Zamkati
August 15, 2014
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
YOPHUNZILA
SEPTEMBER 29, 2014–OCTOBER 5, 2014
Malo a Akazi m’Kakonzedwe ka Yehova
TSAMBA 6 • NYIMBO: 86, 104
OCTOBER 6-12, 2014
Gwilitsilani Nchito Mau a Mulungu—Ndi Amoyo
TSAMBA 11 • NYIMBO: 114, 101
OCTOBER 13-19, 2014
Mmene Yehova Amayandikilila kwa Ife
TSAMBA 16 • NYIMBO: 51, 91
OCTOBER 20-26, 2014
Muzimvetsela Mau a Yehova Kulikonse Kumene Mungakhale
TSAMBA 21 • NYIMBO: 26, 89
NKHANI ZOPHUNZILA
▪ Malo a Akazi m’Kakonzedwe ka Yehova
Tidzaphunzila mmene kupandukila Mulungu m’Edeni kwakhudzila amuna ndi akazi. Tidzakambilana zocita za akazi ena oopa Mulungu a m’nthawi yakale. Ndipo, tidzaphunzilanso malo a akazi Acikristu m’kakonzedwe ka Mulungu masiku ano.
▪ Gwilitsilani Nchito Mau a Mulungu—Ndi Amoyo
Wofalitsa aliyense amafuna kulalikila mogwila mtima. Tidzaphunzila mfundo zothandiza za mmene tingagwilitsile nchito Baibulo ndi tumapepala twauthenga kuti tiyambitse makambilano, ndi mmene tingafikile anthu pamtima ndi Mau a moyo a Yehova.
▪ Mmene Yehova Amayandikilila kwa Ife
Tifunikila kukhala paubale wabwino ndi Mlengi wathu. Tidzaphunzila mmene dipo ndi Mau a Yehova olembedwa, zimaonetsela kuti iye wacitapo kanthu kuti timuyandikile.
▪ Muzimvetsela Mau a Yehova Kulikonse Kumene Mungakhale
Kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, tiyenela kumvetsela zimene Yehova amatiuza. Tidzaphunzila zimene zingatithandize kuti tizimvetsela mau a Yehova mosasamala kanthu za macenjela a Satana ndi zilakolako zathu zoipa. Nkhani ino idzatithandiza kuyamikila ubwino wolankhula ndi Mulungu woona.
NKHANI ZINA M’MAGAZINI INO
3 Kodi Mumalandila “Cakudya pa Nthawi Yoyenela”?
26 ‘Bwelelani Mukalimbikitse Abale Anu’
CIKUTO: Alongo alalikila m’Cirasha, m’mbali mwa nyanja ku Tel-Aviv. Cakumbuyo kuli tumapili twa miyala mu mzinda wa makono wa Jaffa, umene unali gombe lakale la ku Yopa
KU ISRAEL
KULI ANTHU
8,050,000
CIŴELENGELO CA PAMWAMBA CA OFALITSA MU 2013
1,459
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO MU 2013
2,671