LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp16 na. 4 masa. 14-15
  • Kuyelekezela Zinthu Kopindulitsa Kwambili

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kuyelekezela Zinthu Kopindulitsa Kwambili
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MMENE MUNGAYELEKEZELE ZIMENE MUMAKHULUPILILA NDI ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Ufumu Wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
wp16 na. 4 masa. 14-15

Kuyelekezela Zinthu Kopindulitsa Kwambili

KODI ndinu Mkhiristu? Ngati n’conco, ndinu mmodzi mwa anthu oposa 2 biliyoni pa dziko lapansi amene amakamba kuti ndi Akhiristu. Ciŵelengelo cimeneci cionetsa kuti pafupifupi munthu mmodzi pa atatu aliwonse amakamba kuti ndi otsatila a Khiristu. Masiku ano, pali machechi ambili amene amati ndi Acikhiristu. Koma machechi amenewa ni ogaŵikana kaamba ka kusiyana pa zimene amakhulupilila, ndi mmene amaonela zinthu. Conco, zimene mumakhulupilila zingakhale zosiyana kwambili ndi za anthu ena amene amati ni Akhiristu. Kodi zimene inu mumakhulupilila n’zofunika kwenikweni? Inde, malinga ngati mufuna kucita zimene Baibulo imaphunzitsa.

Otsatila oyambilila a Yesu Khiristu, anali kudziŵika ndi dzina lakuti “Akhiristu.” (Machitidwe 11:26) Iwo sanali kufunikila dzina lina lapadela cifukwa Akhiristu onse anali ndi cikhulupililo cimodzi. Akhiristu onse anali kutsatila zimene Yesu Khiristu, Woyambitsa Cikhiristu, anali kuphunzitsa. Nanga bwanji chechi yanu? Kodi mukhulupilila kuti zimene imaphunzitsa n’zimene Khiristu anali kuphunzitsa, ndiponso n’zimene otsatila ake oyambilila anali kukhulupilila? Kodi mungadziŵe bwanji kuti n’zoona? Njila yokha imene mungadziŵile, ndi kuseŵenzetsa Baibulo.

Dziŵani izi: Yesu Khiristu anali kulemekeza kwambili Malemba. Anali kuwaona kuti ni Mawu a Mulungu. Sanali kukondwela ndi anthu amene anali kupeputsa zimene Baibulo imaphunzitsa mwa kulemekeza miyambo ya anthu. (Maliko 7:9-13) Conco, tingakambe motsimikiza kuti otsatila oona a Yesu akhulupilila zimene Baibulo imakamba. Cotelo, Mkhiristu aliyense ayenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene chechi yanga imaphunzitsa zigwilizana ndi zimene Baibulo imakamba?’ Kuti mupeze yankho, muyenela kuyelekezela zimene chechi yanu imaphunzitsa ndi zimene Baibulo imakamba.

Yesu anakamba kuti tiyenela kulambila Mulungu m’coonadi. Coonadi cimeneci cipezeka m’Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17) Ndipo mtumwi Paulo anakamba kuti ngati tifuna kukapulumuka tiyenela ‘kudziŵa coonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Motelo, zimene timakhulupilila zifunika kukhala zogwilizana ndi coonadi ca m’Baibulo. N’cifukwa ciani? Cifukwa ngati munthu sakhulupilila zimene Baibulo imaphunzitsa sangapulumuke.

MMENE MUNGAYELEKEZELE ZIMENE MUMAKHULUPILILA NDI ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

Tikupemphani kuŵelenga mafunso 6 amene ali m’nkhani ino, n’kuona mmene Baibulo iyankhila mafunso amenewa. Onani mau ocokela m’Baibulo, ndi kuganizila mayankho amene apelekedwa. Ndiyeno, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimene chechi yanga imaphunzitsa zigwilizana ndi zimene Baibulo ikamba?’

Mafunso aŵa ndi mayankho ake angakuthandizeni kuyelekezela zimene mumaphunzila ku chechi kwanu na zimene Baibulo imaphunzitsa. Kucita izi n’kofunika kwambili. Kodi mungakonde kudziŵa zinthu zina zimene Baibulo imakamba ndi kuziyelekezela na zimene mumaphunzila kuchechi kwanu? A Mboni za Yehova angakuthandizeni kudziŵa bwino coonadi ca m’Baibulo. Mungapemphe wa Mboni kuti aziphunzila nanu Baibulo kwaulele. Mungapitenso pa webusaiti yathu ya, jw.org.

1 FUNSO: Kodi Mulungu n’ndani?

YANKHO: Yehova, Atate wa Yesu, ni Mulungu wosatha, Wamphamvuyonse, ndipo ni Mlengi wa zinthu zonse.

ZIMENE BAIBULO IKAMBA:

“Nthawi zonse tikamakupemphelelani, timayamika Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khiristu.”—Akolose 1:3.

“Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse.”—Chivumbulutso 4:11.

Mungaonenso Aroma 10:13; ndi 1 Timoteyo 1:17.

2 FUNSO: Kodi Yesu n’ndani?

YANKHO: Yesu ni Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu. Yesu anacita kulengedwa. Conco, ali na ciyambi. Yesu amamvela Mulungu ndi kucita cifunilo Cake.

ZIMENE BAIBULO IKAMBA:

“Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yohane 14:28.

“[Yesu] ndiye cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo, woyamba kubadwa wa cilengedwe conse.”—Akolose 1:15.

Mungaonenso Mateyu 26:39; ndi 1 Akorinto 15:28.

3 FUNSO: Kodi mzimu woyela n’ciani?

YANKHO: Mzimu woyela ni mphamvu imene Mulungu amaseŵenzetsa pokwanilitsa cifunilo cake. Mzimu woyela si munthu. Anthu angadzazidwe ndi mzimu woyela, ndipo ungawapatse mphamvu.

ZIMENE BAIBULO IKAMBA:

“Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali m’mimba mwakemo linadumpha. Ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyela.”—Luka 1:41.

“Mzimu woyela ukadzafika pa inu, mudzalandila mphamvu.”—Machitidwe 1:8.

Mungaonenso Genesis 1:2; ndi Machitidwe 2:1-4; 10:38.

4 FUNSO: Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani?

YANKHO: Ufumu wa Mulungu ni boma lakumwamba. Mfumu yake ni Yesu. Posacedwa Ufumu umenewu udzapangitsa cifunilo ca Mulungu kucitika pa dziko lonse.

ZIMENE BAIBULO IKAMBA:

“Mngelo wa 7 analiza lipenga lake. Ndipo kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: ‘Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khiristu wake. Iye adzalamulila monga mfumu kwamuyaya.’”—Chivumbulutso 11:15.

Mungaonenso Danieli 2:44; ndi Mateyu 6:9, 10.

5 FUNSO: Kodi anthu onse abwino amapita kumwamba?

YANKHO: Iyai. Kagulu kocepa ka anthu okhulupilika kocedwa “kagulu ka nkhosa” n’kamene kanasankhidwa ndi Mulungu kuti kapite kumwamba. Iwo pamodzi na Yesu adzalamulila anthu monga mafumu.

ZIMENE BAIBULO IKAMBA:

“Musaope, kagulu ka nkhosa inu, cifukwa Atate wanu wavomeleza kukupatsani ufumu.”—Luka 12:32.

“Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khiristu, ndipo adzalamulila monga mafumu limodzi naye.”—Chivumbulutso 20:6.

Mungaonenso Chivumbulutso 14:1, 3.

6 FUNSO: Kodi colinga ca Mulungu kwa anthu ndi dziko lapansi n’ciani?

YANKHO: Ufumu wa Mulungu ukayamba kulamulila, dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Ndipo anthu okhulupilika adzakhala ndi thanzi labwino. Adzakhala pa mtendele ndi kukhala ndi moyo wosatha.

ZIMENE BAIBULO IKAMBA:

“Ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.

“Adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21: 3, 4.

Mungaonenso Salimo 37:29; ndi 2 Petulo 3:13.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani