Mbili Yanga
Madalitso “m’Nthawi Yabwino ndi m’Nthawi Yovuta”
NDINABADWILA m’mudzi wa Namkumba pafupi ndi mzinda wa Lilongwe ku Malawi mu March, 1930. Ndipo acibale anga onse komanso anzanga anali kutumikila Yehova mokhulupilika. Mu 1942, ndinadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa mu umodzi wa mitsinje yathu yokongola. Pa zaka 70 zotsatilapo, ndinaganiza zocita monga mmene Paulo analangizila Timoteo kuti, “lalikila mau. Lalikila modzipeleka, m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta.”—2 Tim. 4:2.
Mu 1948, mbale Nathan H. Knorr ndi mbale Milton G. Henschel anabwela kudzacititsa msonkhano ku Malawi kwa nthawi yoyamba, ndipo kucoka nthawiyo cikhumbo cakuti nditumikile Yehova mu utumiki wanthawi zonse cinakula kwambili. Ndikumbukila bwinobwino mfundo zolimbikitsa zimene abale amenewa oimila likulu la Mboni za Yehova ananena. Tinali okwanila 6,000 ndipo tinaimilila m’munda wamatope kuti timvetsele nkhani yolimbikitsa imene M’bale Knorr anakamba ya mutu wakuti: “Wolamulila Wosatha wa Mitundu ya Anthu.”
Ndinakumana ndi mlongo wina wokongola dzina lake Lidasi amenenso anakulila m’banja la Mboni za Yehova, ndipo tinali ndi colinga cofanana ca kucita utumiki wa nthawi zonse. Mu 1950 tinakwatilana, ndipo podzafika mu 1953 tinali ndi ana aŵili. Ngakhale kuti udindo unaonjezeka wolela ana, tinaganiza zakuti ndiyambe upainiya wanthawi zonse. Patapita zaka ziŵili, ndinauzidwa kuti ndizitumikila monga mpainiya wapadela.
Patangopita nthawi yocepa, ndinapatsidwa mwai wocezela mipingo monga woyang’anila dela. Ndinakwanitsa kusamalila banja langa mwakuthupi ndi mwa kuuzimu cifukwa ca thandizo la Lidasi mkazi wanga.a Koma cifuno cathu cinali cakuti tonse tikhale mu utumiki wanthawi zonse. Pambuyo polinganiza bwino zinthu komanso cifukwa cothandizidwa ndi ana athu asanu, Lidasi naye anayamba utumiki wa nthawi zonse mu 1960.
Misonkhano ikuluikulu inatithandiza kukonzekela cisautso cimene cinali kubwela
Tinasangalala kwambili pamene tinali kutumikila abale ndi alongo athu m’mipingo yosiyanasiyana. Pa nchitoyi tinayenda m’madela okongola a m’mbali mwa mapili a Mulanje m’cigawo ca kum’mwela, mpaka m’madela a m’mbali mwa Nyanja ya Malawi imene ili kum’maŵa kwa dzikoli. Tinaona ciŵelengelo ca ofalitsa ndi ca mipingo cikukwela kwambili m’madela amene tinali kutumikila.
Mu 1962, tinasangalala ndi Msonkhano Wacigawo wakuti, “Atumiki Olimba Mtima.” Timaona kuti msonkhanowo unali wofunika kwa tonsefe m’Malawi cifukwa unatikonzekeletsa zimene zinali kudzacitika mtsogolo. Caka cotsatila, m’bale Henschel anabwelanso ku Malawi kudzacititsa msonkhano wacigawo wapadela umene unacitikila kunja kwa mzinda wa Blantyre, ndipo anthu 10,000 anapezekapo. Msonkhanowo unatilimbikitsa kwambili ndi kutithandiza kupilila ziyeso zimene zinali kubwela mtsogolo.
NTHAWI YA MAVUTO IYAMBA
Nchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa, ndipo boma linalanda ofesi ya nthambi
Mu 1964 Mboni zinazunzidwa koopsa cifukwa cokana kutengako mbali m’ndale. Nyumba za Ufumu zoposa 100 ndi nyumba za Mboni za Yehova zoposa 1,000 zinaonongedwa panthawiyo. Ngakhale zinali conco, tinapitilizabe kuyendela mipingo mpaka mu 1967 pamene boma la Malawi linaletsa cipembedzo ca Mboni za Yehova. Ofesi ya nthambi imene inali ku Blantyre inalandidwa, ndipo amishonale anapitikitsidwa komanso Mboni za kumeneko, kuphatikizapo ine ndi Lidasi, tinaikidwa m’ndende. Titamasulidwa, tinapitiliza kuyendela mipingo mwakabisila.
Tsiku lina mu October 1972, mamembala 100 a m’gulu linalake la ndale (Malawi Youth League) anakonza zobwela kunyumba kwathu. Koma m’modzi wa mamembala a gululo anathamanga n’kundiuza kuti ndibisale cifukwa gululo linali ndi colinga cakuti lindiphe. Conco ndinauza mkazi wanga ndi ana anga kuti abisale munthoci zimene zinali pafupi. Ndiyeno ine ndinathawa ndi kukwela mumtengo waukulu wa mango. Ndili mu mtengowo ndinaona nyumba yathu ndi katundu wathu zikuonongedwa.
Cifukwa cakuti abale athu sanatengeko mbali m’ndale, nyumba zao zinatenthedwa
Cizunzo citafika pacimake m’dziko la Malawi, ife ndi Mboni zina masauzande ambili tinathawa m’dzikoli. Ine ndi banja langa tinakakhala m’kampu ya othawa kwao imene inali kumadzulo kwa dziko la Mozambique mpaka kufika mu June 1974. Panthawiyo, ine ndi Lidasi tinapemphedwa kukatumikila monga apainiya apadela ku Dómue, dela limene lili ku Mozambique pafupi ndi dziko la Malawi. Tinapitiliza kucita utumiki umenewo mpaka mu 1975, pamene dziko la Mozambique linakhala ndi ufulu wodzilamulila kucokela ku dziko la Portugal. Ndiyeno, ife ndi Mboni zina tinakakamizidwa kubwelelanso ku Malawi kumene anali kutizunza.
Titabwelela ku Malawi, ndinauzidwa kuti ndikacezele mipingo mumzinda wa Lilongwe, umene ndi likulu la dzikoli. Ngakhale kuti kunali cizunzo ndi mavuto ena, mipingo inaonjezeka m’madela amene tinali kutumikila.
YEHOVA ANATITHANDIZA
Nthawi ina, mosadziwa tinafika pa mudzi wina ndipo tinapeza kuti akucita msonkhano wandale. Anthu ena ocilikiza cipani anazindikila kuti tinali a Mboni za Yehova, ndipo anatiuza kuti tikhale pakati pa gulu landale la acinyamata (Malawi Young Pioneers). Tinapemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima kuti atithandize ndi kutiteteza panthawi yovutayi. Koma msonkhano utatha, io anayamba kutimenya. Ndiyeno mai wina wacikulile anabwela akuthamanga uku akulila, n’kumanena kuti: “Conde alekeni. Munthu uyu ndi mwana wa m’bale wanga. Mulekeni apite!” Ndiyeno woyang’anila msonkhanowo anati: “Alekeni apite!” Sitikudziŵa cifukwa cimene mayiyo anacitila zimenezo cifukwa sanali wacibale wathu. Timaona kuti Yehova anamva pemphelo lathu.
Khadi la cipani
Mu 1981, tinakumananso ndi gulu lina landale la acinyamata. Iwo anatilanda njinga, katundu, makatoni a mabuku ndi mafaelo a dela. Ife tinathaŵila ku nyumba ya mkulu. Tinapemphelanso kuti Yehova atithandize. Atatitengela mafaelo, tinada nkhaŵa cifukwa munali makalata ambili ofunika. Pamene acinyamatawo anaona m’mafaelowo, anapezamo makalata ambili amene abale m’madela osiyanasiyana m’dziko lonse la Malawi anandilembela. Zimenezi zinaŵacititsa mantha cifukwa anaganiza kuti ndine mmodzi wa akuluakulu a boma. Conco, mwamsanga anabweza zonse kwa akulu a m’delalo monga mmene anazipezela.
Pa nthawi ina, tinali kuoloka mtsinje pa bwato. Mwiniwake bwatolo anali cheyamani wacipani m’delalo. Motelo anaganiza zofufuza kuti aone ngati aliyense m’bwatolo anali ndi khadi la cipani. Atatsala pang’ono kufika pamene panali ife, anazindikila mbala imene akuluakulu a boma anali kuifunafuna. Zimenezi zinacititsa msokonezo ndipo analeka kufufuza makadiwo. Apanso tinaona kuti Yehova anatithandiza mwacikondi.
NDINAGWIDWA NDI KUIKIDWA M’NDENDE
Mu February, 1984, ndili pa ulendo wopita ku Lilongwe kuti ndikasiye malipoti opita ku ofesi ya nthambi ya ku Zambia, wapolisi anandiimitsa n’kuyamba kufufuza m’cola canga. Iye anapezamo mabuku ofotokoza Baibulo. Conco ananditenga ndi kupita nane ku polisi ndipo anayamba kundimenya. Ndiyeno anandimanga ndi zingwe n’kundiika m’nyumba imene munali akaidi amene anagwidwa cifukwa ca kuba.
Tsiku lotsatila, mkulu wa apolisi ananditenga ndi kupita nane ku cipinda cina, kumene analemba cikalata cimene cinali ndi mau akuti: “Ine Trophim R. Nsomba, ndasiya kukhala wa Mboni za Yehova ndi colinga cakuti ndimasulidwe.” Koma ndinamuuza kuti: “Ndine wokonzeka kufa, osati kumangidwa cabe. Sindingaleke kukhala Mboni ya Yehova.” Conco, ndinakana kusaina cikalataco. Zimenezo zinakwiitsa kwambili mkulu wa apolisiyo cakuti anamenya pa desiki mwamphamvu mpaka wapolisi wina amene anali m’cipinda cina anathamanga kuti adzaone zimene zinacitika. Mkulu wa apolisiyo anamuuza kuti: “Munthu uyu akukana kusaina kuti waleka kukhala wa Mboni. Conco, mulekeni asaine apa kuti ndi wa Mboni za Yehova, ndipo timutumiza ku Lilongwe kuti akamumange.” Nthawi yonseyi, mkazi wanga anali ndi nkhawa cifukwa sanali kudziŵa kumene ndinali. Patapita masiku anai, abale ena anamuuza kumene ndinali.
Ku polisi ya ku Lilongwe anandicitila zinthu mokoma mtima. Mkulu wa apolisi anati: “Ane mpunga uwu popeza wamangidwa cifukwa ca Mau a Mulungu. Koma enawa anamangidwa cifukwa ca kuba.” Ndiyeno ananditumiza ku ndende ya Kachere kumene ndinakhalako miyezi isanu.
Woyang’anila ndende wa kumeneko anakondwela kuona kuti ndabwela, ndipo anafuna kuti ndikhale “mbusa” pandendepo. Iye anacotsa mbusa amene anali pa udindowo ndi kumuuza kuti: “Sindifunanso kuti uziphunzitsa Mau a Mulungu muno popeza unamangidwa cifukwa ca kuba za m’chalichi!” Conco ndinapatsidwa udindo wophunzitsa Baibulo mlungu uliwonse pa misonkhano imene inakonzedwela akaidi.
Patapita nthawi, zinthu zinafika poipa kwambili. Akuluakulu a ndende anandilamula kuti ndiwauze ciŵelengelo ca Mboni m’Malawi. Koma cifukwa cakuti sindinawauze zimene anali kufuna, anayamba kundimenya mpaka ndinakomoka. Nthawi ina, io anandiuza kuti ndiwafotokozele kumene kuli likulu lathu. Ndinayankha kuti, “Mwafunsa funso losavuta, ndipo ndikuuzani.” Apolisiwo anakondwela kumva zimenezo cakuti anachela tepi kuti ajambule mau anga. Ndinawauza kuti likulu la Mboni za Yehova limachulidwa m’Baibulo. Iwo anadabwa kwambili, ndipo anandifunsa kuti, “Ndi pati makamaka m’Baibulo?”
Ndinawayankha kuti: “Pa Yesaya 43:12.” Iwo anafunafuna lembalo ndi kuliŵelenga mosamala kwambili. Lembali limati: “‘Inu ndinu Mboni zanga’ akutelo Yehova ‘ndipo ine ndine Mulungu wanu.’” Anaŵelenga lembali katatu. Kenako anandifunsa kuti: “Iwe, likulu la Mboni za Yehova lingakhale bwanji m’Baibulo osati ku America?” Ndinaŵayankha kuti: “Mboni za Yehova za ku America nazonso zikaŵelenga lembali zimadziŵa kuti likuchula likulu lao.” Popeza kuti sindinawauze zimene anali kufuna, ananditumiza ku ndende ya Dzaleka, kumpoto kwa mzinda wa Lilongwe.
TINADALITSIDWA NGAKHALE PANTHAWI YOVUTA
Mu July 1984, ndinatumizidwa ku ndende ya Dzaleka kumene kunali Mboni zina 81. Kumeneko tinaliko akaidi 300, ndipo tinali kugona mopanikizana kwambili. M’kupita kwa nthawi, ife Mboni tinagaŵana m’tumagulu kuti tsiku lililonse tizikambilana lemba limene wina waganizila. Kucita izi kunali kutilimbikitsa kwambili.
Conco woyang’anila ndende anatipatula kwa akaidi ena. Mwakabisila, mlonda wa ndendeyo anatiuza kuti: “Sikuti boma limakuzondani. Komabe tikukusungani m’ndende pa zifukwa ziŵili izi: Coyamba, boma likufuna kukutetezani kwa anyamata andale kuti angakupheni. Caciŵili, popeza kuti mumalalikila kuti kudzabwela nkhondo, boma likuopa kuti asilikali adzathawa cifukwa ca nkhondoyo.”
Abale akuwatenga pambuyo poimbidwa mlandu
Mu October 1984, tonse tinakaonekela m’bwalo la milandu. Ndipo tonse tinaweluzidwa kuti tikhale m’ndende zaka ziŵili. Kundendeko anatiikanso pamodzi ndi akaidi ena amene sanali a Mboni. Koma woyang’anila ndende analengeza kuti: “A Mboni za Yehova sakoka fodya. Conco, inu alonda musaŵavutitse mwa kuŵapempha fodya kapena kuŵatuma kuti akakutengeleni nkhuni yamoto kuti muyatsile fodya. Iwo ndi anthu a Mulungu! Mboni za Yehova zonse ziyenela kupatsidwa cakudya kaŵili pa tsiku, popeza kuti io sanalakwe koma ali kuno cifukwa ca zikhulupililo zao zocokela m’Baibulo.”
Tinapindulanso cifukwa ca khalidwe lathu labwino m’njila zina. Kukada kapena ngati kukugwa mvula, akaidi sanali kuloledwa kuyendayenda. Koma ife tinali kuloledwa kucoka ndi kupita kulikonse kumene tafuna. Iwo anali kudziŵa kuti sitingathawe. Tsiku lina mlonda amene anali kutiyang’anila m’munda umene tinali kulima anadwala, ndipo tinamunyamula ndi kubwelela naye kundende kuti akalandile thandizo. Oyang’anila ndende anadziŵa kuti tinali okhulupilika. Cifukwa ca khalidwe lathu labwino, tinadalitsidwa kuona anthu amene anatigwila akulemekeza dzina la Yehova.—1 Pet. 2:12.b
TSOPANO TILINSO M’NTHAWI YABWINO
Pa May 11, mu 1985, ndinamasulidwa ku ndende ya Dzaleka. Ndinasangalala kwambili kugwilizananso ndi banja langa. Timayamikila Yehova cifukwa cotithandiza kukhalabe okhulupilika panthawi yovuta kwambili imeneyo. Tikaganizila nthawiyo, timamva ngati mmene mtumwi Paulo anamvela pamene analemba kuti: “Abale sitikufuna kuti mukhale osadziŵa za masautso amene tinakumana nao . . . Tinalibenso ciyembekezo coti tikhala ndi moyo. Ngakhalenso m’mitima yathu tinali kumva ngati talandila ciweluzo ca imfa. Zinatelo kuti tisakhale ndi cikhulupililo mwa ife tokha, koma mwa Mulungu amene amaukitsa akufa. Iye anatipulumutsadi ku cinthu coopsa, ndico imfa.”—2 Akor. 1:8-10.
M’bale Nsomba ndi akazi ao a Lidasi ali kutsogolo kwa Nyumba ya Ufumu mu 2004
Kunena zoona, nthawi zina zinali kuoneka ngati tiphedwa. Koma nthawi zonse tinali kupempha Yehova kuti atilimbitse ndi kutipatsa nzelu zotithandiza kukhala odzicepetsa n’colinga cakuti zocita zathu zipeleke ulemelelo ku dzina lake lalikulu.
Yehova watidalitsa pogwila nchito yake m’nthawi zovuta ndi m’nthawi zabwino. Tsopano, timakondwela kwambili tikaona ofesi ya nthambi ku Lilongwe imene inamalizidwa m’caka ca 2000 ndiponso Nyumba za Ufumu zatsopano zoposa 1,000 zimene zamangidwa m’dziko lonse la Malawi. Madalitso ocokela kwa Yehova amenewa amatilimbikitsa kwambili mwa kuuzimu, ndipo ine ndi Lidasi timaona ngati ndi maloto cabe.c
a Masiku ano, abale amene ali ndi ana aang’ono panyumba saikidwa kukhala woyang’anila dela.
b Kuti mumve zambili zokhudza cizunzo ca ku Malawi, onani Buku Lapacaka la Mboni za Yehova la mu 1999, patsamba 171 mpaka 223.
c Pamene nkhaniyi inali kukonzedwa kuti ifalitsidwe, M’bale Nsomba anamwalila ali ndi zaka 83.