Kuyankha Mafunso a M’baibulo
Kodi zipembedzo zonse zimalemekeza Mulungu?
Mukamamvetsela nkhani za padziko lonse, mwina mwaona kuti zinthu zoipa nthawi zina zimacitidwa m’dzina la cipembedzo. Zipembedzo zonse si zocokela kwa Mulungu woona. (Mateyu 7:15) Inde, anthu ambili asoceletsedwa.—Ŵelengani 1 Yohane 5:19.
Ngakhale zili conco, Mulungu amaona anthu oona mtima amene amakonda zabwino ndi coonadi. (Yohane 4:23) Mulungu akufuna kuti anthu otelo aphunzile coonadi ca Mau ake, Baibulo.—Ŵelengani 1 Timoteyo 2:3-5.
Kodi cipembedzo coona mungacidziŵe bwanji?
Yehova Mulungu akugwilizanitsa anthu ocokela m’zipembedzo zambili mwa kuwaphunzitsa coonadi komanso kukondana. (Mika 4:2, 3) Conco Akristu oona mungawadziwe mwa kuona mmene amaonetselana cikondi.—Ŵelengani Yohane 13:35.
Yehova Mulungu akugwilizanitsa anthu onse mwa kugwilitsila nchito kulambila koona.—Salimo 133:1.
Akristu oona amakhulupilila zimene Baibulo limanena ndipo amakhalanso moyo mogwilizana ndi zimene limanena. (2 Timoteyo 3:16) Iwo amalemekezanso dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Komanso amalengeza kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo ciyembekezo cokha ca anthu. (Danieli 2:44) Iwo amatsatila citsanzo ca Yesu mwakuonetsa“kuwala” kwao ndipo zimenezi zimaonekela pamene acitila anansi ao zinthu zabwino. (Mateyu 5:16) Conco Akristu oona tingawadziŵe cifukwa ca cikondi cimene amaonetsa kwa anansi ao powacezela n’colinga cowauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Ŵelengani Mateyu 24:14; Machitidwe 5:42; 20:20.