LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 1 tsa. 3
  • N’cifukwa Ciani Mufunika Kuŵelenga Baibo?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Mufunika Kuŵelenga Baibo?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Nkhani Zofanana
  • Zimene Mungacite Kuti Muzipindula Kwambili Poŵelenga Baibo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Mungayambe Bwanji Kuŵelenga Baibo?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 1 tsa. 3
Mkazi atenga Baibo pa shelufu

NKHANI YA PACIKUTO MUNGACITE CIANI KUTI MUPINDULE NA ZIMENE MUŴELENGA M’BAIBO?

N’cifukwa Ciani Mufunika Kuŵelenga Baibo?

“N’nali kuganiza kuti Baibo ni yovuta kumvetsetsa.”—Jovy

“N’nali kuona kuti Baibo si yosangalatsa kuŵelenga.”—Queennie

“N’taona kukula kwa Baibo, cilakolako cofuna kuiŵelenga cinasila.”—Ezekiel

Kodi munaganizapo zakuti muŵelenge Baibo, koma munagwa mphwayi cifukwa cokhala na maganizo olingana ndi a anthu amene tawachula pamwambapa? Anthu ambili amaona kuti kuŵelenga Baibo n’kolemetsa. Koma bwanji ngati mwadziŵa kuti Baibo ingakuthandizeni kukhala na umoyo wabwino ndi wacimwemwe? Komanso bwanji ngati mwapeza njila zina zimene zingakuthandizeni kuti muzisangalala poiŵelenga? Kodi mungakonde kuiŵelenga kuti muone mmene ingakuthandizileni?

Tiyeni tione zitsanzo za anthu amene anapeza mapindu ambili atayamba kuŵelenga Baibo.

Ezekiel, amene ali na zaka za m’ma 20 anati: “Kale, n’nali monga munthu amene ayendetsa motoka koma sadziŵa kumene ayenda. Koma kuŵelenga Baibo kwanithandiza kukhala na umoyo watanthauzo. M’Baibo muli malangizo othandiza kwambili amene ningaseŵenzetse tsiku lililonse.”

Frieda, amenenso ali na zaka za m’ma 20 anakamba kuti: “N’nali kukwiya msanga. Koma kaamba koŵelenga Baibo, naphunzila kukhala wodziletsa. Izi zanithandiza kukhala munthu wocezeka, ndipo tsopano nili na anzanga ambili.”

Mayi wina wa zaka za m’ma 50, dzina lake Eunice, anakamba kuti: “Baibo ikunithandiza kukhala munthu wabwino, ndiponso kusintha zizoloŵezi zanga zoipa.”

Malinga n’zimene anthu amenewo anakamba, kuphatikizapo ena mamiliyoni ambili, kuŵelenga Baibo kungakuthandizeni kukhala na umoyo wacimwemwe. (Yesaya 48:17, 18) Mwacitsanzo, Baibo ingakuthandizeni (1) kupanga zosankha mwanzelu, (2) kupeza anzanu eni-eni, (3) kucepetsa nkhawa, komanso (4) koposa zonse, kudziŵa zoona ponena za Mulungu. Malangizo amene ali m’Baibo ni ocokela kwa Mulungu ndipo mudzapindula ngati muwatsatila. Iye sapeleka malangizo oipa.

Conco, mungacite bwino kuyamba kuiŵelenga. N’ciani cingakuthandizeni kuti musavutike kuyamba kuŵelenga Baibo ndi kuti muzisangalala pamene muŵelenga?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani