Kutenga anthu ukapolo mu Africa na kupita nawo ku America anali malonda opindulitsa
Kumasuka mu Ukapolo Kale na Masiku Ano
Blessinga anafika ku Europe ali na ciyembekezo coloŵa nchito yokonza tsitsi. Koma pambuyo pomenyedwa kwa masiku 10, komanso cifukwa comuwopseza kuti adzacitila zaciwawa banja lake kudziko limene anacokela, anam’kakamiza kuyamba uhule.
Pikica yoonetsa anthu ogwidwa ukapolo ku Iguputo wakale
Pa usiku umodzi, Blessing anafunika kupanga ndalama pafupi-fupi madola 200 mpaka 300 a ku America. Ndalamazo zinali zakuti alipile nkhongole imene abwana ake aakazi anamuikila, yokwana madola pafupi-fupi 40,000. Blessing anati: “Nthawi zambili n’nali kuganiza zothaŵa, koma n’nali kuopa zimene adzacitila banja lathu. N’nali mu ukapolo.” Blessing ni mmodzi mwa anthu 4 miliyoni amene analoŵapo mu ukapolo wocita malonda a uhule a padziko lonse.
Zaka pafupi-fupi 4,000 zapitazo, wacicepele Yosefe anagulutsidwa ndi abale ake. Iye anapezeka kuti akutumikila monga kapolo m’nyumba ya munthu wochuka waciiguputo. Mosiyana ndi Blessing, poyamba Yosefe sanacitilidwe nkhanza. Koma atakana kugona ndi mkazi wa abwana ake, iye anapatsidwa mlandu wabodza wakuti anafuna kugwilila mkazi wa abwana ake. Anamuika m’ndende na kum’manga maunyolo.—Genesis 39:1-20; Salimo 105:17, 18.
Yosefe anali kapolo wa m’nthawi yakale kwambili, koma Blessing anali kapolo wa m’zaka za m’ma 2000 zino. Onse anakhudzidwa ndi mwambo wakale kwambili wa kuba anthu, n’colinga cakuti awacite malonda ndi kupezelapo ndalama basi.
NKHONDO INAPANGITSA UKAPOLO KUKHALA MALONDA AAKULU
Maiko ambili anaona kuti nkhondo zinali kuthandiza kupeza akapolo m’njila yosavuta. Mfumu yaciiguputo dzina lake Thutmose Wacitatu, akuti inagwila akaidi 90,000 pambuyo pomenya nkhondo ku Kanani. Aiguputo anapanga anthuwo kukhala akapolo okumba migodi, kumanga akacisi, na kukumba mifolo ya madzi.
Mu Ufumu wa Roma, nkhondo zinacititsa kuti akhale na akapolo ambili. Nthawi zina, akapolo akacepa, anali kupita kukamenya nkhondo. Zikuoneka kuti podzafika ca m’ma 30 B.C.E., pafupi-fupi hafu ya anthu okhala m’dziko la Roma anali akapolo. Akapolo ambili a ku Iguputo ndi ku Roma anali kucitilidwa nkhanza kwambili. Mwacitsanzo, ku Roma, akapolo anafunika kugwila nchito m’migodi kwa zaka pafupi-fupi 30.
M’kupita kwa nthawi, ukapolo unapita patsogolo kwambili. Kucokela zaka za m’ma 1500 mpaka m’ma 1800, kutenga anthu ukapolo kuwacotsa mu Africa ndi kuyenda nawo ku America, anali amodzi mwa malonda opindulitsa kwambili padziko. Lipoti yocokela ku bungwe la UNESCO, inati: ‘Zikuoneka kuti anthu kuyambila pa 25 miliyoni mpaka 30 anawagwila ndi kuwagulitsa. Panali amuna, akazi, ndi ana.’ Anthu ofika m’ma sauzande akuti anafa pamene anali kuoloka nyanja ya Atlantic. Olaudah Equiano, kapolo amene anapulumuka, anati: “Zimene tinakunana nazo zinali zomvetsa cisoni kwambili cakuti zinali zovuta kuzifotokoza.”
N’zomvetsa cisoni kuti ukapolo ukupitilizabe ngakhale masiku ano. Malinga na Bungwe lochedwa International Labour Organization, anthu 21 miliyoni amuna, akazi, ndi ana, amagwilabe nchito monga akapolo. Iwo alibe ufulu ndipo amalandila malipilo ocepa, ngakhale kusalandila kumene. Masiku ano, akapolo amaseŵenza m’migodi, kugwila nchito yoŵaŵa koma yamalipilo ocepa, ndi kuumba nchelwa. Ena amacita uhule, ndipo ena amaseŵenza m’nyumba za anthu. Olo kuti ukapolo waconco ni wosaloleka, ukupitila-pitila patsogolo.
Anthu mamiliyoni akali mu ukapolo
KUMENYELA UFULU
Nkhanza zapangitsa akapolo ambili kumenyela ufulu. Mwacitsanzo, mu 73 B.C.E., Spartacus, wocita maseŵela omenyana ndi anthu kapena nyama, pamodzi ndi akapolo 100,000 anaukila boma la Aroma koma sanapambane. M’zaka za m’ma 1700, akapolo a m’dziko la Hispaniola, limene ndi cisumbu panyanja ya Caribbean, anaukila mabwana awo. Akapolo amenewo anacitilidwa nkhanza kwambili pogwila nchito m’minda ya nzimbe. Izi zinayambitsa nkhondo yapaciweni-weni imene inatenga zaka 13. Nkhondoyo inacititsa kuti dziko la Haiti lidziimile payokha mu 1804.
Kumasuka kwa Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo kumaposa kumasuka kulikonse kwa akapolo m’mbili ya anthu. Mtundu wonse wa Aisiraeli—mwina okwana 3 miliyoni—anamasulidwa mu ukapolo ku Iguputo. Zoona, iwo anafunikadi kumasuka. Baibo imafotokoza mmene umoyo wa Aisiraeli unalili ku Iguputo. Imati anali mu “ukapolo wa mtundu uliwonse umene anatha kuwagwilitsa nchito mwankhanza.” (Ekisodo 1:11-14) Farao wina anafika polamula kuti ana acimuna amene abadwa kwa Aisiraeli aziphedwa. Anacita izi pofuna kucepetsa ciŵelengelo cawo.—Ekisodo 1:8-22.
Kumasuka kwa Aisiraeli mu ukapolo wankhanza ku Iguputo kunali kwapadela, cifukwa Mulungu analoŵelelapo. Mulungu anauza Mose kuti: “Ndikudziŵa bwino zoŵaŵa zawo. Conco nditsikila kwa iwo kuti ndiwalanditse.” (Ekisodo 3:7, 8) Caka ndi caka, Ayuda kulikonse amacita cikondwelelo ca Pasika kuti akumbukile kumasulidwa kwawo.—Ekisodo 12:14.
KUMASUKILATU MU UKAPOLO
Baibo imati “Yehova Mulungu wathu si wopanda cilungamo,” ndipo imatitsimikizila kuti iye sanasinthe. (2 Mbiri 19:7; Malaki 3:6) Mulungu anatuma Yesu “kudzalalikila za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo . . . , kudzamasula opondelezedwa kuti akhale mfulu.” (Luka 4:18) Kodi izi zinatanthauza kumasuka mu ukapolo weni-weni? Iyai. Yesu anatumidwa kudzamasula anthu mu ukapolo wa ucimo na imfa. Pa nthawi ina iye anati: “Coonadi cidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Masiku anonso, coonadi cimene Yesu anaphunzitsa cikumasula anthu m’njila zambili.—Onani bokosi yakuti “Kumasuka mu Ukapolo wa Mtundu Wina.”
Zoonadi, Mulungu anathandiza Yosefe na Blessing kumasuka mu ukapolo m’njila zosiyana. Mungaŵelenge nkhani ya Yosefe yocititsa cidwi m’buku ya Genesis, macaputa 39 mpaka 41. Kumasuka kwa Blessing mu ukapolo nakonso ni kodabwitsa.
Blessing atacotsedwa m’dziko lina la ku Europe, anapita ku Spain. Kumeneko anakumana ndi Mboni za Yehova, ndipo anayamba kuphunzila Baibo. Iye anatsimikiza mtima kusintha umoyo wake. Conco, analoŵa nchito ndi kupempha abwana ake akale kuti amucepetseleko malipilo a pamwezi obweza nkhongole. Tsiku lina, abwana ake akale anam’tumila foni Blessing. Iwo anali kufuna kum’cotsela nkhongole yonse ndi kumupempha kuti awakhululukile. N’ciani cinacititsa zimenezi? Abwana ake nawonso anali atayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Blessing anati: “Coonadi cimakumasula m’njila zodabwitsa.”
Yehova Mulungu anamvela cisoni cifukwa ca masautso amene Aisiraeli anakumana nawo mu ukapolo ku Iguputo. Iye amamvelanso cimodzi-modzi akaona zinthu zopanda cilungamo masiku ano. N’zoona kuti, kuti ukapolo wa mtundu uliwonse uthe, padzafunikila masinthidwe aakulu pakati pa anthu. Koma Mulungu analonjeza kuti adzabweletsa masinthidwe aakulu amenewo. Baibo imati: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezela mogwilizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala cilungamo.”—2 Petulo 3:13
a Dzina lasinthidwa.