NKHANI YA PACIKUTO | ZIMENE MULUNGU WAKUCITILANI
Cocitika Cimene Simuyenela Kuphonya
Usiku wakuti maŵa apeleka moyo wake, Yesu anauza otsatila ake okhulupilika kuti azikumbukila imfa yake. Pogwilitsila nchito mkate wopanda cotupitsa ndi vinyo wofiila, iye anayambitsa cimene cimachedwa kuti Cakudya ca Madzulo kapena kuti Mgonelo wa Ambuye ndipo anawauza kuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.”—Luka 22:19.
Caka ciliconse, Mboni za Yehova padziko lonse zimasonkhana kuti zikumbukile imfa ya Yesu. Cikumbutso ca mu 2014 cidzacitika pa Mande, April 14 dzuŵa litaloŵa.
Tikuitanani kuti mukapezeke pamsonkhano umenewu. Padzakambidwa nkhani imene idzafotokoza cifukwa cake imfa ya Yesu ndi yofunika. Simufunikila kupeleka ndalama kuti mukapezeke pa cocitika cimeneci. Ndiponso sipadzakhala kusonkhetsa ndalama. Munthu amene wakupatsani magazini ino adzakuuzani nthawi ndi malo kumene kudzacitikila Cikumbutso m’dela lanu, kapena mungafufuze pa Webusaiti yathu ya jw.org. Conde lembani penapake zimenezi kuti musakaphonye cocitika cimeneci.