“Tumikilani Yehova Monga Akapolo”
“Musakhale aulesi pa nchito yanu. . . . Tumikilani Yehova monga akapolo.”—AROMA 12:11.
KODI MUGANIZA BWANJI?
Kodi ukapolo wochulidwa pa Aroma 12:11 umatanthauza ciani?
Kodi tingapewe bwanji kukhala akapolo a Satana ndi dziko lake?
Ndi madalitso otani amene Yehova amapeleka kwa akapolo ake?
1. Kodi ukapolo wochulidwa pa Aroma 12:11, umasiyana bwanji ndi zimene anthu ambili amaganiza ponena za ukapolo?
UKAPOLO wa Akristu umasiyana kwambili ndi zimene anthu ambili amaganiza ponena za ukapolo. Iwo akamva kuti kapolo amaganiza za munthu amene akuvutitsidwa ndi kucitilidwa zinthu zopanda cilungamo. Koma Mau a Mulungu ouzilidwa amakamba za ukapolo wotumikila Mbuye wacikondi modzifunila. Pamene mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu ‘kutumikila Yehova monga akapolo,’ iye anali kuwauza kuti azitumikila Mulungu cifukwa comukonda. (Aroma 12:11) Kodi ukapolo wa Akristu umenewu umatanthauza ciani? Kodi tingapewe bwanji kukhala akapolo a Satana ndi dziko lake? Nanga kutumikila Yehova mokhulupilika monga akapolo kumabweletsa madalitso otani?
“NDIMAM’KONDA KWAMBILI MBUYE WANGA”
2. (a) N’cifukwa ciani akapolo ena aciisiraeli anali kusankha kukhalabe akapolo? (b) Kodi kapolo akalola kubooledwa khutu, zinali kuonetsa ciani?
2 Malamulo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli amatithandiza kudziŵa zimene tifunika kucita monga akapolo a Yehova. Kapolo waciheberi anali kumasulidwa m’caka ca 7 ca ukapolo wake. (Eks. 21:2) Koma Yehova anapanga makonzedwe akuti kapolo amene anali kukonda kwambili mbuye wake angapitilize kutumikila monga kapolo ngati afuna. Mbuye wake anayenela kupita naye pacitseko kapena pafelemu ndi kumuboola khutu ndi coboolela. (Eks. 21:5, 6) N’cifukwa ciani iye anali kucita zimenezi? M’cinenelo ca Ciheberi, liu lakuti kumvela ndi logwilizana ndi lakuti kumvetsela. Conco, kapolo amene analola kubooledwa khutu anali kuonetsa kuti afuna kupitiliza kutumikila mbuye wake mokhulupilika. Zimenezi zimaonetsa kuti kudzipeleka kwathu kwa Yehova kumafuna kuti tizimumvela cifukwa comukonda.
3. N’cifukwa ciani tinadzipeleka kwa Mulungu?
3 Pa ubatizo wathu tinali titasankha kale kutumikila Yehova monga akapolo ake. Tinadzipeleka cifukwa cakuti timafuna kumvela Yehova ndi kucita cifunilo cake. Palibe munthu anatikakamiza kucita zimenezi. Ngakhale acicepele amene amabatizika, amadzipeleka kwa Yehova mwa kufuna kwao osati cifukwa cofuna kukondweletsa makolo ao. Ife Akristu timadzipeleka kwa Mbuye wathu wakumwamba, Yehova, cifukwa timam’konda. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.”—1 Yoh. 5:3.
NDIFE AUFULU, KOMA NDIFE AKAPOLO
4. Kodi tifunika kucita ciani kuti tikhale “akapolo a cilungamo”?
4 Timayamikila kwambili Yehova kaamba kotithandiza kuti tikhale akapolo ake. Kukhulupilila nsembe ya dipo la Kristu kumatithandiza kuti tisakhale akapolo a ucimo. Ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, tinasankha ndi mtima wonse kukhala ku mbali ya ulamulilo wa Yehova ndi Yesu. Paulo anafotokoza bwino zimenezi mu imodzi mwa makalata ake. Iye anati: “Dzioneni ngati akufa ku ucimo koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.” Ndiyeno anacenjeza kuti: “Kodi simukudziŵa kuti ngati mudzipelekabe kwa winawake monga akapolo kuti muzimumvela, mumakhala akapolo ake cifukwa cakuti mumamumvela, kaya mukhale akapolo a ucimo umene umatsogolela ku imfa, kapena mukhale akapolo a kumvela kumene kumatsogolela ku cilungamo? Koma tikuyamika Mulungu kuti ngakhale poyamba munali akapolo a ucimo, munamvela mocokela pansi pa mtima mtundu wa ciphunzitso cimene cinapelekedwa kwa inu. Inde, popeza munamasulidwa ku ucimo, munakhala akapolo a cilungamo.” (Aroma 6:11, 16-18) Onani kuti mtumwi Paulo anakamba kuti tiyenela ‘kumvela mocokela pansi pa mtima.’ Conco, tikadzipeleka kwa Yehova timakhala “akapolo a cilungamo.”
5. Kodi tonsefe tifunika kulimbana ndi ciani? Ndipo n’cifukwa ciani?
5 Koma pali zopinga ziŵili zimene tiyenela kulimbana nazo kuti tizicita zinthu mogwilizana ndi kudzipeleka kwathu. Copinga coyamba ndi kupanda ungwilo kwathu. Paulo nayenso analimbana ndi vuto limeneli. Iye analemba kuti: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambili ndi cilamulo ca Mulungu, koma ndimaona cilamulo cina m’ziwalo zanga cikumenyana ndi cilamulo ca m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa cilamulo ca ucimo cimene cili m’ziwalo zanga.” (Aroma 7:22, 23) Monga Paulo, ife tonse ndife opanda ungwilo. Conco, nthawi zonse timalimbana ndi zilako-lako za thupi lathu. Mtumwi Petulo anatilangiza kuti: “Khalani mfulu, koma ufulu wanu usakhale ngati cophimbila zoipa, koma monga akapolo a Mulungu.”—1 Pet. 2:16.
6, 7. Kodi Satana amapangitsa bwanji dzikoli kuoneka ngati labwino?
6 Copinga caciŵili cimene tiyenela kulimbana naco ndi dzikoli limene limasonkhezeledwa ndi ziwanda. Wolamulila wa dzikoli, Satana, amalimbana nafe kuti aticotse kumbali ya Yehova ndi Yesu. Iye amafuna kutipanga kukhala akapolo ake mwa kutikopa kuti tikhale mbali ya dziko lake. (Ŵelengani Aefeso 6:11, 12) Njila imodzi imene Satana amacitila zimenezi ndi mwa kupangitsa dziko lake kuoneka ngati labwino. Mtumwi Yohane anacenjeza kuti: “Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate. Pakuti ciliconse ca m’dziko, monga cilako-lako ca thupi, cilako-lako ca maso ndi kudzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake, sizicokela kwa Atate, koma kudziko.”—1 Yoh. 2:15, 16.
7 Anthu ambili m’dzikoli amafunitsitsa kukhala olemela. Satana amacititsa anthu kuganiza kuti kukhala ndi cuma cambili ndi kumene kumabweletsa cimwemwe. Masitolo akulu-akulu ali paliponse. Anthu otsatsa malonda amalimbikitsa anthu kukhala ndi katundu wambili ndi kukonda zosangulutsa. Makampani okonza zamaulendo amakonza maulendo opeleka anthu ku malo ochuka, ndipo ena mwa anthu amenewa amakhala ndi mzimu wa dziko. Kulikonse m’dzikoli anthu amatilimbikitsa kucita zinthu motengela mzimu wa dziko.
8, 9. Kodi ndi ngozi yaikulu iti imene Mkristu angakumane nayo? Ndipo n’cifukwa ciani imeneyi ndi ngozi yaikulu?
8 Petulo anacenjeza Akristu a m’nthawi ya atumwi ponena za anthu ena mumpingo wacikristu amene anatengela maganizo a dziko. Iye anati: “Iwo amaona kuti kucita masana zinthu zokhutilitsa cilako-lako ca thupi lao n’kosangalatsa. Anthu amenewa ali ngati maŵanga ndi zilema pakati panu, ndipo amakondwela kwadzaoneni akamakuphunzitsani zinthu zonyenga pamene akudya nanu limodzi. Pakuti amalankhula mau odzitukumula opanda pake, ndipo pogwilitsa nchito zilako-lako za thupi komanso makhalidwe otayilila, amakopa amene akungopulumuka kumene kwa anthu ocita zolakwa. Pamene akuwalonjeza ufulu, eni akewo ndi akapolo a khalidwe loipa. Pakuti aliyense amene wagonjetsedwa, amakhala kapolo kwa womugonjetsayo.”—2 Pet. 2:13, 18, 19.
9 Munthu amene amakhutilitsa ‘cilako-lako cake ca maso’ sakhala waufulu. Koma amakhala kapolo wa Satana Mdyelekezi, mbuye wosaoneka wa dzikoli. (1 Yoh. 5:19) Pamakhala ngozi yaikulu ngati munthu wakhala kapolo wa cuma. Zili conco cifukwa cakuti ndi zovuta kuti munthu amasuke ku ukapolo umenewu.
NCHITO YOKHUTILITSA
10, 11. Kodi masiku ano Satana amakonda kusoceletsa anthu otani? Kodi maphunzilo masiku ano angawakhudze bwanji acinyamata?
10 Monga mmene anacitila mu Edeni, Satana masiku ano amakonda kusoceletsa anthu osadziŵa zambili. Iye amafunitsitsa kusoceletsa acinyamata. Satana sakondwela akaona kuti wacinyamata kapena munthu wina wadzipeleka kutumikila Yehova monga kapolo. Mdani wa Mulungu ameneyu amafuna kuti onse amene anadzipeleka kwa Yehova alephele kum’tumikila mokhulupilika.
11 Ganizilaninso citsanzo ca akapolo amene anali kulola kubooledwa khutu ndi mbuye wao. Mwacionekele, akapolo amenewo anali kumva kuwawa kwakanthawi, koma kubooledwa kwao kunasiya cizindikilo cokhalitsa ca utumiki wao monga akapolo. Mofananamo, wacinyamata amene wapanga cosankha cosiyana ndi ca anzake angavutike maganizo kapena kupwetekedwa mtima. Satana amapangitsa anthu kuganiza kuti munthu amakhala ndi umoyo wabwino ngati ali pa nchito yapamwamba. Koma Akristu afunika kuzindikila kuti kukhutilitsa zosoŵa zao za kuuzimu ndi kofunika kwambili. Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zao zauzimu.” (Mat. 5:3) Akristu amadzipeleka kucita cifunilo ca Mulungu, osati ca Satana. Iwo amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amasinkha-sinkha cilamulo cake usana ndi usiku. (Ŵelengani Salimo 1:1-3.) Koma maphunzilo ambili masiku ano sapeleka mpata wokwanila wakuti mtumiki wa Yehova azisinkha-sinkha Mau a Mulungu ndi kukhutilitsa zosoŵa zake za kuuzimu.
12. Kodi acinyamata ambili masiku ano amafunikila kupanga cosankha cotani?
12 Mbuye wa dzikoli angapangitse moyo wa Mkristu kukhala wovuta. M’kalata yake yoyamba yopita kwa Akorinto, Paulo anafunsa kuti: “Kodi unaitanidwa uli kapolo?” Ndiyeno iye anapeleka malangizo akuti: “Usade nazo nkhawa zimenezo, koma ngati ungathenso kumasuka, tengelapo mwai pamenepo.” (1 Akor. 7:21) Ngati kapolo anali kuvutitsidwa ndi mbuye wake anali ndi ufulu womasuka. M’maiko ambili masiku ano muli lamulo loonetsa zaka zimene munthu ayenela kukhala pa sukulu. Pambuyo pake, wophunzila amakhala ndi ufulu wosankha kupitiliza kuphunzila kapena ai. Kuonjezela maphunzilo kuti munthu apeze nchito yapamwamba m’dziko lino kungamulepheletse kucita utumiki wa nthawi zonse.—Ŵelengani 1 Akorinto 7:23.
MAPHUNZILO APAMWAMBA KAPENA ABWINO KWAMBILI
13. Kodi ndi maphunzilo ati amene amapindulitsa kwambili atumiki a Yehova?
13 Paulo anacenjeza Akristu a ku Kolose kuti: “Samalani: mwina wina angakugwileni ngati nyama, mwa nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Kristu.” (Akol. 2:8) Masiku ano aphunzitsi ambili apamwamba amaphunzitsa “nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.” Maphunzilo apamwamba, nthawi zambili sathandiza ophunzilawo kukhala ndi maluso othandiza panchito. Zimenezi zimapangitsa ophunzilawo kulephela kulimbana ndi mavuto amene angakumane nao pa umoyo wao. Koma atumiki a Yehova amasankha maphunzilo amene angawathandize kupeza maluso ofunika kuti azitumikila Mulungu ndi umoyo wosafuna zambili. Iwo amatsatila malangizo amene Paulo anapatsa Timoteyo akuti: “Ndithudi, kukhala wodzipeleka kwa Mulungu kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutila ndi zimene tili nazo, ndi njiladi yopezela phindu lalikulu. Conco, pokhala ndi cakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutila ndi zinthu zimenezi.” (1 Tim. 6:6, 8) M’malo mofuna kukhala ndi madigili ndi maina aulemu, Akristu oona amayesetsa kupeza ‘makalata owacitila umboni’ mwa kutengako mbali mokwanila mu utumiki wa kumunda.—Ŵelengani 2 Akorinto 3:1-3.
14. Malinga ndi Afilipi 3:8, kodi Paulo anaona bwanji mwai wake wokhala kapolo wa Mulungu ndi Kristu?
14 Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anaphunzitsidwa ndi mphunzitsi wa Malamulo a Ayuda wochedwa Gamaliyeli. Maphunzilo amene Paulo anaphunzila tingawayelekezele ndi maphunzilo a ku yunivesite. Kodi Paulo anawaona bwanji maphunzilo amenewa poyelekezela ndi mwai wake wokhala kapolo wa Mulungu ndi Kristu? Iye analemba kuti: “Ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, cifukwa cakuti ndinadziŵa Kristu Yesu Ambuye wanga, cimene ndi cinthu camtengo wapatali kwambili.” Ndipo anapitiliza kuti: “Cifukwa ca iye, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, ndipo ndimaziyesa mulu wa zinyalala, kuti ndikhale pa ubwenzi weni-weni ndi Kristu.” (Afil. 3:8) Citsanzo ca Paulo cimeneci cingathandize Akristu acinyamata ndi makolo ao oopa Mulungu kusankha zinthu mwanzelu pankhani ya maphunzilo. (Onani zithunzi-thunzi.)
PINDULANI NDI MAPHUNZILO ABWINO KWAMBILI
15, 16. Ndi maphunzilo otani amene gulu la Yehova limapeleka? Nanga colinga cake cacikulu n’ciani?
15 Kodi n’ciani cimacitika ku masukulu ambili a maphunzilo apamwamba? Kodi si zoona kuti nthawi zambili ana a sukulu amacita zaciwelewele, zipolowe za ndale, kumwa kwambili ndi kuphunzila za cisanduliko? (Aef. 2:2) Koma gulu la Yehova limapeleka maphunzilo abwino kwambili amene amacitika mwa mtendele m’mipingo yacikristu. Tonse tingapindule ndi Sukulu ya Ulaliki imene imacitika mlungu uliwonse. Ndiponso pali sukulu yapadela ya abale osakwatila amene ndi apainiya (Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Abale Osakwatila) ndi ya Akristu okwatilana amene ndi apainiya (Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Akristu Okwatilana). Maphunzilo aumulungu amenewa amatithandiza kumvela Yehova, Mbuye wathu wakumwamba.
16 Tingaphunzile mfundo zozama za coonadi mwa kugwilitsila nchito buku la Watch Tower Publications Index kapena CD ya Watchtower Library. Colinga cacikulu ca maphunzilo amenewa ndi kulambila Yehova. Timaphunzila mmene tingathandizile ena kugwilizananso ndi Mulungu. (2 Akor. 5:20) Ndipo zimenezi zimathandiza kuti naonso aziphunzitsako ena.—2 Tim. 2:2.
MPHOTO YA KAPOLO
17. Kodi kucita maphunzilo abwino kwambili kumabweletsa madalitso otani?
17 M’fanizo la Yesu lonena za matalente, akapolo aŵili okhulupilika anawayamikila cifukwa ca zimene anacita. Iwo anasangalala pamodzi ndi mbuye wao ndipo anapatsidwa nchito yoonjezeleka. (Ŵelengani Mateyu 25:21, 23.) Ngati tisankha maphunzilo abwino kwambili masiku ano, tidzapeza cimwemwe ndi kulandila mphoto. Ganizilani citsanzo ca Michael. Iye anaphasa bwino mayeso cakuti aphunzitsi ake anamuitana kuti akambitsilane naye zopita ku yunivesite. Koma io anadabwa kuti Michael anasankha kucita kosi ya nthawi yocepa imene inamuthandiza kudzisamalila pocita upainiya. Kodi iye amaona kuti anataya mwai? Iye anati: “Maphunzilo aumulungu amene ndinalandila monga mpainiya ndiponso monga mkulu mumpingo ndi amtengo wapatali kwambili. Madalitso ndiponso mwai zimene ndapeza zimaposa ndalama zimene ndikanapeza. Ndine wosangalala kwambili kuti sindinasankhe kucita maphunzilo apamwamba.”
18. Kodi n’ciani cimakulimbikitsani kusankha maphunzilo abwino kwambili?
18 Maphunzilo abwino kwambili amatithandiza kudziŵa cifunilo ca Mulungu ndi kutumikila Yehova monga akapolo. Amatipatsa ciyembekezo ‘codzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda’ ndi kudzakhala “ndi ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Koposa zonse, timaphunzila mmene tingaonetsele kuti timakonda kwambili Mbuye wathu wakumwamba, Yehova.—Eks. 21:5.
[Caption on page 16, 17]
Kodi mudzatumikila kapolo uti?