Mau Oyamba
MUGANIZA BWANJI?
Kodi Baibo ni yothandiza masiku ano kapena si yothandiza? Baibo imayankha yokha kuti: “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16, 17.
Nsanja ya Mlonda iyi ifotokoza ena mwa malangizo othandiza opezeka m’Baibo, ndipo ikambanso zimene mungacite kuti mupindule na zimene mumaŵelenga m’Baibo.