LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 10 nkhani 96-105
  • Kodi Zolengedwa Zauzimu Zimatikhudza Bwanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Zolengedwa Zauzimu Zimatikhudza Bwanji?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ANGELO AMATILIMBIKITSA NDI KUTICHINJILIZA
  • ZOLENGEDWA ZAUZIMU ZIMENE ZILI ADANI ATHU
  • MMENE ZIŴANDA ZIMASOCELETSELA ANTHU
  • MMENE TINGAPEWELE MIZIMU YOIPA
  • Kudziŵa Bwino Za Angelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Angelo Ndani Kwenikweni, Ndipo Amacita Ciyani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Kukaniza Mizimu Yoipa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 10 nkhani 96-105

NKHANI 10

Kodi Zolengedwa Zauzimu Zimatikhudza Bwanji?

  • Kodi angelo amathandiza anthu?

  • Kodi mizimu yoipa imacita ciani kwa anthu?

  • Kodi tiyenela kuiopa?

1. N’cifukwa ninji tiyenela kuphunzila za angelo?

KUTI munthu mum’dziŵe bwino muyenela kudziŵanso banja lake. Mofananamo, kum’dziŵa bwino Yehova Mulungu kumaphatikizapo kudziŵa bwino banja lake la angelo. Baibo imacha angelo kuti ‘ana a Mulungu.’ (Yobu 38:7) Conco, kodi angelo ali ndi udindo wanji pa kukwanilitsidwa kwa colinga ca Mulungu? Kodi io akhala akucita mbali iliyonse m’mbili ya anthu? Kodi angelo amakhudza umoyo wanu? Ngati ni conco, amaukhudza bwanji?

2. Kodi angelo anakhalako bwanji? Ndipo aliko angati?

2 Baibo imachula angelo nthawi zambili-mbili. Kuti tidziŵe zambili za angelo, tiyeni tione malemba angapo amene amakamba za angelo. Kodi angelo anakhalako bwanji? Lemba la Akolose 1:16 limakamba kuti: “Mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” Conco, angelo onse anacita kulengedwa ndi Yehova Mulungu kupyolela mwa Mwana wake woyamba. Nanga angelo aliko angati? Baibo imaonetsa kuti Mulungu analenga angelo mamiliyoni ambili-mbili, ndipo onse ndi amphamvu.—Salimo 103:20.a

3. Kodi lemba la Yobu 38:4-7 limatiuza ciani za angelo?

3 Mau a Mulungu, Baibo, amatiuza kuti pamene dziko lapansi linakhazikitsidwa, “ana onse a Mulungu anayamba kufuula ndi cisangalalo.” (Yobu 38:4-7) Zimenezi zimaonetsa kuti angelo anakhalako kale kwambili anthu akalibe kulengedwa, ngakhale dziko lapansi likalibe kulengedwa. Lembali limaonetsanso kuti angelo nao amakhudzidwa mtima, cifukwa limakamba kuti “anafuula pamodzi mokondwela.” Onani kuti “ana onse a Mulungu anayamba kufuula ndi cisangalalo.” Panthawi imeneyo, angelo onse anali m’banja limodzi logwilizana pakutumikila Yehova Mulungu.

ANGELO AMATILIMBIKITSA NDI KUTICHINJILIZA

4. Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti angelo okhulupilika amakhala ndi cidwi pa umoyo wa anthu?

4 Kucokela cabe pamene angelo okhulupilika anaona kulengedwa kwa anthu, akhala akuonetsa cidwi ndi mmene banja la anthu likukulila ndi mmene colinga ca Mulungu cikukwanilitsidwila. (Miyambo 8:30, 31; 1 Petulo 1:11, 12) Komabe m’kupita kwa nthawi, angelo aona kuti anthu ambili aleka kutumikila Mlengi wao wacikondi. N’zosakaikitsa kuti angelo amamva cisoni kwambili poona zimenezi. Koma pamene munthu ngakhale mmodzi cabe wabwelela kwa Yehova, “kumakhala cisangalalo coculuka kwa angelo.” (Luka 15:10) Poona kuti angelo amasamala kwambili za umoyo wa anthu otumikila Mulungu, Yehova wakhala akuwagwilitsila nchito mobweleza-bweleza kudzapeleka cilimbikitso ndi chinjilizo kwa atumiki ake okhulupilika padziko lapansi. (Aheberi 1:7, 14) Tiyeni tioneko zitsanzo zina.

An angel protecting Daniel in the lions’ pit

“Mulungu wanga watumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango.”—Danieli 6:22.

5. Kodi m’Baibo muli zitsanzo ziti zoonetsa mmene angelo anathandizila anthu?

5 Angelo aŵili anathandiza munthu wolungama Loti ndi ana ake kuti apulumuke cionongeko ca mizinda iŵili ya Sodomu ndi Gomora, mwa kuwatsogolela kuti acoke kudela limenelo. (Genesis 19:15, 16) Patapita zaka zambili, mneneli Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango, koma sanavulazidwe kapena kuphedwa. Iye anati: “Mulungu wanga watumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango.” (Danieli 6:22) M’nthawi ya atumwi, mngelo anathandiza mtumwi Petulo kucoka m’ndende. (Machitidwe 12:6-11) Komanso, angelo anacilikiza Yesu kuciyambi kwa utumiki wake wa padziko lapansi. (Maliko 1:13) Ndipo kutatsala pang’ono kuti Yesu aphedwe, mngelo anaonekela kwa iye ndi “kumulimbikitsa.” (Luka 22:43) Zimenezi zinali zolimbikitsa kwambili kwa Yesu panthawi yofunika kwambili paumoyo wake.

6. (a) Kodi angelo amawachinjiliza bwanji anthu a Mulungu masiku ano? (b) Kodi tsopano tidzakambitsilana mafunso ati?

6 Masiku ano, angelo samaonekelanso kwa anthu a Mulungu padziko lapansi. Koma ngakhale kuti angelo a Mulungu amphamvuwo samaonekela kwa anthu ake, amawachinjilizabe, maka-maka ku ciliconse cimene cingawavulaze mwa kuuzimu. Baibo imakamba kuti: “Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulila onse oopa Mulungu, Ndipo amawapulumutsa.” (Salimo 34:7) N’cifukwa ciani mau amenewa ayenela kukhala otilimbikitsa kwambili ife? Cifukwa cakuti pali zolengedwa zauzimu zoopsa zimene zimafuna kutiononga. Kodi n’ziti zimenezi? Ndipo zinacokela kuti? Nanga zimayesa bwanji kutivulaza? Kuti tidziŵe, tiyeni tione nkhani ina imene inacitika kuciyambi kwa mbili ya anthu.

ZOLENGEDWA ZAUZIMU ZIMENE ZILI ADANI ATHU

7. Kodi Satana anakwanitsa kupandutsa anthu oculuka motani kwa Mulungu?

7 Monga tinaphunzilila m’Nkhani 3 ya m’buku lino, mngelo wina anakulitsa mtima wofuna kulamulila ena, conco anapandukila Mulungu. Pambuyo pake mngelo ameneyu anachedwa Satana Mdyelekezi. (Chivumbulutso 12:9) Pazaka pafupi-fupi 1,600 kucokela pamene Satana ananama Hava, iye anakwanitsa kupandutsanso anthu oculuka kwa Mulungu, kusiyapo ocepa cabe okhulupilika, monga Abele, Inoki ndi Nowa.—Aheberi 11:4, 5, 7.

8. (a) Kodi angelo ena anakhala bwanji ziŵanda? (b) Kodi ziŵanda zinacita ciani kuti zipulumuke Cigumula ca m’nthawi ya Nowa?

8 M’masiku a Nowa, angelo enanso anapandukila Yehova. Iwo anasiya malo ao m’banja la Mulungu la kumwamba. Anabwela padziko lapansi ndi kuvala matupi aumunthu. Cifukwa ciani? Pa Genesis 6:2 timaŵelenga kuti: “Ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Cotelo, anayamba kudzitengela okha akazi alionse amene anawasankha.” Koma Yehova Mulungu sanalekelele zimene angelowa anacita, kuti apitilize kuononga mtundu wa anthu. Mwai ici, Mulungu anabweletsa cigumula padziko lonse cimene cinaononga anthu onse oipa, koma atumiki ake okhulupilika anapulumuka. (Genesis 7:17, 23) Conco, angelo opanduka amenewo, kapena kuti ziŵanda, anakakamizika kuvula matupi ao aumunthu ndi kubwelela kumwamba monga zolengedwa zauzimu. Mwa kucita zimenezi, io anadziika okha kumbali ya Mdyelekezi, amene anakhala “wolamulila ziŵanda.”—Mateyu 9:34.

9. (a) Kodi n’ciani cinacitikila ziŵanda pamene zinabwelela kumwamba? (b) Kodi tsopano tidzakambitsilana ciani ponena za ziŵanda?

9 Pamene angelo osamvela aja anabwelela kumwamba, anakhala ana okanidwa, mofanana ndi wolamulila wao Satana. (2 Petulo 2:4) Ngakhale kuti tsopano sangakwanitse kuvalanso matupi aumunthu, io ali ndi mphamvu zocitila anthu zinthu zoipa kwambili. Ndipo kupitila mwa ziŵanda zimenezi, Satana “akusoceletsa dziko lonse lapansi.” (Chivumbulutso 12:9; 1 Yohane 5:19) Kodi amacita bwanji zimenezi? Kwakukulu-kulu, ziŵanda zimagwilitsila nchito njila zimene zimasoceletsa anthu. (2 Akorinto 2:11) Tiyeni tione zina mwa njila zimenezo.

MMENE ZIŴANDA ZIMASOCELETSELA ANTHU

10. Kodi kukhulupilila mizimu kumatanthauzanji?

10 Pofuna kusoceletsa anthu, ziŵanda zimagwilitsila nchito kukhulupilila mizimu. Kukhulupilila mizimu kumatanthauza kucita zinthu ndi ziŵanda, kaya mwacindunji kapena kupitila mwa munthu wina monga sing’anga. Baibo imaletsa kukhulupilila mizimu, ndipo imacenjeza kuti tiyenela kupewa ciliconse cokhudzana ndi zamizimu. (Agalatiya 5:19-21) Kukhulupilila mizimu ndiyo nyambo ya ziŵanda. Munthu woŵedza nsomba amagwilitsila nchito nyambo zosiyana-siyana kuti agwile nsomba za mitundu yosiyana-siyana. Mofananamo, mizimu yoipa nayonso imagwilitsila nchito mitundu yosiyana-siyana ya zamizimu kuti isoceletse anthu osiyana-siyana.

11. Kodi kuombeza n’ciani? Ndipo n’cifukwa ciani tiyenela kukupewa?

11 Mtundu wina wa nyambo imene ziŵanda zimagwilitsila nchito ndi kuombeza. Kodi kuombeza n’ciani? Ndiko kufuna kudziŵa za mtsogolo kapena cinthu cina cosadziŵika. Mitundu ina ya kuombeza ndiyo kumvetsela ku nsupa yamatsenga, kukhulupilila nyenyezi, kuona pagalasi lamatsenga, kuyang’ana mizela yapamanja, kukhulupilila maloto, kukhulupilila kulila kwa mbalame, ndi zina za conco. Ngakhale kuti anthu ambili amaganiza kuti kukhulupilila zamizimu kulibe vuto, Baibo imaonetsa kuti anthu olosela za mtsogolo amagwila nchito pamodzi ndi mizimu yoipa. Mwacitsanzo, lemba la Machitidwe 16:16-18 limakamba za “ciŵanda colosela zamtsogolo” cimene cinathandiza mtsikana wina “kumacita zolosela.” Koma mphamvu zimenezo zinatha mwa mtsikanayo pamene anam’cotsa ciŵanda cimeneco.

1) An astrology chart; 2) A palm-reader examines a woman’s hand; 3) A man using tarot cards; 4) A crystal ball

Ziŵanda zimaseŵenzetsa njila zosiyana-siyana pofuna kusoceletsa anthu

12. N’cifukwa ciani tiyenela kupewelatu kukamba ndi anthu akufa?

12 Njila ina imene ziŵanda zimasoceletsa nayo anthu ndiyo kuonekela monga munthu amene anafa. Kaŵili-kaŵili anthu amene anafeledwa amauzidwa mabodza ponena za munthu amene anafa. Anthu ena amakhulupilila kuti amavutitsidwa ndi anthu amene anafa. Nthawi zina amati anaona munthu amene anafa kapena kumva mau ake. Cifukwa ca zimenezi ambili amakhulupilila kuti m’ceni-ceni anthu akufa amapitiliza kukhalabe ndi moyo, ndi kuti akhoza kuwathandiza kapena kuwavulaza. Koma ‘cithandizo’ ciliconse cimene cingakhalepo n’cacinyengo komanso covulaza. Cifukwa ninji? Cifukwa ziŵanda zimakhoza kutengela mau a munthu amene anafa, ndipo zimatha kuuza munthu wokamba ndi mizimu zinthu zina ponena za munthu amene anafa. (1 Samueli 28:3-19) Ndiponso, monga tinaonela mu Nkhani 6, akufa sakhalanso ndi moyo. (Salimo 115:17) Mwa ici, munthu aliyense amene ‘afunsila kwa anthu akufa’ amakhala atasoceletsedwa ndi mizimu yoipa, ndipo kucita zimenezo n’kosemphana ndi cifunilo ca Mulungu. (Deuteronomo 18:10, 11; Yesaya 8:19) Conco, khalani wosamala kuti muzipewa nyambo yoopsa imeneyi imene ziŵanda zimagwilitsila nchito.

13. Kodi anthu ambili amene kale anali kuopa ziŵanda akwanitsa kucita ciani?

13 Mizimu yoipa siimangosoceletsa anthu, komanso imawaopseza. Satana ndi ziŵanda zake amadziŵa kuti angotsala ndi “kanthawi kocepa” kuti acotsedwepo. Pa cifukwa cimeneci, io tsopano akalipilatu kuposa ndi kale lonse. (Chivumbulutso 12:12, 17) Ngakhale ndi conco, anthu ambili amene anali m’mantha oopa mizimu yoipa tsopano anamasuka. Kodi anamasuka bwanji? Nanga munthu angacite bwanji ngati amakhulupilila zamizimu?

MMENE TINGAPEWELE MIZIMU YOIPA

14. Potengela citsanzo ca Akristu oyambilila a ku Efeso, kodi tingacitenji kuti timasuke ku mizimu yoipa?

14 Baibo imatiuza mmene tingapewele mizimu yoipa ndi mmene tingamasukile ku zamizimu. Ganizilani citsanzo ca Akristu oyambilila mu mzinda wa Efeso. Ena anali kukhulupilila zamizimu akalibe kukhala Akristu. Koma kodi anacita ciani pamene anafuna kuleka zamizimu? Baibo imakamba kuti: “Ambili ndithu amene anali kucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.” (Machitidwe 19:19) Mwa kuononga mabuku ao a zamatsenga, Akristu atsopano amenewo anapeleka citsanzo cabwino kwa amene amafuna kupewa mizimu yoipa masiku ano. Anthu amene amafuna kutumikila Yehova afunikila kuononga cinthu ciliconse cokhudza zamizimu. Zinthu zimenezo zingaphatikizepo mabuku, magazini, mafilimu, zithunzi-thunzi zomatika, ndi nyimbo zimene zimalimbikitsa zamizimu ndi kuzionetsa kukhala zabwino ndi zokondweletsa. Zingaphatikizeponso zithumwa, kapena zinthu zina zovala kuti ziteteze munthu ku zinthu zoipa—1 Akorinto 10:21.

15. Kodi tifunikila kucitanji kuti tidziteteze ku mizimu yoipa?

15 Patapita zaka zingapo kucokela pamene Akristu a ku Efeso anaononga mabuku ao a zamatsenga, mtumwi Paulo anawalembela kuti, tikulimbana “ndi makamu a mizimu yoipa.” (Aefeso 6:12) Ziŵanda sizinaleke kulimbana nao. Zinali kuyesa-yesabe kuti ziwasoceletse. Nanga cinanso n’ciani cimene Akristuwo anayenela kucita kuti adziteteze? Paulo anawauza kuti: “Koposa zonse, nyamulani cishango cacikulu cacikhulupililo, cimene mudzathe kuzimitsila mivi yonse yoyaka moto ya woipayo [Satana].” (Aefeso 6:16) Conco, cishango cathu ca cikhulupililo ciyenela kukhala colimba, kuti tikwanitse kudziteteza bwino ku mizimu yoipa.—Mateyu 17:20.

16. Kodi tiyenela kucitanji kuti cikhulupililo cathu cilimbe?

16 Nanga tingacite ciani kuti tilimbitse cikhulupililo cathu? Tiyenela kuphunzila Baibo. Kuti nyumba ilimbe imadalila maziko ake olimba. Mofananamo, kuti cikhulupililo cathu cilimbe cimadalila maziko ake, amene ndi cidziŵitso colongosoka ca Mau a Mulungu, Baibo. Ngati tiŵelenga Baibo tsiku lililonse, cikhulupililo cathu cidzakhala colimba kwambili. Mofanana ndi nyumba yolimba, cikhulupililo colimba cidzatichinjiliza ku mizimu yoipa.—1 Yohane 5:5.

17. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tipewe mizimu yoipa?

17 Kodi n’cianinso cimene Akristu a ku Efeso anafunikila kucita? Iwo anafunikila citetezo coonjezeleka cifukwa anali kukhala mu mzinda umene anthu ambili anali kukhulupilila zamizimu. Conco, Paulo anawauza kuti: “Muzipemphela pa cocitika ciliconse mu mzimu, mwa mtundu uliwonse wa pemphelo ndi pembedzelo.” (Aefeso 6:18) Popeza kuti ifenso tikukhala m’dziko limene anthu ambili amakhulupilila zamizimu, tiyenela kucita khama kupemphela kwa Yehova kuti azititeteza ku mizimu yoipa. Tiyenela kumachula ndithu dzina la Yehova m’mapemphelo athu. (Miyambo 18:10). Conco, tipitilize kupemphela kwa Mulungu kuti ‘atilanditse kwa woipayo,’ Satana Mdyelekezi. (Mateyu 6:13) Inde, Yehova adzayankha mapemphelo ocokela pansi pamtima amenewo.—Salimo 145:19.

18, 19. (a) Kodi n’cifukwa ciani tingakhale otsimikiza kuti tidzapambana pa kulimbana ndi mizimu yoipa? (b) Nanga ndi funso liti limene lidzayankhidwa m’nkhani yotsatila?

18 Ngakhale kuti mizimu yoipa ndi yoopsa, ngati tiyandikila kwa Mulungu mwa kucita cifunilo cake, ndi kutsutsa Mdyelekezi, sitidzaiopa. (Yakobo 4:7, 8) Mizimu yoipa ili ndi mphamvu zocepa poyelekezela ndi Mulungu. M’masiku a Nowa Mulungu anailanga mizimuyo, ndipo mtsogolo adzaionongelatu. (Yuda 6) Kumbukilaninso kuti angelo a Yehova amphamvu amatichinjiliza. (2 Mafumu 6:15-17) Angelo olungama amafuna kwambili kuti tiziipewa mizimu yoipa. Zili ngati kuti io amaticemelela kuti tilimbikile. Conco, tiyeni tikangamilebe kwa Yehova ndi banja lake la angelo okhulupilika. Tizipewanso zamizimu za mtundu ulionse, ndiponso nthawi zonse tizigwilitsila nchito uphungu wa m’Mau a Mulungu. (1 Petulo 5:6, 7; 2 Petulo 2:9) Tikacita zimenezo, tidzakhala otsimikiza kuti tidzapambana pankhondo yolimbana ndi mizimu yoipa.

19 N’cifukwa ciani Mulungu walola kuti mizimu yoipa izivutitsa anthu conco, ndi kuti anthu azivutikanso ndi zinthu zoipa? Funso limeneli lidzayankhidwa m’nkhani yotsatila.

a Ponena za angelo olungama, lemba la Chivumbulutso 5:11 limakamba kuti: “Ciŵelengelo cao cinali miyanda kuculukitsa ndi miyanda ndiponso masauzande kuculukitsa ndi masauzande,” kapena kuti “10,000 kuculukitsa ndi ma 10,000.” (Mau apansi) Conco, Baibo imaonetsa kuti Mulungu analenga angelo mamiliyoni ambili-mbili.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Angelo okhulupilika amathandiza anthu amene amatumikila Yehova.—Aheberi 1:7, 14.

  • Satana ndi ziŵanda zake amasoceletsa anthu ndi kuwapatutsa kwa Mulungu.—Chivumbulutso 12:9.

  • Ngati mucita cifunilo ca Mulungu ndi kutsutsa Satana Mdyelekezi, adzakuthaŵani.—Yakobo 4:7, 8.

MMENE TINGAPEWELE MIZIMU YOIPA

  • Onongani zinthu zonse zokhudzana ndi zamizimu

  • Muziphunzila Baibo

  • Muzipemphela kwa Mulungu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani