Khalanibe ndi Mzimu Wodzimana
“Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha.”—MAT. 16:24.
1. Kodi Yesu anapeleka citsanzo cabwino citi ca kudzimana?
ALI padziko lapansi, Yesu anapeleka citsanzo cabwino ca kudzimana. Iye anaika cifunilo ca Mulungu patsogolo m’malo mwa zofuna zake ndi kudzitsangalatsa. (Yoh. 5:30) Mwa kukhalabe wokhulupilika mpaka imfa pa mtengo wozunzikilapo, iye anaonetsa kuti analidi ndi mzimu wodzimana.—Afil. 2:8.
2. Kodi tingaonetse bwanji mzimu wodzimana? Nanga kuonetsa mtima umenewu n’kofunika bwanji?
2 Pokhala otsatila a Yesu, ifenso tiyenela kukhala ndi mzimu wodzimana. Kodi kukhala ndi mzimu wodzimana kumatanthauzanji? Kunena mwacidule, kumatanthauza kudzimana zinthu zina kuti tithandize ena. Munjila ina tingati ndi kusadzikonda. (Ŵelengani Mateyu 16:24.) Kupewa mtima wodzikonda kungatithandize kuika zofuna za ena patsogolo m’malo mwa zofuna zathu. (Afil. 2:3, 4) Yesu anakamba kuti kupewa mtima wodzikonda n’kofunika kwambili pa kulambila kwathu. N’cifukwa ciani anatelo? Cifukwa cakuti kupewa mtima umenewu kudzatithandiza kukhala ndi cikondi cacikristu, khalidwe limene ophunzila a Yesu amadziŵika nalo. (Yoh. 13:34, 35) Ganizilani madalitso amene tili nao pokhala m’gulu lapadziko lonse la abale odzimana.
3. Kodi n’ciani cingaononge mzimu wathu wodzimana?
3 Komabe, tili ndi mdani amene mwamacenjela angaononge mzimu wathu wodzimana. Mdani ameneyu ndi mtima wodzikonda. Ganizilani mmene Adamu ndi Hava anakhalila odzikonda. Hava anaonetsa mtima wodzikonda pofuna kukhala ngati Mulungu. Ndipo Adamu anaonetsa mtima wodzikonda pofuna kukondweletsa Hava. (Gen. 3:5, 6) Kucokela pamene Mdyelekezi anapatutsa Adamu ndi Hava pa kulambila koona, iye anapitilizabe kucititsa anthu kukhala ndi mtima wodzikonda. Anacitanso cimodzi-modzi poyesa Yesu. (Mat. 4:1-9) Masiku ano, Satana wakwanitsa kusoceletsa anthu ambili, ndipo wawacititsa kuti adzionetsa mtima wodzikonda m’njila zosiyana-siyana. Ngati sitisamala ifenso tingatengele mtima wodzikonda umene wafala m’dzikoli.—Aef. 2:2.
4. (a) Kodi pali pano tingauthetse mtima wodzikonda? Fotokozani. (b) Kodi tikambilana mafunso ati?
4 Kudzikonda kuli ngati dzimbili. Ngati citsulo canyowa cingacite dzimbili. Kulekelela dzimbili pa citsulo kungacititse kuti cionongeke. Mofananamo, ngakhale kuti pali pano sitingathetse kupanda ungwilo kwathu ndi mtima wodzikonda, tifunika kuzindikila makhalidwe amene angayambitse mtima wodzikonda ndi kuyetsetsa kuwapewa. (1 Akor. 9:26, 27) Kodi tingadziŵe bwanji ngati tili ndi mtima wodzikonda? Nanga tingakulitse bwanji mzimu wodzimana?
GWILITSILANI NCHITO BAIBULO KUTI MUONE NGATI NDINU WODZIKONDA
5. (a) Kodi Baibulo limafanana bwanji ndi galasi? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino) (b) Kodi tiyenela kupewa ciani pamene tigwilitsila nchito Baibulo kuti tione ngati ndife odzikonda?
5 Monga mmene timaseŵenzetsela galasi kuti tione maonekedwe athu, tifunika kugwilitsila nchito Baibulo kuti tione mmene umunthu wathu wamkati ulili ndi kukonza zolakwika zilizonse. (Ŵelengani Yakobo 1:22-25.) Komabe, galasi ingatithandize kuona maonekedwe athu kokha ngati tiiseŵenzetsa bwino. Mwacitsanzo, ngati tiyang’ana pagalasi mofulumila, tingalephele kuona tolakwika twatung’ono koma tofunikila kukonza. Ndiponso ngati tiyang’anitsa galasi kwina, tingaone cithunzi ca munthu wina. Mofananamo, pamene tigwilitsila nchito Baibulo kuti tidziŵe zophophonya zathu monga kudzikonda, sitifunikila kungoliŵelenga mofulumila kapena kuliŵelenga kuti tione zolakwa za ena.
6. Kodi ‘tingalimbikile’ bwanji kutsatila lamulo langwilo?
6 Mwacitsanzo, tingadziŵelenga Mau a Mulungu nthawi zonse, koma osazindikila kuti tayamba kukhala ndi mtima wodzikonda. Kodi zimenezo zingatheke bwanji? Ganizilani izi: M’citsanzo ca munthu amene “amadziyang’ana” pagalasi, Yakobo anagwilitsila nchito liu lacigiliki limene limatanthauza kudzifufuza mosamalitsa. Ngakhale kuti munthuyo anali kudziyang’ana mosamalitsa pagalasi, anali ndi vuto. Yakobo anati: “Akacokapo, nthawi yomweyo amaiŵala kuti ndi munthu wotani.” Conco, iye amacoka pagalasi popanda kukonza zolakwika. Mosiyana ndi zimenezi, munthu wocita mau ‘amayang’anitsitsa m’lamulo langwilo’ ndipo “amalimbikila kutelo.” M’malo mosiya lamulo langwilo la Mau a Mulungu, iye amalimbikila kutsatila ziphunzitso zake. Pofotokoza mfundo imeneyi Yesu anati: “Mukamasunga mau anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga.”—Yoh. 8:31.
7. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji Baibulo kuti tione ngati tili ndi mtima wodzikonda?
7 Conco, kuti tikwanitse kupewa mtima wodzikonda, coyamba tiyenela kuŵelenga Mau a Mulungu mosamalitsa. Zimenezo zidzatithandiza kudziŵa zimene tiyenela kukonza. Koma pali zina zimene tiyenela kucita. Tiyenela kudziŵa zambili mwa kufufuza. Pamene muŵelenga nkhani ina yake m’Baibulo, dziyelekezeleni kuti munaliko. Mungadzifunse mafunso monga akuti: ‘Kodi ndikanakhala ineyo ndikanacita bwanji? Kodi ndikanacita zinthu mwanzelu?’ Cofunika kwambili ndico kusinkha-sinkha ndi kuyesetsa kucita zimene mwaŵelenga. (Mat. 7:24, 25) Tiyeni tikambilane mmene citsanzo ca Mfumu Sauli ndi mtumwi Petulo cingatithandizile kukhalabe ndi mzimu wodzimana.
CITSANZO COIPA CA MFUMU SAULI
8. Ndi makhalidwe ati amene Sauli anali nao atakhala mfumu? Nanga anaonetsa bwanji makhalidwe amenewa?
8 Citsanzo ca Mfumu Sauli cionetsa mmene kudzikonda kungaonongele mzimu wodzimana. Pamene Sauli anayamba kulamulila, anali wofatsa ndi wodzicepetsa. (1 Sam. 9:21) Iye anakana kulanga Aisiraeli amene ananyoza ulamulilo wake, ngakhale kuti kunali koyenela kucita zimenezo kuti ateteze udindo wopatsidwa ndi Mulungu. (1 Sam. 10:27) Mfumu Sauli analola mzimu wa Mulungu kuti umutsogolele ndi kuthandiza Aisiraeli kugonjetsa Aamoni. Kenako, iye modzicepetsa anatamanda Yehova kaamba ka cipambano.—1 Sam. 11:6, 11-13.
9. Kodi Sauli anakhala bwanji ndi mtima wodzikonda?
9 Pambuyo pake, Sauli analola mtima wodzikonda ndi kunyadakuyamba mwa iye monga dzimbili. Atagonjetsa Aamaleki, iye anaika zofuna zake patsogolo m’malo momvela Yehova. Cifukwa ca dyela, Sauli anatenga zinthu zimene Mulungu analamula kuti zionongedwe. Ndipo cifukwa conyada, Sauli anapanga cipilala ca cikumbutso cake. (1 Sam. 15:3, 9, 12) Pamene mneneli Samueli anauza Sauli kuti Yehova sanakondwele ndi zocita zake, Sauli anapeleka zifukwa zodzikhululukila ndi kuchula mbali ya lamulo ya Yehova imene iye anamvela. Ndipo analoza cala ena pa zolakwa zake. (1 Sam. 15:16-21) Ndiponso, kunyada kunacititsa Sauli kuganizila kwambili za kudzipangila dzina m’malo mokondweletsa Mulungu. (1 Sam. 15:30) Kodi nkhani ya Sauli ingatithandize bwanji monga galasi kuti tikhalebe ndi mzimu wodzimana?
10, 11. (a) Kodi citsanzo ca Sauli cionetsa bwanji kuti kukhalabe ndi mzimu wodzimana n’kofunika? (b) Kodi tingapewe bwanji citsanzo coipa ca Sauli?
10 Coyamba, nkhani ya Sauli itiphunzitsa kuti ngati tili ndi mzimu wodzimana sitiyenela kukhutila ndi kuganiza kuti tidzapitilizabe kukhala nao. (1 Tim. 4:10) Kumbukilani kuti kwa kanthawi Sauli anali kucita bwino ndipo Mulungu anamukonda, koma analephela kuthetsa mzimu wodzikonda umene anayamba kukhala nao. Pambuyo pake, Yehova anakana Sauli cifukwa ca kusamvela kwake.
11 Caciŵili, tiyenela kusamala kuti tisamangoyang’ana zimene timacita bwino pa umoyo ndi kunyalanyaza zimene timafunikila kukonza. Kucita zimenezi kuli ngati kugwilitsila nchito galasi kuti tione zovala zathu zatsopano koma kulephela kuona zolakwika pankhope yathu. Ngakhale kuti sitingakhale onyada monga Sauli, tiyenela kuyesetsa kupewa zilizonse zimene zingaticititse kukhala osamvela. Tikapatsidwa uphungu, sitiyenela kupeleka zifukwa zodzikhululukila, kupeputsa colakwa cathu kapena kuloza ena cala. Conco, n’kofunika kulandila uphungu ndi mtima wonse.—Ŵelengani Salimo 141:5.
12. Kodi mzimu wodzimana ungatithandize bwanji tikacita chimo lalikulu?
12 Koma bwanji ngati tacita chimo lalikulu? Sauli anafuna kuteteza dzina lake, ndipo zimenezi zinam’lepheletsa kulandila thandizo la kuuzimu. Mosiyana ndi zimenezi, mzimu wodzimana ungatithandize kulandila thandizo ngakhale kuti zimenezi zingaticititse manyazi. (Miy. 28:13; Yak. 5:14-16) Mwacitsanzo, m’bale wina anayamba kupenyelela zamalisece ali ndi zaka 12, ndipo anacita zimenezi mwakabisila kwa zaka zoposa 10. Iye anati: “Zinandivuta kwambili kuti ndiuze mkazi wanga ndi akulu zimene ndinali kucita. Koma popeza kuti tsopano ndaulula, ndimamva ngati kuti ndatula cikatundu colema. Anzanga ena anakhumudwa pamene ndinasiya kutumikila monga mtumiki wothandiza. Tsopano ndidziŵa kuti Yehova amasangalala kwambili ndi utumiki wanga kuposa pamene ndinali kupenyelela zamalisece. Ndipo cofunika kwambili ndi kukondweletsa Mulungu.”
CITSANZO CABWINO CA PETULO
13, 14. Kodi Petulo anaonetsa bwanji kuti anali ndi mtima wodzikonda?
13 Mtumwi Petulo anaonetsa mzimu wodzimana pophunzitsidwa ndi Yesu. (Luka 5:3-11) Ngakhale n’conco, iye anafunika kugonjetsa mtima wodzikonda. Mwacitsanzo, pamene mtumwi Yakobo ndi Yohane anafuna kuti akakhale pa malo apamwamba pamodzi ndi Yesu mu Ufumu wa Mulungu, Petulo anakwiya kwambili. Mwina Petulo anaganiza kuti iye ndiye adzakhala pa malo apamwamba amenewo popeza Yesu anali atanenapo kuti Petulo adzapatsidwa udindo wapadela. (Mat. 16:18, 19) Yesu anacenjeza Yakobo, Yohane, Petulo ndi atumwi ena kuti sayenela kukhala odzikonda kapena kudziona kuti io ndi ofunika kuposa abale ao.—Maliko 10:35-45.
14 Ngakhale pambuyo pakuti Yesu wamuongolela, Petulo anapitilizabe kulimbana ndi mtima wodzikonda. Pamene Yesu anauza atumwi kuti adzamuthaŵa kwa kanthawi, Petulo anadzikweza pamaso pa ena mwa kunena kuti iye yekha sadzathaŵa. (Mat. 26:31-33) Kudzidalila kwa Petulo kunali kosathandiza cifukwa usiku umenewo, iye analephela kuonetsa mzimu wodzimana. Pofuna kudziteteza, Petulo anakana Yesu katatu.—Mat. 26:69-75.
15. Kodi citsanzo ca Petulo cimatilimbikitsa bwanji?
15 Ngakhale kuti nthawi zina Petulo analephela kugonjetsa mtima wodzikonda, citsanzo cake cimatilimbikitsa. Cifukwa ca khama lake ndi thandizo la mzimu woyela wa Mulungu, Petulo anagonjetsa mtima wodzikonda ndipo anaonetsa kudziletsa ndi cikondi codzimana. (Agal. 5:22, 23) Anapilila mayeselo aakulu kuposa amene analephela kupilila poyamba. Ndipo iye anaonetsa kudzicepetsa pamene mtumwi Paulo anamudzudzula pamaso pa anthu. (Agal. 2:11-14) Pambuyo podzudzulidwa, Petulo sanasunge cakukhosi kapena kuona kuti dzina lake laipa cifukwa ca uphungu wa Paulo. Iye anapitilizabe kukonda Paulo. (2 Pet. 3:15) Citsanzo ca Petulo cingatithandize kukhala ndi mzimu wodzimana.
16. Kodi tingasoyenze bwanji mzimu wodzimana panthawi yovuta?
16 Ganizilani mmene mumacitila panthawi zovuta. Pamene Petulo ndi atumwi ena anaikidwa m’ndende ndi kumenyedwa cifukwa colalikila, io anakondwa “cifukwa cakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucitilidwa cipongwe cifukwa ca dzina la Yesu.” (Mac. 5:41) Inunso mukakumana ndi cizunzo muyenele kutengelapo mwai wotsatila citsanzo ca Petulo, ndi kutsatila mapazi a Yesu mwa kuonetsa mzimu wodzimana. (Ŵelengani 1 Petulo 2:20, 21.) Kukhala ndi mzimu wodzimana kudzakuthandizani kulandila thandizo la akulu. M’malo mosunga cakukhosi, tsatilani citsanzo ca Petulo.—Mlal. 7:9.
17, 18. (a) Kodi tiyenela kudzifunsa funso liti lokhudza zolinga zathu za kuuzimu? (b) Kodi tiyenela kucita ciani ngati tayamba kudzikonda?
17 Mungapindulenso ndi citsanzo ca Petulo pankhani ya zolinga za kuuzimu. Mungacite zimenezi mwa kuonetsa mzimu wodzimana. Koma muyenela kusamala kuti musadziikile zolinga za kuuzimu cabe kuti muchuke. Conco dzifunseni kuti, ‘Kodi colinga canga coonjezela utumiki ndi kufuna kuchuka kapena kukhala ndi udindo, monga mmene zinalili ndi Yakobo ndi Yohane pamene anapempha Yesu kuti akakhale pamalo apamwamba?’
18 Ngati muona kuti mwayamba kudzikonda, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuongolela maganizo ndi mtima wanu. Ndipo yesetsani kulemekeza Mulungu m’malo modzifunila ulemelelo. (Sal. 86:11) Muyenelanso kukhala ndi zolinga zimene sizingakuchukitseni. Mwacitsanzo, mungakhale ndi colinga cokulitsa cipatso ca mzimu cimene muona kuti cimakuvutani kukulitsa. Mwinanso, ngati mumacita khama kukonzekela nkhani zanu za pamsonkhano koma mulibe cidwi coyeletsa Nyumba ya Ufumu, mungadziikile colinga kuti muzigwilitsila nchito malangizo opezeka pa Aroma 12:16.—Ŵelengani.
19. Kodi tingacite ciani kuti tisafooke ndi zimene timaona mu galasi imene ndi Mau a Mulungu?
19 Ngati timadziyang’ana mosamalitsa pagalasi imene ndi Mau a Mulungu ndi kuona zolakwika zina, monga kudzikonda, tingafooke. Zimenezi zikakucitikilani, muzikumbukila citsanzo ca munthu wa m’fanizo la Yakobo. Yakobo sanagogomeze kuti munthuyo anakonza zolakwika zake mwamsanga kapena kuti anakonza zolakwika zonse. M’malo mwake, Yakobo anakamba kuti munthuyo ‘analimbikila kutelo m’lamulo langwilo.’ (Yak 1:25) Iye anakumbukila mmene anaonekela pagalasi ndipo anapitiliza kudzikonza. Conco, tidzidziona moyenela ndi kukumbukila kuti ndife opanda ungwilo. (Ŵelengani Mlaliki 7:20.) Pitilizani kuyang’ana m’lamulo langwilo ndipo yesetsani kukhala ndi mzimu wodzimana. Yehova ndi wofunitsitsa kukuthandizani monga mmene wathandizilanso abale anu ambili kupeza ciyanjo ndi madalitso a Mulungu, ngakhale kuti ndi opanda ungwilo.