NKHANI YA PACIKUTO | ANGELO KODI ALIKO ZOONA? CIFUKWA CAKE TIFUNA KUDZIŴA
Kodi Muli na Mngelo Wokutetezani?
Baibo siphunzitsa kuti munthu aliyense ali na mngelo amene amamuteteza. N’zoona kuti panthawi ina Yesu anati: “Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati [ophunzila a Khristu], cifukwa ndikukutsimikizilani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.” (Mateyu 18:10) Komabe, apa Yesu sanali kutanthauza kuti munthu aliyense ali na mngelo womuteteza, koma anali kungokamba kuti angelo amacita cidwi na wophunzila wake aliyense. Conco, alambili oona saika dala moyo wawo paciswe poganiza kuti angelo a Mulungu adzawateteza.
Kodi izi zitanthauza kuti angelo sathandiza anthu? Iyai. (Salimo 91:11) Anthu ena amakhulupilila kwambili kuti Mulungu amawateteza na kuwatsogolela kupitila mwa angelo. Kenneth, amene tam’chula m’nkhani yoyamba, nayenso amakhulupilila zimenezi. Koma sitingatsimikizile mfundo imeneyi, mwina akamba zoona. Nthawi zambili, a Mboni za Yehova amaona maumboni oonetsa kuti angelo amawathandiza pa nchito yawo yolalikila. Popeza angelo saoneka, sitingadziŵe kuti Mulungu amawaseŵenzetsa kufika pati pothandiza anthu pa zocitika zosiyana-siyana. Ngakhale n’conco, si kulakwa kuyamikila Wamphamvuyonse pa thandizo limene amapeleka.—Akolose 3:15; Yakobo 1:17, 18.