Zamkati
3 Mbili Yanga—Kukhala “Zinthu Zonse Kwa Anthu Osiyana-siyana”
MLUNGU WA JANUARY 30, 2017–FEBRUARY 5, 2017
8 Tinamasulidwa mwa Cisomo ca Mulungu
MLUNGU WA FEBRUARY 6-12, 2017
13 ‘Kuika Maganizo Athu pa Zinthu za Mzimu Kumabweletsa Moyo na Mtendele’
M’caputa 6 na 8 ca Aroma, muli malangizo ofunika okhudza umoyo wa ise Akhiristu. Kuphunzila malemba amenewo kudzatithandiza kupindula na cisomo ca Mulungu ndi kuikabe maganizo athu pa zinthu zimene zidzatipindulitsa kwamuyaya.
MLUNGU WA FEBRUARY 13-19, 2017
19 Tulilani Yehova Nkhawa Zanu Zonse
MLUNGU WA FEBRUARY 20-26, 2017
24 Yehova Amapeleka Mphoto kwa Anthu Omufuna-funa na Mtima Wonse
Nkhani yoyamba idzafotokoza mmene tingatulile Mulungu nkhawa zathu. Nkhani yaciŵili idzafotokoza mmene tingalimbitsile cikhulupililo cathu mwa kukhala otsimikiza na mtima wonse kuti Mulungu amadalitsa anthu amene amam’funa-funa na mtima wonse. Idzaonetsanso mmene tingapindulile na ciyembekezo codzalandila mphoto.