NKHANI YA PACIKUTO | N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUPEMPHELA?
N’cifukwa Ciani Anthu Amapemphela?
Kodi inu mumapemphela nthawi zonse? Anthu ambili amatelo, ngakhale amene sakhulupilila Mulungu. Nanga n’cifukwa ciani anthu amapemphela? Malinga ndi kauniuni wa ku France, hafu ya anthu kumeneko anakamba kuti amapemphela kapena kusinkhasinkha kuti “amveko bwino.” Mofanana ndi anthu a ku Europe, anthu a ku France samapemphela kuti alambile Mulungu. M’malo mwake, “amapemphela kuti atonthozedwe basi.” Kumbali ina, anthu ena amapemphela kwa Mulungu kokha akakumana ndi mavuto, ndipo amayembekezela kuti pempho lao liyankhidwe pamenepo.—Yesaya 26:16.
Nanga bwanji inuyo? Kodi mumaona pemphelo kukhala cabe njila yokuthandizani kukhala ndi maganizo oyenela? Ngati mumakhulupilila Mulungu, kodi mumaona kuti pemphelo limakuthandizani paumoyo wanu? Kapena mumaona kuti mapemphelo anu samayankhidwa? Baibulo lingakuthandizeni kupemphela kuti mukhale paubwenzi wabwino ndi Mulungu, osati kupemphela pofuna kutonthozedwa cabe.