MFUNDO YOTHANDIZA PA KUWELENGA KWANU
Ligwilitsileni Nchito Bwino Galasi
Wophunzila Yakobo anayelekezela Baibulo ndi galasi limene limatithandiza kuona munthu wathu wamkati. (Yak. 1:22-25) Ndi motani mmene tingaligwilitsile nchito Baibulo moyenela ngati galasi?
Muziliwelenga mosamala. Tikangodziyang’ana mwacidule pagalasi, sitingaone zofunika kukonza pathupi lathu. Mofananamo, kuti tione mbali za munthu wathu wam’kati zimene tiyenela kukonza, tiyenela kuwelenga Baibulo mosamala.
Muziika kwambili maganizo pa inu osati pa ena. Nthawi zina tikamadziyang’ana pagalasi, tingaone anthu ali kumbuyo kwathu n’kuika maganizo athu pa zolakwika ndi kaonekedwe kawo. Mofananamo, ngati sitinaligwilitse nchito bwino Baibulo, tingamaliwelenge n’colinga cofuna kuonamo zophophonya za ena. Koma kutelo sikungatithandize kuwongolela zophophonya zathu.
Khalani ololela. Tingaleke kusangalala tikamaika kwambili maganizo athu pa zimene sizioneka bwino tikadziyang’ana pagalasi. Tikamawelenga Baibulo, tiyenela kukhala ololela mwa kusaganiza kuti tiyenela kucita zambili kuposa zimene Yehova amafuna kuti ticite.—Yak. 3:17.