa kusoŵa cikhulupililo kumeneko? Mitima yao inasungunuka ndi mantha cifukwa ca uthenga woipa umene anthu ena amene anapita kukazonda dzikolo anabweletsa. (Num. 14:1-4) Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? M’badwo wonse umenewo sunaloledwe kulowa ‘m’dziko labwino’ limenelo. (Deut. 1:34, 35) Kodi tikuphunzilapo ciani pa cocitika cimeneci? Tikuphunzilapo kuti sitiyenela kulola zonena zoipa za anthu ena kufooketsa cikhulupililo cathu ndi kutipangitsa kudandaula cifukwa ca mmene Yehova amacitila zinthu.

8. N’ciani cinapangitsa anthu a Mulungu m’nthawi ya Yesaya kuyamba kuimba mlandu Yehova cifukwa ca mavuto ao?

8 Mavuto angatilefule. (Ŵelengani Yesaya 8:21, 22.) M’nthawi ya Yesaya, mtundu wa Yuda unakumana ndi mavuto aakulu. Iwo anali atazungulilidwa ndi adani. Cakudya cinali cosowa, ndipo anthu ambili anali ndi njala. Koma vuto lao lalikulu linali njala ya kuuzimu. (Amosi 8:11) M’malo modalila Yehova kuti awathandize pa mavuto ao, io anayamba “kutukwana” mfumu yao ndi Mulungu wao. Inde, io anaimba mlandu Yehova cifukwa ca mavuto ao. Kodi ifenso tikakumana ndi mavuto timayamba kudandaula mumtima ndi kunena kuti, ‘N’cifukwa ciani Yehova sanandithandize pamene ndinali kuvutika?’

9. N’cifukwa ciani Aisiraeli anakhala ndi maganizo olakwika m’nthawi ya Ezekieli?

9 Ngati sitikudziŵa mfundo zonse zokhudza nkhani inayake. Cifukwa cakuti Aisiraeli m’nthawi ya Ezekieli sanali kudziŵa bwino mfundo zonse zokhudza njila za Yehova, io anayamba kuona monga njila zake zinali “zopanda cilungamo.” (Ezek. 18:29) Iwo anadziika kukhala monga oweluza Mulungu mwa kuika miyezo yao ya cilungamo pamwamba pa miyezo ya Yehova, ndipo anamuweluza mogwilizana ndi mmene io anali kuonela zinthu. Ngati nthawi zina sitikumvetsetsa bwino nkhani inayake ya m’Baibo kapena mmene zinthu zikuyendela pa umoyo wathu, kodi ifenso timayamba kuganiza kuti njila ya Yehova ndi yokondela kapena ‘yopanda cilungamo’?—Yobu 35:2.

10. Kodi munthu angatengele bwanji citsanzo coipa ca Adamu?

10 Timaimba ena mlandu cifukwa ca macimo athu ndi zolakwa zathu. Munthu woyambilila, Adamu, anaimba Mulungu mlandu cifukwa ca chimo lake. (Gen. 3:12) Ngakhale kuti Adamu anacimwila dala ndipo anali kudziŵa zotsatilapo za kuswa lamulo la Mulungu, iye anaimba Yehova mlandu cifukwa ca chimo lake. Tinganene kuti iye anali kukamba kuti Yehova anam’patsa mkazi woipa. Mpaka pano, anthu enanso akhala akuimba mlandu Mulungu cifukwa ca zolakwa zao monga mmene Adamu anacitila. Tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi kukhumudwa ndi kulefulidwa cifukwa ca zolakwa zanga kungandipangitse kuti ndiziona ngati miyezo ya Yehova ndi yoipa?’

11. Kodi zimene Yona anacita zimatiphunzitsa ciani?

11 Tikakhala odzikonda kwambili. Mneneli Yona anakhumudwa cifukwa cakuti Yehova anacitila cifundo anthu a ku Nineve. (Yona 4:1-3) N’cifukwa ciani iye anakhumudwa? Iye anali kuopa kucita manyazi ciweluzo cimene anali kulengeza cikalepheleka. Cifukwa coganizila kuti mbili yake idzaipa, Yona analephela kumvela cifundo anthu olapa a ku Nineve. Kodi ifenso cifukwa codzikonda ‘tingakwiile Yehova’ poona kuti sakubweletsa cionongeko mwamsanga? Ngati takhala tikulalikila kwa nthawi yaitali kuti tsiku la Yehova lili pafupi, kodi tingakwiile Yehova pamene ena akutitsutsa cifukwa colengeza uthenga wa m’Baibo?—2 Pet. 3:3, 4, 9.

KODI TINGAPEWE BWANJI ‘KUKWIILA YEHOVA’?

12, 13. Kodi tiyenela kucita ciani ngati tayamba kukaikila zocita za Yehova mumtima mwathu?

12 Kodi n’ciani cimene tingacite ngati mtima wathu wocimwa uyamba kukaikila zocita za Yehova? Musaiwale kuti kucita zimenezo ndi kupanda nzelu. Tili ndi mfundo imeneyi m’maganizo, tiyeni tsopano tikambitsilane mfundo zisanu zimene zingatithandize kupewa kuimba mlandu Yehova tikalefuka.

13 Limbitsani ubwenzi wanu ndi Yehova. Tingapewe cizolowezi coipa cokonda kukwiila Mulungu ngati tikhalabe paubwenzi wolimba ndi iye. (Ŵelengani Miyambo 3:5, 6.) Tiyenela kukhulupilila Yehova. Sitiyenela kudziona kuti ndife anzelu kapena kukhala odzikonda. (Miy. 3:7; Mlal. 7:16) Tikatelo, sitidzaimba mlandu Yehova zinthu zoipa zikacitika.

14, 15. N’ciani cingatithandize kuti tisafooke ndi zinthu zoipa zimene anthu ena anganene?

14 Musalole zonena za ena kukufooketsani. Aisiraeli m’nthawi ya Mose anali ndi zifukwa zambili zokhulupilila kuti Yehova sadzalephela kuwalowetsa m’Dziko Lolonjezedwa. (Sal. 78:43-53) Koma pamene anamva mau ofooketsa a azondi 10 osakhulupilika, io “sanakumbukile dzanja la Mulungu.” (Sal. 78:42) Ngati timasinkha-sinkha pa nchito za Yehova ndi kukumbukila zinthu zonse zabwino zimene waticitila, tidzalimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. Mwa kutelo, zinthu zoipa zimene anthu ena anganene sizidzaononga ubwenzi wathu ndi Yehova.—Sal. 77:11, 12.

15 Komabe, ngati timaganizila okhulupilila anzathu zinthu zoipa, zimenezo zingakhudze ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Yoh. 4:20) Pamene Aisiraeli anatsutsa kuti Aroni akhale paudindo, Yehova anaona kuti io anali kudandaula motsutsana ndi Iye. (Num. 17:10) Mofananamo, ngati ife tayamba kung’ung’udza ndi kudandaula ponena za anthu amene Yehova akuwagwilitsila nchito kutsogolela gulu lake la padziko lapansi, ndiye kuti tikudandaula motsutsana ndi Yehova.—Aheb. 13:7, 17.

16, 17. Kodi tiyenela kukumbukila ciani tikakumana ndi mavuto?

16 Musaiwale kuti Yehova sindiye amacititsa mavuto athu. Ngakhale kuti Aisiraeli m’nthawi ya Yesaya anali atasiya Yehova, Iye anali kufunabe kuwathandiza. (Yes. 1:16-19) Mosasamala kanthu za mavuto amene tingakumane nao, timalimbikitsidwa kudziŵa kuti Yehova amatikonda ndipo amafuna kutithandiza. (1 Pet. 5:7) Ndipo iye watilonjeza kuti adzatipatsa mphamvu zimene timafunikila kuti tipitilize kupilila.—1 Akor. 10:13.

17 Ngati tikuvutika cifukwa ca kupanda cilungamo monga mmene zinalili ndi munthu wokhulupilika Yobu, tiyenela kukumbukila kuti Yehova sindiye amene amacititsa zinthu zoipa zimenezo. Yehova amadana ndi zinthu zopanda cilungamo koma amakonda cilungamo. (Sal. 33:5) Ifenso tiyenela kuvomeleza mau a bwenzi la Yobu, Elihu, akuti: “Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.” (Yobu 34:10) M’malo mocititsa mavuto athu, Yehova amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.”—Yak. 1:13, 17.

18, 19. N’cifukwa ciani sitiyenela kukaikila Yehova ngakhale pang’ono? Pelekani citsanzo.

18 Musamukaikile Yehova. Mulungu ndi wangwilo, ndipo maganizo ake ndi apamwamba kuposa maganizo athu. (Yes. 55:8, 9) Conco, kudzicepetsa ndi kudziŵa kuti sitingakwanitse kucita zinthu zonse kuyenela kutipangitsa kuvomeleza kuti nzelu zathu n’zocepa. (Aroma 9:20) Nthawi zambili sitidziŵa mfundo zonse zokhudza zocitika zinazake. Mosakaikila, inu mwadzionela nokha kuti mwambi wa pa Miyambo 18:17 ndi woona. Lembali limati: “Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, koma mnzake amabwela n’kumufufuza-fufuza.”

19 Ngati tili ndi bwenzi lokhulupilika ndipo lacita cinthu cinacake cimene poyamba ndi covuta kucimvetsetsa kapena tikuona kuti n’cosayenela, kodi tingafulumile kumukaikila? Kapena kodi tingamukhulupilile maka-maka ngati takhala tikum’dziŵa kwa zaka zambili? Ngati timakwanitsa kucita zinthu mwacikondi conco ndi anzathu opanda ungwilo, tiyenelanso kukhulupilila kwambili Atate wathu wakumwamba cifukwa cakuti zocita zake ndi maganizo ake ndi zapamwamba kuposa zathu.

20, 21. N’cifukwa ciani tiyenela kudziŵa cimene cimacititsa mavuto amene timakumana nao?

20 Dziŵani cimene cimacititsa mavuto. N’cifukwa ciani tiyenela kutelo? Cifukwa cakuti mwina tikukumana ndi mavuto kaamba ka zolakwa zathu. Ngati zili conco, tiyenela kuvomeleza mfundo imeneyi. (Agal. 6:7) Musayese kuimba mlandu Yehova cifukwa ca mavutowo. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kupanda nzelu? Ganizilani citsanzo ici: Galimoto ingathe kuthamanga kwambili. Ndiyeno yelekezelani kuti galimotoyo yacita ngozi cifukwa cakuti dalaivala anali kuithamangitsa kwambili. Kodi kungakhale kwanzelu kuimba mlandu amene anapanga galimoto imeneyo cifukwa ca ngoziyo? Iyai. Mofanana ndi zimenezi, Yehova anatilenga ndi ufulu wodzisankhila zocita. Koma watipatsanso malangizo amene angatithandize kupanga zosankha zanzelu. Conco, sitiyenela kuimba mlandu Mlengi wathu cifukwa ca zolakwa zathu.

21 Koma sikuti mavuto onse amene timakumana nao ali kaamba ka zolakwa zathu. Zinthu zina zimacitika cifukwa ca “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka” zimene tingakumane nazo. (Mlal. 9:11) Koma koposa zonse, tisaiwale kuti Satana Mdyelekezi ndiye amacititsa mavuto ambili. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:9) Iye ndiye mdani wathu osati Yehova.—1 Pet. 5:8.

ONANI UBWENZI WANU NDI YEHOVA KUKHALA WAMTENGO WAPATALI

22, 23. Kodi n’ciani cimene tiyenela kukumbukila tikalefuka ndi mavuto athu?

22 Mukakumana ndi mavuto, kumbukilani citsanzo ca Yoswa ndi Kalebe. Mosiyana ndi azondi ena 10, amuna okhulupilika amenewa ananena zinthu zolimbikitsa. (Num. 14:6-9) Anasonyeza kuti anali kukhulupilila Yehova. Ngakhale ndi conco, io anayenda-yenda m’cipululu kwa zaka 40 pamodzi ndi Aisiraeli ena onse. Kodi Yoswa ndi Kalebe anadandaula kapena kukhumudwa cifukwa coona kuti sanayenele kulangidwa pamodzi ndi Aisiraeli ena osakhulupilika? Iyai. Iwo anali kukhulupilila Yehova. Kodi anadalitsidwa cifukwa ca cikhulupililo cao? Inde anadalitsidwa. Pamene kuli kwakuti m’badwo wonse wa Aisiraeli amenewo unafa m’cipululu, amuna aŵili amenewo pomalizila pake analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:30) Mofananamo, ifenso tidzalandila madalitso a Yehova “tikapanda kutopa” kucita cifunilo cake.—Agal. 6:9; Aheb. 6:10.

23 Ngati mwalefuka cifukwa ca mavuto, kupanda ungwilo kwa ena, kapena cifukwa ca kupanda ungwilo kwanu, kodi muyenela kutani? Muziganizila kwambili za makhalidwe abwino a Yehova. Muziyesa kuona m’maganizo anu mmene zinthu zidzakhalila ciyembekezo cimene Yehova watipatsa cikadzakwanilitsidwa. Dzifunseni kuti, ‘Kodi moyo wanga ukanakhala wotani ndikanapanda kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?’ Nthawi zonse khalani pa ubwenzi wolimba ndi iye, ndipo musalole kuti mtima wanu ukwiile Mulungu.

[Caption on page 15]

Kumvetsela nkhani zosalimbikitsa kungakufooketseni (Onani ndime 7)

[Caption on page 17]

Yoswa ndi Kalebe anadalitsidwa cifukwa cokhulupilila Yehova (Onani ndime 22)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani