Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi
Kodi Gogi wa Magogi wochulidwa m’buku la Ezekieli ndani?
Kwa zaka zambili, zofalitsa zathu zakhala zikufotokoza kuti Gogi wa Magogi ndi dzina limene Satana Mdyelekezi anapatsidwa kucokela pamene anacotsedwa kumwamba. Tinali kukhulupilila zimenezi cifukwa buku la Chivumbulutso limanena kuti Satana Mdyelekezi adzatsogolela anthu amene adzaukila anthu a Mulungu. (Chiv. 12:1-17) Conco, tinali kukhulupilila kuti Gogi ndi dzina lina laulosi la Satana.
Koma mfundo imeneyi inabutsa mafunso angapo. N’cifukwa ciani? Ganizilani izi: Ponena za nthawi imene Gogi adzagonjetsedwa, Yehova anakamba za iye kuti: “Ndidzakupelekani kwa mbalame zodya nyama, mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakuchile kuti mukhale cakudya cao.” (Ezek. 39:4) Ndiyeno Yehova anati: “Pa tsiku limenelo Gogi ndidzam’patsa malo kuti akhale manda ake mu Isiraeli. . . Kumeneko io adzaika m’manda Gogi pamodzi ndi khamu lake lonse.” (Ezek. 39:11) Koma kodi colengedwa cauzimu cingadyedwe ndi “mbalame zodya nyama, mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakuchile”? Nanga Satana angapatsidwe bwanji “malo kuti akhale manda” ake padziko lapansi? Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti Satana adzatsekeledwa kuphompho kwa zaka 1,000, osati kudyedwa kapena kuikidwa m’manda.—Chiv. 20:1, 2.
Baibulo limanenanso kuti zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa kuphompho, ndipo “adzatuluka kukasoceletsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi, ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kunkhondo.” (Chiv. 20:8) Koma kodi Satana angasoceletse bwanji Gogi ngati iyeyo ndiye Gogi? Motelo, “Gogi” wochulidwa mu ulosi wa Ezekieli kapena m’buku la Chivumbulutso, si Satana.
Nanga Gogi wa Magogi ndani? Kuti tiyankhe, tiyenela kufufuza Malemba kuti tidziŵe amene adzaukila anthu a Mulungu. Baibulo silinena cabe za kuukila kwa ‘Gogi wa Magogi,’ koma limanenanso za kuukila kwa “mfumu ya kumpoto” ndi kuukila kwa “mafumu a dziko lapansi.” (Ezek. 38:2, 10-13; Dan. 11:40, 44, 45; Rev. 17:14; 19:19) Kodi kuukila kumeneku ndi kosiyana? Iyai. Mosakaikila Baibulo limagwilitsila nchito maina osiyana ponena za kuukila kumodzi. N’cifukwa ciani tikunena telo? Cifukwa cakuti Malemba amanena kuti mitundu yonse ya padziko lapansi, idzatengamo mbali pa kuukila komaliza kumene kudzayambitsa nkhondo ya Aramagedo.—Chiv. 16:14, 16.
Tikaganizila Malemba onsewa okamba za kuukilidwa komaliza kwa anthu a Mulungu, timatha kuona kuti Gogi wa Magogi si Satana, koma ndi mgwilizano wa mitundu. Kodi mitunduyo idzatsogoleledwa ndi “mfumu ya kumpoto” yophiphilitsa? Sitinganene motsimikiza. Koma zimenezi n’zogwilizana ndi mau amene Yehova anakamba ponena za Gogi. Iye anati: “Udzabwela kucokela kumalo ako, kumadela akutali a kumpoto. Udzabwela ndi mitundu yambili ya anthu. Anthuwo adzakhala khamu lalikulu, adzakhala cigulu cacikulu cankhondo. Onsewo adzabwela atakwela pamahachi.”—Ezek. 38:6, 15.
Komanso mneneli Danieli, amene anakhalapo panthawi imodzi ndi Ezekieli, anakamba mau awa ponena za mfumu ya kumpoto: “Kotulukila dzuŵa ndi kumpoto kudzacokela mauthenga amene adzaisokoneza. Pamenepo iyo idzapita ndi ukali waukulu kuti ikafafanize ndi kuwononga ambili. Ndipo idzamanga mahema okhala ngati nyumba yacifumu pakati pa nyanja yaikulu ndi phili lopatulika la Dziko Lokongola. Ndiyeno iyo idzafika kumapeto a moyo wake ndipo sipadzapezeka woithandiza.” (Dan. 11:44, 45) Zimenezi zimagwilizana ndi zimene buku la Ezekieli limanena zokhudza Gogi.—Ezek. 38:8-12, 16.
N’ciani cidzacitika cifukwa ca kuukila kwa Gogi? Danieli anati: “Pa nthawi imeneyo Mikayeli [Yesu Kristu], kalonga wamkulu amene waimilila [kuyambila mu 1914] kuti athandize anthu a mtundu wako, adzaimilila [pa Aramagedo]. Ndiyeno padzafika nthawi ya masautso [cisautso cacikulu] imene sinakhalepo kuyambila pamene mtundu woyambilila wa anthu unakhalapo kufikila nthawi imeneyo. Pa nthawi imeneyo aliyense mwa anthu a mtundu wako amene dzina lake lidzakhala litalembedwa m’buku adzapulumuka.” (Dan. 12:1) Zimenezi ndi zimene Yesu adzacita moimilako Mulungu, ndipo zimafotokozedwanso pa Chivumbulutso 19:11-21.
Nanga “Gogi ndi Magogi” wochulidwa pa Chivumbulutso 20:8 ndani? Pa ciyeso comaliza kumapeto kwa za 1,000, anthu ena adzapandukila Yehova. Iwo adzaonetsa mtima woipa ngati wa ‘Gogi wa Magogi,’ amene ndi mitundu ya anthu imene idzaukila anthu a Mulungu kumapeto kwa cisautso cacikulu. Cilango cimene magulu onse aŵiliwa adzalandila cidzakhala cofanana. Iwo adzaonongedwa kothelatu. (Chiv. 19:20, 21; 20:9) Conco, n’zosadabwitsa kuti anthu onse amene adzapandukila Mulungu pambuyo pa Ulamulilo wa Zaka 1,000 amachedwa “Gogi ndi Magogi.”
Monga ophunzila Baibulo akhama, timayembekezela mwacidwi kudzaona amene adzakhala “mfumu ya kumpoto” posacedwapa. Sitikudziŵa amene adzatsogolela mitundu ya anthu poukila anthu a Mulungu, koma ndife otsimikiza kuti (1) Gogi wa Magogi ndi asilikali ake adzagonjetsedwa ndi kuonongedwa, ndipo (2) Mfumu yathu, Yesu Kristu, idzapulumutsa anthu a Mulungu ndi kuwaloŵetsa m’dziko latsopano mmene mudzakhala mtendele ndi citetezo ceniceni.—Chiv. 7:14-17.