LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 9/1 tsa. 15
  • Ndani Anapanga Mulungu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ndani Anapanga Mulungu?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Nkhani Zofanana
  • N’zotheka Kudzakhala na Moyo Kwamuyaya
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Mulungu N’ndani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Dzina la Mulungu N’ndani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 9/1 tsa. 15

Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi

Ndani Anapanga Mulungu?

Ganizilani tate amene akukambilana ndi mwana wake wazaka 7. Iye akumuuza kuti: “Kale kwambili, Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zonse zimene zilimo. Anapanganso dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi.” Mwanayo aganizila zimene atate ake amuuza kenako afunsa kuti: “Atate, kodi ndani anapanga Mulungu?”

Atateyo akumuyankha kuti: “Palibe amene anapanga Mulungu. Iye wakhala aliko kuyambila kalekale.” Panthawiyi, mwanayo anakhutila ndi yankho losavuta limeneli. Koma pamene mwanayo akula, apitilizabe kuganizila funsolo. Zim’vuta kumvetsa mmene munthu angakhalile alibe ciyambi. Iye aganizila kuti ngakhale cilengedwe cili ndi ciyambi, ‘nanga Mulungu anacokela kuti?’

Kodi Baibulo limayankha bwanji? Mogwilizana ndi yankho limene atate wa m’citsanzo cathu anapeleka, Mose anati: “Inu Yehova, . . . mapili asanabadwe, kapena musanakhazikitse dziko lapansi ndi malo okhalapo anthu, Inu ndinu Mulungu kuyambila kalekale mpaka kalekale.” (Salimo 90:1, 2) Ngakhalenso mneneli Yesaya anati: “Kodi iwe sukudziŵa kapena kodi sunamve? Yehova, Mlengi wa malekezelo a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.” (Yesaya 40:28) Mofananamo, kalata ya Yuda imanena kuti Mulungu wakhalako “kucokela kalekale.”—Yuda 25.

Malembawo aonetsa kuti Mulungu ndi “Mfumu yamuyaya,” monga mmene mtumwi Paulo anafotokozela. (1 Timoteyo 1:17) Izi zitanthauza kuti Mulungu wakhalapo kuyambila kalekale kuposa pamene maganizo athu angafike tikamaganizila za m’mbuyo. Ndipo adzakhalapobe nthawi zonse mpaka muyaya. (Chivumbulutso 1:8) Conco, popeza Mulungu ndi wamuyaya sizitidabwitsa kuti iye ndi Wamphamvuyonse.

N’cifukwa n’ciani mfundo imeneyi ndi yovuta kumvetsa? Cifukwa cakuti nthawi yocepa kwambili imene timakhala ndi moyo imasiyana ndi mmene Yehova amaonela nthaŵi. Popeza Mulungu ndi wamuyaya, kwa iye zaka 1000 zili ngati tsiku limodzi. (2 Petulo 3:8) Mwacitsanzo: Kodi ciwala cimene cimakhala cabe masiku 50, cingamvetse mfundo yakuti anthufe timakhala zaka 70 kapena 80? Kutalitali! Ndiye cifukwa cake, Baibulo limanena kuti anthufe tili ngati ciwala akatiyelekezela ndi Mlengi Wamkulu. Ngakhale kaganizidwe kathu n’kocepa kwambili poyelekeza ndi ka Mulungu. (Yesaya 40:22; 55:8, 9) Conco n’zosadabwitsa kuti pali mfundo zina zokhudza Mulungu zimene anthufe sitingathe kuzimvetsa.

Ngakhale kuti mfundo yakuti Mulungu ndi wamuyaya ndi yovuta kuimvetsa, tikhoza kuona kuti ndi yomveka. Ngati winawake analenga Mulungu, ndiye kuti munthu ameneyo akanakhala Mlengi. Komabe, Baibulo limanena kuti, Yehova ndiye ‘analenga zinthu zonse.’ (Chivumbulutso 4:11) Kuonjezela pamenepo, tidziŵa kuti panthawi inayake cilengedwe kunalibe. (Genesis 1:1, 2) Kodi cinacokela kuti? Kuti cilengedwe cikhaleko Mlengi wake anafunika kukhalako coyamba. Iye analiko pasanakhale anthu, angelo ndi Mwana wake wobadwa yekha. (Yobu 38:4, 7; Akolose 1:15) N’zoonekelatu kuti poyamba analiko yekhayekha. Iye sanacite kulengedwa ndipo panalibe cina ciliconse cimene cikanamlenga.

Kukhalapo kwathu komanso kwa cilengedwe conse ndi umboni wakuti kuli Mulungu wamuyaya. Iye wakhala aliko nthaŵi zonse. Ndi amene anacititsa kuti zinthu zonse m’cilengedwe zizigwila nchito ndipo ndi amenenso anakhazikitsa malamulo akuti ziziyendela. Iye yekha ndi amene akanatha kuuzila mpweya wa moyo m’zinthu zonse.—Yobu 33:4.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani