Zamkati
November 15, 2014
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
YOPHUNZILA
DECEMBER 29, 2014–JANUARY 4, 2015
Kodi Kuukitsidwa kwa Yesu Kumatanthauza Ciani kwa Ife?
TSAMBA 3 • NYIMBO: 5, 60
JANUARY 5-11, 2015
Cifukwa Cake Tifunika Kukhala Oyela
TSAMBA 8 • NYIMBO: 119, 17
JANUARY 12-18, 2015
Tifunika Kukhala Oyela m’Makhalidwe Athu Onse
TSAMBA 13 • NYIMBO: 65, 106
JANUARY 19-25, 2015
“Anthu Amene Mulungu Wao Ndi Yehova”
TSAMBA 18 • NYIMBO: 46, 63
JANUARY 26, 2015–FEBRUARY 1, 2015
‘Tsopano Ndinu Anthu a Mulungu’
TSAMBA 23 • NYIMBO: 112, 101
NKHANI ZOPHUNZILA
▪ Kodi Kuukitsidwa kwa Yesu Kumatanthauza Ciani kwa Ife?
M’nkhani ino, tidzaphunzila cifukwa cake timakhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa ndipo ali moyo. Tidzaphunzilanso mmene kuukitsidwa kwa Kristu ku moyo wosafa wakumwamba kumatikhudzila, ndi mmene kumakhudzila nchito yathu monga alengezi a Ufumu.
▪ Cifukwa Cake Tifunika Kukhala Oyela
▪ Tifunika Kukhala Oyela m’Makhalidwe Athu Onse
Nkhani ziŵilizi, zimene ndi zozikidwa m’buku la Levitiko, zidzafotokoza cifukwa cake Yehova amafuna kuti anthu ake akhale oyela, ndi mmene tingaonetsele khalidwe limeneli. Tidzaphunzilanso mmene tingaonetsele kuti ndife oyela m’makhalidwe athu onse.
▪ “Anthu Amene Mulungu Wao Ndi Yehova”
▪ ‘Tsopano Ndinu Anthu a Mulungu’
Anthu ena amene timaphunzila nao Baibulo, samakhulupilila kuti Yehova ali ndi gulu limodzi cabe padziko lapansi. Iwo amaganiza kuti kungokhala munthu wabwino n’kokwanila kuti ukondweletse Mulungu, mosasamala kanthu za cipembedzo cako. Nkhani ziŵilizi, zidzatithandiza kuzindikila anthu a Mulungu, ndi kugwilizana nao potumikila Yehova.
PACIKUTO: Ofalitsa a Ufumu alalikila ku Santiago de Cuba, mzinda wina waukulu wa pa cilumba umene ndi wochuka cifukwa ca nyimbo za kumaloko ndi magule ake
KU CUBA
KULI ANTHU
11,163,934
OFALITSA
96,206
APAINIYA ANTHAWI ZONSE
9,040