Kodi Yesu Anali Kuoneka Bwanji Kweni-kweni?
Palibe munthu amene ali na pikica yeni-yeni ya Yesu. Iye sanakopeseko sinapu kapena kudiloing’iwa penapake. Komabe, kwa zaka zambili wakhala akuonekela m’mapikica a anthu ambili ojambula zithunzi.
Ojambula zithunziwo sanali kudziŵa mmene Yesu anali kuonekela maka-maka. Koma anali kujambula Yesu malinga na cikhalidwe ca panthawiyo, zikhulupililo za cipembedzo, na zofuna za anthu amene ajambulitsa zithunzi zimenezo. Ngakhale n’conco, zithunzi zawo zingacititse anthu kulemekeza Yesu na ziphunzitso zake, kapenanso kumusuliza.
Ojambula zithunzi ena amaonetsa Yesu ali wofooka thupi, wa tsitsi yaitali, na ndevu zing’ono kwambili kapena wa nkhope yacisoni. M’mapikica ena, Yesu amaoneka ngati mngelo, kumutu kwake kuli nkhata yaciyelo, komanso wokonda kukhala yekha. Kodi mapikica amenewa amaonetsa Yesu molondola? Kodi tingadziŵe bwanji zenizeni? Njila imodzi ni kufufuza mau ena a m’Baibo amene angatiunikileko mmene anali kuonekela. Mau amenewa angatithandizenso kumuona moyenelela.
“MUNANDIKONZELA THUPI”
Zioneka kuti Yesu anakamba mau amenewa m’pemphelo pa nthawi ya ubatizo wake. (Aheberi 10:5; Mateyu 3:13-17) Kodi thupi limenelo linali kuoneka bwanji? Kukali zaka 30, mngelo Gabirieli anauzilatu Mariya kuti: “Udzakhala ndi pakati ndipo udzabeleka mwana wamwamuna, . . Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:31, 35) Conco, Yesu anali munthu wangwilo, monga mmene Adamu analili atalengedwa. (Luka 3:38; 1 Akorinto 15:45) Yesu ayenela kuti anali na thupi loumbika bwino, ndipo anali kulinganako na Mariya, amayi wake waciyuda.
Yesu anali kusunga ndevu, potsatila cikhalidwe ca Ayuda mosiyana ndi Aroma. Ndevu zimenezo zinali kuonetsa ulemu; sizinali zazitali ndi zosasamalika ayi. Mosakaikila, Yesu anali kusamalila ndevu zake na kuzidulila bwino. Anali kudulilanso bwino tsitsi lake. Anthu okhawo amene anali kudzakhala Anaziri, monga Samisoni, ndiwo amene sanali kugela tsitsi lawo.—Numeri 6:5; Oweruza 13:5.
Kwa zaka 30 Yesu anali kugwila nchito ya ukalipentala, ndipo sanali kuseŵenzetsa zitsulo zamakono. (Maliko 6:3) Conco, ayenela kuti anali wamphamvu. Kuciyambi kwa utumiki wake, yekha anakwanitsa ‘kuthamangitsa onse amene anali na nkhosa na ng’ombe ndipo anawatulutsa m’kacisimo. Anakhuthula makobidi a osintha ndalama na kugubuduza matebulo awo.’ (Yohane 2:14-17) Munthu wolimba ndi wamphamvu ndiye angakwanitse kucita zimenezo. Yesu anaseŵenzetsa thupi limene Mulungu anamukonzela pokwanilitsa nchito imene iye anam’patsa. Yesu anati: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.” (Luka 4:43) Anafunika kukhala na mphamvu zapadela kuti akwanitse kuyenda na mendo m’madela onse a ku Palesitina kukalalikila uthenga umenewu.
“BWELANI KWA INE, . . . NDIPO NDIDZAKUTSITSIMUTSANI”
Nkhope ya ubwenzi ya Yesu na khalidwe lake labwino, zinacititsa ciitano cake kukhala cokopa makamaka kwa anthu “ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa.” (Mateyu 11:28-30) Cifukwa cakuti anali waubwenzi ndi wokoma mtima kwa onse, anakwanilitsa lonjezo lake lotsitsimula anthu ofunitsitsa kuphunzila kwa iye. Ngakhale acicepele anali kufuna kukhala pafupi na Yesu, cifukwa Baibo imati: “Anatenga anawo m’manja mwake.”—Maliko 10:13-16.
Olo kuti Yesu anavutika kwambili akalibe kufa, sanali kukhala wacisoni kwambili. Mwacitsanzo, iye anathandiza pa phwando la cikwati ku Kana mwa kusandutsa madzi kukhala vinyo wabwino. (Yohane 2:1-11) Pa zocitika zina, iye anaphunzitsa mfundo zosaiŵalika.—Mateyu 9:9-13; Yohane 12:1-8.
Koposa zonse, ulaliki wa Yesu unapeleka ciyembekezo ca moyo wosatha kwa anthu omumvetsela. (Yohane 11:25, 26; 17:3) Pamene ophunzila ake 70 anabweletsa lipoti la mmene nchito yolalikila inayendela, iye “anakondwela kwambili” na kufuula kuti: “Kondwelani cifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.”—Luka 10:20, 21.
“INU MUSAKHALE OTELO”
Atsogoleli azipembedzo a m’nthawi ya Yesu anakonza njila zakuti anthu aziwalemekeza na kuti azionetsa ulamulilo wawo. (Numeri 15:38-40; Mateyu 23:5-7) Koma mosiyana na iwo, Yesu analangiza atumwi ake kuti ‘asamacite ulamulilo pa’ ena. (Luka 22:25, 26) Ndipo anawacenjeza kuti: “Cenjelani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ndi kupatsidwa moni m’misika.”—Maliko 12:38.
Mosiyana na iwo, Yesu sanali kudzisiyanitsa na gulu la anthu, cakuti nthawi zina anthu sanali kumuzindikila. (Yohane 7:10, 11) Iye sanali kuoneka mosiyanako ngakhale pakati pa atumwi ake 11 okhulupilika. Yudasi amene anam’peleka anacita kum’psompsona monga “cizindikilo cimene anagwilizana,” kuti gulu la anthu limuzindikile Yesu.—Maliko 14:44, 45.
Conco, olo kuti sitidziŵa zambili, n’zoonekelatu kuti Yesu sanali kuoneka monga mmene anthu ambili amamuonetsela. Komabe, cofunika kwambili si mmene anali kuonekela kweni-kweni, koma mmene timudziŵila masiku ano.
“KWATSALA KANTHAWI PANG’ONO NDIPO DZIKO SILIDZANDIONANSO”
Pa tsiku limene Yesu anakamba mawu amenewa, anamwalila na kuikidwa m’manda. (Yohane 14:19) Iye ‘anapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.’ (Mateyu 20:28) Pa tsiku lacitatu, Mulungu anamuukitsa “monga mzimu” “ndi kumulola kuonekela” kwa ena mwa ophunzila ake. (1 Petulo 3:18; Machitidwe 10:40) Kodi Yesu anali kuoneka bwanji ataonekela kwa ophunzila ake? Mwacionekele anali kuoneka mosiyana ndi poyamba, cifukwa ngakhale anzake apamtima sanamuzindikile mwamsanga. Mariya Mmagadala atamuona, anaganiza kuti anali wosamalila munda; ndipo ophunzila ake aŵili amene anali kuyenda ku Emau, anaganiza kuti ni mlendo.—Luka 24:13-18; Yohane 20:1,14, 15.
Kodi tiyenela kumuona bwanji Yesu masiku ano? Patapita zaka zoposa 60 Yesu atafa, Yohane amene Yesu anali kumukonda anaona masomphenya a Yesu. Yohane sanaone munthu wakufa pa mtanda. Koma anaona “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,” Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, amene adzagonjetsa adani a Mulungu posacedwa, amene ni viŵanda na anthu oipa, ndipo adzabweletsa madalitso osatha kwa anthu.—Chivumbulutso 19:16; 21:3, 4.