LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 5/1 masa. 4-7
  • Pulogalamu Yophunzila Baibulo ya Anthu Onse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pulogalamu Yophunzila Baibulo ya Anthu Onse
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MAYANKHO A MAFUNSO OFUNSIDWA KAŴILIKAŴILI OKHUDZA PULOGALAMU YATHU YOPHUNZITSA BAIBULO
  • Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?
    Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?
  • Kodi mwazikonda zimene mwaphunzila?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
  • N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • N’ciyani Cingakuthandizeni Kuti Musaleke Kuphunzila Baibo?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 5/1 masa. 4-7
Phunzilo la Baibulo

NKHANI YA PACIKUTO|KODI MUNGAKONDE KUPHUNZILA BAIBULO?

Pulogalamu Yophunzila Baibulo ya Anthu Onse

Mboni za Yehova zimadziŵika bwino ndi nchito yao yolalikila. Koma kodi mumadziŵa kuti tilinso ndi pulogalamu yophunzitsa Baibulo padziko lonse?

Mwamuna akuphunzila Baibulo kunchito

Mu 2014, Mboni zoposa 8 miliyoni m’maiko 240 zinaphunzitsa Baibulo anthu pafupifupi 9.5 miliyoni mwezi uliwonse.a Ciŵelengelo ca amene timaphunzila nao Baibulo cimaposa ciŵelengelo ca anthu m’maiko ena 140 paokhapaokha.

Kuti zikwanitse kugwila nchito yophunzitsa imeneyi, Mboni za Yehova zimasindikiza Mabaibulo pafupifupi 1.5 biliyoni, mabuku, magazini, ndi zofalitsa zina zothandiza pophunzila Baibulo caka ciliconse m’zinenelo 700. Kusindikizidwa kwa zofalitsa m’zinenelo zosiyanasiyana, kwathandiza kuti anthu aphunzile Baibulo m’cinenelo cimene afuna.

“Sindinali kukonda zophunzila kusukulu, koma phunzilo la Baibulo linali losangalatsa kwambili. Zimene ndinaphunzila zinali zotonthoza kwambili”—Katlego, South Africa.

“Pa phunzilo limeneli ndinapeza mayankho a mafunso anga onse ndi enanso ambili.”—Bertha, Mexico.

“Ndinali kucitila phunziloli pa nyumba pathu ndiponso pa nthawi imene ndinali kufuna. Zimenezi zinandikondweletsa kwambili.”—Eziquiel, Brazil.

“Ndinali kuphunzila mphindi 15 kapena 30 mwinanso kuposapo malinga ndi nthawi imene ndinali nayo.”—Viniana, Australia.

“Kosi imeneyi inali yaulele ndipo inali yosangalatsa kwambili”—Aimé, Benin.

“Munthu amene anali kundiphunzitsa Baibulo anali woleza mtima ndi wokoma mtima. Conco, tinakondana kwambili.”—Karen, Northern Ireland.

“Anthu ambili amaphunzila Baibulo koma sakhala a Mboni za Yehova.”—Denton, England.

MAYANKHO A MAFUNSO OFUNSIDWA KAŴILIKAŴILI OKHUDZA PULOGALAMU YATHU YOPHUNZITSA BAIBULO

Kodi phunzilo la Baibulo limacitika bwanji?

Timasankha nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo ndi kukambilana malemba ogwilizana ndi zimene tikuphunzila. Mwacitsanzo, Baibulo limayankha mafunso monga akuti: Kodi Mulungu ndani? Nanga ali ndi makhalidwe abwanji? Kodi ali ndi dzina? Nanga akhala kuti? Kodi n’zotheka kumuyandikila? Vuto ndi lakuti anthu sadziŵa mmene angapezele mayankho m’Baibulo.

Kuti tithandize anthu kupeza mayankho, timagwilitsila nchito buku lakuti, Zimene Baibo Imaphunzitsa.b Bukuli linakonzedwa kuti lithandize anthu kumvetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibulo. Lili ndi nkhani zokhudza Mulungu, Yesu Kristu, kuvutika kwa anthu, ciukililo, pemphelo, ndi zina zambili.

Ndi liti ndipo ndi kuti kumene kumacitikila phunzilo la Baibulo?

Mungacite phunzilo limeneli panthawi ndi malo amene mufuna.

Kodi phunzilo limatenga utali wotani?

Anthu ambili amapatula ola limodzi kapena angapo mlungu uliwonse kuti aphunzile Baibulo. Palibe nthawi yoikika ya kutalika kwa phunzilo, zimadalila mmene inuyo mwalinganizila zinthu. Ena amaphunzila mphindi 10 kapena 15 mlungu uliwonse.

Ndi ndalama zingati zimene mungalipile kuti muphunzile Baibulo?

Kosi imeneyi limodzi ndi mabuku ogwilitsila nchito pophunzila ndi zaulele. Izi ndi zogwilizana ndi zimene Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.”—Mateyu 10:8.

Kodi kosi yophunzila Baibulo imeneyi imatenga utali wotani?

Utali wa phunzilo limeneli ukudalila zimene inuyo mufuna kuphunzila. Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa Mceni-ceni lili ndi nkhani 19. Mungasankhe kuculuka kwa zimene mufuna kuphunzila.

Ngati ndavomela kuti ndiziphunzila Baibulo, kodi ndiyenela kukhala wa Mboni za Yehova?

Ai. Ife timazindikila kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene afuna kuti azikhulupilila. Conco, anthu amene aphunzila mfundo zoyambilila za m’Baibulo, angasankhe zimene afuna.

N’kuti kumene ndingadziŵile zambili?

Webusaiti ya jw.org ili ndi mfundo zolondola zokhudza zikhulupililo za Mboni za Yehova ndi zimene zimacita.

Ndingapemphe bwanji phunzilo la Baibulo?

Anthu akupempha phunzilo la Baibulo: pa intaneti, kalata, ndi pa foni
  • Lembani fomu ya pa Intaneti yofunsila phunzilo la Baibulo pa www.jw.org.

  • Lembani kalata pogwilitsila nchito keyala imene ili pa tsamba 2 la magazini ino.

  • Kambani ndi Mboni za Yehova za kwanuko.

a Timacita phunzilo limeneli ndi munthu aliyense payekha kapenanso m’tumagulu.

b Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Makope oposa 230 miliyoni a buku limeneli asindikizidwa m’zinenelo zoposa 260.

MPHATSO YOTHANDIZA KWA MABANJA

Eziquiel

“Pamene mkazi wanga anayamba kuphunzila Baibulo, ndinaona kuti wasintha kwakukulu. Umoyo wa banja lathu unakhala wabwino kwambili. Nditacita cidwi ndi zimene anali kuphunzila, inenso ndinayamba kuphunzila. Zimene ndinaphunzila zinandithandiza kukhala munthu wabwino. Ndipo zimene tinaphunzila m’Baibulo zinapangitsa banja lathu kukhala logwilizana kwambili.”—Eziquiel.

Karen

“Nditayamba kuphunzila Baibulo, ndinaleka cizoloŵezi canga cakumwa mankhwala osokoneza ubongo, kuledzela, ndipo ndaphunzila kuugwila mtima. Tsopano, nyumba yanga ndi yaukhondo. Ndimakonda kwambili banja langa ndipo ndimacita zinthu zimene zimalisangalatsa. Ndine wokondwela kwambili.”—Karen.

Viniana

“Anthu ena anali kunditsutsa kaamba ka kuphunzila Baibulo. Koma mwamuna wanga anandilimbikitsa mwa kundiuza kuti: ‘Usavutike ndi zimene anthu amakamba. Ndikakuona ukusintha kukhala munthu wabwino, ndimakondwela kwambili. Pitiliza kuphunzila Baibulo.’ Banja lathu silinakhalepo labwino ngati mmene lilili palipano.”—Viniana.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani