Zamkati
May 15, 2015
© 2015 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
YOPHUNZILA
JUNE 29, 2015–JULY 5, 2015
Khalani Maso! Satana Akufuna Kukumezani
TSAMBA 9 • NYIMBO: 54, 43
JULY 6-12, 2015
Mungapambane Polimbana Ndi Satana
TSAMBA 14 • NYIMBO: 60, 100
JULY 13-19, 2015
TSAMBA 19 • NYIMBO: 81, 134
JULY 20-26, 2015
Muzitsanzila Mulungu Amene Watilonjeza Moyo Wosatha
TSAMBA 24 • NYIMBO: 12, 69
NKHANI ZOPHUNZILA
▪ Khalani Maso! Satana Akufuna Kukumezani
▪ Mungapambane Polimbana Ndi Satana
Baibulo limayelekezela Satana ndi mkango wobangula umene ukuŵendelela nyama. Iye ndi wamphamvu, wankhanza, ndi wacinyengo. Nkhani ziŵilizi zidzatithandiza kuona cifukwa cake tifunika kulimbana ndi mdani wathu wamkulu ameneyu. Zidzatithandizanso kudziŵa mmene tingadzitetezele ku njila zake zacinyengo.
▪ ‘Anaona’ Malonjezo a Mulungu
▪ Muzitsanzila Mulungu Amene Watilonjeza Moyo Wosatha
Mphamvu imene tili nayo yotha kuganizila zinthu zimene sitinazionepo tingaigwilitsile nchito mwanzelu kapena molakwika. M’nkhani ziŵilizi, tidzakambilana zitsanzo za m’Baibulo zimene zingatithandize pankhaniyi. Tidzaphunzila mmene mphamvu yotha kuganizila zinthu zimene sitinazionepo ingatithandizile kukhala ndi cikhulupililo colimba, ndi kutsanzila makhalidwe a Yehova monga cikondi, kukoma mtima, nzelu, ndi cimwemwe.
NKHANI ZINA M’MAGAZINI INO
3 Kukumbukila Cikondi Canga ca Poyamba Kwandithandiza Kupilila
PACIKUTO: Abale aŵili akucititsa phunzilo la Baibulo
KU ARMENIA
KULI ANTHU
3,026,900
OFALITSA
11,143
APAINIYA ANTHAWI ZONSE:
2,205
23,844
Anthu amene anapezeka pa Cikumbutso ku Armenia pa April 14, 2014 anali oculuka kuwilikiza kaŵili poyelekezela ndi ciŵelengelo ca ofalitsa a m’dzikolo