LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 7/1 masa. 8-9
  • Baibulo Limasintha Anthu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Baibulo Limasintha Anthu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Mbili ya Ricardo na Andres
    Galamuka!—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 7/1 masa. 8-9

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Kulikonse kumene ndinali kupita ndinali kukhala ndi mfuti yanga

Yosimbidwa ndi Annunziato lugarà

  • CAKA COBADWA: 1958

  • DZIKO: ITALY

  • MBILI YANGA: NDINALI M’GULU LA ZIGAŴENGA

KUKULA KWANGA:

Ndinabadwa ndi kukulila m’komboni yaing’ono ku Rome imenenso munali ogwila nchito ovutika kwambili. Umoyo unali wovuta. Amai anga enieni sindinali kuwadziŵa ndiponso sindinali pa ubwenzi wabwino ndi atate anga. Ndinaphunzila mmene ndingakhalile m’komboni imeneyo popeza umoyo unali wovuta.

Nditakhala ndi zaka 10, ndinali nditayamba kale kuba. Pamene ndinakhala ndi zaka 12, ndinathaŵa pa nyumba kwa nthawi yoyamba. Nthawi zingapo, atate anadzanditenga ku likulu la apolisi n’kupita nane ku nyumba. Ndinali kukangana kwambili ndi anthu. Ndinali waukali ndi wankhanza kwa aliyense. Nditakwanitsa zaka 14, ndinacokelatu pa nyumba. Ndiyeno ndinayamba kukhala m’miseu n’kuyamba kumwa mankhwala osokoneza ubongo. Kuti ndipeze malo ogona ndinali kuphwanya galimoto za anthu ndi kugonamo mpaka m’bandakuca. Ndikauka ndimafunafuna kumene kuli madzi akuti ndisambe.

Ndinakhala katswili pankhani yakuba. Ndinali kuba macola, m’nyumba zamdadada ndi kuthyola nyumba zikuluzikulu usiku. Ndinayamba kudziŵika ndi mbili yoipa kwambili ndipo posapita nthawi ndinaitanidwa kuti ndikhale m’gulu la zigaŵenga. Zimenezi zinandipatsa mwai wakuti ndikhale wakuba m’mabanki. Ndinakhala wolemekezeka kwambili m’gulu la zigaŵengalo cifukwa ca ukali umene ndinali nao. Kulikonse kumene ndinali kupita ndinali kunyamula mfuti. Pogona ndinali kucita kuiika ku pilo. Ndimangokhalila kucitila anthu nkhanza, kumwa mankhwala osokoneza ubongo, kuba, kutukwana ndi kucita zinthu zoipa. Apolisi amangokhalila kundifunafuna. Ndinamangidwa kambilimbili, ndipo kwa zaka zambili ndimangoloŵa ndi kutuluka m’ndende.

MMENE BAIBULO LINASINTHILA UMOYO WANGA:

Nthawi ina nditatuluka m’ndende, ndinaganiza zakuti ndikaone ang’ono a amai anga. Sindinali kudziŵa kuti io limodzi ndi ana ao aŵili anakhala a Mboni za Yehova. Anandiitanila ku msonkhano wa Mboni. Pocita cidwi, ndinaganiza zopita nao. Titafika pa Nyumba ya Ufumu, ndinakana kukakhala kutsogolo m’malo mwake ndinakhala pafupi ndi khomo n’colinga cakuti ndiziona anthu otuluka ndi oloŵa. Apo n’kuti n’nali n’tainyamula mfuti yanga.

Msonkhano umenewo unasintha umoyo wanga. Ndikumbukila kuti pa nthawi imeneyo ndinamva ngati kuti ndili ku dziko lina. Ndinapatsidwa moni wotentha, wacikondi ndipo ndinaona nkhope zomwetulila. Ndikumbukila bwinobwino mmene Mboni zinali kuonekela zokoma mtima ndi zacilungamo pa nkhope zao. Zimenezi zinali zosiyana kwambili ndi umoyo umene ndinazolowela.

Ndinayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni. Zilizonse zimene ndinali kuphunzila zinali kundithandiza kuona bwinobwino kuti ndifunika kusinthilatu umoyo wanga. Ndinatsatila malangizo opezeka pa Miyambo 13:20 akuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Ndinaona kuti ndifunika kucoka m’gulu la zigaŵenga. Ngakhale kuti kucita zimenezi sikunali kopepuka, Yehova anandithandiza kuti ndikwanitse kucokamo.

Kwa nthawi yoyamba pa umoyo wanga, ndinayamba kudziletsa pa zocita zanga

Ndinadziyeletsanso mwakuthupi. Ndinayesetsa kuleka kukoka fodya ndi kumwa mankhwala osokoneza ubongo. Ndinagela tsitsi langa lalitali, kutaya masikiyo anga, ndi kusiya kutukwana. Kwa nthawi yoyamba pa umoyo wanga, ndinayamba kudziletsa pa zocita zanga.

Ndinali munthu wosakonda kuŵelenga ndi kuphunzila, conco ndinali kuvutika kwambili kuti ndiike maganizo pa zimene ndinali kuphunzila m’Baibulo. Koma ngakhale zinali conco, ndinayesayesa mpaka ndinayamba kukonda Yehova. Ndinaonanso kuti cinacake casintha mwa ine—cikumbumtima canga cinayamba kundivutitsa. Nthawi zonse ndimakhalila kudziimba mlandu ndipo ndinali kukaikila ngati Yehova angandikhululukile pa zoipa zonse zimene ndinacita. Pa nthawi imeneyo, ndinali kutonthozedwa kwambili pamene ndinali kuŵelenga za Yehova akukhululukila Mfumu Davide atacita macimo akuluakulu.—2 Samueli 11:1–12:13.

Vuto lina linali kuuzako ena za cikhulupililo canga pocita ulaliki wa ku nyumba ndi nyumba. (Mateyu 28:19, 20) Ndinali kuopa kuti mwina ndingakumane ndi munthu amene ndinamucitila zinthu zoipa kapena kumulakwila nthawi yakale. Koma pang’onopang’ono ndinakwanitsa kuthetsa mantha. Conco ndinayamba kukondwela kwambili kuuza ena za Atate wathu wakumwamba, amene ndi wacikondi ndipo amakhululukila ndi mtima wonse.

MAPINDU AMENE NDAPEZA:

Ndinapulumuka cifukwa cophunzila za Yehova. Anzanga ambili akale anafa ndipo ena ali m’ndende, koma ine ndili ndi moyo wokhutilitsa ndi tsogolo labwino kwambili limene ndi kuliyembekezela. Ndaphunzila kukhala munthu wodzicepetsa, womvela ndi wodziletsa makamaka pa khalidwe langa lokhwiya msanga. Zotsatilapo zake ndi zakuti, ndili pa ubwenzi wabwino ndi anthu ambili. Ndinakwatilanso Carmen mkazi wanga wokongola, ndipo tikukondwela m’cikwati cathu. Ine ndi mkazi wanga, timakondwela kuthandiza ena kuphunzila Baibulo.

Tsopano ndikugwila nchito moona mtima. Nthawi zina ndimakagwilila nchito ku mabanki, koma m’malo mwa kuba m’mabanki amenewa ndine amene ndimawayeletsa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani