NKHANI YA PACIKUTO: N’cifukwa Ciani Pali Mavuto Ambili?
N’cifukwa Ciani Anthu Akuvutika Kwambili?
Kuti timvetsetse cifukwa cake anthu akukumana ndi mavuto ambili ndiponso cifukwa cake anthu alephela kuwathetsa, tiyenela kudziŵa bwino zimene zimapangitsa mavuto. Ngakhale kuti pali zinthu zambili zosiyana-siyana zimene zimacititsa mavuto, ndife oyamikila cifukwa cakuti Baibo ingatithandize kuzidziŵa. M’nkhani ino, tidzakambilana zifukwa zikulu-zikulu zisanu zimene zimapangitsa mavuto. Tikupemphani kuti muŵelenge mosamala zimene Baibo imanena ndi kuona mmene Mau a Mulungu amatithandizila kudziŵa zifukwa zeni-zeni zimene zimacititsa mavuto.—2 Timoteyo 3:16.
◼ ZOCITA ZA MABOMA OIPA
Baibo imati: “Aliyense woipa akayamba kulamulila, anthu amabuula.”—Miyambo 29:2.
Mbili ya anthu ili ndi nkhani zambili za olamulila oipa amene anali kulamulila mwankhanza ndi kubweletsa mavuto osaneneka kwa anthu ao. N’zoona kuti si olamulila onse amene ndi oipa. Ena angakhale ndi zolinga zabwino zofuna kuthandiza anzao. Komabe, io akakhala pa ulamulilo, nthawi zambili amaona kuti zolinga zao zimalepheleka cifukwa ca mikangano ndi kulimbilana ulamulilo. Kapena angagwilitsile nchito mphamvu zao molakwika pofuna kupeza phindu, ndipo zimenezo zimabweletsa mavuto kwa anthu. Henry Kissinger, amene anali nduna yakale ya za m’dziko ku United States, anati: “Mbili ili ndi nkhani zoculuka zonena za zoyesa-yesa za anthu zimene zinalepheleka ndi zolinga zimene sizinakwanilitsidwe.”
Baibo imafotokozanso kuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Anthu opanda ungwilo sangakwanitse kudzilamulila bwino-bwino cifukwa cakuti alibe nzelu zokwanila. Ngati anthu sangakwanitse kuwongolela mapazi ao, kodi angakwanitse kutsogolela bwino dziko? Kodi mwaona cifukwa cake olamulila aumunthu sangakwanitse kuthetsa mavuto? Ndithudi, nthawi zambili ulamulilo woipa ndi umene umapangitsa mavuto.
◼ ZOCITA ZA CIPEMBEDZO CONAMA
Yesu anati: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:35.
Abusa a zipembedzo zonse amaphunzitsa za cikondi ndi mgwilizano. Koma io alephela kuthandiza otsatila ao kukhala ndi cikondi ceni-ceni cimene cimathetsa tsankho. M’malo mothandiza anthu kukondana, nthawi zambili cipembedzo cimasonkhezela magawano, tsankho ndi mikangano pakati pa mitundu ya anthu. Kumapeto kwa buku lake, katswili wina wamaphunzilo a zacipembedzo, dzina lake Hans Küng, analemba kuti: “Mikangano yandale yoopsa ndi yankhanza kwambili inacitika cifukwa cosonkhezeledwa kapena kuvomelezedwa ndi cipembedzo.”—Christianity and the World Religions.
Kuonjezela pamenepa, atsogoleli ambili a zipembedzo amavomeleza kugonana kwa anthu osakwatilana, kugonana ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wake ndi kugonana kwa akazi ndi amuna okha-okha. Zimenezi zapangitsa mavuto monga kufalikila kwa matenda, mimba zapathengo, kucotsa mimba, kutha kwa zikwati ndi mabanja, ndipo zacititsa mavuto osaneneka.
◼ KUPANDA UNGWILO KWA ANTHU NDI ZOLINGA ZADYELA
“Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’cilako-lako cake. Ndiye cilako-lako cikatenga pakati, cimabala chimo.”—Yakobo 1:14, 15.
Cifukwa ca kupanda ungwilo, tonsefe timalakwa ndipo timafunikila kulimbana ndi cilako-lako cofuna “kucita zofuna za thupi.” (Aefeso 2:3) Zimakhala zovuta kwambili kugonjetsa cilako-lako coipa maka-maka ngati tili ndi mpata wocita zimene tikulaka-lakazo. Ngati tigonjela ku cilako-lako coipa, tingakumane ndi mavuto oopsa kwambili.
Wolemba nkhani wina wochedwa P. D.Mehta anati: “Mavuto ambili amayamba cifukwa ca zilako-lako zathu, kufuna zosangulutsa mopambanitsa, ndiponso kukhala ndi zolinga zadyela.” Zilako-lako ndi zizolowezi zoipa monga ucidakwa, kumwa mankhwala osokoneza ubongo, kuchova njuga, ciwelewele ndi zina zaononga anthu ambili abwino-bwino. Zimenezi zabweletsa mavuto ku mabanja ao, mabwenzi ao ndi anthu ena. Popeza kuti anthu ndi opanda ungwilo, sitingadabwe ndi zimene Baibo imanena kuti: “Tikudziŵa kuti cilengedwe conse cikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.”—Aroma 8:22.
◼ CISONKHEZELO CA MIZIMU YOIPA
Baibo imanena kuti Satana ndi “mulungu wa nthawi ino.” Imanenanso kuti iye ali ndi mizimu yoipa [kapena kuti angelo oipa] yamphamvu yochedwa ziwanda. —2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:9.
Mofanana ndi Satana, ziwanda zili kaliki-liki kulamulila ndi kusoceletsa anthu. Mtumwi Paulo anatsimikizila mfundo imeneyi pamene anati: “Sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma, maulamulilo, olamulila dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.”—Aefeso 6:12.
Ziwanda zimakondwela zikamavutitsa anthu, koma colinga cao cacikulu si cimeneco. Colinga cao cacikulu ndi kupatutsa anthu kwa Yehova, Mulungu wam’mwamba-mwamba. (Salimo 83:18) Kupenda nyenyezi, matsenga, nyanga ndi kulosela zamtsogolo ndi zina mwa zinthu zimene ziwanda zimagwilitsila nchito kusoceletsa ndi kulamulila zocita za anthu. Ndiye cifukwa cake Yehova amaticenjeza za kuopsa kwa zinthu zimenezi ndipo amateteza anthu amene amatsutsa Satana ndi ziwanda.—Yakobo 4:7.
◼ TIKUKHALA ‘M’MASIKU OTSILIZA’
Zaka pafupi-fupi 2000 zapitazo, Baibo inanenelatu kuti: “Dziŵa kuti, masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta.”
Pofotokoza zimene zimapangitsa masiku otsiliza kukhala ovuta, Baibo imati: “Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, . . . osakonda acibale ao, osafuna kugwilizana ndi anzao, onenela anzao zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, aciwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” Conco, cifukwa cacikulu cimene cimacititsa mavuto masiku ano ndi cakuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza.’—2 Timoteyo 3:1-4.
Malinga ndi zimene takambilana, kodi mwaona cifukwa cake anthu alephela kuthetsa mavuto ngakhale kuti ali ndi zolinga zabwino? Nanga ndi kuti kumene tingapeze thandizo? Tiyenela kudalila Mlengi wathu amene walonjeza kuti ‘adzaononge nchito za Mdyelekezi’ ndi otsatila ake. (1 Yohane 3:8) Nkhani yotsatila idzafotokoza zimene Mulungu adzacita kuti athetse zinthu zonse zimene zimacititsa mavuto.