Yophunzila
DECEMBER 2016
NKHANI ZOPHUNZILA M’MLUNGU WA: JANUARY 30–FEBRUARY 26, 2017
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
PIKICA YA PACIKUTO:
KU PORTUGAL
Anthu ambili okaona malo amapita ku mzinda wa Aveiro, kumpoto kwa dziko la Portugal, kukaona maiŵe a mcele. Mboni za kumaloko zimatengela mwayi kulalikila uthenga wabwino kwa anthu ogulitsa mcele kumeneko
OFALITSA
48,840
MAPHUNZILO A BAIBO
28,687
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO (2015)
91,472
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika padziko lonse lapansi. Ndalama zoyendetsela nchitoyi ni zimene anthu amapeleka mwa kufuna kwawo.
Ngati mufuna kupeleka ndalama zothandizila nchitoyi, yendani pa www.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa ina. Komabe, ena mwa masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lakuti A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages