LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 3/1 masa. 30-31
  • Mgwilizano wa Zipembedzo—Kodi Mulungu Amauvomeleza?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mgwilizano wa Zipembedzo—Kodi Mulungu Amauvomeleza?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • KODI COLINGA CA MGWILIZANOWU N’CIANI?
  • KODI KUNGOLIMBIKITSA MAKHALIDWE ABWINO N’KOKWANILA?
  • ZIMENE BAIBULO LIMANENA PANKHANI YA MGWILIZANO WA ZIPEMBEDZO
  • KULIMBIKITSA MGWILIZANO WENI-WENI
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 3/1 masa. 30-31

Mgwilizano wa Zipembedzo—Kodi Mulungu Amauvomeleza?

“Kodi cipembedzo cimatigwilizanitsa kapena cimatigaŵanitsa?” Funso limeneli linafunsidwa kwa oŵelenga nyuzipepala ya ku Australia yochedwa The Sydney Morning Herald. 89 pelesenti ya anthu amene anapeleka mayankho anakamba kuti cipembedzo cimatigaŵanitsa.

KOMA anthu ocilikiza mgwilizano wa zipembedzo amaona nkhaniyi mosiyanako. Eboo Patel amene anayambitsa bungwe lochedwa Interfaith Youth Core anati: “Palibe cipembedzo cimene sicimaonetsa cikondi . . . , cimene sicimasamalila zacilengedwe . . . , cimene sicimathandiza anthu.”

Abuda, Akatolika, Apulotesitanti, Ahindu, Asilamu ndi zipembedzo zina zimayesa kugwilila nchito pamodzi kuti zithetse umphaŵi, zibweletse ufulu wa anthu, ziletse kufocela mabomba kapena kusamalila zacilengedwe. Zipembedzo zambili zimakumana pamodzi kuti zigwilizane pa mfundo imodzi ndi kulimbikitsana. Zimacita miyambo ya zikondwelelo yogwilitsila nchito makandulo, kuimba nyimbo, kupemphela, ndi kucita zinthu zina.

Kodi kugwilizana kwa zipembedzo kungathetse mavuto pakati pao? Kodi Mulungu amagwilitsila nchito mgwilizano wa zipembedzo kuti athetse mavuto padziko lapansi?

KODI COLINGA CA MGWILIZANOWU N’CIANI?

Bungwe lina lalikulu la mgwilizano wa zipembedzo limadzitama kuti lili ndi mamembala a zipembedzo zoposa 200 zocokela m’maiko 76. Colinga ca bungweli ndi “kukhazikitsa mgwilizano wa zipembedzo wokhalitsa.” Koma zimenezi ndi nkhambakamwa cabe. Mwacitsanzo, anthu oyambitsa mgwilizanowu ananena kuti analemba cipepala cao ca mgwilizano mosamalitsa kuti asakhumudwitse zipembedzo zina zimene zili mumgwilizano umenewu. Kodi anacitilanji zimenezi? N’cifukwa cakuti panali kusagwilizana pankhani yokhudza Mulungu mumgwilizano wao. Conco, anapewelatu kuchula Mulungu kapena ciliconse cokhudza Mulungu.

Ngati Mulungu sachulidwa mumgwilizano wao, kodi ungakhale wothandiza? Kodi zipembedzo zimene sizifuna kuchula dzina la Mulungu zingasiyane bwanji ndi mabungwe ena onse othandiza anthu? Ndiye cifukwa cake bungwe la mgwilizano wa zipembedzo limadzicha kuti ndi “bungwe lolimbikitsa mgwilizano,” osati gulu lacipembedzo.

KODI KUNGOLIMBIKITSA MAKHALIDWE ABWINO N’KOKWANILA?

Mwamuna wina wochuka pakucilikiza mgwilizano wa zipembedzo wochedwa Dalai Lama anati: “Miyambo yonse ya zipembedzo imacilikiza cikondi, cifundo ndi kukhululukilana. N’kofunika kuonetsa makhalidwe onse amenewa paumoyo wathu.”

Kunena zoona, cikondi, cifundo ndi kukhululukila ndi makhalidwe ofunika kwambili. Pofotokoza lamulo la makhalidwe abwino, Yesu anati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.” (Mateyu 7:12) Koma kodi cipembedzo coona cimangolimbikitsa makhalidwe abwino?

Ponena za anthu amene anali kunena kuti anali kutumikila Mulungu, mtumwi Paulo anati: “Ndikuwacitila umboni kuti ndi odzipeleka potumikila Mulungu, koma samudziŵa molondola.” N’cifukwa ciani anatelo? Paulo anati: “Posadziŵa cilungamo ca Mulungu, io sanagonjele cilungamoco koma anayesetsa kukhazikitsa cao-cao.” (Aroma 10:2, 3) Popeza analibe cidziŵitso ceni-ceni ca zimene Mulungu anali kufuna kuti io acite, cangu ndi cikhulupililo cao zinalibe phindu.—Mateyu 7:21-23.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA PANKHANI YA MGWILIZANO WA ZIPEMBEDZO

Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amabweletsa mtendele.” (Mateyu 5:9) Yesu anacita zimene anali kuphunzitsa mwa kupewa ciwawa ndi kulalikila uthenga wa mtendele kwa anthu a zipembedzo zosiyana-siyana. (Mateyu 26:52) Anthu amene analabadila uthengawo anakhala ndi cikondi colimba. (Akolose 3:14) Koma kodi Yesu anali kungofuna kugwilizanitsa anthu a zikhalidwe zosiyana-siyana kuti azikhala mwamtendele? Kodi iye anagwilizana nao pa kulambila kwao?

Mwankhanza Atsogoleli acipembedzo a Afalisi ndi a Asaduki anatsutsa Yesu, ngakhale kufuna kumupha. Kodi Yesu anacita ciani? Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleli akhungu.” (Mateyu 15:14) Yesu sanagwilizane ndi atsogoleli acipembedzo amenewa ngakhale pang’ono.

Patapita nthawi, mpingo wacikristu unakhazikitsidwa mumzinda wa Korinto, ku Girisi. Mumzinda umenewo munali zocitika za zipembedzo zosiyana-siyana. Kodi Akristu a kumeneko anafunikila kucita ciani? Mtumwi Paulo anawalembela kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupilila, cifukwa ndinu osiyana.” N’cifukwa ciani? Paulo anati: “Pali mgwilizano wotani pakati pa Kristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupilila angagaŵane ciani ndi wosakhulupilila?” Ndiyeno anapeleka malangizo awa: “Conco tulukani pakati pao, lekanani nao.”—2 Akorinto 6:14, 15, 17.

Ndithudi, Baibulo limatsutsa mgwilizano wa zipembedzo. Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi mgwilizano weni-weni ungakhalepo bwanji?’

KULIMBIKITSA MGWILIZANO WENI-WENI

Makina opimila zinthu za mlenga-lenga ochedwa Space Station anapangidwa ndi anthu ocokela m’maiko 15. Kodi muganiza kuti anthu amene anapanga makinawo akanakwanitsa kuwapanga ngati sanagwilizane pa pulani limodzi?

N’cimodzi-modzi ndi mgwilizano wa zipembedzo masiku ano. Ngakhale kuti amanena kuti bungwe lao limabweletsa mgwilizano ndi kulemekezana, io kweni-kweni samagwilizana pa mfundo imodzi kuti alimbitse cikhulupililo cao. Cifukwa ca zimenezi io amasiyanabe maganizo pankhani ya makhalidwe ndi ziphunzitso.

Baibulo lili ndi miyezo ya Mulungu imene ili monga pulani, ndipo tingatsatile miyezo imeneyi paumoyo wathu. Anthu amene amatsatila mfundo za m’Baibulo agonjetsa kusankhana mitundu ndipo amalambilila capamodzi. Iwo aphunzila kuseŵenzela pamodzi mogwilizana ndi mwamtendele. Mulungu ananenelatu zimenezi pamene anati: “Ndidzapatsa mitundu ya anthu cilankhulo coyela kuti onse aziitanila pa dzina la Yehova ndi kum’tumikila mogwilizana.” Mgwilizano umenewo wakhalapo cifukwa ca “cilankhulo coyela,” cimene ndi miyezo ya Mulungu yolambilila.—Zefaniya 3:9; Yesaya 2:2-4.

Mwacikondi, Mboni za Yehova zikuitanani kuti mukabwele ku Nyumba ya Ufumu imene ili kufupi ndi kwanu kuti mukaone nokha mtendele ndi mgwilizano weni-weni umene uli pakati pao.—Salimo 133:1.

Kodi Coonadi Cilikodi?

Anthu ocilikiza mgwilizano wa zipembedzo amakamba kuti palibe cipembedzo cimene cingakhale ndi coonadi pacokha. Iwo amanena kuti kusagwilizana kwa zipembedzo ndiye kwabweletsa mavuto amene alipo masiku ano.

Mosiyana ndi maganizo amenewo, Yehova amanenedwa kuti ndi “Mulungu wacoonadi,” ndipo anakamba kuti “sindinasinthe.” (Salimo 31:5; Malaki 3:6) Ponena za Mulungu Yesu anati: “Mau anu ndiwo coonadi.” (Yohane 17:17) Coonadi cimeneci cimapezeka m’Malemba ouzilidwa ndi Mulungu, Baibulo. Limatilangiza ndi kutithandiza kuti tikhale oyenelela “kucita nchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteyo 3:16, 17.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani