LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 11/1 masa. 3-6
  • Kodi Anthu Adzaononga Dziko Lapansi Kothelatu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Anthu Adzaononga Dziko Lapansi Kothelatu?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI LAFIKA PAKUTI SILINGAKONZEDWENSO?
  • CILENGEDWE CIKUONONGEKA PANG’ONOPANG’ONO
  • COLINGA CA MLENGI
  • DZIKO LAPANSI NDI MUDZI WATHU KOSATHA
  • Mulungu Analonjeza Kuti Dziko Lapansi Lidzakhalapo Kwamuyaya
    Galamuka!—2023
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 11/1 masa. 3-6

NKHANI YA PACIKUTO

Kodi Anthu Adzaononga Dziko Lapansi Kothelatu?

“M’badwo umapita ndipo m’badwo wina umabwela, koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”—Anatero MFUMU SOLOMO WA M’ZAKA ZA M’MA 1000 B.C.E.a

Munthu wakale amene analembako Baibulo, anaona kuti moyo ndi waufupi kuyelekezela ndi mfundo yakuti dziko lapansi linalengedwa kuti likhale kosatha. Zoonadi, kwa zaka zambili pakhala mibadwo yosiyanasiyana koma Dziko Lapansi lili cikhalile lolimba ndi losagwedezeka pocilikiza zamoyo zosiyanasiyana mpaka pano.

Dziko lapansi lasintha kwambili makamaka kuyambila pa nthawi ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse. M’zaka pafupifupi 70 zapitazo, anthu akhala akuona kusintha pankhani ya mayendedwe, kulankhulana ndiponso pali zipangizo zina zamakono zimene zapangitsa kuti zacuma zisinthenso kwambili padziko lapansi. Anthu ambili masiku ano akusangalala ndi umoyo wabwino umene kale unali kuoneka wosatheka. Panthawi ino, ciŵelengelo ca anthu padziko lapansi caculuka kwambili.

Komabe, zinthu zimenezi zacititsanso mavuto ena. Ena amakamba kuti zocita za anthu n’zimene zikuononga dziko ndipo zimenezi zacititsa mavuto ambili okhudza mmene zinthu zacilengedwe zimayendela. Asayansi ena akuona kuti kwa zaka mahandilendi angapo apitawo, anthu akhala akucita zinthu zimene zasintha dziko lapansi kwambili.

Baibulo linakambilatu za nyengo imene anthu ‘adzaononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Ena amafuna kudziŵa ngati tikukhala m’nyengo imeneyo. Kodi adzaononga dzikoli kufika pati? Kodi lidzafika poti silingathe kukonzedwanso? Kodi zoona anthu adzaononga dziko lapansi kothelatu?

KODI LAFIKA PAKUTI SILINGAKONZEDWENSO?

Kodi dziko laonongedwa mpaka kufika pakuti silingakonzedwenso? Asayansi ena akuona kuti n’zovuta kudziŵilatu zotulukapo zimene zingakhalepo cifukwa ca kuonongedwa kwa dziko. Conco, io akucita mantha kwambili kuti mwina tikufika m’nthawi imene zocita za anthu zikuonongelatu dzikoli, ndipo amakamba kuti zimenezi zingapangitse nyengo kusintha mwadzidzidzi ndi kucititsa mavuto oopsa.

Mwacitsanzo, ganizilani za madzi oundana a ku West Antarctic. Anthu ena amati ngati kutentha kupitilizabe padziko lapansi, ndiye kuti panthawi ina madzi onse oundana amenewa adzasungunukilatu cakuti sadzaundananso. Izi zili conco cifukwa cakuti madzi oundana amenewa mwacilengedwe samalola mphamvu ya dzuŵa kulowa pansi pa nyanja. Komabe, madzi oundanawo akapitiliza kusungunuka cifukwa ca kutentha, madzi a pansi pa nyanjayo pang’onopang’ono adzayamba kuonekela. Popeza kuti pansi pa nyanjayo pali mdima, n’kosavuta kuti mphamvu ya dzuŵa ilowe pansi pa nyanja ndipo zimenezi zingapangitse kuti madzi oundanawo apitilize kusungunuka. Ngati zimenezi zingapitilize, pangakhale mavuto aakulu. Madzi oundana akasungunuka, zingapangitse nyanja zing’onozing’ono kudzaza ndi kusefukila cakuti anthu mamiliyoni ambili angakumane ndi mavuto aakulu.

CILENGEDWE CIKUONONGEKA PANG’ONOPANG’ONO

Anthu apeleka njila zosiyanasiyana za mmene “mavuto a mwadzidzidzi amene pulaneti” lathu likukumana nao angathetsedwele. Njila imodzi yothetsela mavutowo imachedwa citukuko cosaononga cilengedwe. Zimenezi zikutanthauza kulimbikitsa anthu kugwilitsila nchito zinthu zacilengedwe kutukula cuma ndi khalidwe lao. Kodi zotsatilapo zake zakhala zotani?

N’zomvetsa cisoni kuti mavuto acilengedwe akungoculukilaculukila. Anthu akupitilizabe kuononga zacilengedwe mofulumila kwambili kuposa mmene dziko limadzibwezeletsela. Kodi pali ciliconse cimene tingacitepo? Katswili wina wa zam’nkhalango anakamba mosapita m’mbali kuti: “Kunena zoona, sitidziŵa kuti tingayambile pati kukonza pulaneti lathuli.” Zimenezi zikugwilizana ndi mau a m’Baibulo akuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

Koma Baibulo limatsimikizila kuti Mulungu, Mlengi wathu, sadzalola anthu kuononga cilengedwe kothelatu. Lemba la Salimo 115:16 limati: “Dziko lapansi [Mulungu] analipeleka kwa ana a anthu.” Zoonadi, dziko lapansi ndi ‘mphatso yabwino’ imene Atate wathu wakumwamba anatipatsa. (Yakobo 1:17) Kodi muganiza kuti Mulungu angatipatse mphatso yabwino kwambili koma yosakhalitsa? Kutalitali! Ndipo mfundo imeneyi imakhala yomveka tikaona mmene dziko linalengedwela.

COLINGA CA MLENGI

Buku la m’Baibulo la Genesis, limatiuza mwatsatanetsatane mmene Mulungu analengela dziko lapansi. Paciyambi, dziko lapansi linali “lopanda maonekedwe enieni ndiponso lopanda kanthu . . . Ndipo pamwamba pake panali mdima wokhawokha.” Komabe, lembali limachula mwacindunji “madzi” omwe ndi ofunika kwambili kwa zamoyo zokhala pa pulaneti limeneli. (Genesis 1:2) Kenako Mulungu anati: “Pakhale kuwala.” (Genesis 1:3) Mwacionekele, mphamvu ya dzuŵa inadutsa m’mitambo, ndiyeno kwa nthawi yoyamba kuwala kunayamba kuonekela padziko lapansi. Baibulo limakambanso za kupangidwa kwa mtunda ndi nyanja. (Genesis 1:9, 10) Kenako ‘udzu, zomela zobala mbewu monga mwa mtundu wake ndi mitengo yobala zipatso’ zinaonekela. (Genesis 1:12) M’kupita kwa nthawi analenganso zinthu zina zofunika kwambili pa umoyo. Kodi colinga cimene analengela zinthu zonsezi cinali ciani?

Mneneli wakale Yesaya anafotokoza Mulungu kuti ndi “amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, amene analikhazikitsa mwamphamvu, amene sanalilenge popanda colinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Ndithudi, colinga ca Mulungu n’cakuti padziko lapansi pakhale anthu kosatha.

Koma n’zomvetsa cisoni kuti anthu agwilitsila nchito molakwika mphatso yokongola imene Mulungu anatipatsa mpaka afika pakuiononga. Komabe, colinga ca Mlengi sicinasinthe. Munthu wina wakale anati: “Mulungu si munthu, woti anganene mabodza, si mwana wa munthu, woti angadzimve kuti ali ndi mlandu. Kodi ananenapo kanthu koma osachita?” (Numeri 23:19) M’malo molola kuti dziko lapansi lionongedwe, nthaŵi ikuyandikila kwambili yakuti Mulungu ‘aononge amene akuononga dziko lapansi.’—Chivumbulutso 11:18.

DZIKO LAPANSI NDI MUDZI WATHU KOSATHA

Paulaliki wake wochuka wa pa phili, Yesu Kristu anati: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, cifukwa adzalandila dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Pambuyo pake mu ulaliki umodzimodziwo, Yesu anachula cimene cidzathandiza kuti anthu asapitilize kuononga dziko. Iye analangiza otsatila ake kupemphela kuti: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” Zoonadi, Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma, ndi limene lidzakwanilitsa colinga ca Mulungu padziko lapansi.—Mateyu 6:10.

Ponena za masinthidwe aakulu amene Ufumu wa Mulungu udzacita, Mulungu anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5) Kodi zimenezi zitanthauza kuti Mulungu adzalenga dziko lina latsopano kuti liloŵe m’malo mwa dziko lino? Iyai. Tikutelo cifukwa cakuti palibe colakwika ciliconse ndi mmene pulaneti lathu linalengedwela. M’malo mwake, Mulungu adzaononga anthu onse “amene akuwononga dziko lapansi,” omwe ndi maboma onse a anthu amene akulamulila masiku ano. Maboma amenewa adzaloŵedwa m’malo ndi “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano” kutanthauza Ufumu wa Mulungu umene ndi boma lakumwamba lolamulila anthu okhala pa dziko lapansi latsopano.—Chivumbulutso 21:1.

Mulungu adzakonza ndi kubwezeletsa zinthu za m’cilengedwe n’colinga cakuti zipitilize kucilikiza zamoyo. Pofotokoza zimene Mulungu adzacita, wamasalimo anati: “Inu mwatembenukila dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zoculuka, mwalilemeletsa kwambili.” Inde, cifukwa ca nyengo yabwino, ndipo koposa zonse madalitso a Mulungu, dziko lapansi lidzakhala paladaiso, ndiponso mudzakhala cakudya coculuka.—Salimo 65:9-13.

A Pyarelal, omwe anali kalembela wa Malemu Mohandas Gandhi, mtsogoleli wacipembedzo ku India, anakamba kuti, a Gandhi anali kuona kuti: “Dziko lapansi lili ndi zinthu zimene zingakwanitse kukhutilitsa zosoŵa zonse za anthu, koma osati kukhutilitsa zikhumbo zadyela za anthu.” Ufumu wa Mulungu udzathetsa gwelo la mavuto onse padziko lapansi mwa kusintha mitima ya anthu. Mneneli Yesaya analosela kuti mu ulamulilo wa Ufumu, anthu ‘sadzavulazana kapena kuwonongana,’ kapenanso kuononga dziko lapansi. (Yesaya 11:9) Ngakhale masiku ano, anthu mamiliyoni ambili azikhalidwe zosiyanasiyana ndiponso a moyo wosiyanasiyana ayamba kale kuphunzila za mfundo zapamwamba za Mulungu. Iwo akuphunzitsidwa kukonda Mulungu ndi anthu anzao, kukhala oyamikila, kusamalila ndi kuteteza cilengedwe, ndiponso kukhala ndi moyo mogwilizana ndi colinga cimene Mlengi analengela anthu ndi dziko lapansi. Iwo akukonzekeletsedwa za moyo wa m’paladaiso padziko lapansi.—Mlaliki 12:13; Mateyu 22:37-39; Akolose 3:15.

Nkhani yofotokoza za kulengedwa kwa zinthu imene ili m’buku la Genesis imamaliza ndi mau akuti: “Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambili.” (Genesis 1:31) Ndithudi, Mulungu sadzalola kuti dziko lokongolali lionongedwe kothelatu. N’zolimbikitsa kudziŵa kuti tsogolo la pulaneti lathu lili m’manja mwa Mlengi wathu wacikondi, Yehova Mulungu. Iye walonjeza kuti: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Inunso mukhoza kukhala pakati pa “olungama” amene adzacha dziko lapansi mudzi wao kwamuyaya.

a Kucokela m’Baibulo pa lemba la Mlaliki 1:4.

Anthu Alephela Kusamala Dziko Lapansi

  • Mlengalenga. “Pali umboni wosatsutsika woonetsa kuti mlengalenga wa padziko lapansi, nyanja, ndiponso mtunda zikutentha kwambili . . . Kuyambila ca m’ma 1950, zocita za anthu n’zimene zapangitsa kutentha kumeneku.”—American Meteorological Society, 2012.

  • Nthaka. “Zocita za anthu zaononga pafupifupi 50 pelesenti ya nthaka yonse ya padziko lapansi ndipo zimenezi zabweletsa mavuto ambili okhudza” nchito yoteteza ndi kusamalila zacilengedwe, zomela zimasoŵa cakudya cokwanila . . . ndiponso mavuto ena okhudza nyengo.”—Global Change and the Earth System.

  • Nyanja. “M’malo ambili kumene kale kunali kupezeka nsomba, sizikupezekanso, kwina zinaonongedwa kapena zikucepa kapenanso m’pamene zikuyambanso kubelekana.”—BBC, September 2012.

  • Nkhalango. “Asayansi ambili amaganiza kuti . . . anthu ndi amene ayenela kuimbidwa mlandu woononga mitundu yosiyanasiyana ya zacilengedwe, ndipo zimenezi zikucitika mofulumila kwambili masiku ano.”—From science.nationalgeographic.com.

Dziko Lathu

Dziko lapansi lili ndi njila yapadela yothandiza anthu, zinyama, ndi zomela kukhala ndi moyo. Mwacitsanzo, zomela zimalandila mphamvu ya dzuŵa, ndipo zimagwilitsila nchito mphamvuyo kusintha mpweya wa carbon dioxide, madzi, ndi zinthu zina ndi kupanga mpweya wa okisijini ndi cakudya. Anthufe ndi zinyama timafunika mpweya wa okisijini ndi cakudya, ndipo timatulutsa mpweya wa carbon dioxide ndi zinthu zina. Kayendedwe ka zinthu kameneka sikaima, kamacitika nthawi zonse. Mwakutelo dziko lingapitilize kucilikiza moyo kwamuyaya.

M’pake kuti Baibulo limafotokoza kuti Mulungu ndi “amene mwanzelu zake anakhazikitsa dziko limene anthu amakhalamo.” (Yeremiya 10:12) Katswili wina wa Baibulo anati: “Dziko lapansi linalengedwa mwaluso kwambili n’colinga cakuti anthu azikhalamo.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani