Zamkati
3 Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Ghana
MLUNGU WA AUGUST 29–SEPTEMBER 4, 2016
7 Muzifuna-funa Ufumu, Osati Zinthu Zakuthupi
Yesu anatiphunzitsa kuti ‘tizifuna-funa Ufumu coyamba’ osati zinthu zakuthupi. Kodi tingapewe bwanji msampha wokonda zinthu zakuthupi? Nanga tingacepetse bwanji zocita zathu mu umoyo kuti tiike zinthu zauzimu patsogolo? M’nkhani ino, tikambilana mau olimbikitsa a Yesu amene anakamba pa Ulaliki wake wa pa Phili wolembedwa pa Mateyu 6:25-34.
MLUNGU WA SEPTEMBER 5-11, 2016
13 N’cifukwa Ciani Tiyenela ‘Kukhalabe Maso’?
Popeza ndife Akhiristu, sitifunika kupepusa malangizo a Yesu akuti ‘tikhalebe maso’ m’masiku ano otsiliza. (Mat. 24:42) Kuti ticite zimenezi, tiyenela kupewa zinthu zimene zingatilepheletse kukhala maso kuti tisazindikile kubwela kwa Yesu. Nkhaniyi ifotokoza mmene tingapewele zinthu zimene zingatilepheletse kukhala maso.
18 “Usacite Mantha. Ndikuthandiza”
MLUNGU WA SEPTEMBER 12-18, 2016
21 Tiziyamikila Kukoma Mtima Kwakukulu Kumene Tinalandila
MLUNGU WA SEPTEMBER 19-25, 2016
26 Lalikilani Uthenga Wabwino Wokamba za Kukoma Mtima
Nkhani ziŵilizi zifotokoza mmene timapindulila ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova. Zifotokozanso cifukwa cake kuyamikila cikondi cimene Mulungu wationetsa m’njila zosiyana-siyana, kuyenela kutilimbikitsa kuuzako ena mmene angapindulile ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova.