NKHANI 15
Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
Kodi zipembedzo zonse n’zovomelezeka kwa Mulungu?
Kodi cipembedzo coona tingacidziŵe bwanji?
Nanga ndani amene amalambila Mulungu m’coonadi padziko lapansi?
1. Ngati tilambila Mulungu m’njila yoyenela, kodi tingapindule bwanji?
YEHOVA MULUNGU amasamala kwambili za ife, ndipo amafuna kuti tizipindula ndi malangizo ake acikondi. Ngati timulambila m’njila yoyenela, tidzakhala anthu acimwemwe ndipo tidzapewa mavuto ambili pa umoyo wathu. Komanso iye adzatidalitsa ndi kutithandiza. (Yesaya 48:17) Koma pali zipembedzo zambili zimene zimakamba kuti zimaphunzitsa coonadi ponena za Mulungu. Ngakhale zili conco, zimaphunzitsa zinthu zosiyana kwambili pa nkhani yakuti Mulungu ndani, ndi zimene amayembekezela kwa ife.
2. Kodi njila yoyenela yolambilila Yehova tingaidziŵe bwanji? Ndipo n’citsanzo citi cimene cingatithandize kumvetsetsa zimenezi?
2 Kodi njila yoyenela yolambilila Yehova mungaidziŵe bwanji? Simufunikila kucita kuphunzila zikhulupililo za zipembedzo zonse, ndi kuyelekezela cina ndi cinzake kuti mudziŵe coona. Mumafunikila cabe kuphunzila zimene Baibo imaphunzitsa m’ceni-ceni pankhani ya kulambila koona. Tiyeni tiyelekezele conco: M’maiko ambili, kupanga ndalama zabodza ndi vuto lalikulu. Tikambe kuti mwapatsidwa nchito yopeza ndalama zabodza, kodi mungagwilitsile nchito njila yanji kuti mudziŵe ndalama zabodza? Kodi mungafune kudziŵa coyamba kuti ndalama iliyonse yabodza imaoneka bwanji? Mwacionekele iyai. M’malo motaya nthawi yocita zimenezo, mufunikila kungodziŵa mmene ndalama yeni-yeni imaonekela. Mukadziŵa mmene ndalama yeni-yeni imaonekela, cingakhale cosavuta kuti mudziŵe ndalama yabodza. Mofananamo, tikaphunzila mmene tingadziŵile cipembedzo coona, cidzakhala cosavuta kudziŵa zipembedzo zonama.
3. Monga mmene Yesu anakambila, kodi tiyenela kucita ciani kuti tikhale olandilika kwa Mulungu?
3 Kulambila Yehova m’njila imene amavomeleza n’cinthu cofunika kwambili. Anthu ambili amakhulupilila kuti zipembedzo zonse ndi zovomelezeka kwa Mulungu. Koma Baibo simaphunzitsa zimenezo. Komanso kungokamba cabe kuti ndine Mkristu sikokwanila. Yesu anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzaloŵa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene acita cifunilo ca Atate wanga wakumwamba.” Conco, kuti tikhale olandilika kwa Mulungu, tiyenela kuphunzila zimene iye amafuna ndi kuzicita. Yesu anacha ao amene sacita cifunilo ca Mulungu kuti “anthu osamvela malamulo.” (Mateyu 7:21-23) Mofanana ndi ndalama yabodza, cipembedzo conama cilibe phindu lililonse. Ndiponso coopsa n’cakuti, cipembedzo conama cimavulaza.
4. Malinga ndi mmene Yesu anakambila, kodi njila ziŵili zimaimila ciani? Ndipo njila iliyonse imapeleka kuti?
4 Yehova amapatsa munthu aliyense mwai wakuti akakhale ndi moyo wosatha padziko lapansi. Koma kuti tikalandile moyo wamuyaya m’Paladaiso, tiyenela kulambila Mulungu m’njila yovomelezeka, ndi kucita zinthu zimene iye amafuna. N’zomvetsa cisoni kuti anthu ambili sacita zimenezi. Ndiye cifukwa cake Yesu anakamba kuti: “Loŵani pacipata copapatiza. Pakuti mseu waukulu ndi wotakasuka ukupita kucionongeko, ndipo anthu ambili akuyenda mmenemo. Koma cipata coloŵela ku moyo n’copapatiza komanso mseu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi oŵelengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Cipembedzo conama cimapeleka ku cionongeko. Koma cipembedzo coona cimapeleka ku moyo wosatha. Yehova safuna kuti munthu aliyense akaonongeke, ndiye cifukwa cake amapeleka mwai wakuti anthu kulikonse aphunzile za iye. (2 Petulo 3:9) Conco, njila imene timalambilila Mulungu ingatipeleke ku moyo kapena ku imfa.
MMENE TINGADZIŴILE CIPEMBEDZO COONA
5. Kodi anthu a m’cipembedzo coona tingaŵadziŵe bwanji?
5 Kodi ‘njila yopita ku moyo’ tingaipeze bwanji? Yesu anakamba kuti cipembedzo coona cidzadziŵika mwa kuona makhalidwe a anthu a cipembedzo cimeneco. Iye anati: “Mudzawazindikila ndi zipatso zao, . . . mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino.” (Mateyu 7:16, 17) M’mau ena tingati, anthu a m’cipembedzo coona amadziŵika ndi zimene amakhulupilila ndi makhalidwe ao. Ngakhale kuti olambila oona naonso si angwilo, ndipo amatha kulakwitsa zinthu, io amafunitsitsa kucita cifunilo ca Mulungu. Tiyeni tione zinthu 6 zimene zimadziŵikitsa anthu amene ali m’cipembedzo coona.
6, 7. Kodi atumiki a Mulungu amaiona bwanji Baibo? Ndipo Yesu anapeleka bwanji citsanzo pa nkhani imeneyi?
6 Zimene atumiki a Mulungu amaphunzitsa amazicotsa m’Baibo. Baibo imadzikambila yokha kuti: “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuongola zinthu ndi kulangiza m’cilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenelela bwino ndi wokonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Polembela Akristu anzake, mtumwi Paulo anati: “Pamene munalandila mau a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandile monga mau a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mau a Mulungu.” (1 Atesalonika 2:13) Conco, zimene anthu a m’cipembedzo coona amakhulupilila ndiponso zimene amacita, sizitsatila maganizo kapena miyambo ya anthu. Zimacokela m’Mau a Mulungu, Baibo.
7 Yesu Kristu anapeleka citsanzo cabwino mwa kuphunzitsa zinthu zocokela m’Mau a Mulungu. Popemphela kwa Atate wake wakumwamba, iye anati: “Mau anu ndiwo coonadi.” (Yohane 17:17) Yesu anakhulupilila Mau a Mulungu, ndipo ciliconse cimene anali kuphunzitsa cinali kugwilizana ndi Mau a Mulungu. Kodi timadziŵa bwanji zimenezi? Yesu akalibe kugwila mau malemba, kaŵili-kaŵili anali kukamba kuti: “Malemba amati.” (Mateyu 4:4, 7, 10) Mofananamo, anthu a Mulungu masiku ano samaphunzitsa za m’maganizo mwao. Iwo amakhulupilila kuti Baibo ndi Mau a Mulungu, ndipo zonse zimene amaphunzitsa zimacokela m’Baibo.
8. Kodi kulambila Yehova kumaphatikizapo kucita ciani?
8 Anthu a m’cipembedzo coona amalambila Yehova yekha, ndipo amadziŵitsa anthu za dzina lake. Yesu anakamba kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.” (Mateyu 4:10) Conco, atumiki a Mulungu amalambila Yehova yekha cabe. Kulambila kumeneku kumaphatikizapo kudziŵitsa anthu dzina la Mulungu woona ndi makhalidwe ake. Lemba la Salimo 83:18 limati: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.” Yesu anapeleka citsanzo pankhani ya kuthandiza anthu kudziŵa Mulungu. Iye anakamba zimenezi m’pemphelo lake pamene anati: “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndaŵadziŵitsa dzina lanu.” (Yohane 17:6) Mofananamo, olambila oona masiku ano amaphunzitsa anthu za dzina la Mulungu, colinga cake, ndi makhalidwe ake.
9, 10. Kodi Akristu oona amaonetsana cikondi m’njila ziti?
9 Anthu a Mulungu amaonetsana cikondi ceni-ceni copanda dyela. Yesu anati: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukondana” wina ndi mnzake. (Yohane 13:35) Cikondi cimeneci n’cimene Akristu oyambilila anali naco kwa wina ndi mnzake. Cikondi ca umulungu cimatithandiza kupewa kukondela anthu ena, kapena kusankhana mitundu. Cimatithandizanso kukonda anthu a mitundu ina, kukhala pamtendele ndi anthu ena, kaya akhale osauka kapena olemela, ophunzila kapena osaphunzila. Cikondi cimeneci cimathandiza anthu kukhala paubale weni-weni. (Akolose 3:14) Anthu a m’zipembedzo zonama sali paubale wacikondi umenewu. Timadziŵa bwanji zimenezi? Iwo amaphana cifukwa ca kusiyana maiko kapena mitundu. Akristu oona satenga zida kuti aphe Akristu anzao, kapena munthu wina aliyense. Baibo imati: “Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyelekezi amaonekela bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sacita zolungama sanacokele kwa Mulungu, cimodzi-modzinso amene sakonda m’bale wake. . . . Tizikondana, osati ngati Kaini, amene anacokela kwa woipayo n’kupha m’bale wake.”—1 Yohane 3:10-12; 4:20, 21.
10 Komabe, cikondi ceni-ceni cimaphatikizapo zambili, osati cabe kupewa kuphana. Akristu oona amalola kuononga nthawi yao ndi cuma cao, kuti athandizane ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake. (Aheberi 10:24, 25) Amathandizana panthawi zovuta, komanso amacitilana zinthu moona mtima. Kweni-kweni, amagwilitsila nchito pa umoyo wao uphungu wa m’Baibo wakuti “ticitile onse zabwino.”—Agalatiya 6:10.
11. N’cifukwa ciani n’kofunika kuvomeleza kuti Yesu Kristu ndi amene Mulungu adzagwilitsila nchito kupulumutsa anthu?
11 Akristu oona amavomeleza kuti Yesu Kristu ndi amene Mulungu adzagwilitsila nchito kupulumutsa anthu. Baibo imati: “Cipulumutso sicipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo, limene lapelekedwa kwa anthu, limene tiyenela kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) Monga mmene tinaonela mu Nkhani 5, Yesu anapeleka moyo wake monga dipo la anthu omvela. (Mateyu 20:28) Kuonjezela pamenepo, Yesu ndiye Mfumu yakumwamba imene Mulungu anasankha kuti idzalamulile dziko lonse lapansi. Ndipo Mulungu amafuna kuti tizimvela Yesu ndi kutsatila ziphunzitso zake ngati tifuna kudzakhala ndi moyo wosatha. N’cifukwa cake Baibo imati: “Iye wokhulupilila mwa Mwanayo ali nao moyo wosatha. Wosamvela Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.”—Yohane 3:36.
12. Kodi kusakhala mbali ya dziko kumaphatikizapo ciani?
12 Olambila oona sali mbali ya dziko. Pamene Yesu anali kuweluzidwa ndi wolamulila wa Roma, Pilato, iye anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Mosasamala kanthu za dziko limene amakhalamo, otsatila oona a Yesu ali nzika za Ufumu wakumwamba. Pa cifukwa cimeneci, io amapewelatu kutenga mbali m’nkhani zandale. Satenganso mbali m’mikangano ya dziko. Komabe, olambila a Yehova saloŵelela m’zimene ena asankha monga kuloŵa cipani ca ndale, kuima pamasankho kapena kuvota. Ngakhale kuti olambila oona a Mulungu satenga mbali m’ndale, io amatsatila malamulo. N’cifukwa ciani amacita zimenezi? Cifukwa Mau a Mulungu amawalamula kuti azimvela “olamulila akulu-akulu” a boma. (Aroma 13:1) Koma pamene zofuna zao zisemphana ndi zofuna za Mulungu, olambila oona amatengela citsanzo ca atumwi, amene anati: “Ife tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”—Machitidwe 5:29; Maliko 12:17.
13. Kodi otsatila oona a Yesu amauona bwanji Ufumu wa Mulungu? Ndipo cifukwa ca zimenezo, io amacita ciani?
13 Otsatila oona a Yesu amalalikila kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo ciyembekezo cokha ca mtundu wa anthu. Yesu anakambilatu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) M’malo molimbikitsa anthu kuti azidalila olamulila aumunthu kuti ndi amene adzathetsa mavuto ao, otsatila oona a Yesu Kristu amalengeza kuti Ufumu wakumwamba wa Mulungu ndiwo ciyembekezo cokha ca mtundu wa anthu. (Salimo 146:3) Yesu anatiphunzitsa kupemphelela boma loyenelela limeneli pamene anati: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Mau a Mulungu anakambilatu kuti Ufumu wakumwamba “udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.
14. Kodi ndi gulu liti lacipembedzo limene muona kuti limatsatila zimene cipembedzo coona ciyenela kucita?
14 Poona zimene tangokambitsilana, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi gulu liti lacipembedzo limene ziphunzitso zake zonse zimacokela m’Baibo ndipo limadziŵitsa dzina la Yehova? Kodi ndi gulu liti limene limaonetsa cikondi caumulungu, limakhulupilila mwa Yesu, siili mbali ya dziko, ndipo limalengeza kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo ciyembekezo cokha ca mtundu wa anthu? Pa zipembedzo zonse zimene zili padziko lapansi, kodi ndi citi cimene cimacita zonsezi?’ Umboni woonekelatu uonetsa kuti ndi Mboni za Yehova.—Yesaya 43:10-12.
KODI INU MUDZACITA CIANI?
15. Kodi Mulungu amafuna ciani kuonjezela pa kukhulupilila kuti aliko?
15 Kungokhulupilila Mulungu sikokwanila kuti tim’kondweletse. Ndipo Baibo imakamba kuti ngakhale ziŵanda zimakhulupilila kuti Mulungu aliko. (Yakobo 2:19) Koma n’zodziŵikilatu kuti ziŵanda sizimacita cifunilo ca Mulungu ndipo iye sakondwela nazo. Kuti tikhale olandilika kwa Mulungu, sitiyenela kukhulupilila cabe kuti aliko, koma tiyenelanso kucita cifunilo cake. Tiyenelanso kucoka m’cipembedzo conama ndi kuyamba kulambila koona.
16. Kodi tiyenela kucita ciani pa nkhani ya kugwilizana ndi cipembedzo conama?
16 Mtumwi Paulo anaonetsa kuti sitiyenela kutenga mbali pa kulambila konama. Iye analemba kuti: “‘Tulukani pakati pao, lekanani nao,’ watelo Yehova. ‘Musakhudze cinthu codetsedwa’; ‘ndipo ndidzakulandilani.’” (2 Akorinto 6:17; Yesaya 52:11) Conco, Akristu oona amapewa ciliconse cokhudzana ndi kulambila konama.
17, 18. Kodi “Babulo Wamkulu” n’ciani? Ndipo n’cifukwa ciani kuli kofunika kwambili ‘kutuluka mwa iye’ msanga-msanga?
17 Baibo imaonetsa kuti mitundu yonse ya cipembedzo conama ili mbali ya “Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 17:5) Dzina limenelo limatikumbutsa za Babulo wakale, kumene cipembedzo conama cinayambila pambuyo pa Cigumula ca m’masiku a Nowa. Ziphunzitso zambili ndi miyambo imene ili m’zipembedzo zonama inacokela ku Babulo wakale. Mwacitsanzo, Anthu a ku Babulo anali kulambila milungu itatu-itatu. Ndipo masiku ano, zipembedzo zambili zimaphunzitsa za Utatu. Koma Baibo imaphunzitsa momveka bwino kuti pali Mulungu woona mmodzi cabe, Yehova, ndi kuti Yesu Kristu ndi Mwana wake. (Yohane 17:3) Anthu a ku Babulo anali kukhulupililanso kuti pali mzimu umene umacoka m’thupi mwa munthu akafa ndi kupitiliza kukakhala ndi moyo kwinakwake, ndi kuti munthu amapita kukazunzika ku moto wa kuhelo. Masiku anonso, zipembedzo zambili zimaphunzitsa cikhulupililo cimeneci.
18 Popeza kuti ciphunzitso ca ku Babulo wakale cinafalikila padziko lonse lapansi, masiku ano Babulo wamkulu amadziŵika kuti ndi ufumu wa padziko lonse wa cipembedzo conama.a Ndipo Mulungu anakambilatu kuti ufumu wa padziko lonse wa cipembedzo conama umenewu udzacotsedwa mwamsanga. (Chivumbulutso 18:8) Kodi mwaona cifukwa cake muyenela kulekelatu kucita kanthu kalikonse kokhudzana ndi Babulo Wamkulu? Yehova Mulungu amafuna kuti ‘mutuluke mwa iye’ msanga-msanga pamene kukali nthawi.—Chivumbulutso 18:4.
Ngati mutumikila Yehova pamodzi ndi anthu ake, mudzapeza zambili kuposa zimene mungataye
19. Kodi mudzapeza ciani ngati mutumikila Yehova?
19 Cifukwa cakuti mwasankha kucoka m’cipembedzo conama, anthu ena angaleke kugwilizana nanu. Komabe, mwa kutumikila Yehova pamodzi ndi anthu ake, mudzapeza zambili kuposa zimene mungataye. Mofanana ndi ophunzila a Yesu amene anasiya zinthu zina ndi kutsatila Yesu, mudzakhala ndi abale ndi alongo anu a kuuzimu ambili. Mudzakhala mbali ya banja lalikulu la padziko lapansi la Akristu oona, amene adzakukondani mocokela pansi pa mtima. Ndipo mudzakhalanso ndi ciyembekezo cabwino ca moyo wosatha “m’nthawi imene ikubwela.” (Maliko 10:28-30) Mwina m’kupita kwa nthawi, ao amene analeka kugwilizana nanu cifukwa ca zimene mumakhulupilila, naonso angayambe kuphunzila zimene Baibo imaphunzitsa ndi kukhala olambila a Yehova.
20. Kodi anthu amene ali m’cipembedzo coona adzapeza ciani mtsogolo?
20 Baibo imaphunzitsa kuti posacedwa Mulungu adzacotsapo dongosolo la zinthu loipa limeneli, ndipo adzabweletsa dziko latsopano la cilungamo limene lidzalamulidwa ndi Ufumu wake. (2 Petulo 3:9, 13) Dziko limenelo lidzakhala labwino kwambili! Ndipo m’dziko latsopano lacilungamo limenelo, mudzakhala cipembedzo coona cimodzi cabe, njila yoona imodzi yolambilila. Kodi si cinthu canzelu kuti inu mucite zofunikila kuti muyambe kugwilizana ndi olambila oona pa nthawi ino?
a Kuti mudziŵe zambili za cifukwa cimene Babulo Wamkulu amaimila ufumu wa padziko lonse wa cipembedzo conama, onani Zakumapeto, pamapeji 219 mpaka 221.