LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 2 tsa. 16
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi tili mu “masiku otsiliza”?
  • Kodi Mapeto A Dziko Ali Pafupi?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Tili mu “Masiku Otsiliza”?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 2 tsa. 16
Akulu ndi ana akusangalala ndi moyo m’Paradaiso

Amene adzapulumuka masiku otsiliza adzakhala m’paradaiso padziko lapansi

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi tili mu “masiku otsiliza”?

Mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Iyai

  • Kapena

Zimene Baibo imakamba

“Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Ulosi wa m’Baibo komanso zimene zicitika masiku ano, zionetsa kuti tili mu “masiku otsiliza.”

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Cizindikilo ca masiku otsiliza cidzakhala nkhondo, njala, zivomezi, na kuwanda kwa matenda akupha.—Mateyu 24:3, 7; Luka 21:11.

  • M’masiku otsiliza, anthu adzavutika cifukwa ca makhalidwe oipa ndi kusakonda zinthu zauzimu.—2 Timoteyo 3:2-5.

Kodi anthu ayembekezela ciani kutsogolo?

Anthu ena amakhulupilila kuti . . . masiku otsiliza adzatha pamene dziko lapansi ndi anthu onse zidzawonongedwa. Koma ena amakhulupilila kuti zinthu zidzakhala bwino. Imwe muganiza bwanji?

Zimene Baibo imakamba

“Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” —Salimo 37:29.

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Masiku otsiliza adzatha pamene zoipa zonse zidzacotsewapo.—1 Yohane 2:17.

  • Dziko lapansi lidzasintha kukhala paradaiso.—Yesaya 35:1, 6.

Kuti mudziŵe zambili zokhudza “masiku otsiliza,” onani nkhani 9 m’buku iyi, Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, yofalitsidwa na Mboni za Yehova

Bukuli ipezekanso pa webusaiti ya www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani