Kodi Yehova Amandiona Bwanji?
1. Kodi Baibulo likufanana bwanji ndi galasi?
1 Kodi mumadziyang’ana kangati pa galasi? Ambili a ife timadziyang’ana tsiku ndi tsiku. Timacita zimenezi kuti tione mmene tikuonekela. Baibulo lili ngati galasi. Kuŵelenga Mau a Mulungu kumatithandiza kuona umunthu wathu wamkati umene Yehova amaona. (1 Sam. 16:7; Yak. 1:22-24) Mau a Mulungu amatha “kuzindikila zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” (Aheb. 4:12) Kodi kuŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kusinkhasinkha kungatithandize bwanji kuona mbali zimene tifunika kukonza kuti tikhale alaliki ogwila mtima?—Sal. 1:1-3.
2. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kudzifufuza?
2 Gwilitsilani Nchito Baibulo Monga Galasi: Nkhani za m’Baibulo za atumiki a Yehova okhulupilika zimatiphunzitsa makhalidwe abwino amene Mulungu amakonda. Mwacitsanzo, Davide anaonetsa cangu pa kukweza dzina la Mulungu. (1 Sam. 17:45, 46) Yesaya molimba mtima anadzipeleka kukalalikila ku gawo lovuta. (Yes. 6:8, 9) Yesu anaona utumiki kukhala wotsitsimula ndi wokhutilitsa. Sanauone ngati cimtolo iyai. Izi zili conco cifukwa cakuti anakonda Atate wake ndi mtima wake wonse. (Yoh. 4:34) Akristu a m’zaka za zana loyamba analalikila mwacangu, anadalila Yehova ndipo sanaganize zosiya utumiki. (Mac. 5:41, 42; 2 Akor. 4:1; 2 Tim. 4:17) Ngati tisinkhasinkha zitsanzo zimenezi, zidzatithandiza kudzifufuza bwinobwino kuti utumiki wathu wopatulika ukhale wovomelezeka.
3. N’cifukwa ciani sitiyenela kuzengeleza kukonza tikaona mbali imene sili bwino?
3 Konzani Zimene Sizili Bwino: N’zosathandiza kudziyang’ana pa galasi koma osakonza zoipa zimene taona. Cofunika ndi kupempha Yehova kuti atithandize kuona mmene mtima wathu ulili ndi kukonza pamene sitikucita bwino. (Sal. 139:23, 24; Luka 11:13) Tiyeni tisazengeleze kukonza tikaona kuti mbali ina sili bwino cifukwa nthawi imene yatsala ndi yocepa ndiponso miyoyo ili pangozi.—1 Akor. 7:29; 1 Tim. 4:16.
4. Ndi ciani cimene cimacitika ngati munthu amayang’anitsitsa m’Mau a Mulungu ndi kucita zimene wapeza?
4 Umunthu wamkati umene Yehova amaona ndiye wofunika kwambili kuposa maonekedwe akunja. (1 Pet. 3:3, 4) Koma kodi ndi ciani cimene cimaticika ngati munthu amayang’anitsitsa m’Mau a Mulungu ndi kucita zimene wapeza? Iye ‘amakhala wosangalala cifukwa cakuti sali wongomva n’kuiŵala koma wocita’ zimene wamva. (Yak. 1:25) Ndithudi, timakhala okondwela ndipo timakhala alaliki ogwila mtima cifukwa cakuti ‘timaonetsa ulemelelo wa Yehova monga magalasi oonela.’—2 Akor. 3:18.