Zamkati
3 Mau Amene Anali Atanthauzo Kwambili
MLUNGU WA DECEMBER 26, 2016–JANUARY 1, 2017
4 ‘Pitilizani Kulimbikitsana Tsiku na Tsiku’
Yehova Mulungu na Yesu Khiristu ni zitsanzo zabwino ngako pankhani yolimbikitsa ena. Nayenso mtumwi Paulo anaona kuti kulimbikitsa ena n’kofunika ngako. Kutengela citsanzo cawo kudzatithandiza kumakonda anthu ena na kuwalimbikitsa pa nyumba yathu na ku Nyumba ya Ufumu.
MLUNGU WA JANUARY 2-8, 2017
9 Gulu Lake Ladongosolo Monga mwa Buku la Mau Ake
MLUNGU WA JANUARY 9-15, 2017
14 Kodi Mumalemekeza Buku Lake la Yehova?
Nkhani izi zidzayankha mafunso aya: N’cifukwa ciani olambila Yehova ayenela kucita zinthu mwadongosolo? Tingakhale bwanji adongosolo molingana na Buku la Mau a Mulungu? Nanga tingaonetse bwanji kuti timacilikiza mokhulupilika gulu la Yehova?
MLUNGU WA JANUARY 16-22, 2017
MLUNGU WA JANUARY 23-29, 2017
26 Anamasuka Kucoka ku Cipembedzo Conama
Nkhanizi zidzafotokoza nthawi imene anthu a Mulungu analoŵa mu ukapolo wa m’Babulo Wamkulu, ndi khama limene Akhiristu odzozedwa anaonetsa cakumapeto kwa ma 1800 kuti amvetse Mau a Yehova molongosoka. Tidzaphunzilanso za kaimidwe kolimba kamene Ophunzila Baibo anatenga kulinga kwa Babulo Wamkulu. Tidzaonanso kuti n’liti pamene Akhiristu anamasuka mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu.