Mau Oyamba
Kodi n’zotheka kukhala ndi banja lacimwemwe m’nthawi ino yovuta pamene cikwati ndi banja zili m’mavuto? Nanga n’zotheka kuti banja likhale lacimwemwe? Imeneyi si nkhani ya maseŵela? Koma thandizo lilipo. Ngakhale kuti kabuku kano sikodzala ndi malangizo a cikwati, kali ndi mfundo ndi malangizo othandiza a m’Baibulo. Ngati muwagwilitsila nchito bwino malangizo amenewa angathandize kuti banja lanu likhale lacimwemwe.