KODI MUDZIŴA?
Kodi oyenda panyanja akalekale anali kupanga bwanji ngalawa zao kuti madzi asaziloŵa?
Katswili wa ngalawa zakale, Lionel Casson, anafotokoza zimene omanga ngalawa m’nthawi ya Roma anali kucita akaika zomatila m’malo amene matabwa a ngalawa awalumikiza. Nthawi zambili anali “kupaka phula malo olumikizana ndipo ngakhale kunja konse kwa ngalawa, ndi mkati momwe anali kupakamo phula.” Aroma asanayambe kugwilitsila nchito phula popanga ngalawa zao kuti madzi asaziloŵa, Aakediya ndi Ababulo akalekale anali atayamba kale kucita zimenezi.
Malemba Aciheberi amachula njila yofanana pa Genesis 6:14. Mau aciheberi amene agwilitsidwa nchito pa vesi limeneli amatanthauza “phula” zinthu zamadzimadzi zopezeka m’cilengedwe.
Phula lopezeka m’cilengedwe lili mitundu iŵili, lamadzimadzi ndi louma. Opanga ngalawa akale anali kugwilitsila nchito mtundu wamadzimadzi. Anali kupaka ngalawa zao ndi phula limeneli. Phula lamadzimadzi linali kuuma ndi kulimba cakuti linali kupanga muyalo umene unali kuteteza kuti madzi asaziloŵa m’ngalawa.
Phula linali loculuka m’madela oculidwa m’Baibulo. Cigwa ca Sidimu, cimene cinali m’dela la Dead Sea “cinali ndi maenje ambili okhala ndi phula.”—Genesis 14:10.
Kodi anthu akale anali kugwilitsila nchito njila zotani posunga nsomba?
Kuyambila kale nsomba yakhala cakudya cofunika kwambili. Asanayambe kuyenda ndi Yesu, atumwi ena anali asodzi a nsomba m’nyanja ya Galileya. (Mateyu 4:18-22) Nsomba zina zimene anthuwo anali kugwila m’nyanja imeneyo anali kuzikonzela ku mafakitale amene anali pafupi.
Buku lina linafotokoza luso linalake limene anthu a mu mzinda wa Galileya anali kugwilitsila nchito kuti asunge bwino nsomba. Ngakhale masiku ano, anthu akugwilitsilabe nchito luso limeneli m’malo ena. Coyamba io anali kutenga nsombazo n’kuzitumbula kenako n’kuzitsuka ndi madzi. Bukulo linanena kuti “anali kuzithila mcele wamiyala kuyambila mopumila mwake, kukamwa ndi m’mamba ake. Nsombazo zikathilidwa mcele, amayalapo mphasa pamwamba pake. Ndiyeno anali kuziyanika pa dzuŵa. Pambuyo pakuti zakhala pa dzuŵa masiku atatu kapena asanu io anali kuzitembenuza n’kuzisiyanso padzuŵa masiku ofananao. Panthawi youmika imeneyi madzi anali kucoka m’nsombazo ndipo mcele unali kuloŵa. Akaziumika conco nsombazo zimakhala zolimba bwino ndithu ndiponso zosakhoza kuonongeka.”—Studies in Ancient Technology.
Sizidziŵika ngati nsombazo zinali kukhala utali wotani akazikonza mwanjila imeneyi. Koma popeza kuti Aiguputo akale anali kutumiza nsomba zouma ku Siriya zikuonetsa kuti njila zimene anali kugwilitsila nchito zinali zabwino.