LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 5 tsa. 6
  • Kodi Angelo Oipa Alikodi?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Angelo Oipa Alikodi?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Nkhani Zofanana
  • Kudziŵa Bwino Za Angelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Zolengedwa Zauzimu Zimatikhudza Bwanji?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Zoona Zake Ponena za Angelo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Kodi Angelo Ndani Kwenikweni, Ndipo Amacita Ciyani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 5 tsa. 6
Angelo oipa, kapena kuti ziŵanda

NKHANI YA PACIKUTO | ANGELO KODI ALIKO ZOONA? CIFUKWA CAKE TIFUNA KUDZIŴA

Kodi Angelo Oipa Alikodi?

Inde, alikodi. Nanga anacokela kuti? Kumbukilani kuti Mulungu analenga angelo na mphatso ya ufulu wosankha. Mwamuna ndi mkazi woyamba, Adamu na Hava, atangolengedwa, mngelo wangwilo anaseŵenzetsa molakwa ufulu wake wosankha mwa kuyambitsa cipanduko padziko lapansi. Iye anacititsa Adamu na Hava kupandukila Mulungu. (Genesis 3:1-7; Chivumbulutso 12:9) Baibo sikamba dzina la mngelo ameneyo kapena udindo wake akalibe kupanduka. Koma atapanduka, Baibo imam’chula dzina lomuyenelela kuti Satana, kutanthauza “Wotsutsa,” komanso Mdyerekezi, kutanthauza “Woneneza.”—Mateyu 4:8-11.

N’zacisoni kuti kupandukila Mulungu kunapitiliza. M’nthawi ya Nowa, angelo ena osadziŵika ciŵelengelo, “anasiya malo awo okhala” m’banja la Mulungu kumwamba. Iwo anabwela padziko lapansi na kuvala matupi aumunthu kuti acite zaciwelewele. Izi zinali zosiyana ndi colinga cimene Mulungu anawalengela.—Yuda 6; Genesis 6:1-4; 1 Petulo 3:19, 20.

N’ciani cinacitikila angelo oipawo? Pamene Mulungu anabweletsa cigumula kuti ayeletse dziko lonse lapansi, iwo anavula matupi awo na kubwelela kumwamba. Koma Mulungu sanawalole kuti akhalenso ‘m’malo awo oyambilila.’ M’malo mwake, anawatsekela m’malo a “mdima [wauzimu] wandiweyani” ochedwa Tatalasi. (Yuda 6; 2 Petulo 2:4) Ziŵanda zimenezo zinagwilizana ndi Satana Mdyelekezi “wolamulila ziŵanda,” amene “amadzisandutsa mngelo wa kuwala.”—Mateyu 12:24; 2 Akorinto 11:14.

Baibo imaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu Waumesiya, umene ni boma la kumwamba, unayamba kulamulila mu 1914.a Ufumuwo utakhazikitsidwa, Satana ndi ziŵanda zake anathamangitsidwa kumwamba na kuponyedwa padziko lapansi. Zinthu zoipa komanso makhalidwe oipa amene akuculukila-culukila masiku ano, ni umboni wakuti iwo ni okwiya maningi.—Chivumbulutso 12:9-12.

Koma kuwonjezeleka kwa makhalidwe oipa na ciwawa kumatitsimikizila kuti mapeto a ulamulilo wawo woipa ali pafupi. Posacedwa, zolengedwa zauzimu za nkhanza zimenezo zidzacotsedwapo. Pambuyo pakuti Ufumu wa Mulungu walamulila zaka 1,000 padziko lapansi la paradaiso, angelo oipa amenewo adzapatsidwa kanthawi kocepa kuti ayese anthu komaliza. Potsilizila, adzawonongedwa kothelatu.—Mateyu 25:41; Chivumbulutso 20:1-3, 7-10.

a Kuti mudziŵe zambili za Ufumu wa Mulungu, onani nkhani 8 m’buku yakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse yofalitsidwa na Mboni za Yehova. Bukuli ipezekanso pa webusaiti ya www.jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani